Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Amatsatira Mwanawankhosa” Nthawi Zonse

“Amatsatira Mwanawankhosa” Nthawi Zonse

“Amatsatira Mwanawankhosa” Nthawi Zonse

“Amenewa ndiwo amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene apitako.”​—CHIV. 14:4.

1. Kodi ophunzira oona a Yesu ankaona motani nkhani yotsatira Yesu?

PATATHA zaka pafupifupi ziwiri ndi theka chiyambireni utumiki wake, Yesu “anali kuphunzitsa m’bwalo losonkhanira ku Kaperenao.” “Ophunzira ake ambiri” atakhumudwa ndi zimene anaphunzitsa, “anam’siya nabwerera ku zinthu zakumbuyo, ndipo sanayendenso naye.” Yesu atafunsa atumwi ake 12 ngati nawonso akufuna kusiya kum’tsatira, Simoni Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha; ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera wa Mulungu.” (Yoh. 6:48, 59, 60, 66-69) Ophunzira oona a Yesu sanasiye kum’tsatira. Ngakhale pambuyo podzozedwa ndi mzimu woyera, iwo anapitirizabe kumvera malangizo ake.​—Mac. 16:7-10.

2. (a) Kodi ndani amene ali “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kapena kuti “mdindo wokhulupirika”? (b) Kodi gulu la kapolo lasonyeza motani mbiri yabwino pankhani ‘yotsatira Mwanawankhosa’?

2 Nanga bwanji za Akhristu odzozedwa a masiku ano? Panthawi ina, Yesu anapereka ulosi wonena za “chizindikiro cha kukhalapo [kwake] ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu.” Mu ulosiwo, iye anatchula za gulu la otsatira ake odzozedwa omwe ali padziko lapansi pano kuti ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” kapena kuti “mdindo wokhulupirika.” (Mat. 24:3, 45; Luka 12:42) Gulu la kapololi, lili ndi mbiri yabwino pankhani ‘yotsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.’ (Werengani Chivumbulutso 14:4, 5.) Anthu a m’gululi, amakhalabe anamwali mwauzimu chifukwa chakuti sadzidetsa ndi zikhulupiriro komanso zochita za “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. (Chiv. 17:5) “M’kamwa mwawo” simupezeka ziphunzitso zachinyengo ndipo “alibenso chilema” cha dziko la Satanali. (Yoh. 15:19) M’tsogolo muno, odzozedwa omwe ali padziko pano, ‘adzatsatira’ Mwanawankhosa kumwamba kumene iye ali.​—Yoh. 13:36.

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira gulu la kapolo?

3 Yesu wasankha kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti ‘aziyang’anira antchito ake a pakhomo,’ omwe ndi Akhristu onse odzozedwa amene amapanga gulu la kapololi, ndiponso kuti ‘aziwapatsa chakudya chawo panthawi yoyenera.’ Wasankhanso kapoloyu kuti ‘aziyang’anira zinthu zake zonse.’ (Mat. 24:45-47) Zina mwa “zinthu” zimenezi ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” lomwe likukula kwambiri. (Chiv. 7:9; Yoh. 10:16) Choncho, Mkhristu aliyense wodzozedwa ndiponso aliyense wa “nkhosa zina,” ayenera kukhulupirira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Pali zifukwa zambiri zimene tiyenera kukhulupirira kapoloyu. Zifukwa zikuluzikulu ziwiri ndi izi: (1) Yehova amakhulupirira gulu la kapololi. (2) Yesu nayenso amalikhulupirira. Tiyeni tione umboni wakuti Yehova Mulungu ndiponso Yesu Khristu amakhulupirira kwambiri kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.

Yehova Amakhulupirira Kapoloyu

4. N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira chakudya chauzimu chimene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa?

4 Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatha kupereka chakudya chauzimu cha panthawi yake ndiponso chopatsa thanzi chifukwa chakuti Yehova anati: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” (Sal. 32:8) N’zoonekeratu kuti Yehova ndi amene amatsogolera kapoloyu. Choncho, nafenso tiyenera kukhulupirira mfundo za m’Malemba zimene timalandira kuchokera kwa kapoloyu, zomwe ndi zothandiza kwambiri.

5. N’chiyani chikusonyeza kuti mzimu wa Mulungu ukugwira ntchito m’gulu la kapolo?

5 Komanso, Yehova amadalitsa gulu la kapolo ndi mzimu wake woyera. Ngakhale kuti mzimu wa Yehova sitingauone, koma timaona zimene umachita mwa anthu amene ali ndi mzimuwu. Umboni wa zimenezi ndi zimene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wakwanitsa kuchita. Iye wakhala akuchitira umboni padziko lonse lapansi za Yehova Mulungu, Mwana wake ndiponso za Ufumu. Atumiki a Yehova akulengeza mwachangu uthenga wa Ufumu m’zilumba ndiponso m’mayiko oposa 230. Kodi zimenezi sizikukuchititsani kukhulupirira kuti mzimu wa Mulungu ukugwira ntchito mwa kapoloyu? (Werengani Machitidwe 1:8.) Kuti gulu la kapolo lipereke chakudya chauzimu cha panthawi yake kwa anthu a Yehova padziko lonse, limayenera kusankha zochita mwanzeru pankhani zina zofunika kwambiri. Gululi, limachita zimenezi mwachikondi, mofatsa ndiponso mogwirizana ndi zipatso zina za mzimu.​—Agal. 5:22, 23.

6, 7. Perekani umboni wotsimikizira kuti Yehova amakhulupirira kwambiri kapolo wokhulupirika.

6 Tingamvetse mfundo yoti Yehova amakhulupirira kwambiri kapolo wokhulupirikayu tikaona zimene anamulonjeza. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lipengalo lidzalira, ndipo akufa adzaukitsidwa osakhoza kuwonongeka, ndipo tidzasandulika. Pakuti chokhoza kuwonongeka ichi chidzavala kusawonongeka, ndipo chokhoza kufa ichi chidzavala kusafa.” (1 Akor. 15:52, 53) Akhristu odzozedwa akamwalira ali okhulupirika kwa Mulungu, amaukitsidwa ndi matupi auzimu oposa a angelo ndipo matupi amenewa amakhala oti sangawonongeke. Iwo amapatsidwa moyo wosafa. Lemba la Chivumbulutso 4:4 limafotokoza za oukitsidwawa atakhala pa mipando yachifumu komanso atavala akolona achifumu agolide pamitu pawo. Akhristu odzozedwa akuyembekezera kudzalandira Ufumu wa Mulungu. Komatu si zokhazi.

7 Lemba la Chivumbulutso 19:7, 8 limati: “Ukwati wa Mwanawankhosa wafika, ndipo mkazi wake wadzikongoletsa. Inde, iye waloledwa kuvala zonyezimira, ndi zofewa, pakuti zovala zofewa zikuimira ntchito zolungama za oyera.” Yehova wasankha Akhristu odzozedwa kuti adzakhale mkwatibwi wa Mwana wake. Odzozedwawa akuyembekezera moyo wosawonongeka, moyo wosakhoza kufa, ufumu ndiponso ‘ukwati ndi Mwanawankhosa,’ ndipotu zimenezi ndi mphatso zamtengo wapatali kwambiri. Umenewu ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Mulungu amakhulupirira odzozedwa amene “amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene apitako.”

Yesu Amakhulupirira Kapoloyu

8. Kodi Yesu wasonyeza bwanji kuti amakhulupirira Akhristu odzozedwa?

8 Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yesu amakhulupirira kwambiri Akhristu odzozedwa? Usiku woti aphedwa mawa lake, Yesu analonjeza atumwi ake okhulupirira 11 aja kuti: “Inu ndinu amene mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga. Choncho ndikuchita nanu chipangano, mmene Atate wanga wachitira chipangano cha ufumu ndi ine, kuti mukadye ndi kumwa patebulo langa mu ufumu wanga, ndipo mukakhala m’mipando yachifumu kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.” (Luka 22:28-30) Akhristu onse odzozedwa okwana 144,000 ali m’pangano limeneli. (Luka 12:32; Chiv. 5:9, 10; 14:1) Kodi akanakhala kuti Yesu sakhulupirira odzozedwawa, akanachita nawo pangano loti adzalamulire nawo mu Ufumu wake?

9. Kodi zina mwa ‘zinthu zonse’ za Khristu ndi ziti?

9 Kuwonjezera pamenepa, Yesu Khristu wasankha kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti ‘aziyang’anira zinthu zake zonse,’ kutanthauza chinthu chilichonse chokhudza Ufumu padziko pano. (Mat. 24:47) Zina mwa izo ndi zinthu zonse zimene zili ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova, maofesi a nthambi m’mayiko osiyanasiyana, Malo a Misonkhano ndiponso Nyumba za Ufumu padziko lonse. Komanso zikuphatikizapo ntchito yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira. Kodi akanakhala kuti Yesu sakhulupirira kapoloyu, akanamupatsa udindo wosamalira ndi kugwiritsa ntchito zinthu zonsezi?

10. N’chiyani chikusonyeza kuti Yesu Khristu ali pamodzi ndi otsatira ake odzozedwa?

10 Atatsala pang’ono kubwerera kumwamba, Yesu yemwe anali ataukitsidwa, anaonekera kwa ophunzira ake okhulupirika ndipo anawalonjeza kuti: “Dziwani ichi! Ine ndili nanu pamodzi masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mat. 28:20) Kodi Yesu wakwaniritsadi lonjezo limeneli? Kwazaka 15 zapitazi, mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse yawonjezeka kuchoka pa 70,000 kufika pa mipingo yoposa 100,000. Zimenezi zikutanthauza kuti pamipingo 100 iliyonse, panawonjezeka mipingo yoposa 40. Nanga bwanji za chiwerengero cha Akhristu? M’zaka 15 zimenezi, anthu pafupifupi 4,500,000 anabatizidwa ndipo tinganene kuti anthu oposa 800 ankabatizidwa tsiku lililonse. Zimenezi ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Khristu akutsogolera otsatira ake odzozedwa pamisonkhano yawo yampingo ndiponso akuwathandiza pantchito yawo yopanga ophunzira.

Kapoloyu Ndi Wokhulupirika Ndiponso Wanzeru

11, 12. Kodi kapolo wasonyeza bwanji kuti ndi wokhulupirika ndiponso wanzeru?

11 Popeza kuti Yehova Mulungu ndiponso Yesu Khristu amakhulupirira kwambiri kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, kodi ifeyo sitiyenera kuchita chimodzimodzi? Ndipotu kapoloyu wagwira mokhulupirika ntchito imene wapatsidwa. Mwachitsanzo, magazini a Nsanja ya Olonda akhala akufalitsidwa kwazaka 130. Komanso, tikupitirizabe kulimbikitsidwa ndi misonkhano ya mpingo ndiponso misonkhano ikuluikulu.

12 Kapolo wokhulupirikayu wasonyezanso kuti ndi wanzeru chifukwa amachita zinthu modzichepetsa potsatira malangizo a Yehova. Safotokoza zinthu asanalandire malangizo ochokera kwa Mulungu, komanso sanyalanyaza malangizo aliwonse amene wapatsidwa. Mwachitsanzo, pamene atsogoleri a zipembedzo zonyenga akulekerera kapenanso kuvomereza makhalidwe oipa, kapoloyu amachenjeza za kuopsa kochita zinthu za m’dziko la Satanali. Kapoloyu amakwanitsa kupereka machenjezo anzeru ndiponso a panthawi yake, chifukwa Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu akumudalitsa. Choncho, tiyenera kukhulupirira kwambiri kapoloyu. Komano tingasonyeze motani kuti timakhulupirira kapoloyu?

‘Mukani’ ndi Odzozedwa Pamene Akutsatira Mwanawankhosa

13. Malinga ndi ulosi wa Zekariya, n’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?

13 Buku la Zekariya limanena za “amuna khumi” amene akuuza ‘munthu yemwe ndi Myuda’ kuti: “Tidzamuka nanu.” (Werengani Zekariya 8:23.) Popeza kuti amuna khumi akuuza ‘munthu yemwe ndi Myuda’ kuti tidzamuka “nanu,” zimenezi zikusonyeza kuti Myudayu akuimira gulu la anthu. Masiku ano, Myudayu akuimira Akhristu odzozedwa ndi mzimu omwe ali padziko pano, amene ndi mbali ya “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) “Amuna khumi . . . a manenedwe onse a amitundu,” akuimira khamu lalikulu la nkhosa zina. Mofanana ndi Akhristu odzozedwa amene amatsatira Yesu kulikonse kumene akupita, akhamu lalikulu nawonso amatsatira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Akhamu lalikulu sayenera kuchita manyazi kudzidziwikitsa kuti ndi anzawo a “otenga mbali m’chiitano cha kumwamba.” (Aheb. 3:1) Ndipotu, Yesu sachita manyazi kutchula Akhristu odzozedwa kuti “abale” ake.​—Aheb. 2:11.

14. Kodi abale ake a Khristu tingawathandize motani?

14 Yesu Khristu amaona kuti tikamathandiza abale ake, ndiye kuti tikuthandiza iyeyo. (Werengani Mateyo 25:40.) Choncho, kodi anthu amene akuyembekezera kudzalandira dziko lapansi angathandize bwanji abale ake a Khristu odzozedwa ndi mzimu? Njira yaikulu ndiyo kuwathandiza pa ntchito yolalikira za Ufumu. (Mat. 24:14; Yoh. 14:12) Pamene chiwerengero cha odzozedwa chakhala chikucheperachepera pa zaka zapitazi, chiwerengero cha nkhosa zina chikuchulukirachulukira. Ankhosa zina akamagwira nawo ntchito yolalikira, mwinanso kuchita utumiki wanthawi zonse, amakhala akuthandiza odzozedwa pokwaniritsa ntchito yawo yopanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Njira inanso imene amathandizira pantchitoyi ndiyo kupereka ndalama m’njira zosiyanasiyana.

15. Kodi Mkhristu aliyense ayenera kuona motani chakudya chauzimu chapanthawi yoyenera chochokera kwa kapolo ndiponso zinthu zimene kapoloyu amasankha kuti gulu lichite?

15 Kodi ifeyo patokha timaona bwanji chakudya chauzimu chimene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa kudzera m’mabuku ofotokoza Baibulo ndiponso kudzera m’misonkhano yachikhristu? Kodi timadya moyamikira ndiponso timapindula ndi chakudya chimenechi? Kodi timaona bwanji zinthu zimene kapoloyu wasankha kuti gulu lichite? Tikamatsatira mofunitsitsa malangizo a kapoloyu timasonyeza kuti timagonjera dongosolo la Yehova.​—Yak. 3:17.

16. N’chifukwa chiyani Akhristu onse amafunika kumvera abale ake a Yesu?

16 Yesu anati: “Nkhosa zanga zimamva mawu anga, ine ndimazidziwa, izonso zimanditsatira.” (Yoh. 10:27) Izi ndi zimene Akhristu odzozedwa amachita. Nanga bwanji anthu amene amatsatira odzozedwawo? Nawonso amafunika kumvera Yesu ndi abale ake. Ndipotu abale ake a Yesu amenewa anapatsidwa udindo waukulu wolangiza ndi kusamalira mwauzimu anthu a Mulungu. Kodi tingasonyeze motani kuti timamvera mawu a abale ake a Khristu?

17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timamvera kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?

17 Masiku ano, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amaimiridwa ndi Bungwe Lolamulira limene likutsogolera ntchito yolalikira za Ufumu padziko lonse. Abale amene ali m’Bungwe Lolamulira ndi akulu odzozedwa ndi mzimu amene akhala akutumikira Mulungu kwanthawi yaitali ndipo ndi ‘amenedi akutitsogolera.’ (Aheb. 13:7) Abale odzozedwawa ali ndi “zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye,” chifukwa amasamalira anthu olengeza Ufumu pafupifupi 7,000,000, m’mipingo yoposa 100,000 padziko lonse. (1 Akor. 15:58) Kuti tisonyeze kuti timamvera kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, tiyenera kugwirizana kwambiri ndi Bungwe Lolamulira.

Anthu Omvera Kapoloyu Amadalitsidwa

18, 19. (a) Kodi anthu amene amamvera kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amadalitsidwa motani? (b) Malinga ndi zimene taphunzirazi, kodi tiyenera kutsimikiza mtima za chiyani?

18 Kuyambira pamene kapolo wokhulupirika ndi wanzeru anaikidwa, iye wakhala ‘akutembenuza ambiri kuti atsate chilungamo.’ (Dan. 12:3) Ena mwa anthu amenewa ndi omwe akuyembekezera kudzapulumuka pamene dongosolo la zinthu loipali likuwonongedwa. Amenewatu ndi madalitso ochititsa chidwi kwambiri.

19 M’tsogolo muno, ‘mzinda woyera, Yerusalemu watsopano, [yemwe ndi anthu 144,000] udzatsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu, utakonzedwa ngati mkwatibwi wokongoletsedwera mwamuna wake.’ Zikadzatero, kodi n’chiyani chidzachitikire anthu omwe akhala akumvera mawu a kapolo? Baibulo limati: “Mulungu mwini adzakhala nawo. Iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” (Chiv. 21:2-4) Motero, tiyeni tipitirize kumvera Khristu ndiponso abale ake okhulupirika odzozedwa ndi mzimu.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yehova amakhulupirira kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?

• Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yesu Khristu amakhulupirira kwambiri gulu la kapolo?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira mdindo wokhulupirika?

• Kodi tingasonyeze motani kuti timakhulupirira kapolo?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 25]

Kodi mukudziwa amene Yehova wam’sankha kuti adzakhale mkwatibwi wa Mwana wake?

[Zithunzi patsamba 26]

Yesu Khristu waika kapolo wokhulupirika ndi wanzeru kuti aziyang’anira “zinthu” zake

[Chithunzi patsamba 27]

Tikamagwira ntchito yolalikira, timakhala tikuthandiza Akhristu odzozedwa