Kodi Muyenera Kuumirira Zokonda Zanu?
Kodi Muyenera Kuumirira Zokonda Zanu?
YEREKEZERANI kuti mukuona ana awiri akusewera pamodzi. Mwana wina akulanda mnzake chidole chimene amachikonda kwambiri ndipo akufuula kuti: “Ndi changa chimenechi!” Zimenezi zikusonyeza kuti kungoyambira tili ana, anthu opanda ungwirofe timakhala ndi mtima wodzikonda. (Gen. 8:21; Aroma 3:23) Ndipotu dzikoli limalimbikitsa mtima umenewu, choncho pamafunika khama kuti tiupewe. Tikapanda kusamala ndi mtima wodzikondawu, tikhoza kumangokhumudwitsa ena ndiponso kuwononga ubwenzi wathu ndi Yehova.—Aroma 7:21-23.
Pofuna kutilimbikitsa kuti tiziganizira mmene zochita zathu zingakhudzire anthu ena, mtumwi Paulo analemba kuti: “Zinthu zonse ndi zololeka; koma si zonse zimene zili zaphindu. Zinthu zonse ndi zololeka; koma si zonse zili zomanga.” Paulo analembanso kuti: “Pewani kukhala okhumudwitsa.” (1 Akor. 10:23, 32) Choncho, pankhani zokhudza zokonda zathu, tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimalolera kusachita zokonda zanga n’cholinga choti ndisasokoneze mtendere mumpingo? Kodi ndine wokonzeka kutsatira mfundo za m’Baibulo ngakhale kuti kuchita zimenezo kungakhale kovuta?’
Posankha Ntchito
Anthu ambiri amaona kuti ndi ufulu wawo kusankha ntchito imene akufuna ndipo amati zimene asankhazo sizingakhudze anthu ena. Koma taonani zimene zinachitikira bambo wina wamalonda m’tawuni ina yaing’ono ku South America. Iye anali wokonda kutchova njuga ndiponso kumwa mowa mwauchidakwa. Koma moyo wake unasintha kwambiri atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, n’kumagwiritsa ntchito zimene anali kuphunzirazo. (2 Akor. 7:1) Atasonyeza chidwi chofuna kumalalikira limodzi ndi mpingo, mkulu wina mumpingomo anam’pempha kuti aganizire mofatsa za mtundu wa bizinesi yake. Kwazaka zambiri, bamboyu ankagulitsa mowa winawake wamphamvu kwambiri wopangidwa kuchokera ku nzimbe. Mowawu umagwiritsidwa ntchito zosiyanasiyana koma anthu a m’tawuni ya bamboyu amausakaniza ndi zakumwa zina zoziziritsa kukhosi n’cholinga choti akamwa, aledzere. Anthu ambiri a m’tawuniyi ankagula mowa umenewu kuchokera kwa iyeyo.
Bamboyu anazindikira kuti angaipitse mbiri ya mpingo ndiponso ubwenzi wake ndi Mulungu ungawonongeke ngati atamalalikira koma akupitirizabe kugulitsa mowawo. Ngakhale kuti anali ndi udindo wosamalira banja lake lalikulu, iye anasiya bizinesi yakeyi. Tsopano akuchita bizinesi yogulitsa mapepala, yomwe imamuthandiza kusamalira banja lake. Panopa, bamboyu, mkazi wake ndiponso awiri mwa ana awo asanu, anabatizidwa ndipo akulalikira uthenga wabwino mwachangu ndiponso ndi ufulu wa kulankhula.
Posankha Anthu Ocheza Nawo
Kodi kucheza ndi anthu omwe si Akhristu anzathu ndi nkhani yaing’ono yoti munthu akhoza kungosankha zimene akufuna, kapena ndi nkhani yokhudza mfundo zina za m’Baibulo? Taganizirani zimene zinachitikira mlongo wina yemwe ankafuna kupita ku phwando ndi mnyamata wina amene si Mboni. Ngakhale kuti anthu ena anamuchenjeza za kuopsa kochita zimenezi, iye anaumirira n’kunena kuti ndi ufulu wake kupita ku phwandolo. Atangofika kuphwandoko anapatsidwa zakumwa zimene anathiramo mankhwala amphamvu kwambiri ogonetsa tulo. Koma patapita maola angapo, anadzuka n’kuzindikira kuti mnyamata yemwe ankati ndi mnzake uja wamugwiririra.—Yerekezerani ndi Genesis 34:2.
Ngakhale kuti sinthawi zonse pamene kucheza ndi anthu omwe si Akhristu anzathu kungatilowetse m’mavuto ngati amenewa, Baibulo limatichenjeza kuti: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: Koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miy. 13:20) N’zodziwikiratu kuti kucheza ndi anthu olakwika kungatilowetse m’mavuto. Lemba la Miyambo 22:3 limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” Zochita za anthu amene timacheza nawo zingakhudze moyo wathu ndiponso ubwenzi wathu ndi Mulungu.—1 Akor. 15:33; Yak. 4:4.
Pankhani ya Kavalidwe ndi Kudzikongoletsa
Masitayilo ndi mafashoni a zovala amasintha nthawi ndi nthawi. Koma mfundo za m’Baibulo pankhani ya kuvala ndi kudzikongoletsa sizisintha. Paulo analangiza akazi achikhristu kuti “azidzikongoletsa mwa kuvala moyenera, mwaulemu ndi mwanzeru,” ndipo mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa amuna. (1 Tim. 2:9) Apa, Paulo sankalimbikitsa Akhristu kuvala zovala zosaoneka bwino, kapena kuti azikonda zovala zofanana. Kuvala mwaulemu kumatanthauza kuvala modzilemekeza komanso molemekeza anthu ena.
Tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndinganene moona mtima kuti ndimachita zinthu mwaulemu, ngati ndimaumirira kuti ndi ufulu wanga kuvala zovala zimene zingachititse anthu kumangondicheukira? Kodi anthu amandiganizira molakwika ndiponso kukayikira makhalidwe anga chifukwa cha mmene ndimavalira?’ Pankhaniyi, tingapewe ‘kuchita chilichonse chokhumudwitsa’ anthu, mwa ‘kusasamala zofuna zathu zokha, koma kusamalanso zofuna za ena.’—2 Akor. 6:3; Afil. 2:4.
Pankhani Zokhudza Ndalama
Anthu ena mumpingo wa ku Korinto atalakwirana ndi kuchitirana zachinyengo, Paulo anawalembera kuti: “Bwanji osangolola kulakwiridwa? Bwanji osalola kuberedwa?” Paulo analangiza Akhristuwo kuti azikhululukirana m’malo motengerana kukhoti. (1 Akor. 6:1-7) M’bale wina m’dziko la United States, yemwe analembedwa ntchito ndi m’bale, anagwiritsa ntchito malangizo amenewa. Iye anasemphana maganizo ndi m’baleyo pankhani ya malipiro ake. Potsatira mfundo za m’Malemba, iwo anakambirana nkhaniyi maulendo angapo, koma sizinathandize. Kenako, abalewa anapita ndi nkhaniyi kwa akulu ‘mumpingo.’—Mat. 18:15-17.
Koma n’zomvetsa chisoni kuti nkhaniyi sinathe ngakhale kuti iwo anachita zimenezi. M’bale yemwe analembedwa ntchitoyu atapemphera kwanthawi yaitali za nkhaniyi, anaganiza zongosiya ndalama zimene ankaona kuti anayenera kupatsidwazo. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Iye anati: “Nkhani imeneyi inkandisowetsa mtendere ndiponso kundithera nthawi imene ndikanaigwiritsa ntchito pazinthu zauzimu.” Atachita zimenezi, m’baleyu anaona kuti wayambiranso kukhala ndi chimwemwe komanso anaona kuti Yehova wayambiranso kudalitsa utumiki wake.
Ngakhale Pazinthu Zazing’ono
Kusaumirira pa zokonda zathu ngakhale pazinthu zazing’ono kumabweretsa madalitso. Patsiku loyamba la msonkhano wachigawo, m’bale ndi mkazi wake omwe ndi apainiya, anafika mwamsanga pamalo a msonkhanowo ndi kukhala pamipando imene ankaifuna. Msonkhanowo utangoyamba, banja lina lomwe lili ndi ana ambiri linafika pamalo a msonkhanowo. Apainiya aja ataona kuti banjalo likufunafuna malo okhala okwanira, iwo anachoka pamipando yomwe anakhala. Izi zinachititsa kuti banja lalikulu lija likhale pamodzi. Patatha masiku angapo pambuyo pa msonkhanowo, apainiya aja analandira kalata yowathokoza yochokera ku banja limene analipatsa malo lija. M’kalatayo, banjali linafotokoza kuti linakhumudwa kwambiri chifukwa chofika mochedwa pamsonkhano uja. Koma linakhala ndi chimwemwe chifukwa cha kukoma mtima kwa apainiya aja.
Tikapeza mwayi wochita zinthu zimene anzathu amakonda m’malo mwa zathu, tiyeni tichite zimenezo mofunitsitsa. Posonyeza chikondi chimene “sichisamala zofuna zake zokha,” timathandizira kuti mumpingo mukhale mtendere ndiponso kuti tizikhala pamtendere ndi anzathu. (1 Akor. 13:5) Komanso chofunika kwambiri n’chakuti timapitiriza kukhala paubwenzi ndi Yehova.
[Chithunzi patsamba 20]
Kodi ndinu wofunitsitsa kusaumirira zokonda zanu pankhani yosankha zovala?
[Chithunzi pamasamba 20, 21]
Kodi ndinu wokonzeka kupatsa abale anu malo amene munakhala?