Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Taonani Mtumiki Amene Yehova Amakondwera Naye

Taonani Mtumiki Amene Yehova Amakondwera Naye

Taonani Mtumiki Amene Yehova Amakondwera Naye

“Taona Mtumiki wanga, . . . amene moyo wanga ukondwera naye.”​—Yes. 42:1.

1. Kodi anthu a Yehova akulimbikitsidwa kuchita chiyani, makamaka panthawi inoyo pamene Chikumbutso chikuyandikira, nanga n’chifukwa chiyani akulimbikitsidwa kutero?

NTHAWI yokumbukira imfa ya Khristu yayandikira, choncho anthu a Mulungu ayenera kutsatira malangizo a mtumwi Paulo akuti ‘tiyang’anitsitse Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu.’ Paulo anatinso: “Ndithudi, lingalirani mozama za munthu amene wapirira malankhulidwe onyoza ngati amenewo a ochimwa, amene anadzichimwitsa nawo iwo okha. Inde, lingalirani za iye kuti musatope, ndi kuti moyo wanu usalefuke.” (Aheb. 12:2, 3) Kulingalira mozama za kukhulupirika kwa Khristu pa moyo wake wonse mpaka pamene anapereka moyo wake nsembe, kungathandize Akhristu odzozedwa ndiponso anzawo a nkhosa zina kupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika ndi kupewa ‘kuti moyo wawo usalefuke.’​—Yerekezerani ndi Agalatiya 6:9.

2. Kodi ulosi wa Yesaya wonena za Mwana wa Mulungu ukutiphunzitsa chiyani?

2 Yehova anauzira mneneri Yesaya kuti alembe ulosi onena za Mwana Wake. Ulosi umenewu utithandiza kuti ‘tiyang’anitsitse Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu,’ Yesu Khristu, chifukwa umafotokoza khalidwe lake, mmene anazunzikira, ndiponso mmene anakwezedwera kukhala Mfumu komanso Mombolo. * Utithandiza kumvetsa bwino mwambo wa Chikumbutso, umene chaka chino tidzachite Lachinayi pa April 9, dzuwa litalowa.

Kodi Mtumikiyu Ndi Ndani?

3, 4. (a) Kodi mawu akuti “mtumiki” m’buku la Yesaya amanena za ndani? (b) Kodi Baibulo limasonyeza kuti Mtumiki wotchulidwa mu Yesaya chaputala 42, 49, 50, 52, ndi 53 ndi ndani?

3 M’buku la Yesaya mawu akuti “mtumiki” amapezeka kambirimbiri. Nthawi zina amanena za Yesaya yemweyo. (Yes. 20:3; 44:26) Nthawi zinanso amanena za mtundu wonse wa Isiraeli, kapena wa Yakobo. (Yes. 41:8, 9; 44:1, 2, 21) Koma kodi Mtumiki amene akutchulidwa mu ulosi wochititsa chidwi wa pa Yesaya chaputala 42, 49, 50, 52 ndi 53 ndi ndani? Malemba Achigiriki Achikristu amatithandiza kudziwa bwinobwino kuti Mtumiki wa Yehova ameneyu ndi ndani. N’zochititsa chidwi kuti mdindo wa ku Aitiopiya amene amatchulidwa m’buku la Machitidwe ankawerenga ulosi umenewu pamene mzimu unatsogolera Filipo, mlaliki wa uthenga wabwino, kuti akakumane naye. Mdindoyo anali atawerenga mbali ya m’Baibulo imene masiku ano imapezeka pa Yesaya 53:7, 8, motero anam’funsa Filipo kuti: “Ndiuzeni chonde, Kodi mneneriyu akunena za ndani? Za iye mwini kapena za munthu wina?” Filipo sanazengereze kufotokoza kuti Yesaya anali kunena za Mesiya, Yesu.​—Mac. 8:26-35.

4 Yesu adakali mwana, Simiyoni, yemwe anali munthu wolungama, ananena motsogozedwa ndi mzimu woyera kuti “mwana wamng’onoyo, Yesu,” adzakhala “kuwala kochotsa nsalu yophimba amitundu,” mogwirizana ndi ulosi wa pa Yesaya 42:6 ndi Yesaya 49:6. (Luka 2:25-32) Komanso zinthu zonse zochititsa manyazi zimene anthu anam’chitira Yesu pa tsiku limene ankaweruzidwa zinanenedwa kale mu ulosi wa pa Yesaya 50:6-9. (Mateyo 26:67; Luka 22:63) Pambuyo pa Pentekoste 33 C.E., mtumwi Petulo ananena momveka bwino kuti Yesu ndiye “Mtumiki” wa Yehova. (Yes. 52:13; 53:11; werengani Machitidwe 3:13, 26.) Kodi tingaphunzire chiyani pa ulosi onena za Mesiyawu?

Yehova Anaphunzitsa Mtumiki Wake

5. Kodi Mtumikiyu anaphunzitsidwa motani?

5 Ulosi umodzi wa Yesaya wonena za Mtumiki wa Mulungu umatithandiza kumvetsa ubwenzi umene Yehova anali nawo kumwamba ndi Mwana wake woyamba kubadwa, mwanayo asanabadwe padziko lapansi. (Werengani Yesaya 50:4-9.) Mtumikiyo ananena yekha kuti Yehova ankamuphunzitsa nthawi zonse. Iye anati: ‘Iye agalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.’ (Yes. 50:4) Panthawi yonseyo, Mtumiki wa Yehovayu anali wophunzira womvera, chifukwa Atate wake akamamuuza zinthu ankamvetsera. Uwutu unali mwayi waukulu kwambiri chifukwa anaphunzitsidwa ndi Mlengi wa chilengedwe chonse.

6. Kodi Mtumikiyo anasonyeza bwanji kuti anali kugonjera Atate wake pa zinthu zonse?

6 Muulosi umenewu, Mtumikiyu anatchula Atate wake kuti “Ambuye Yehova,” kutanthauza kuti Yehova ndiye wolamulira wamkulu koposa. Mawu amenewa akusonyeza kuti Mtumikiyu anali ataphunzira mfundo yakuti Yehova ndiye wolamulira wa chilengedwe chonse. Posonyeza kuti amagonjera Atate wake pa zonse, iye anati: “Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m’mbuyo.” (Yes. 50:5) Iye ‘anali pa mbali ya Yehova ngati mmisiri,’ polenga kumwamba, dziko lapansi komanso anthu. ‘Mmisiri’ ameneyu anali “kukondwera pamaso [pa Yehova] nthawi zonse, ndi kukondwera ndi dziko lake lokhalamo anthu, ndi kusekerera ndi ana a anthu.”​—Miy. 8:22-31.

7. Kodi n’chiyani chimasonyeza kuti Mtumikiyu sankakayika kuti Atate wake anali naye pamayesero ake onse?

7 Mtumikiyu anaphunzitsidwa bwino komanso ankakonda kwambiri anthu. Zimenezi zinam’thandiza panthawi imene anatsutsidwa kwambiri padziko lapansi pano. Iye anapitirirabe kusangalala ndi kuchita chifuniro cha Atate wake, ngakhale pamene anazunzidwa kwambiri. (Sal. 40:8; Mat. 26:42; Yoh. 6:38) Panthawi yonse imene ankakumana ndi mayesero padziko pano, Yesu ankadziwa kuti Atate wake ali naye ndipo akusangalala naye. Monga mmene ulosi wa Yesaya unanenera, n’zomveka Yesu kunena mawu akuti: “Iye ali pafupi amene alungamitsa ine; ndani adzakangana ndi Ine? . . . Taonani, Ambuye Yehova adzathandiza ine.” (Yes. 50:8, 9) Inde, Yehova anathandiza Mtumiki wake wokhulupirikayu pa utumiki wake wonse ali padziko lapansi, monga mmene ulosi winanso wa Yesaya ukusonyezera.

Utumiki Wake Ali Padziko Lapansi

8. Kodi pali umboni wotani umene ukutsimikizira kuti Yesu analidi “wosankhidwa” wa Yehova, mogwirizana ndi lemba la Yesaya 42:1?

8 Baibulo limatiuza zimene zinachitika pamene Yesu anali kubatizidwa mu 29 C.E. Limati: “Mzimu woyera . . . unatsika kudzatera pa iye, ndiyeno panamveka mawu ochokera kumwamba akuti: ‘Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndimakondwera nawe.’” (Luka 3:21, 22) Pamenepa Yehova ananena momveka bwino kuti ‘Wosankhidwa wake,’ wotchulidwa mu ulosi wa Yesaya uja ndi Yesu. (Werengani Yesaya 42:1-7.) Muutumiki wake ali padziko pano, Yesu anakwaniritsa ulosi umenewu m’njira yodabwitsa kwambiri. M’nkhani imene analemba m’buku lake la uthenga wabwino, Mateyo anagwira mawu a pa Yesaya 42:1-4 n’kunena kuti mawuwo ankanena za Yesu.​—Mat. 12:15-21.

9, 10. (a) Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji lemba la Yesaya 42:3 pautumiki wake? (b) Kodi Yesu ‘anatulutsa’ bwanji “chiweruzo” ali padziko lapansi pano, ndipo kodi ‘adzakhazikitsa’ liti “chiweruzo m’dziko lapansi”?

9 Atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankanyoza Ayuda osauka. (Yoh. 7:47-49) Ankawachitira nkhanza moti anali ngati ‘mabango ophwanyika’ kapena ‘nyali yofuka’ yoti yangotsala pang’ono kuzima. Koma Yesu ankachitira chifundo anthu osauka ndi ovutika. (Mat. 9:35, 36) Iye anawaitana mokoma mtima kuti: “Bwerani kwa ine, nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Mat. 11:28) Komanso Yesu ‘anatulutsa chiweruzo,’ kapena kuti chilungamo pophunzitsa anthu mfundo za Yehova zokhudza chabwino ndi choipa. (Yes. 42:3) Iye anasonyezanso kuti Chilamulo cha Mulungu chiyenera kugwiritsidwa ntchito m’njira yoyenera ndiponso mwachifundo. (Mat. 23:23) Yesu anasonyezanso chilungamo polalikira mopanda tsankho kwa olemera ndi osauka omwe.​—Mat. 11:5; Luka 18:18-23.

10 Ulosi wa Yesaya umanenanso kuti “Wosankhidwa “ wa Yehova ‘adzakhazikitsa chiweruzo m’dziko lapansi.’ (Yes. 42:4) Iye achita zimenezi posachedwapa. Monga Mfumu ya Ufumu wa Mesiya, adzawononga maufumu onse a anthu n’kukhazikitsa ulamuliro wake wolungama. Ndipo adzabweretsa dziko latsopano, limene “mudzakhala chilungamo.”​—2 Pet. 3:13; Dan. 2:44.

“Kuunika” Ndiponso “Pangano”

11. Kodi Yesu wakhala “kuunika kwa amitundu” m’njira yotani, m’nthawi ya atumwi komanso masiku ano?

11 Pokwaniritsa lemba la Yesaya 42:6, Yesu anasonyeza kuti iye ndi “kuunika kwa amitundu.” Pamene ankachita utumiki wake padziko lapansi pano, anaunikira anthu mwauzimu, makamaka Ayuda. (Mat. 15:24; Mac. 3:26) Yesu anatinso: “Ine ndine kuwala kwa dziko.” (Yoh. 8:12) Iye anakhala kuunika kwa Ayuda ndiponso anthu amitundu ndipo anatero powaunikira mwauzimu komanso popereka moyo wake wangwiro kuti awombole anthu onse. (Mat. 20:28) Ataukitsidwa, iye analamula ophunzira ake kuti akhale mboni zake “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Pantchito yawo yolalikira, Paulo ndi Baranaba anagwira mawu akuti “kuunika kwa amitundu,” ndipo anati mawuwa ankanena za ntchito imene iwowo ankachita yolalikira anthu amene sanali Ayuda. (Mac. 13:46-48; yerekezerani ndi Yesaya 49:6.) Ntchito imeneyi ikupitirirabe chifukwa abale ake a Yesu limodzi ndi anzawo a nkhosa zina, akufalitsabe uthenga wabwino umene umaunikira anthu mwauzimu. Iwo akuthandizanso anthu kuyamba kukhulupirira Yesu, yemwe ali “kuunika kwa amitundu.”

12. Kodi Yehova anapereka motani Mtumiki wake kuti akhale “pangano la anthu”?

12 Muulosi womwewo, Yehova anauza Mtumiki wake wosankhidwa kuti: ‘Ndikusunga iwe, ndi kukupatsa ukhale pangano la anthu.’ (Yes. 42:6) Satana anayesetsa kupha Yesu komanso kumuletsa kutsiriza utumiki wake padziko lapansi, koma Yehova anamuteteza mpaka itafika nthawi yoti adzafe. (Mat. 2:13; Yoh. 7:30) Kenaka Yehova anamuukitsa Yesu n’kumupereka kuti akhale “pangano,” kapena kuti lonjezo kwa anthu a padziko lapansi. Lonjezo limenelo linapereka chitsimikizo chakuti Mtumiki wokhulupirika wa Mulunguyu adzakhalabe “kuunika kwa amitundu,” kuunikira anthu onse okhala mumdima wauzimu.​—Werengani Yesaya 49:8, 9. *

13. Kodi Yesu anapulumutsa motani “amene akhala mumdima” pamene anali kuchita utumiki wake padziko pano, komanso panopo?

13 Mogwirizana ndi pangano limeneli, Mtumiki wa Yehova wosankhidwayu ‘adzatsegula maso akhungu,’ ‘adzatulutsa am’nsinga m’ndende,’ ndi kupulumutsa “amene akhala mumdima.” (Yes. 42:7) Yesu akuchita utumiki wake padziko lapansi pano, anakwaniritsa ulosi umenewu polalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kutsutsa miyambo ya chipembedzo chonyenga. (Mat. 15:3; Luka 8:1) Motero Ayuda amene anakhala ophunzira ake anawapulumutsa ku chipembedzo chonyenga. (Yoh. 8:31, 32) Mofanana ndi zimenezi, Yesu wathandizanso anthu mamiliyoni ambiri omwe si Ayuda kuphunzira choonadi. Iye analamula anthu om’tsatira kuti: “Pitani mukapange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse,” ndipo anawalonjeza kuti adzakhala nawo “mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mat. 28:19, 20) Panopo, Khristu Yesu akuyang’anira ntchito yolalikira ya padziko lonse ali kumwamba.

Yehova Anakweza “Mtumiki” Wake

14, 15. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anakweza Mtumiki wake ndipo anam’kweza bwanji?

14 Muulosi wina wonena za Mtumiki wake Mesiya, Yehova anati: “Taonani, Mtumiki wanga adzachita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.” (Yes. 52:13) Yehova anakweza Mwana wake chifukwa anali wogonjera ku ulamuliro Wake ndiponso anali wokhulupirika ngakhale ali pamayesero aakulu zedi.

15 Mtumwi Petulo ananena kuti Yesu “ali ku dzanja lamanja la Mulungu, pakuti anapita kumwamba; ndipo angelo ndi maulamuliro ndi mphamvu zinakhala pansi pake.” (1 Pet. 3:22) Mtumwi Paulo analembanso kuti Yesu “anadzichepetsa nakhala womvera mpaka imfa, inde, imfa ya pa mtengo wozunzikirapo. Pachifukwa chimenechinso, Mulungu anam’kweza pamalo apamwamba. Ndipo anam’komera mtima kum’patsa dzina loposa lina lililonse. Anatero kuti m’dzina la Yesu, onse apinde maondo awo, aja akumwamba, a padziko lapansi, ndi a pansi pa nthaka. Kutinso aliyense avomereze poyera ndi lilime lake kuti Yesu Khristu ndiye Ambuye, polemekeza Mulungu Atate.”​—Afil. 2:8-11.

16. Kodi mu 1914 Yesu ‘anatukulidwa pamwamba’ motani, ndipo wachita zotani kuyambira pamenepo?

16 Mu 1914, Yehova anam’kwezanso kwambiri Yesu. Iye ‘anam’tukula pamwamba’ atamuika kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya. (Sal. 2:6; Dan. 7:13, 14) Kuyambira nthawi imeneyo Khristu wakhala ‘akuchita ufumu pakati pa adani ake.’ (Sal. 110:2) Choyamba iye anagonjetsa Satana ndi ziwanda zake, ndipo anawaponyera kudziko. (Chiv. 12:7-12) Kenaka, monga Koresi Wamkulu, Khristu anapulumutsa otsalira a abale ake odzozedwa padziko pano, powachotsa mu “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 18:2; Yes. 44:28) Iye wakhala akutsogolera ntchito yapadziko lonse yolalikira imene yathandiza kusonkhanitsa “otsala” a abale ake auzimu ndipo kenaka yathandizanso kusonkhanitsa anthu mamiliyoni a “nkhosa zina,” omwe ndi anzawo okhulupirika a anthu a “kagulu ka nkhosa.”​—Chiv. 18:2; Yes. 44:28; Chiv. 12:17; Yoh. 10:16; Luka 12:32.

17. Kodi taphunzira chiyani muulosi wa Yesaya wonena za “mtumiki”?

17 N’zosakayikitsa kuti kuphunzira ulosi wochititsa chidwi umenewu wa m’buku la Yesaya kwatithandiza kuyamba kuyamikira kwambiri Mfumu ndiponso Mombolo wathu, Khristu Yesu. Akuchita utumiki wake padziko pano, iye anali Mwana womvera kwambiri, ndipo zimenezi zinaonetsa kuti anaphunzitsidwa bwino kwambiri ndi Atate wake pamene anali kumwamba. Utumiki wakewu ndiponso zimene akuchita poyang’anira ntchito yolalikira masiku ano zasonyezadi kuti iye ndiye “kuunika kwa amitundu.” Monga mmene tionere m’nkhani yotsatirayi, palinso ulosi wina wonena za Mtumiki Mesiya umene ukusonyeza kuti iye anayenera kudzavutika ndi kudzapereka moyo wake kuti atipulumutse. Nkhani zimenezi n’zofunika kuti ‘tizilingalire’ bwino pamene tikuyandikira nthawi ya Chikumbutso.​—Aheb. 12:2, 3.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti mumve tsatanetsatane wa ulosi wa pa Yesaya 49:1-12, onani buku la Ulosi wa Yesaya​—Muuni wa Anthu Onse, Gawo 2, masamba 136 mpaka 145.

Tibwereze

• Kodi “mtumiki” wotchulidwa muulosi wa Yesaya ndi ndani, nanga tikudziwa bwanji zimenezi?

• Kodi Mtumikiyu anaphunzira chiyani kwa Yehova?

• N’chifukwa chiyani Yesu akutchedwa “kuunika kwa amitundu”?

• Kodi Mtumikiyu anatukulidwa motani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Filipo ananena momveka bwino kuti “mtumiki” wotchulidwa ndi Yesaya anali Yesu, Mesiya

[Chithunzi patsamba 23]

Monga Mtumiki wa Yehova wosankhidwa, Yesu anachitira chifundo anthu osauka ndi ovutika

[Chithunzi patsamba 24]

Yesu anakwezedwa ndi Atate wake ndi kumuika kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mesiya