Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amishonale Analimbikitsidwa Kutsanzira Yeremiya

Amishonale Analimbikitsidwa Kutsanzira Yeremiya

Mwambo Womaliza Maphunziro A Gileadi​—Gulu la Nambala 125

Amishonale Analimbikitsidwa Kutsanzira Yeremiya

“KALASI ya Gileadi imeneyi ndi yosaiwalika,” anatero Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira. Iye ananena mawu amenewa polankhula kwa anthu 6,156, amene anasonkhana pa mwambo womaliza maphunziro wa kalasi ya nambala 125 ya Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo. Mwambo umenewu unachitika pa September 13, 2008. Anthu 56 amene anamaliza maphunziro awo m’kalasiyi achititsa kuti chiwerengero cha amishonale amene akhala akutumizidwa kuchokera ku Sukulu ya Gileadi kupita ku mayiko osiyanasiyana “mpaka kumalekezero a dziko lapansi,” chipose 8,000.​—Mac. 1:8.

M’bale Jackson yemwe anali tcheyamani pamwambowu anati: “Utumiki wanu udzapita patsogolo anthu akamakukhulupirirani.” Kenako, iye anafotokozera amishonalewo zinthu zinayi zimene zingachititse kuti anthu aziwakhulupirira. Zinthuzo ndi izi: Kukhala ndi maganizo abwino, kusonyeza chitsanzo chabwino, kuphunzitsa zinthu zochokera m’Mawu a Mulungu ndiponso kukhala ndi cholinga chodziwikitsa dzina la Yehova.

David Schafer, yemwe amathandizira m’Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa, anakamba nkhani yakuti, “Kodi Mudzamvetsa Chilichonse?” Iye anatsimikizira ophunzirawo kuti ‘angamvetse zonse’ zofunika pautumiki wawo ngati atapitiriza kufuna Yehova ndiponso kutsatira modzichepetsa malangizo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Miy. 28:5; Mat. 24:45.

Kenako, John E. Barr wa m’Bungwe Lolamulira anakamba nkhani yakuti, “Musalole Chilichonse Kukusiyanitsani ndi Chikondi cha Mulungu.” Malangizo achikondi amene M’bale Barr anapereka, analimbikitsa ophunzirawo ndiponso makolo awo kuti asadere nkhawa ndi zimene ophunzirawo angakakumane nazo mu utumiki wawo. Iye anafotokoza kuti: “Munthu amakhala wotetezeka kwambiri akakhala m’chikondi cha Mulungu.” Palibe chilichonse chimene chingasiyanitse amishonalewo ndi chikondi cha Mulungu, pokhapokha ngati iwowo asankha kudzisiyanitsa okha.

Sam Roberson wa m’Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu za ku Patterson analimbikitsa omverawo kuti avale “chovala chabwino kwambiri.” Mwa kuphunzira ndi kugwiritsa ntchito zimene Yesu anachita, amishonalewo ‘angavale Ambuye Yesu Khristu.’ (Aroma 13:14) Kenako, M’bale William Samuelson amene amayang’anira Dipatimenti Yoyang’anira Sukulu za ku Patterson anafotokoza kuti zimene zimachititsa kuti munthu azilemekezedwa si mmene anthu ena amaonera munthuyo, koma mmene Mulungu amamuonera.

Michael Burnett, mmodzi wa aphunzitsi a sukuluyi, anafunsa ophunzirawo kuti afotokoze zimene anakumana nazo muutumiki wa kumunda. Ophunzirawa anapezabe anthu achidwi ngakhale kuti panthawi ya sukuluyi, ambiri mwa iwo ankalalikira m’gawo limene limalalikidwa kawirikawiri. Gerald Grizzle wa m’Dipatimenti Yoona za Misonkhano Yachigawo, anafunsa mafunso abale atatu omwe panthawiyi ankachita maphunziro a m’Sukulu ya Anthu a m’Komiti za Nthambi. Zimene abalewa ananena zinathandiza amishonale atsopanowo kukonzekera zimene angakakumane nazo kumayiko amene angatumizidwe.

David Splane, wa m’Bungwe Lolamulira amenenso anachita maphunziro a Gileadi m’kalasi ya nambala 42, anakamba nkhani yakuti, “Tsanzirani Yeremiya.” Ngakhale kuti Yeremiya ankachita mantha ndi ntchito imene anapatsidwa, Yehova anamulimbikitsa. (Yer. 1:7, 8) Mulungu adzachitanso chimodzimodzi ndi amishonale atsopanowo. M’bale Splane anati: “Mukasemphana maganizo ndi winawake, ganizirani makhalidwe abwino 10 a munthuyo ndi kuwalemba. Ngati mukulephera kulemba makhalidwe okwanira 10, ndiye kuti simukumudziwa bwino munthu ameneyo.”

Yeremiya anali ndi mtima wodzipereka. Panthawi ina atafuna kusiya ntchito imene anapatsidwa, anapemphera ndipo Yehova anamulimbikitsa. (Yer. 20:11) M’bale Splane anati: “Mukakhumudwa ndi zinazake, m’fotokozereni Yehova zimenezo. Ndipo mungadabwe kwambiri kuona mmene Yehova angakuthandizireni.”

Pamapeto pamwambowu, tcheyamani anakumbutsa omvera kuti amishonalewo aphunzira njira zambiri zimene zingachititse kuti anthu aziwakhulupirira. Zimenezi zingawathandize kuti akamakalalikira kumayiko amene angawatumize, uthenga wawo uzikakhala wogwira mtima kwambiri.​—Yes. 43:8-12.

[Bokosi patsamba 22]

ZA OPHUNZIRAWO

Chiwerengero cha mayiko amene ophunzira achokera: 6

Chiwerengero cha mayiko amene atumizidwa: 21

Chiwerengero cha ophunzira: 56

Avereji ya zaka za kubadwa: 32.9

Avereji ya zaka zimene akhala m’choonadi: 17.4

Avereji ya zaka zimene akhala mu utumiki wa nthawi zonse: 13

[Chithunzi patsamba 23]

Gulu la Nambala 125 la Omaliza Maphunziro a Sukulu ya Gileadi ya Watchtower Yophunzitsa Baibulo

Pam’ndandanda umene uli pansipa, mizera yayambira kutsogolo kupita kumbuyo, ndipo mumzera uliwonse mayina tawandandalika kuyambira kumanzere kupita kumanja.

(1) Hodgson, A.; Wall, A.; Beerens, K.; Hortelano, M.; Newman, L.; De Caso, A. (2) Jenkins, J.; Jarzemski, T.; Méndez, N.; Corona, V.; Canalita, L. (3) Fryer, H.; Savage, M.; Tidwell, K.; Erickson, N.; Dyck, E.; McBeath, R. (4) Perez, L.; Puse, L.; Skidmore, A.; Young, B.; McBride, N.; Rondón, P.; Goodman, E. (5) Beerens, M.; Ferguson, J.; Pearson, N.; Chapman, L.; Wardle, J.; Canalita, M. (6) Perez, P.; De Caso, D.; Young, T.; Rondón, D.; Goodman, G.; Jenkins, M.; Dyck, G. (7) Corona, M.; Wall, R.; Puse, S.; Méndez, F.; Jarzemski, S.; Savage, T. (8) Newman, C.; Ferguson, D.; Skidmore, D.; Erickson, T.; McBride, J.; Pearson, M.; Chapman, M. (9) Hodgson, K.; Wardle, A.; McBeath, A.; Tidwell, T.; Fryer, J.; Hortelano, J.