Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mwambo wa Maliro Achikhristu Umakhala Wolemekezeka, Wosadzionetsera Ndiponso Wokondweretsa Mulungu

Mwambo wa Maliro Achikhristu Umakhala Wolemekezeka, Wosadzionetsera Ndiponso Wokondweretsa Mulungu

Mwambo wa Maliro Achikhristu Umakhala Wolemekezeka, Wosadzionetsera Ndiponso Wokondweretsa Mulungu

M’MADERA ena a dziko lapansili, pamaliro pamakhala phokoso lalikulu kwambiri la kubuma. Anamalira amavala zovala zapadera zakuda, ndipo akamalira amafika mpaka podzigwetsa pansi chifukwa cha chisoni. Ena amakhala akuvina nyimbo zaphokoso kwambiri. Ndipo enanso amakhala akudya ndi kusangalala kwambiri, pamene ena amakhala ali gone, ataledzera ndi uchema ndiponso mowa wamitundu ina, womwe umakhalapo wambiri pamaliropo. Akamachita zimenezi iwo amati akutsanzikana ndi womwalirayo.

Mboni za Yehova zambiri zimakhala m’madera amene anthu amakhulupirira kwambiri zamizimu ndiponso amaopa akufa. Ndipo ena mwa anthu amenewa ndi achibale a Mbonizo. Anthu ambiri amakhulupirira kuti munthu akamwalira amakakhala mzimu, womwe ungathandize kapena kuvulaza anthu amoyo. Choncho, miyambo yambiri ya maliro imachitika mogwirizana ndi chikhulupiriro chimenechi. N’zoona kuti mwachibadwa anthu amalira wina akamwalira. Yesu ndiponso ophunzira ake, analirapo munthu amene anali kum’konda atamwalira. (Yoh. 11:33-35, 38; Mac. 8:2; 9:39) Komabe, iwo sanalirepo motsatira miyambo imene inali yofala m’nthawi yawo. (Luka 23:27, 28; 1 Ates. 4:13) N’chifukwa chiyani sanatsatire miyambo imeneyo? Chifukwa chimodzi chinali chakuti, iwo ankadziwa bwino zimene zimachitika munthu akamwalira.

Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi . . . Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano . . . Mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.” (Mlal. 9:5, 6, 10) Mawu ouziridwa amenewa akusonyezeratu kuti munthu akafa sadziwa chilichonse. Iye sangathe kuganiza, kumva, kulankhula kapena kuzindikira chilichonse. Kodi kudziwa mfundo ya choonadi imeneyi kuyenera kukhudza motani mmene Akhristu angayendetsere mwambo wa maliro?

‘Musakhudze Chonyansa’

Mboni za Yehova zonse zimapeweratu miyambo iliyonse yokhudzana ndi chikhulupiriro chakuti akufa amatha kudziwa zimene zikuchitika ndiponso angathe kuthandiza kapena kuvulaza anthu amoyo. Pali miyambo monga kulondera maliro, kuchita phwando la maliro, kukumbukira tsiku limene munthu winawake anamwalira, kupereka nsembe kwa akufa komanso miyambo ya mmene munthu ayenera kulirira maliro a mwamuna kapena mkazi wake, monga mwambo wa kulowa kapena kulowedwa chokolo. Miyambo yonseyi ndi yonyansa ndipo Mulungu sasangalala nayo, chifukwa chakuti imachitika potsatira chiphunzitso chakuti munthu ali ndi mzimu umene sufa. Chiphunzitso chimenechi chimachokera kwa ziwanda ndipo n’chotsutsana ndi Malemba. (Ezek. 18:4) Akhristu oona sachita nawo miyambo imeneyi chifukwa chakuti ‘sizingatheke kuti azidya pa “tebulo la Yehova” komanso pa tebulo la ziwanda.’ (1 Akor. 10:21) Iwo amatsatira lamulo lakuti: ‘Dzilekanitseni . . . ndipo musakhudze chonyansa.’ (2 Akor. 6:17) Komabe, kuchita zimenezi kungakhale kovuta nthawi zina.

Ku Africa kuno, anthu ambiri amakhulupirira kuti angathe kukwiyitsa mizimu ya makolo akapanda kutsatira miyambo inayake ya maliro. Ndipo amati munthu akapanda kutsatira miyambo imeneyo, mizimu imakwiya kwambiri n’kubweretsa tsoka kwa anthu a m’dera lonselo. Chifukwa chokana kuchita nawo miyamboyi, Mboni za Yehova zambiri zimaimbidwa mlandu, kunyozedwa ndiponso kuonedwa ngati anthu osafunika. Ena mwa anthu amene amachita zimenezi ndi achibale awo ndiponso anthu a m’midzi imene Mbonizo zikukhala. Mboni zina zimanenedwa kuti ndi zokhwimitsa zinthu ndiponso sizilemekeza anthu akufa. Ndipo nthawi zina, anthuwa amafika polanda mwambo wa maliro a Mkhristu. Choncho, kodi tingachite chiyani kuti tisamalimbane ndi anthu oterewa? Komanso, funso lofunika kuliganizira kwambiri ndi lakuti, Kodi tingachite chiyani kuti tidzilekanitse ku miyambo yodetsa imene ingawonongetse ubwenzi wathu ndi Yehova?

Afotokozereni Bwinobwino Maganizo Anu

M’madera ena a dziko lapansili, muli mwambo woti enimbumba ndiponso achibale ena azikhala nawo pokonza dongosolo la mwambo wa maliro. Choncho, ndi bwino kuti Mkhristu wokhulupirika, afotokozere achibalewo momveka bwino kuti mwambowo ukonzedwa ndi kuyendetsedwa ndi Mboni za Yehova, motsatira mfundo za m’Baibulo. (2 Akor. 6:14-16) Zochitika za pamaliro a Mkhristu siziyenera kuvulaza chikumbumtima cha Akhristu ena kapena kukhumudwitsa anthu ena amene amadziwa zimene timakhulupirira pankhani ya akufa.

Banja loferedwa likapempha m’bale kuti ayendetse mwambo wa maliro, akulu angachite bwino kufotokozera banjalo mfundo za m’Baibulo zofunika kutsatira kuti mwambowo uchitike mogwirizana ndi malangizo a m’Malemba. Tisachite mantha ngati anthu ena amene si Mboni akufuna kuti pamaliropo pachitike miyambo ina yoipa. M’malomwake tiwafotokozere mokoma mtima ndiponso mwaulemu mfundo zachikhristu zimene timatsatira. (1 Pet. 3:15) Koma kodi tingatani ngati anthuwo akuumirirabe? Zikatero, banja lachikhristulo lingakonze zongowasiyira malirowo. (1 Akor. 10:20) Kenako, m’bale angakambe nkhani ya maliro pa Nyumba ya Ufumu kapena pamalo ena abwino. Cholinga chochitira zimenezi ndicho kupereka “chitonthozo cha m’Malemba” kwa amene akhudzidwadi ndi imfayo. (Aroma 15:4) Ngakhale kuti nkhaniyi ingakambidwe popanda mtembo, koma mwambowu ndi wolemekezeka ndithu ndipo palibe cholakwika chilichonse kuchita zimenezi. (Deut. 34:5, 6, 8) N’zoona kuti anthu amene si Mboni akalowerera mwambo wa maliro, zimangowonjezera chisoni ndiponso zimasokoneza maganizo kwambiri. Komabe, n’zolimbikitsa kudziwa kuti Mulungu, amene angatipatse “mphamvu yoposa yachibadwa,” amaona khama lathu lofuna kuchita zabwino.​—2 Akor. 4:7.

Lembani Zimene Mukufuna

Munthu akalemberatu malangizo a mmene mwambo wa maliro ake udzayendetsedwere, zimakhala zosavuta kuti Mboni zikambirane zimenezo ndi achibale ake, chifukwa chakuti iwo angalemekeze zimene womwalirayo anasankha. Mfundo zikuluzikulu zofunika kulemba ndi izi: Mmene mwambo wa maliro udzayendetsedwere, malo a mwambowo, komanso amene adzakonze dongosolo ndi kuyendetsa mwambo wonse. (Gen. 50:5) Ndi bwino kuti polemba zimenezi pakhalenso anthu ena ndiponso musainire bwinobwino zimene mwalembazo. Anthu amene amatsatira mfundo za m’Baibulo pokonzekera za m’tsogolo, amadziwa kuti si bwino kudzalemba zimenezi atakalamba kapena atadwala kwambiri.​—Miy. 22:3; Mlal. 9:12.

Anthu ena amaopa kulemba zimenezi. Komabe, kulemberatu kungasonyeze kuti munthu ndi wokhwima maganizo mwauzimu ndiponso woganizira ena. (Afil. 2:4) Zingakhale bwino kwambiri kuti munthu afotokoze yekha zimene akufuna kuti zidzachitike pamaliro ake, m’malo mosiyira achibale amene angadzakakamizidwe kutsatira miyambo yoipa imene womwalirayo sankaikhulupirira n’komwe ndiponso sangafune kuti ichitike pamaliro ake.

Musachulutse Zochita Pamaliro

M’madera ambiri a mu Africa muno, anthu amakhulupirira kuti mwambo wa maliro uyenera kukhala ndi anthu ambiri ndiponso wogometsa, kuti mizimu ya makolo isakwiye. Anthu ena amapezerapo mwayi ‘wodzionetsera’ kuti iwo ndi apamwamba ndiponso olemera. (1 Yoh. 2:16) Iwo amawononga nthawi yambiri ndiponso chuma kuti m’bale wawoyo aikidwe bwino. Pofuna kuti anthu ambiri adzabwere pamwambowo, iwo amakhoma zithunzi zikuluzikulu za nkhope ya womwalirayo m’malo osiyanasiyana. Amapangitsa malaya okhala ndi nkhope ya munthu womwalirayo, n’kugawira anamalira kuti adzavale pamwambowo. Komanso, amagula bokosi lapamwamba kwambiri pofuna kugometsa anthu. M’dziko lina la mu Africa muno, anthu ena pofuna kusonyeza kuti ndi olemera kwambiri, amafika mpaka pokonzetsa mabokosi ooneka ngati galimoto, ndege, boti ndiponso zinthu zina. Nthawi zina amatha kuchotsa mtembo m’bokosi, n’kuuika pabedi lokongoletsedwa mwapadera kwambiri. Mtembowo ukakhala wa munthu wamkazi, amatha kuuveka diresi loyera la ukwati, komanso zinthu zina monga ndolo ndi zibangiri zambirimbiri, ndipo nkhope yake amaikongoletsa ndi zinthu zambiri. Kodi mtumiki wa Mulungu ayenera kuchita nawo miyambo yotereyi?

Akhristu okhwima maganizo mwauzimu amadziwa kuti ndi bwino kupewa kuchita zinthu monyanyira ngati mmene amachitira anthu amene sadziwa ndiponso salemekeza mfundo za Mulungu. Ife tikudziwa kuti kuchita zinthu monyanyira komanso mosatsatira Malemba ‘sikuchokera kwa Atate, koma ku dziko limene likupitali.’ (1 Yoh. 2:15-17) Choncho, tikufunika kukhala osamala kwambiri kuti tisalowetsedwe m’mipikisano, n’kumakhala ndi maganizo ofuna kuposa anthu ena. (Agal. 5:26) Zaoneka kuti anthu akamachita zinthu ndi maganizo oopa akufa, nthawi zambiri pamwambo wamaliro pamakhala zochitika zambirimbiri ndiponso zinthu zimasokonekera kwambiri. Kawirikawiri, anthu amene si Mboni amatha kuchita zinthu zolakwika, chifukwa cholemekeza akufa. Pamaliro oterowo, anthu amalira mofuula ndiponso mosatonthozeka, amakumbatira mtembo, kuyankhula nawo ngati kuti ndi wamoyo ndiponso kuika ndalama komanso zinthu zina pamtembowo. Zinthu zoterezi zitachitika pamaliro a Mkhristu, anthu anganyoze kwambiri dzina la Yehova komanso atumiki ake.​—1 Pet. 1:14-16.

Pamwambo wa maliro a Mkhristu sipayenera kuchitika china chilichonse chotsutsana ndi Malemba, chifukwa chakuti ifeyo timadziwa bwino zimene zimachitika munthu akamwalira. (Aef. 4:17-19) Ngakhale kuti Yesu anali munthu wofunika kwambiri pa anthu onse padziko lapansi pano, koma poika mtembo wake, anthu sanachite zinthu monyanyira ndiponso modzionetsera. (Yoh. 19:40-42) Kwa anthu amene ali ndi “maganizo a Khristu,” mwambo woterewu si wochititsa manyazi. (1 Akor. 2:16) Kunena zoona, kusachita zinthu monyanyira n’kumene kungatithandize kuti tipewe kuchita zinthu zotsutsana ndi Malemba ndiponso kuti mwambo wa maliro uyende bwino.

Kodi M’pofunika Kuchita Phwando?

M’madera ena muli mwambo woti maliro akaikidwa, achibale, anthu oyandikana nawo nyumba ndiponso ena ambirimbiri, azisonkhana kuti achite madyerero ndiponso kuvina nyimbo zaphokoso kwambiri. Nthawi zambiri pamiyambo imeneyi, pamakhala kumwa mowa kwambiri ndiponso pamachitika makhalidwe ena oipa. Anthu ena amanena kuti mapwando amenewa amathandiza kuthetsa chisoni. Ena amaona kuti kuchita zimenezi ndi mbali ya chikhalidwe chawo. Koma anthu ambiri amakhulupirira kuti ayenera kuchita mwambowu pofuna kulemekeza akufa ndiponso kuti mzimu wa womwalirayo upite kumene kuli mizimu ya makolo ake.

Akhristu oona amadziwa kuti ndi bwino kutsatira mfundo ya m’Malemba iyi: “Chisoni chiposa kuseka; pakuti nkhope yakugwa ikonza mtima.” (Mlal. 7:3) Komanso amadziwa kuti kupatula nthawi yoganizira mofatsa mfundo yakuti moyo ndi waufupi ndiponso kuganizira za chiyembekezo chakuti akufa adzaukitsidwa, n’kothandiza kwambiri. Zoonadi, kwa anthu amene ali paubwenzi wolimba ndi Yehova, ‘tsiku lakumwalira limaposa tsiku limene anabadwa.’ (Mlal. 7:1) Choncho, kudziwa kuti anthu amakonza mapwando a maliro chifukwa chokhulupirira mizimu, komanso kuti pamapwandowo pamachitika makhalidwe oipa, kumathandiza Akhristu kudziwa kuti sayenera kukonza mapwandowa kapenanso kupezekapo. Kuchita nawo mapwando a maliro kungasonyeze kuti sitilemekeza Mulungu komanso chikumbumtima cha Akhristu anzathu.

Tizisonyeza Kuti Ndife Osiyana ndi Ena

Anthu ambiri amene ali mu mdima wauzimu amaopa imfa, koma ife ndife osangalala kwambiri chifukwa tinamasulidwa ku mantha amenewa. (Yoh. 8:32) Monga “ana a kuwala,” amene timadziwa choonadi, timalira ndiponso kusonyeza chisoni chathu mosachita kunyanyira, mwaulemu komanso mogwirizana ndi chiyembekezo chathu chakuti akufa adzauka. (Aef. 5:8; Yoh. 5:28, 29) Chiyembekezo chimenechi chimatithandiza kuti tisatengere mmene anthu “opanda chiyembekezo” amalilira maliro. (1 Ates. 4:13) Chimatithandizanso kukhala olimba mtima potsatira mfundo za choonadi, ndiponso kuti tisamaope anthu.​—1 Pet. 3:13, 14.

Tikamayesetsa kutsatira mfundo za m’Malemba, anthu amatha ‘kuzindikira pakati pa iye wotumikira Mulungu ndi iye wosam’tumikira.’ (Mal. 3:18) M’tsogolo muno imfa sidzakhalaponso. (Chiv. 21:4) Choncho, pamene tikuyembekezera kukwaniritsidwa kwa lonjezo losangalatsa limeneli, tiyeni tiyesetse kuti Yehova adzatipeze opanda thotho, opanda chilema ndiponso osachita nawo makhalidwe oipa a m’dzikoli.​—2 Pet. 3:14.

[Chithunzi patsamba 30]

Ndi bwino kulemberatu zimene tikufuna kuti zidzachitike pamwambo wa maliro athu

[Chithunzi patsamba 31]

Mwambo wa maliro a Mkhristu uyenera kukhala wosadzionetsera komanso wolemekezeka