Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mtumiki wa Yehova “Analasidwa Chifukwa cha Zolakwa Zathu”

Mtumiki wa Yehova “Analasidwa Chifukwa cha Zolakwa Zathu”

Mtumiki wa Yehova “Analasidwa Chifukwa cha Zolakwa Zathu”

“Iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu. . . . Ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.”​—YES. 53:5.

1. Kodi tiyenera kukumbukira chiyani tikamachita mwambo wa Chikumbutso, nanga ndi ulosi uti umene ungatithandize kuchita zimenezi?

TIMACHITA mwambo wa Chikumbutso pofuna kukumbukira imfa ya Khristu komanso zinthu zonse zimene zatheka chifukwa cha kufa ndi kuuka kwa Yesu. Mwambo umenewu umatikumbutsa kuti Yehova ndiye ayenera kulamulira. Umatikumbutsanso za kuyeretsedwa kwa dzina lake, ndiponso za kukwaniritsidwa kwa cholinga chake, chomwe chikuphatikizapo kupulumutsa anthu. Mwina tingati ulosi wa pa Yesaya 53:3-12 ndi umene umalongosola bwino kwambiri nsembe ya Khristu ndi zimene inakwaniritsa kuposa ulosi wina uliwonse m’Baibulo. Yesaya analosera kuti Mtumiki adzavutika m’njira zosiyanasiyana ndipo analongosola zimene zidzachitike pa imfa yake. Analongosolanso madalitso amene imfa yake idzabweretse kwa abale ake odzozedwa ndiponso kwa a “nkhosa zina.”​—Yoh. 10:16.

2. Kodi ulosi wa Yesaya ukuchitira umboni chiyani, ndipo utithandiza motani?

2 Patatsala zaka 700 kuti Yesu abadwe padziko lapansi, Yehova anamuuza Yesaya kuti alembe ulosi wonena kuti Mtumiki Wake wosankhidwa adzakhala wokhulupirika ngakhale atadzakumana ndi mayesero aakulu bwanji. Umenewutu ndi umboni wosonyeza kuti Yehova sankakaika ngakhale pang’ono za kukhulupirika kwa Mwana wake. Kuphunzira ulosi umenewu kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndiponso kutithandiza kukhala oyamikira kwambiri.

‘Ananyozedwa Ndipo Sanam’lemekeze’

3. N’chifukwa chiyani Ayuda anayenera kulandira Yesu mwaulemu, komano kodi anamulandira motani?

3 Werengani Yesaya 53:3. Tangoganizirani zimene Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anachita. Iye analolera kusiya utumiki umene ankasangalala nawo ali kumwamba limodzi ndi Atate wake. Kenako anabwera padziko lapansi pano n’kudzapereka moyo wake nsembe kuti apulumutse anthu ku uchimo ndi imfa. (Afil. 2:5-8) Cholinga cha nsembeyi chinali chokhululukira machimo, ndipo nsembe za nyama zimene zinkaperekedwa potsatira Chilamulo cha Mose zinali chithunzithunzi chabe cha zimenezi. (Aheb. 10:1-4) N’chifukwa chaketu iyeyu anali woyenera kulandiridwa mwaulemu, makamaka ndi Ayuda amene ankayembekezera kubwera kwa Mesiya. (Yoh. 6:14) Koma m’malomwake, Khristu “ananyozedwa” ndi Ayudawo ndipo monga mmene Yesaya ananenera iwo ‘sanamulemekeze.’ Mtumwi Yohane analemba kuti: “Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanam’landire.” (Yoh. 1:11) Komanso mtumwi Petulo anawauza Ayuda kuti: “Mulungu wa makolo athu, . . . walemekeza Mtumiki wake Yesu. Amene inu munam’pereka ndi kum’kana pamaso pa Pilato, iye atafuna kum’masula. Inde, inu munam’kana woyera ndi wolungamayo.”​—Mac. 3:13, 14.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu ankadziwa zowawa?

4 Yesaya analoseranso kuti Yesu adzakhala “wodziwa zowawa,” kapena kuti matenda. Palibe umboni wosonyeza kuti Yesu anayamba wadwalapo panthawi imene anali padziko lapansi koma tikudziwa kuti nthawi zina ankatopa. (Yoh. 4:6) Komabe matenda sanali achilendo kwa iye chifukwa polalikira ankakumana ndi anthu odwala, omwe ankawamvera chisoni ndipo anachiritsa odwala ambiri. (Maliko 1:32-34) Motero Yesu anakwaniritsa ulosi wakuti: “Zoonadi Iye ananyamula zowawa zathu, ndi kusenza zisoni zathu.”​—Yes. 53:4a; Mat. 8:16, 17.

Anali Ngati “Wokanthidwa ndi Mulungu”

5. Kodi Ayuda ambiri ankaganiza kuti Yesu akuphedwa chifukwa chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zinam’pweteka kwambiri?

5 Werengani Yesaya 53:4b. Anthu ambiri m’nthawi ya Yesu sanamvetse chifukwa chimene iye anazunzidwira mpaka kuphedwa. Iwo ankakhulupirira kuti Mulungu ndi amene akumulanga. (Mat. 27:38-44) N’chifukwa chake Ayuda anamuimba mlandu wonyoza Mulungu. (Maliko 14:61-64; Yoh. 10:33) Komatu zimenezi zinali zonama chifukwa Yesu sananyoze Mulungu ndipo sanachimwe. Kumuimba mlandu wonyoza Mulungu kuyenera kuti kunam’pweteka kwambiri chifukwa iye, monga Mtumiki wa Yehova, ankakonda kwambiri Atate wake. Komabe Yesu anagonjera Yehova kuti chifuniro chake chichitike.​—Mat. 26:39.

6, 7. Kodi Yehova ‘anatundudza’ motani Mtumiki wake wokhulupirika, ndipo zimenezi ‘zinam’komera’ m’njira yotani?

6 Mungadabwe kuona kuti Yesaya sanangonena kuti anthu ena adzaganiza kuti Khristu ‘akukanthidwa ndi Mulungu, koma analoseranso kuti, “kunakomera Yehova kum’tundudza.” (Yes. 53:10) Komansotu Yehova anali atanena kale kuti: “Taona Mtumiki wanga, wosankhika wanga, amene moyo wanga ukondwera naye.” Ndiyeno zinatheka bwanji kuti iye akondwere ndi kutundudza, kapena kuzunza Yesu? (Yes. 42:1) Kodi tingati Yehova anakondwera m’njira yotani ndi kuzunzika kwa Yesu?

7 Kuti timvetse ulosi umenewu tiyenera kukumbukira kuti pamene Satana anatsutsa zokuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse, ananenanso kuti n’zokayikitsa kuti atumiki onse a Mulungu a kumwamba komanso padziko lapansi pano angakhale okhulupirika kwa Yehova. (Yobu 1:9-11; 2:3-5) Komabe Yesu anakhala wokhulupirika mpaka pamene anaphedwa, motero iye anatsutsiratu bodza la Satana. Motero, ngakhale kuti Yehova analola kuti adani ake aphe Khristu, ndithu zinam’pweteka kwambiri kuona Mtumiki wake wosankhidwa akuphedwa. Komabe Yehova anasangalala kwabasi chifukwa Mwana wake anakhala wokhulupirika kwambiri. (Miy. 27:11) Anakondweranso kwambiri chifukwa anadziwa kuti imfa ya Mwana wake idzabweretsa madalitso kwa anthu olapa.​—Luka 15:7.

“Analasidwa Chifukwa cha Zolakwa Zathu”

8, 9. (a) Kodi Yesu “analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu” m’njira yotani? (b) Nanga Petulo anatsimikizira motani mfundo imeneyi?

8 Werengani Yesaya 53:6. Anthu ochimwa akhala akungolowera uku ndi uku ngati nkhosa zosochera, kufunafuna woti awapulumutse ku matenda ndi imfa, zomwe zinachokera kwa Adamu. (1 Pet. 2:25) Koma popeza kuchimwa kwa Adamu kunachititsa kuti ana ake onse akhale opanda ungwiro, palibe aliyense amene angawombole zimene Adamu anataya. (Sal. 49:7) Komano chifukwa cha chikondi chake chachikulu, ‘Yehova anaika mphulupulu ya ife tonse’ pa Mwana wake wokondedwa, yemwenso ndi Mtumiki wake wosankhidwa. Inde, Khristu ananyamula machimo athu pamtengo wozunzirapo ndi kufa m’malo mwa ifeyo. Kuti achite zimenezi, iye analolera kuti ‘alasidwe chifukwa cha zolakwa zathu’ “natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu.”

9 Mtumwi Petulo analemba kuti: “Anakuitanirani ku moyo umenewu, pakuti ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa. Iye ananyamula machimo athu m’thupi lake pa mtengo, kuti tilekane ndi machimo ndi kukhala amoyo m’chilungamo.” Kenaka pogwira mawu ulosi wa Yesaya, Petulo ananenanso kuti: “Ndipo ‘mwa mabala ake munachiritsidwa.’” (1 Pet. 2:21, 24; Yes. 53:5) Zimenezi zinatsegula njira yakuti anthu ochimwa ayanjanitsidwe ndi Mulungu, monga Petulo ananeneranso kuti: “Khristu anafera machimo kamodzi kokha basi. Munthu wolungama kufera anthu osalungama, kuti akufikitseni kwa Mulungu.”​—1 Pet. 3:18.

“Ngati Nkhosa Yotsogoleredwa Kukaphedwa”

10. (a) Kodi Yohane M’batizi ananena chiyani za Yesu? (b) N’chifukwa chiyani mawu a Yohane anali oyenerera?

10 Werengani Yesaya 53:7, 8Yohane M’batizi ataona Yesu akubwera poteropo, ananena kuti: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akuchotsa uchimo wa dziko!” (Yoh. 1:29) Potchula Yesu kuti Mwanawankhosa, Yohane ayenera kuti ankaganizira mawu a Yesaya akuti, Mesiya adzakhala “ngati nkhosa yotsogoleredwa kukaphedwa.” (Yes. 53:7) Yesaya analosera kuti: “Iye anathira moyo wake kuimfa.” (Yes. 53:12) N’zochititsa chidwi kuti usiku umene anakhazikitsa Chikumbutso cha imfa yake, Yesu anapereka chikho cha vinyo kwa atumwi ake 11 okhulupirika n’kunena kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi anga a chipangano,’ amene adzakhetsedwa chifukwa cha anthu ambiri kuti machimo akhululukidwe.”​—Mat. 26: 28.

11, 12. (a) Kodi kulolera kwa Isake kuti aperekedwe nsembe kumasonyeza chiyani za nsembe ya Khristu? (b) Kodi tikamachita mwambo wa Chikumbutso tiyenera kukukumbukira chiyani za Abulahamu Wamkulu, Yehova?

11 Mofanana ndi Isake, Yesu analolera kuti aperekedwe nsembe mogwirizana ndi zimene Yehova anafuna. (Gen. 22:1, 2, 9-13; Aheb. 10:5-10) Ngakhale kuti Isake analolera kuti aperekedwe nsembe, Abulahamu ndi amene anakonza zopereka nsembeyo. (Aheb. 11:17) Mofanana ndi zimenezi, ngakhale kuti Yesu analolera kuti afe, Yehova ndi amene anakonza zoti nsembe ya dipo iperekedwe m’njira imeneyi. Nsembe ya Mwana wake inasonyeza kuti Mulungu amakonda kwambiri anthu.

12 Yesu ananena yekha kuti: “Mulungu anakonda kwambiri dziko mwakuti anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira mwa iye asawonongeke, koma akhale nawo moyo wosatha.” (Yoh. 3:16) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu akuonetsa chikondi chake kwa ife, mwakuti pamene tinali ochimwabe, Khristu anatifera ife.” (Aroma 5:8) Motero, ngakhale kuti tiyenera kulemekeza Khristu pokumbukira imfa yake, tisamaiwale kuti amene anakonza zoti paperekedwe nsembe imeneyi ndi Abulahamu Wamkulu, yemwe ndi Yehova. Motero, timachita mwambo wa Chikumbutso n’cholinga chotamanda Yehova.

Mtumiki ‘Alungamitsa Ambiri’

13, 14. Kodi Mtumiki wa Yehova ‘analungamitsa anthu ambiri’ m’njira yotani?

13 Werengani Yesaya 53:11, 12. Ponena za Mtumiki wake wosankhidwa, Yehova anati: “Mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri.” Kodi zimenezi anazichita motani? Mawu a kumapeto kwa vesi 12 akutithandiza kuyankha funso limeneli. Mawu ake ndi akuti Mtumikiyu ‘anapembedzera olakwa.’ Anthu onse ochokera kwa Adamu, amabadwa “olakwa” kapena kuti ochimwa, motero amalandira “malipiro a uchimo,” omwe ndi imfa. (Aroma 5:12; 6:23) Motero m’pofunika kuti anthu ochimwafe tiyanjanitsidwenso ndi Yehova. Chaputala 53 cha ulosi wa Yesaya chimafotokoza bwino mmene Yesu ‘anatipembedzera’ kapena kuti kutiyanjanitsa anthu ochimwafe ndi Mulungu, ponena kuti: “Chilango chotitengera ife mtendere chinam’gwera Iye; ndipo ndi mikwingwirima yake ife tachiritsidwa.”​—Yes. 53:5.

14 Posenza machimo athu n’kutifera, Khristu ‘analungamitsa anthu ambiri.’ Paulo analemba kuti: “Kunam’komera Mulungu kuti kudzala konse kukhale mwa iye. Kutinso kudzera mwa [Khristu], ayanjanitsenso zinthu zina zonse kwa iye mwini, pokhazikitsa mtendere mwa magazi amene iye anakhetsa pa mtengo wozunzikirapo, kaya zikhale zinthu za padziko lapansi kapena zinthu za kumwamba.”​—Akol. 1:19, 20.

15. (a) Kodi “zinthu za kumwamba” zimene Paulo anatchula zikuimira ndani? (b) Kodi ndi anthu ati amene ali oyenerera kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Chikumbutso, nanga n’chifukwa chiyani?

15 “Zinthu za kumwamba” zimene zayanjanitsidwa ndi Yehova kudzera mwa magazi amene Yesu anakhetsa ndi Akhristu odzozedwa, amene anaitanidwa kuti akalamulire ndi Khristu kumwamba. Akhristu “otenga mbali m’chiitano cha kumwamba” akuyesedwa “olungama kuti akhale ndi moyo.” (Aheb. 3:1; Aroma 5:1, 18) Kenaka Yehova amawatenga kukhala ana ake auzimu. Mzimu woyera umawachitira umboni kuti ndi “olowa ufumu anzake a Khristu,” oitanidwa kuti akakhale mafumu ndi ansembe mu Ufumu wake wakumwamba. (Aroma 8:15-17; Chiv. 5:9, 10) Iwo amakhala mbali ya Isiraeli wauzimu, “Isiraeli wa Mulungu,” ndipo amalowa mu “pangano latsopano.” (Yer. 31:31-34; Agal. 6:16) Chifukwa choti ali m’pangano latsopano iwowa amakhala oyenerera kudya mkate komanso kumwa vinyo wa pa Chikumbutso. Ponena za vinyoyu Yesu anati: “Chikho ichi chikutanthauza chipangano chatsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa chifukwa cha inu.”​—Luka 22:20.

16. Kodi “zinthu za padziko lapansi,” zikuimira ndani ndipo kodi zimatheka bwanji kuti afike poyesedwa olungama pamaso pa Yehova?

16 “Zinthu za padziko lapansi” ndizo nkhosa zina za Khristu, zimene zili ndi chiyembekezo chokhala padziko lapansi kosatha. Mtumiki wosankhidwa wa Yehova amachititsanso kuti anthu amenewa ayesedwe olungama pamaso pa Yehova. Chifukwa choti amakhulupirira nsembe yadipo imene Khristu anapereka, iwo “achapa mikanjo yawo ndi kuiyeretsa m’magazi a Mwanawankhosa,” motero Yehova amawayesa olungama, osati monga ana ake auzimu, koma monga mabwenzi ake, ndipo wawalonjeza kuti angathe kudzapulumuka pa “chisautso chachikulu.” (Chiv. 7:9, 10, 14; Yak. 2:23) Iwowa sali m’pangano latsopano ndipo sayembekezera kukakhala kumwamba, motero a nkhosa zinawa sadya nawo mkate kapena kumwa nawo vinyo wa pa Chikumbutso. Amachita nawo mwambowu monga odzaonerera chifukwa choulemekeza.

Titamande Yehova ndi Mtumiki Wake Amene Amakondwera Naye

17. Kodi kuphunzira ulosi wa Yesaya wonena za Mtumiki kwatithandiza bwanji kukonzekera m’maganizo mwathu kudzachita Chikumbutso?

17 Kuphunzira ulosi wa Yesaya wonena za Mtumiki kwatithandiza kwambiri kukhala okonzeka m’maganizo athu kudzachita Chikumbutso cha imfa ya Khristu. Kwatithandizanso ‘kuyang’anitsitsa Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu.’ (Aheb. 12:2) Taphunzira kuti Mwana wa Mulungu si wogalukira. Mosiyana ndi Satana, iye amasangalala kuphunzitsidwa ndi Yehova, popeza amadziwa kuti Yehovayo ndiye Wolamulira Wamkulu. Taonanso kuti muutumiki wake padziko lapansi pano, Yesu anachitira chifundo anthu amene ankawalalikira, ndipo ambiri mwa anthuwo ankawachiritsa mwakuthupi ndiponso mwauzimu. Potero iye anali kusonyeza zimene adzachite akadzakhala Mfumu Mesiya m’dongosolo latsopano la zinthu pamene ‘adzakhazikitse chiweruzo m’dziko lapansi.’ (Yes. 42:4) Iye, monga “kuunika kwa amitundu,” anachita khama kwambiri pa ntchito yolalikira za Ufumu ndipo zimenezi zikutithandiza kuona kuti otsatira ake ayenera kulalikira uthenga wabwino mwakhama padziko lonse.​—Yes. 42:6.

18. N’chifukwa chiyani kuphunzira ulosi wa Yesaya kwachititsa kuti tiyamikire kwambiri Yehova ndiponso Mtumiki wake wokhulupirika?

18 Ulosi wa Yesaya watithandizanso kumvetsa kuti zinali zopweteka kwambiri kwa Yehova kutumiza Mwana wake wokondedwa padziko lapansi kuti adzavutike n’kudzatifera. Chimene chinam’sangalatsa Yehova si kuona Yesu akuvutika, koma kuona Mwana wakeyu akuchita zinthu zonse mokhulupirika mpaka kufa. Nafenso tizisangalala monga Yehova, poganizira zinthu zonse zimene Yesu anachita kuti Satana aoneke kuti ndi wabodza ndi kuti dzina la Yehova liyeretsedwe, n’kutsimikizira kuti Iye ndiye ali woyenerera kulamulira. Komanso, Khristu anasenza machimo athu n’kutifera. Motero n’zotheka kuti anthu a m’kagulu ka nkhosa ka abale ake odzozedwa ndiponso a nkhosa zina akhale olungama kwa Yehova. Inde, Yehova ndiponso Mtumiki wake wokhulupirika watichitira zambiri zimene ziyenera kutithandiza kukhala oyamikira kwambiri tikamadzachita mwambo wa Chikumbutso.

Tibwereze

• Kodi mawu akuti “kunakomera Yehova kum’tundudza” Mwana wake akutanthauza chiyani?

• Kodi Yesu “analasidwa” motani “chifukwa cha zolakwa zathu”?

• Kodi Mtumiki ‘analungamitsa ambiri’ m’njira yotani?

• Kodi kuphunzira maulosi onena za Mtumiki kwakuthandizani bwanji kukonzekera m’maganizo ndiponso mumtima mwanu kudzachita Chikumbutso?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 26]

‘Ananyozedwa ndipo sanam’lemekeze’

[Chithunzi patsamba 28]

“Iye anathira moyo wake kuimfa”

[Chithunzi patsamba 29]

A “nkhosa zina” amachita nawo mwambo wa Chikumbutso monga odzaonerera chifukwa choulemekeza