Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 2
Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 2
KODI n’chiyani chomwe chidzachitikire anthu omwe amalambira Yehova Mulungu ndiponso amene samulambira? Nanga n’chiyani chidzachitikire Satana ndi ziwanda zake? Kodi anthu omvera adzalandira madalitso otani mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu? Mayankho a mafunso amenewa ndiponso a mafunso ena ofunika kwambiri akupezeka mu Chivumbulutso 13:1 mpaka 22:21. * Machaputala amenewa ali ndi masomphenya 9 omalizira mwa masomphenya 16 omwe mtumwi Yohane anaona cha m’ma 90 C.E.
Yohane analemba kuti: “Wosangalala ali iye amene awerenga mokweza, ndi iwo amene akumva mawu a ulosi umenewu,” ndiponso “aliyense wosunga mawu a ulosi a mpukutu uwu.” (Chiv. 1:3; 22:7) Kuwerenga ndi kugwiritsa ntchito zimene zili m’buku la Chivumbulutso kungatilimbikitse kuti tizitumikira Mulungu ndiponso kum’khulupirira kwambiri pamodzi ndi Mwana wake, Yesu Khristu. Zimenezi zingatithandizenso kukhala ndi chiyembekezo chabwino pa zam’tsogolo. *—Aheb. 4:12.
MBALE ZISANU NDI ZIWIRI ZA MKWIYO WA MULUNGU ZITHIRIDWA PADZIKO LAPANSI
Lemba la Chivumbulutso 11:18 limati: “Mitundu inakwiya, ndipo mkwiyo [wa Mulungu] unafika. Inafikanso nthawi yoikika . . . ya kuwononga iwo owononga dziko lapansi.” Posonyeza chifukwa chimene Mulungu anakwiyira, masomphenya achisanu ndi chitatu anatchula ntchito za ‘chilombo . . . chanyanga khumi ndi mitu isanu ndi iwiri.’—Chiv. 13:1.
M’masomphenya achisanu ndi chinayi, Yohane anaona “Mwanawankhosa ataimirira pa Phiri la Ziyoni” limodzi ndi anthu ‘144,000 . . . ogulidwa kuchokera mwa anthu.’ (Chiv. 14:1, 4) Zitatero, angelo anapereka mauthenga osiyanasiyana. M’masomphenya otsatira, Yohane anaona “angelo asanu ndi awiri okhala ndi miliri isanu ndi iwiri.” Yehova analamula angelo amenewa kuti athire ‘mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu’ pa mbali zosiyanasiyana za dziko la Satanali. Mbalezo zinali ndi mauthenga ndiponso mawu ochenjeza a chiweruzo chimene Mulungu adzapereke. (Chiv. 15:1; 16:1) Masomphenya awiriwa analongosola bwino za ziweruzo zinanso zimene Ufumu wa Mulungu udzapereke mogwirizana ndi tsoka lachitatu ndiponso kulira kwa lipenga lachisanu ndi chiwiri.—Chiv. 11:14, 15.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
13:8—Kodi “mpukutu wa moyo wa Mwanawankhosa” n’chiyani? Umenewu ndi mpukutu wophiphiritsa womwe uli ndi mayina a anthu okhawo amene akulamulira ndi Yesu Khristu mu Ufumu wake wakumwamba. Mu mpukutuwu mulinso mayina a Akhristu odzozedwa omwe ali padziko lapansi pano ndipo akuyembekezera kukalandira moyo kumwamba.
13:11-13—Kodi chilombo chanyanga ziwiri chimachita zinthu motani ngati chinjoka, n’kupangitsa moto kugwa kuchokera kumwamba? Chilombochi chikuimira ulamuliro wamphamvu padziko lonse wa Britain ndi America. Mfundo yakuti chilombochi chimalankhula ngati chinjoka, ikusonyeza kuti chimaopseza anthu ndiponso kuchita nawo nkhondo powakakamiza kuti avomereze ulamuliro wake. Kupangitsa moto kugwa kuchokera kumwamba kukutanthauza kuti chimachita zinthu ngati mneneri. Chimachita zimenezi ponena kuti chinagonjetsa magulu oipa pankhondo ziwiri zikuluzikulu za padziko lonse ndiponso kuti chinathetsa ulamuliro wa Chikomyunizimu.
16:17—Kodi “mpweya” umene anakhuthulirapo mbale yachisanu ndi chiwiri ndi chiyani? “Mpweya” umenewu ukuimira maganizo a Satana, omwe ndi “mzimu [kapena kuti maganizo] umene tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera.” Anthu onse amene ali kumbali ya dongosolo la zinthu la Satanali akupuma mpweya woipa umenewu.—Aef. 2:2.
Zimene Tikuphunzirapo:
13:1-4, 18. “Chilombo” choimira maboma a anthu ‘chinatuluka m’nyanja,’ yomwe ikuimira anthu ambiri osokonezeka. (Yes. 17:12, 13; Dan. 7:2-8, 17) Chilombochi chinapangidwa ndiponso kupatsidwa mphamvu ndi Satana, ndipo chili ndi nambala ya 666, kusonyeza kuti ndi choipitsitsa. Kumvetsa tanthauzo la chilombochi kungatithandize kuti tisamasirire kukhala ku mbali yake kapena kuchilambira, ngakhale kuti anthu ambiri amachita zimenezi.—Yoh. 12:31; 15:19.
13:16, 17. Ngakhale kuti tingavutike kwambiri pochita zinthu zatsiku ndi tsiku, monga “kugula kapena kugulitsa,” tisalole kukakamizidwa mpaka kufika poti chilombochi chizilamulira moyo wathu. Kulola kupatsidwa ‘chizindikiro cha chilombo pa dzanja lathu kapena pamphumi pathu’ kungachititse kuti chilombochi chizilamulira zochita ndiponso maganizo athu.
14:6, 7. Zimene mngelo analengeza zikutithandiza kuona kuti tiyenera kulengeza mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Tiyenera kuthandiza anthu amene timaphunzira nawo Baibulo kuti aziopa Yehova ndiponso kum’patsa ulemerero.
14:14-20. Pambuyo pa ‘kukolola za dziko lapansi,’ kumene kukutanthauza ntchito yosonkhanitsa anthu amene adzapulumuke, mngelo adzatenga “mpesa wa pa dziko lapansi” n’kuuponya “m’choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu.” Kenako, mpesa wa padziko lapansi umenewu, womwe ndi maboma onse a anthu a dongosolo la Satanali ndiponso “masango” ake a zipatso zoipa, udzawonongedwa kotheratu. Choncho tiyenera kuonetsetsa kuti tisatengere zochita za mpesa wa padziko lapansi.
16:13-16. Mawu akuti “mauthenga . . . onyansa ouziridwa” akutanthauza bodza limene ziwanda zikulimbikitsa, lomwe cholinga chake ndi kuonetsetsa kuti mafumu a dziko lapansi asachite mantha ndi kukhuthulidwa kwa mbale zisanu ndi ziwiri za mkwiyo wa Mulungu. M’malomwake ziwandazi zikulimbikitsa mafumuwa kuti azitsutsana ndi Yehova.—Mat. 24:42, 44.
16:21. Pamene mapeto akuyandikira, mauthenga a ziweruzo za Yehova pa dongosolo loipa la Satanali angakhale amphamvu kwambiri, omwe akuwayerekezera ndi matalala. Komabe, anthu ambiri adzapitiriza kunyoza Mulungu.
MFUMU YOPAMBANA IYAMBA KULAMULIRA
“Babulo Wamkulu,” yemwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga, ndiye mbali yonyansa kwambiri ya dongosolo loipa la Satanali. Masomphenya a nambala 11 anamusonyeza monga “mkazi wachiwerewere wamkulu” ndipo anali “atakhala pa chilombo chofiiritsa.” Mkaziyu adzawonongedwa kotheratu ndi “nyanga khumi” za chilombo chimene wakwerapo. (Chiv. 17:1, 3, 5, 16) Masomphenya otsatira omwe anayerekezera mkaziyu ndi ‘mzinda waukulu,’ analengeza za kugwa kwake ndipo analimbikitsa anthu a Mulungu kuti asachedwe ‘kutuluka mwa iye.’ Anthu ambiri adzamva chisoni chifukwa cha kugwa kwa mzinda waukuluwu. Koma kumwamba kudzakhala chisangalalo chifukwa cha “ukwati wa Mwanawankhosa.” (Chiv. 18:4, 9, 10, 15-19; 19:7) M’masomphenya a nambala 13, Yohane anaona wokwera pa “kavalo woyera” akupita kukachita nkhondo ndi mayiko. Wokwera pa kavaloyu adzawononga dongosolo lonse loipa la Satanali.—Chiv. 19:11-16.
Kodi n’chiyani chimene chidzachitikire ‘njoka yakale, yomwe ndi Mdyerekezi ndi Satana’? Ndi liti pamene iye “adzaponyedwa m’nyanja ya moto”? Imeneyi ndi imodzi mwa mfundo zimene Yohane anaona m’masomphenya a nambala 14. (Chiv. 20:2, 10) Masomphenya awiri omalizira anapereka chithunzithunzi cha mmene moyo udzakhalire mu Ufumu wa Mulungu wa Zaka 1,000. Chakumapeto kwa masomphenyawo, Yohane anaona ‘mtsinje wa madzi a moyo, ukuyenda kutsikira pakati pa msewu waukulu,’ ndipo anamva mawu oitana “aliyense wakumva ludzu” kuti akamwe.—Chiv. 22:1, 2, 17.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
17:16; 18:9, 10—Pambuyo poti “mafumu a dziko lapansi” awononga Babulo Wamkulu, n’chifukwa chiyani iwo adzayambe kumva chisoni? Iwo adzamva chisoni chifukwa choti ndi adyera. Pambuyo powononga Babulo Wamkulu, mafumu a dziko lapansi adzazindikira kuti iye anali wofunika kwambiri. Iwo adzazindikira kuti iye ankawathandiza pochititsa anthu kuti aziona zochita za mafumuwo ngati zoyenera. Babulo Wamkulu ankawathandizanso kupeza achinyamata oti apite kunkhondo. Komanso iye ankawathandiza kwambiri pochititsa anthu kuti azikhala omvera.
19:12—N’chifukwa chiyani Yesu yekha ndi amene akudziwa dzina lake, lomwe silinatchulidwe? Zikuoneka kuti dzinali likuimira maudindo amene Yesu anakhala nawo kuyambira m’tsiku la Ambuye. Ena mwa maudindowa atchulidwa pa Yesaya 9:6. Ponena kuti palibe amene akudziwa dzina limeneli akutanthauza kuti ndi iye yekha amene akudziwa kuyendetsa maudindowa. Komabe, Yesu akugawirako a kagulu ka mkwatibwi zina mwa ntchito zofunika pa maudindowa, ndipo mwa kuchita zimenezi akukhala ngati ‘akuwalemba dzina lake latsopanoli.’—Chiv. 3:12.
19:14—Pankhondo ya Aramagedo, kodi ndani amene adzakwere pa akavalo limodzi ndi Yesu? ‘M’magulu ankhondo akumwamba’ amene adzakhale ndi Yesu pomenya nkhondo ya Mulungu, mudzakhala angelo ndiponso odzozedwa amene adzakhale atalandira kale mphoto yawo ya kumwamba.—Mat. 25:31, 32; Chiv. 2:26, 27.
20:11-15—Ndani amene mayina awo akulembedwa mu “mpukutu wa [kapena kuti, m’buku la] moyo”? Mpukutu umenewu uli ndi mayina a anthu amene adzalandire moyo wosatha, omwe ndi Akhristu odzozedwa, akhamu lalikulu ndiponso atumiki okhulupirika a Mulungu amene adzaukitsidwe pa “kuuka kwa olungama.” (Mac. 24:15; Chiv. 2:10; 7:9) Mayina a anthu amene adzaukitsidwe pa ‘kuuka kwa osalungama’ adzalembedwa mu “mpukutu wa moyo” pokhapokha akadzatsatira malangizo a ‘m’zolembedwa m’mipukutu’ imene idzatsegulidwe mu Ufumu wa Mulungu wa Zaka 1,000. Komabe, mayinawa adzawalemba moti angathe kufufutidwa. Mkhristu wodzozedwa akamwalira ali wokhulupirika, dzina lake limalembedwa moti silingafufutidwe. (Chiv. 3:5) Koma mayina a anthu onse amene adzalandire moyo padziko lapansi adzawalemba moti sangafufutidwenso akadzapambana mayesero omaliza pambuyo pa Ulamuliro wa Zaka 1,000.—Chiv. 20:7, 8.
Zimene Tikuphunzirapo:
17:3, 5, 7, 16. “Nzeru yochokera kumwamba” imatithandiza kuzindikira ‘chinsinsi cha mkazi, ndi cha chilombo [chofiiritsa] chimene iye wakwerapo.’ (Yak. 3:17) Poyamba, chilombo chophiphiritsa chimenechi chinali bungwe la League of Nations ndipo kenako bungweli linasinthidwa n’kukhala United Nations. Kuzindikira chinsinsi chimenechi kuyenera kutilimbikitsa kulalikira mwachangu uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndiponso kulengeza tsiku lachiweruzo la Yehova.
21:1-6. Sitikukayikira kuti madalitso amene analonjezedwa mu Ufumu adzakwaniritsidwa. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ponena za malonjezo amenewa, Baibulo limati: “Zachitika!”
22:1, 17. “Mtsinje wa madzi a moyo” ukuimira zinthu zimene Yehova wakonza pofuna kupulumutsa anthu okhulupirika ku uchimo ndi imfa. Ndipotu ena mwa madzi amenewa akupezeka panopa. Choncho, kuwonjezera pa kuvomereza ‘kumwa madzi a moyo kwaulere,’ tiyeneranso kuchita khama poitanira ena kuti adzamwe nawo madziwa.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 1 “Mfundo Zazikulu za M’buku la Chivumbulutso—Gawo 1,” zomwe zikufotokoza Chivumbulutso 1:1 mpaka 12:17, zikupezeka mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2009.
^ ndime 2 Kuti mudziwe zambiri za buku la Chivumbulutso, onani buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand! lomwe limafotokoza bukuli vesi ndi vesi.
[Chithunzi patsamba 5]
Anthu okhulupirika adzalandira madalitso ochuluka kwambiri mu Ufumu wa Mulungu