Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mapemphero Anu Amagwirizana ndi Zimene Yesu Anaphunzitsa?

Kodi Mapemphero Anu Amagwirizana ndi Zimene Yesu Anaphunzitsa?

Kodi Mapemphero Anu Amagwirizana ndi Zimene Yesu Anaphunzitsa?

“Yesu atatsiriza mawu amenewa, khamu la anthulo linakhudzidwa moti anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake.”​—MAT. 7:28.

1, 2. N’chifukwa chiyani khamu la anthu linazizwa ndi mmene Yesu anaphunzitsira?

TONSEFE tiyenera kutsatira mfundo zofunika kwambiri zimene Yesu Khristu, yemwe ndi Mwana wobadwa yekha wa Mulungu, anaphunzitsa. Palibe munthu wina amene anaphunzitsapo ngati iyeyo. N’chifukwa chake anthu anadabwa kwambiri ndi mmene Yesu anaphunzitsira pa ulaliki wake wa pa phiri.​—Werengani Mateyo 7:28, 29.

2 Iye sankaphunzitsa ngati alembi, omwe ziphunzitso zawo zinali zochokera kwa anthu opanda ungwiro. Khristu ankaphunzitsa “monga munthu waulamuliro” chifukwa chakuti zimene ankalankhula zinali zochokera kwa Mulungu. (Yoh. 12:50) Tsopano tiyeni tione mmene mfundo zinanso zimene Yesu anaphunzitsa pa ulaliki wake wa pa phiri, zingatithandizire popemphera.

Tisamapemphere Ngati Mmene Onyenga Amachitira

3. Fotokozani mwachidule zimene Yesu ananena pa Mateyo 6:5.

3 Pemphero ndi mbali yofunika kwambiri pa kulambira koona, ndipo tiyenera kupemphera kwa Yehova nthawi zonse. Koma mapemphero athu ayenera kukhala ogwirizana ndi zimene Yesu anaphunzitsa pa ulaliki wake wa pa phiri. Iye anati: “Pamene mukupemphera, musamachite ngati onyengawo; pakuti iwo amakonda kuimirira m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona. Ndithu ndikukuuzani, Amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse.”​Mat. 6:5.

4-6. (a) N’chifukwa chiyani Afarisi ankakonda kupemphera ‘ataimirira m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu’? (b) Kodi anthu onyengawa ‘ankalandiriratu mphoto yawo yonse’ motani?

4 Popemphera, ophunzira a Yesu sanafunike kutsanzira anthu “onyenga,” monga Afarisi, omwe ankadzionetsera ngati olungama akakhala pagulu. (Mat. 23:13-32) Anthu amenewa ankakonda kupemphera ‘ataimirira m’masunagoge ndi m’mphambano za misewu ikuluikulu.’ N’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Iwo ankatero kuti “anthu aziwaona.” Ayuda a m’nthawi ya Yesu ankakonda kusonkhana n’kumapemphera panthawi yopereka nsembe ku kachisi (cha m’ma 9 koloko m’mawa ndi m’ma 3 koloko masana). Anthu ambiri okhala ku Yerusalemu ankapempherera limodzi ndi anthu osonkhana ku kachisiko. Kunja kwa mzindawo, Ayuda okhulupirika kwambiri pachipembedzo chawo ankakonda kupemphera kawiri patsiku ‘ataimirira m’masunagoge.’​—Yerekezerani ndi Luka 18:11, 13.

5 Popeza kuti anthu ambiri nthawi ya mapempherowa inkawakwanira ali kutali ndi kachisi kapena sunagoge, mwina ankangopemphera pamalo alionse pamene anali panthawiyo. Ena ankakonda zoti nthawi ya mapempheroyi iziwakwanira ali “m’mphambano za misewu ikuluikulu.” Cholinga chawo chinali choti anthu odutsa pa mphambanopo “aziwaona.” Anthu onyengawa ankakonda ‘kupereka mapemphero ataliatali’ n’cholinga choti anthu aziwasirira. (Luka 20:47) Koma ife sitiyenera kuchita zimenezi.

6 Yesu ananena kuti onyengawa anali ‘kulandiriratu mphoto yawo yonse.’ Iwo ankafunitsitsa kutamandidwa ndi anthu, ndipo mphoto yawo inali yomweyo basi. Inali mphoto yawo yonse, chifukwa chakuti Yehova sakanayankha mapemphero awo achinyengowo. Komabe mogwirizana ndi zimene Yesu anafotokoza pambuyo pake, Mulungu akanayankha mapemphero a otsatira oona a Khristu.

7. Kodi malangizo akuti tizipemphera tili ‘m’chipinda chathu’ akutanthauza chiyani?

7 “Koma iwe popemphera, lowa m’chipinda chako pawekha ndi kutseka chitseko, ndipo pemphera kwa Atate wako amene ali kosaoneka; ukatero Atate wako amene amaona kuchokera kosaonekako adzakubwezera.” (Mat. 6:6) Ponena kuti munthu ayenera kupemphera ali m’chipinda chotseka, Yesu sanatanthauze kuti munthu sayenera kuimira mpingo m’pemphero. Iye anapereka malangizowa pofuna kuletsa anthu kupemphera pagulu n’cholinga choti atamandidwe. Ifenso tifunika kukumbukira malangizo amenewa tikapatsidwa mwayi woimira anthu a Mulungu m’pemphero. Tiyeneranso kugwiritsa ntchito malangizo otsatirawa amene Yesu anapereka pankhani ya pemphero.

8. Malinga ndi Mateyo 6:7, kodi ndi chinthu cholakwika chiti chimene tiyenera kupewa popemphera?

8 “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza, muja amachitira amitundu, chifukwa iwo amaganiza kuti akanena mawu ambirimbiri awamvera.” (Mat. 6:7) Apa, Yesu anatchulanso chinthu china cholakwika popemphera, chomwe ndi kubwerezabwereza mawu. Iye sankatanthauza kuti tisamabwereze mfundo zochokera pansi pamtima ndiponso mawu osonyeza kuyamikira. Ndipo iye ali m’munda wa Getsemane, usiku woti aphedwa mawa lake, anapemphera mobwerezabwereza ‘potchula mawu omwe’ anali atawatchulapo kale.​—Maliko 14:32-39.

9, 10. Kodi mfundo yakuti mapemphero athu asamakhale obwerezabwereza ikutanthauza chiyani?

9 Sitiyenera kutengera anthu “amitundu” amene amangobwerezabwereza mapemphero awo. Popemphera, iwo amatchula “mobwerezabwereza” mawu ochuluka olowezedwa pamtima amene ndi opanda ntchito. Anthu olambira mulungu wonyenga, Baala, anapemphera “kuyambira m’mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife.” Koma kuchita zimenezi sikunawathandize anthu amenewa. (1 Maf. 18:26) Masiku anonso, anthu ambiri amapemphera mapemphero ataliatali mobwerezabwereza poganiza kuti Yehova “awamvera.” Koma Yesu akutithandiza kuzindikira kuti Yehova sasangalala ndi mapemphero ataliatali, okhala ndi ‘mawu ambirimbiri’ komanso obwerezabwereza. Iye ananenanso kuti:

10 “Chotero inu musafanane nawo, chifukwa Mulungu Atate wanu amadziwa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mat. 6:8) Atsogoleri ambiri a chipembedzo chachiyuda ankakhala ngati anthu amitundu chifukwa choti ankakonda kupemphera mapemphero ataliatali. Mapemphero ochokera pansi pamtima, okhala ndi mawu oyamika ndiponso opempha, n’ngofunika kwambiri pa kulambira koona. (Afil. 4:6) Komabe, si bwino kuti tizibwerezabwereza mawu amene tatchula kale poganiza kuti zimenezi n’zimene zingachititse kuti Mulungu atimvere. Tikamapemphera, tizikumbukira kuti tikulankhula ndi Mulungu amene ‘amadziwa zimene tikufuna, tisanapemphe n’komwe.’

11. Tikapatsidwa mwayi woimira ena m’pemphero, kodi tiyenera kukumbukira mfundo ziti?

11 Zimene Yesu anaphunzitsa pankhani ya mapemphero osavomerezeka, ziyenera kutikumbutsa kuti Mulungu samva pemphero chifukwa choti ndi lalitali kapena lili mawu ogometsa. Tiyeneranso kukumbukira kuti tikapatsidwa mwayi woimira ena m’pemphero, sinthawi yoti tiwagometse ndi zolankhula zathu ndiponso kuti anthuwo achite kufika potopa ndi kutalika kwa pempherolo n’kuyamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi litha nthawi yanji?’ Komanso, si bwino kupezerapo mwayi wopereka zilengezo kapena uphungu kwa anthuwo m’pemphero, chifukwa kuchita zimenezo n’kosagwirizana m’pang’ono pomwe ndi zimene Yesu anaphunzitsa pa ulaliki wake wa pa phiri.

Yesu Anatiphunzitsa Mmene Tingapempherere

12. Kodi mfundo yakuti “dzina lanu liyeretsedwe” mungaifotokoze motani?

12 Ngakhale kuti Yesu anachenjeza ophunzira ake za zinthu zimene ayenera kupewa popemphera, iye anawaphunzitsanso mmene angapempherere. (Werengani Mateyo 6:9-13.) Cholinga cha pemphero lake lachitsanzo sichinali choti anthu azililoweza n’kumalibwerezabwereza. M’malomwake, limatipatsa chithunzi cha mmene mapemphero athu ayenera kukhalira. Mwachitsanzo, m’pempheroli Yesu anayamba ndi kutchula za Mulungu, ndipo anati: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) M’poyenera kutchula Yehova kuti “Atate wathu” chifukwa ndiye Mlengi wathu, yemwe amakhala “kumwamba,” komwe ndi kutali kwambiri ndi dziko lapansili. (Deut. 32:6; 2 Mbiri 6:21; Mac. 17:24, 28) Mawu akuti “wathu” ayenera kutikumbutsa mfundo yakuti okhulupirira anzathu alinso paubwenzi wolimba ndi Mulungu. Ponena kuti “dzina lanu liyeretsedwe,” timakhala tikupempha Yehova kuti achite zinthu zimene zingayeretse dzina lake chifukwa chakuti lakhala likutonzedwa kuchokera pamene anthu anam’pandukira mu Edeni. Poyankha pemphero limeneli, Yehova adzachotsa kuipa konse padziko lapansi pano ndipo akadzatero dzina lake lidzakhala loyera.​—Ezek. 36:23.

13. (a) Kodi pempho lakuti “ufumu wanu ubwere” lidzayankhidwa motani? (b) Kodi kuchitika kwa chifuniro cha Mulungu padziko lapansi pano kudzaphatikizapo chiyani?

13 “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mat. 6:10) Mogwirizana ndi mfundo ya m’pemphero lachitsanzo imeneyi, tizikumbukira kuti ‘ufumuwu’ ndi ulamuliro wa Yehova kudzera m’boma laumesiya limene lili m’manja mwa Khristu limodzi ndi “opatulika” amene amaukitsidwira kumwamba. (Dan. 7:13, 14, 18; Yes. 9:6, 7) Tikamapemphera kuti Ufumu wa Mulungu “ubwere” timakhala tikupempha kuti ufumuwu udzawononge onse omwe amatsutsa ulamuliro wa Mulungu padziko lapansi pano. Zimenezi zichitika posachedwapa ndipo zidzachititsa kuti dziko lonse lapansi likhale paradaiso mmene mudzakhala chilungamo, mtendere ndiponso zinthu zamwanaalirenji. (Sal. 72:1-15; Dan. 2:44; 2 Pet. 3:13) Panopa chifuniro cha Yehova chikuchitika kumwamba, ndipo tikamapemphera kuti chichitike pansi pano, timakhala tikupempha kuti Mulungu achite chifuniro chake padziko lapansili, zimene zikuphatikizapo kuwononga anthu onse otsutsana naye, ngati mmene anachitira m’nthawi zakale.​—Werengani Salmo 83:1, 2, 13-18.

14. N’chifukwa chiyani kupempha “chakudya chathu cha lero” kuli koyenera?

14 “Mutipatse ife lero chakudya chathu cha lero.” (Mat. 6:11; Luka 11:3) Tikamatchula zimenezi m’pemphero lathu timakhala tikupempha Mulungu kuti atipatse chakudya chofunikira ‘patsikulo.’ Tikamachita zimenezi timasonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro kuti Yehova ndi amene angatipatse zinthu zofunika pamoyo wathu watsiku ndi tsiku. Komabe, limeneli si pemphero lakuti Yehova atiwonjezere zinthu zimene tili nazo kale. Pempho limeneli likutikumbutsa zimene Mulungu anauza Aisiraeli pankhani yotola mana, kuti aliyense ‘aziola muyeso wa tsiku pa tsiku lake.’​—Eks. 16:4.

15. Fotokozani tanthauzo la pempho lakuti “mutikhululukire zolakwa zathu, pakuti ifenso takhululukira amene atilakwira.”

15 Pempho lotsatira m’pemphero lachitsanzoli likusonyeza chinthu chimene tiyenera kuchita. Yesu anati: “Ndipo mutikhululukire zolakwa zathu, pakuti ifenso takhululukira amene atilakwira.” (Mat. 6:12) Uthenga Wabwino wa Luka umasonyeza kuti “zolakwa” zimenezi ndi “machimo.” (Luka 11:4) Ngati “takhululukira” anthu amene atilakwira, nafenso Yehova angatikhululukire. (Werengani Mateyo 6:14, 15.) Choncho, tiyenera kukhululukira ena ndi mtima wonse.​—Aef. 4:32; Akol. 3:13.

16. Kodi pempho lokhudza mayesero ndiponso lakuti tipulumutsidwe kwa woipayo likutanthauza chiyani?

16 “Musatilowetse m’mayesero, koma mutilanditse kwa woipayo.” (Mat. 6:13) Kodi pempho lakuti “musatilowetse m’mayesero” ndiponso lakuti “mutilanditse kwa woipayo,” likutanthauza chiyani? Mfundo yodziwika ndi yakuti: Yehova satiyesa kuti tichite tchimo. (Werengani Yakobe 1:13.) ‘Woyesa’ ndi Satana, yemwe ndi ‘woipa.’ (Mat. 4:3) Komabe, Baibulo limasonyeza kuti nthawi zina Mulungu amalola kuti zinthu zina zitichitikire. (Rute 1:20, 21; Mlal. 11:5) Choncho, pempho lakuti “musatilowetse m’mayesero,” likusonyeza kupempha Yehova kuti asalole kuti tigonje poyesedwa. Ndipo pempho lakuti “mutilanditse kwa woipayo,” likusonyeza kupempha Yehova kuti asalole Satana kutigonjetsa. Motero, n’zosakayikitsa kuti ‘Mulungu sadzalola kuti tiyesedwe kufika pamene sitingapirire.’​—Werengani 1 Akorinto 10:13.

‘Pemphanibe, Funafunanibe, Gogodanibe’

17, 18. Kodi mawu akuti ‘pemphanibe, funafunanibe ndiponso gogodanibe’ akutanthauza chiyani?

17 Mtumwi Paulo analimbikitsa okhulupirira anzake kuti: “Limbikiranibe kupemphera.” (Aroma 12:12) Yesu anatchula mfundo yofanana ndi imeneyi pamene anati: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani; funafunanibe, ndipo mudzapeza, gogodanibe, ndipo adzakutsegulirani. Pakuti aliyense wopempha amalandira, ndipo aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.” (Mat. 7:7, 8) N’koyenera kupitiriza ‘kupempha’ chilichonse chimene chikugwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mogwirizana ndi mawu a Yesu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Ife timam’dalira [Mulungu] kuti chilichonse chimene tingapemphe mogwirizana ndi chifuniro chake, amatimvera.”​—1 Yoh. 5:14.

18 Malangizo a Yesu akuti ‘pemphanibe ndiponso funafunanibe,’ akutanthauza kuti tiyenera kumapemphera mwakhama. Ndi bwinonso kuti tipitirize ‘kugogoda’ kuti tidzalowe mu Ufumu wa Mulungu, n’kudzasangalala ndi madalitso a Ufumuwo. Kodi tingakhale ndi chikhulupiririro choti Mulungu adzayankha mapemphero athu? Inde, tikakhala okhulupirika kwa Yehova, chifukwa Khristu anati: “Aliyense wopempha amalandira, ndipo aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.” Zinthu zambiri zimene zachitika pamoyo wa atumiki a Yehova zimasonyeza kuti iye alidi “Wakumva pemphero.”​—Sal. 65:2.

19, 20. Malinga ndi mawu a Yesu a pa Mateyo 7:9-11, kodi Yehova amafanana motani ndi bambo wachikondi?

19 Yesu anayerekezera Mulungu ndi bambo wachikondi amene amapatsa ana ake zinthu zabwino. Tayerekezerani kuti munalipo pa ulaliki wa pa phiriwu pamene Yesu anati: “Ndani pakati panu amene mwana wake atam’pempha mkate, iye angam’patse mwala? Kapena atam’pempha nsomba, iye n’kum’patsa njoka? Chotero ngati inuyo​—ngakhale kuti ndinu oipa​—mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka zinthu zabwino kwa onse om’pempha!”​Mat. 7:9-11.

20 Bambo, ngakhale kuti iye ndi ‘woipa’ chifukwa cha uchimo wobadwa nawo, amakonda ana ake. Iye sangapusitse mwana wake, koma angayesetse kum’patsa “mphatso zabwino.” Yehova amatikonda ndipo amationa ngati ana ake, motero amatipatsa “mphatso zabwino,” monga mzimu wake woyera. (Luka 11:13) Mzimuwu ungatithandize kuti tizitumikira Yehova movomerezeka. Ndipotu Yehova amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi mtulo uliwonse wangwiro.”​—Yak. 1:17.

Pitirizani Kupindula ndi Zimene Yesu Anaphunzitsa

21, 22. Kodi ulaliki wa pa phiri ndi wochititsa chidwi chifukwa chiyani, ndipo inuyo mumamva bwanji mukamaphunzira mfundo zimene Yesu anaphunzitsazi?

21 Zoonadi, ulaliki wa pa phiri umaposa ulaliki wina uliwonse umene unalalikidwapo padziko lapansi pano. Ulalikiwu uli ndi mfundo zambiri zauzimu ndiponso zomveka bwino. Mfundo zimene taona m’nkhani zapitazi ndiponso m’nkhani ino, zatithandiza kuona kuti tingapindule kwambiri pogwiritsa ntchito malangizo a ulalikiwu. Zimene Yesu anaphunzitsa pa ulaliki umenewu zingatithandize kukhala ndi moyo wabwino panopo ndiponso m’tsogolo.

22 M’nkhanizi, taona mfundo zochepa chabe za ulaliki wa Yesu wa pa phiri. N’chifukwa chake anthu amene anamvera ulalikiwu “anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake.” (Mat. 7:28) Sitikukayikira n’komwe kuti nafenso tidzamva chimodzimodzi tikamaphunzira mfundo zimenezi ndi zinanso zamtengo wapatali zimene Mphunzitsi Waluso, Yesu Khristu, anaphunzitsa.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yesu ananena chiyani pankhani ya mapemphero achinyengo?

• N’chifukwa chiyani sitiyenera kupemphera mobwerezabwereza mawu?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene Yesu anatchula m’pemphero lake lachitsanzo?

• Kodi tingapitirize motani ‘kupempha, kufunafuna ndi kugogoda’?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 15]

Yesu anadzudzula anthu onyenga amene ankapemphera n’cholinga choti anthu awaone

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi mukudziwa chifukwa chake kupempha chakudya chathu cha lero kuli koyenera?