Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndinu ‘Mdindo wa Kukoma Mtima kwa M’chisomo cha Mulungu’?

Kodi Ndinu ‘Mdindo wa Kukoma Mtima kwa M’chisomo cha Mulungu’?

Kodi Ndinu ‘Mdindo wa Kukoma Mtima kwa M’chisomo cha Mulungu’?

“Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.”​—AROMA 12:10.

1. Kodi Mawu a Mulungu amatitsimikizira chiyani?

MAWU A MULUNGU amatitsimikizira mobwerezabwereza kuti Yehova adzatithandiza ngati takhumudwa kapena kusweka mtima. Mwachitsanzo, tamverani mawu otonthoza awa: “Yehova agwiriziza onse akugwa, nawongoletsa onse owerama.” “Achiritsa osweka mtima, namanga mabala awo.” (Sal. 145:14; 147:3) Ndiponso, Atate wathu wakumwamba mwiniwakeyo amati: “Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.”​—Yes. 41:13.

2. Kodi Yehova amathandiza bwanji atumiki ake?

2 Koma kodi Yehova, amene amakhala kumwamba kosaoneka, ‘angatigwire bwanji dzanja lathu’? Kodi amatha bwanji ‘kutiwongola ngati tawerama’ chifukwa cha mavuto? Yehova Mulungu amatithandiza m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, iye amapatsa anthu ake “mphamvu yoposa yachibadwa” pogwiritsa ntchito mzimu wake woyera. (2 Akor. 4:7; Yoh. 14:16, 17) Atumiki a Mulungu amalimbikitsidwanso ndi Mawu a Mulungu, Baibulo, omwe ndi amphamvu. (Aheb. 4:12) Kodi pali njira inanso imene Yehova amatilimbikitsira? Yankho la funso limeneli limapezeka m’kalata yoyamba ya Petulo.

‘Kukoma Mtima kwa M’chisomo cha Mulungu Kumasonyezedwa M’njira Zosiyanasiyana’

3. (a) Kodi mtumwi Petulo ananena chiyani za mayesero? (b) Kodi mbali yomaliza ya kalata yoyamba ya Petulo ikufotokoza chiyani?

3 Polembera okhulupirira anzake odzozedwa ndi mzimu, mtumwi Petulo ananena kuti iwo anali ndi chifukwa chabwino chosangalalira popeza anali kudikirira mphoto yaikulu. Kenako iye anati: “Ngakhale kuti pakali pano ndi kwa kanthawi, ngati ziyenera kutero, chifukwa mayesero amitundumitundu akukuchititsani chisoni.” (1 Pet. 1:1-6) M’chinenero choyambirira, Petulo palembali anagwiritsa ntchito mawu akuti “zosiyanasiyana” omwe atchulidwa m’ndime yachiwiri. Zimenezi zikusonyeza kuti mayesero alipo osiyanasiyana. Koma Petulo sanaimire pamenepo, kusiya abale ake m’malere popanda kudziwa ngati angathe kupirira mayesero osiyanasiyanawo. M’malo mwake, iye ananena kuti Akhristu sayenera kukayikira kuti Yehova adzawathandiza kupirira chiyeso chilichonse chimene angakumane nacho, kaya chikhale chamtundu wotani. Mawu otsimikizira amenewa ali m’mbali yomaliza ya kalata ya Petulo, kumene mtumwiyu akufotokoza nkhani zokhudza “mapeto a zinthu zonse.”​—1 Pet. 4:7.

4. N’chifukwa chiyani mawu a pa 1 Petulo 4:10 ndi otonthoza kwa ife?

4 Petulo anati: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana wina ndi mnzake monga adindo abwino a kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu kumene wakusonyeza m’njira zosiyanasiyana.” (1 Pet. 4:10) Apanso Petulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “zosiyanasiyana.” M’mawu ena, iye anati, ‘Mayesero amakhala amitundumitundu, ndipo kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu kumakhalanso kwamitundumitundu.’ N’chifukwa chiyani mfundo imeneyi ndi yotonthoza? Chifukwa chakuti ikusonyeza kuti kaya mayesero athu akhale amtundu wotani, Mulungu nthawi zonse adzasonyeza kukoma mtima kwa m’chisomo chake mogwirizana ndi mtundu wa mayeserowo. Koma kodi mwaona m’mawu a Petulo mmene timalandirira kukoma mtima kwa m’chisomo cha Yehova? Timalandira kukoma mtima kwa m’chisomo chake kudzera mwa Akhristu anzathu.

‘Kutumikirana Wina ndi Mnzake’

5. (a) Kodi Mkhristu aliyense ayenera kuchita chiyani? (b) Kodi ndi mafunso ati amene tifunikira kuyankha?

5 Polankhula ndi anthu onse a mumpingo wachikhristu, Petulo anati: “Koposa zonse, khalani okondana kwambiri wina ndi mnzake.” Kenako anati: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito potumikirana wina ndi mnzake.” (1 Pet. 4:8, 10) Choncho, aliyense mumpingo ayenera kulimbikitsa Akhristu anzake. Yehova watiikiza chinthu chamtengo wapatali ndipo tili ndi udindo wochigawira kwa ena. Koma kodi chinthu chimene taikizidwacho n’chiyani? Petulo ananena kuti ndi “mphatso.” Kodi mphatso imeneyi n’chiyani? Ndipo kodi ‘tingaigwiritse ntchito bwanji potumikirana wina ndi mnzake’?

6. Kodi ndi mphatso zina ziti zimene Akhristu apatsidwa?

6 Mawu a Mulungu amati: “Mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro zimachokera kumwamba.” (Yak. 1:17) N’zoona, mphatso zonse zimene Yehova amapatsa anthu ake zimasonyeza kukoma mtima kwa m’chisomo chake. Mphatso yapadera imene Yehova amatipatsa ndi mzimu woyera. Mphatso imeneyi imatithandiza kuti tikhale ndi makhalidwe abwino monga chikondi, ubwino ndi kufatsa. Ndipo makhalidwe amenewa amatilimbikitsa kukonda kwambiri okhulupirira anzathu ndi kuwathandiza. Komanso nzeru yeniyeni ndiponso kudziwa zinthu ndi zina mwa mphatso zabwino zimene timalandira mothandizidwa ndi mzimu woyera. (1 Akor. 2:10-16; Agal. 5:22, 23) Ndipo tingati mphamvu zathu, nzeru ndi luso lathu lonse ndi mphatso zimene tiyenera kugwiritsa ntchito potamanda ndi kulemekeza Atate wathu wakumwamba. Tili ndi udindo umene Mulungu watipatsa wogwiritsa ntchito nzeru ndi makhalidwe athu ngati njira yosonyezera kukoma mtima kwa chisomo cha Mulungu kwa okhulupirira anzathu.

Kodi Mphatso Zathu Tingazigwiritse Ntchito Bwanji Potumikira?

7. (a) Kodi mawu akuti “molingana” akusonyeza chiyani? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso otani, ndipo chifukwa chiyani?

7 Ponena za mphatso zimene talandira, Petulo anati: “Molingana ndi mphatso imene aliyense walandira, igwiritseni ntchito.” Mawu akuti “molingana” akusonyeza kuti mtundu komanso kukula kwa makhalidwe ndi luso zingasiyane. Ngakhale zili choncho, aliyense akuuzidwa ‘kugwiritsa ntchito [mphatso iliyonse imene walandira] potumikirana wina ndi mnzake.’ Ndipotu, mawu akuti “igwiritseni ntchito . . . monga adindo abwino” ndi lamulo. Choncho, tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimagwiritsadi ntchito mphatso zimene ndapatsidwa polimbikitsa okhulupirira anzanga?’ (Yerekezerani ndi 1 Timoteyo 5:9, 10.) ‘Kapena kodi ndimagwiritsa ntchito luso limene ndalandira kwa Yehova pofuna kudzipindulitsa, mwina kuti ndilemere kapena kuti anthu azindiona kuti ndine wapamwamba?’ (1 Akor. 4:7) Ngati timagwiritsa ntchito mphatso zathu “potumikirana wina ndi mnzake,” Yehova amasangalala.​—Miy. 19:17; werengani Aheberi 13:16.

8, 9. (a) Kodi njira zina zimene Akhristu padziko lonse amatumikirira okhulupirira anzawo n’zotani? (b) Kodi abale ndi alongo mumpingo wanu amathandizana bwanji?

8 Mawu a Mulungu amatchula njira zosiyanasiyana zimene Akhristu a m’nthawi ya atumwi anatumikirana wina ndi mnzake. (Werengani Aroma 15:25, 26; 2 Timoteyo 1:16-18.) Masiku anonso, Akhristu oona amatsatira ndi mtima wonse lamulo lakuti agwiritse ntchito mphatso zawo potumikira okhulupirira anzawo. Taonani njira zina zimene akuchitira zimenezi.

9 Mwezi uliwonse, abale ambiri amathera maola ochuluka kukonzekera nkhani zokakamba ku misonkhano. Iwo akamakamba mfundo zauzimu zamtengo wapatali zimene anapeza pophunzira Baibulo, mawu awo anzeru amalimbikitsa onse mumpingo kuti apirire. (1 Tim. 5:17) Abale ndi alongo ambiri amadziwika ndi chikondi ndiponso chifundo chimene amasonyeza kwa okhulupirira anzawo. (Aroma 12:15) Ena amapita kawirikawiri kukaona anthu amene apanikizika ndi mavuto ndipo amapemphera nawo. (1 Ates. 5:14) Ena amapeza nthawi yolemba makalata olimbikitsa Akhristu anzawo amene akulimbana ndi mayesero. Komanso ena amathandiza anthu amene sangakwanitse kufika okha pamisonkhano yampingo pokawatenga n’kupita nawo. Mboni zambiri zimagwira nawo ntchito yothandiza pakachitika tsoka, ndipo zimathandiza okhulupirira anzawo kumanganso nyumba zawo zimene zawonongedwa ndi tsokalo. Chikondi chenicheni ndi thandizo limene abale ndi alongo achifundo amenewa amapereka, zimasonyeza ‘kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu kumene amakusonyeza m’njira zosiyanasiyana.’​—Werengani 1 Petulo 4:11.

Kodi Chofunika Kwambiri N’chiyani?

10. (a) Kodi Paulo anazindikira mbali ziwiri ziti zokhudza utumiki wake kwa Mulungu? (b) Kodi ife tingamutsanzire bwanji Paulo?

10 Atumiki a Mulungu sanangopatsidwa mphatso yotumikira nayo okhulupirira anzawo, komanso anapatsidwa uthenga woti auze anthu ena. Mtumwi Paulo anazindikira mbali ziwirizi za utumiki wake kwa Yehova. Iye analembera mpingo wa ku Efeso za kukhala kwake “mdindo wa kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu” kuti awathandize. (Aef. 3:2) Komanso ananena kuti: “Tavomerezedwa ndi Mulungu kukhala oyenera kuikizidwa uthenga wabwino.” (1 Ates. 2:4) Monga Paulo, ifenso timazindikira kuti tinapatsidwa ntchito yotumikira ngati alaliki a Ufumu wa Mulungu. Mwa kukhala achangu m’ntchito yolalikira, timayesetsa kutsanzira Paulo yemwe sankatopa polengeza uthenga wabwino. (Mac. 20:20, 21; 1 Akor. 11:1) Timadziwa kuti kulalikira uthenga wa Ufumu kungapulumutse miyoyo ya anthu. Komanso timayesetsa kutsanzira Paulo mwa kufunafuna mipata ‘yogawira mphatso inayake yauzimu’ kwa okhulupirira anzathu.​—Werengani Aroma 1:11, 12; 10:13-15.

11. Kodi ntchito yolalikira ndi yolimbikitsa abale athu tiyenera kuiona bwanji?

11 Kodi pa ntchito zachikhristu ziwirizi, yofunika kwambiri ndi iti? Kufunsa funso ngati limeneli kungafanane ndi kufunsa za mbalame kuti, Kodi pa mapiko ake awiri, lofunika kwambiri ndi liti? Yankho lake ndi lodziwikiratu. Mbalame imafunika mapiko onse awiri kuti izitha kuuluka bwino. Mofanana ndi mbalame, ifenso timafunikira mbali zonse ziwiri za utumiki wathu kwa Mulungu kuti tikhale ndi zonse zofunikira monga Akhristu. Ndiye m’malo moona ntchito yolalikira uthenga wabwino ndi yolimbikitsa okhulupirira anzathu ngati zinthu ziwiri zosagwirizana, timaona ntchitozo ngati mmene Petulo ndi Paulo anazionera. Iwo ankaona kuti zonse ndi zofunika ndipo ndi zogwirizana. Chifukwa chiyani?

12. Kodi timakhala bwanji ngati chida m’manja mwa Yehova?

12 Monga alaliki, tingagwiritse ntchito luso lililonse limene tingakhale nalo kuti tifike pamtima anthu ena ndi uthenga wolimbikitsa wa Ufumu wa Mulungu. Mwa kuchita zimenezi, timafuna kuwathandiza kukhala ophunzira a Khristu. Komabe, tingagwiritsenso ntchito luso lililonse ndi mphatso zina zimene tingakhale nazo kuti tilimbikitse okhulupirira anzathu. Tingatero powauza mawu olimbikitsa komanso kuwathandiza. Zimenezi zimasonyeza kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu. (Miy. 3:27; 12:25) Tikamatero, timafuna kuwathandiza kukhalabe ophunzira a Khristu. Tikamalalikira anthu ndi ‘kutumikirana wina ndi mnzake,’ timakhala ndi mwayi wamtengo wapatali wogwira ntchito ngati chida m’manja mwa Yehova.​—Agal. 6:10.

“Khalani ndi Chikondi Chenicheni kwa Wina ndi Mnzake”

13. Kodi chingachitike ndi chiyani ngati titalephera ‘kutumikirana wina ndi mnzake’?

13 Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Zoonadi, kukonda abale athu kumatilimbikitsa kuwatumikira ndi mtima wonse monga adindo a kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu. Timazindikira kuti ngati Satana atatilepheretsa ‘kutumikirana wina ndi mnzake,’ ndiye kuti mgwirizano wathu ungasokonezeke. (Akol. 3:14) Ndipo kusagwirizanako kungachititse kuti tisakhale achangu m’ntchito yolalikira. Satana amadziwa bwino kuti amangofunika kuthyola phiko limodzi lokha kuti atilepheretse kuuluka.

14. Kodi ndani amapindula ‘tikamatumikirana wina ndi mnzake’? Perekani chitsanzo.

14 ‘Tikamatumikirana wina ndi mnzake’ sitimangopindulitsa okhawo amene amalandira kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu. Ifenso timapindula. (Miy. 11:25) Taganizirani chitsanzo cha Ryan ndi mkazi wake Roni, ku Illinois, U.S.A. Atamva zakuti mphepo ya mkuntho ya Katrina yawononga nyumba zambiri za a Mboni anzawo, chikondi chaubale chinawapangitsa kusiya ntchito ndi nyumba yawo. Ndipo anagula kalavani ndi kuikonza bwinobwino kuti azikagonamo, n’kuyamba ulendo wa makilomita 1,400 kupita Louisiana. Anakhala kumeneko kupitirira chaka chimodzi, ndipo anathera nthawi yawo, mphamvu ndi chuma chawo kuti athandize abale awo. Ryan yemwe ali ndi zaka 29 anati: “Kugwira nawo ntchito yothandiza anthu imeneyi, kunandithandiza kuyandikira Mulungu. Ndinaona mmene Yehova amasamalira anthu ake.” Iye ananenanso kuti: “Kugwira ntchito limodzi ndi abale achikulire kunandiphunzitsa zambiri za mmene tingasamalirire abale athu. Ndinaphunziranso kuti pali zambiri zimene achinyamatafe tingachite m’gulu la Yehova.” Mkazi wake Roni, yemwe ali ndi zaka 25 anati: “Ndikuyamikira kuti ndinagwira nawo ntchito yothandiza ena ndipo panopa ndine wosangalala kwambiri kuposa kale. Ndikudziwa kuti zaka zikubwerazi, ndidzakhala ndikupindulabe chifukwa cha zinthu zosaiwalika zimene ndinachita.”

15. Kodi tili ndi zifukwa zabwino zotani zopitirizira kutumikira monga adindo a kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu?

15 Ndithudi, kumvera lamulo la Mulungu la kulalikira uthenga wabwino ndiponso lolimbikitsa okhulupirira anzathu, kumabweretsa madalitso kwa tonse. Anthu amene timawathandiza amalimbikitsidwa mwauzimu, ndipo ifeyo timakhala osangalala kwambiri chifukwa cha mtima wathu wopatsa. (Mac. 20:35) Mpingo wonse umakhala wachikondi kwambiri ngati aliyense mumpingomo akuyesetsa kusonyeza chikondi. Ndiponso, chikondi ndi kuganizirana zimene timasonyeza zimatidziwikitsa mosavuta kuti ndife Akhristu oona. Yesu anati: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yoh. 13:35) Koposa zonse, ulemu wonse umapita kwa Atate wathu wachikondi, Yehova, pamene cholinga chake cholimbikitsa anthu ofunikira thandizo chikukwaniritsidwa ndi atumiki ake padziko lapansi. Ndiyetu tili ndi zifukwa zabwino kwambiri zogwiritsira ntchito mphatso yathu “potumikirana wina ndi mnzake monga adindo abwino a kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu.” Kodi mupitiriza kuchita zimenezi?​—Werengani Aheberi 6:10.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yehova amalimbikitsa atumiki ake m’njira zotani?

• Kodi taikizidwa chiyani?

• Kodi ndi njira zina ziti zimene tingatumikirire okhulupirira anzathu?

• Kodi n’chiyani chingatilimbikitse kuti tipitirize kugwiritsa ntchito mphatso yathu “potumikirana wina ndi mnzake”?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 13]

Kodi mumagwiritsa ntchito “mphatso” yanu potumikira ena kapena podzisangalatsa nokha?

[Zithunzi patsamba 15]

Timalalikira uthenga wabwino kwa ena ndiponso timalimbikitsa Akhristu anzathu

[Chithunzi patsamba 16]

Anthu ogwira ntchito yothandiza anzawo amafunika kuwayamikira chifukwa cha kudzipereka kwawo