Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kupirira Muutumiki?

Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kupirira Muutumiki?

Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kupirira Muutumiki?

KODI munayamba mwaganizapo zosiya ntchito yolalikira chifukwa chokhumudwa kapena kutopa kwambiri? Nthawi zina kupirira kumavuta chifukwa cha kutsutsidwa kwambiri, nkhawa, matenda, kufooketsedwa ndi anzanu kapenanso kusalabadira kwa anthu amene mukuwalalikira. Komabe, taganizirani za chitsanzo cha Yesu. Iye anapirira mayesero ovuta kwambiri “chifukwa cha chimwemwe chimene anamuikira patsogolo pake.” (Aheb. 12:2) Iye anadziwa kuti adzakondweretsa mtima wa Yehova akasonyeza kuti zimene Mulungu amanenezedwa ndi mabodza amkunkhuniza.​—Miy. 27:11.

Inunso mungathe kukondweretsa mtima wa Yehova ngati mupirira muutumiki. Komabe, bwanji ngati mavuto ena akuoneka kuti akukufooketsani mwauzimu? Mwachitsanzo, Krystyna, yemwe ndi wokalamba komanso amadwaladwala, ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimatopa ndiponso ndimakhumudwa. Mavuto obwera ndi ukalamba, monga kudwaladwala ndiponso nkhawa za moyo, nthawi zina zimachepetsa changu changa.” Kodi n’chiyani chingakuthandizeni kupirira muutumiki mukamakumana ndi mavuto ngati amenewa?

Tsanzirani Aneneri

Kuti ofalitsa Ufumu okhulupirika apirire pantchito yawo yolalikira, amayesetsa kukhala ndi maganizo ngati a aneneri akale. Mwachitsanzo, Yeremiya atapemphedwa kutumikira monga mneneri, poyamba anakana. Komabe, iye anatha kupirira pantchito yake yovuta imeneyi kwa zaka zoposa 40 chifukwa chakuti ankadalira kwambiri Mulungu.​—Yer. 1:6; 20:7-11.

Chitsanzo cha Yeremiya chimalimbikitsa Henryk. Iye ananena kuti: “Ndakhala ndikulalikira kwa zaka zoposa 70. Nthawi zina ndakhumudwapo chifukwa cha zochita za anthu monga ukali ndi kupanda chidwi. Ndikakumana ndi anthu oterewa, ndimakumbukira chitsanzo cha Yeremiya. Iye anapitirizabe ntchito yake ya uneneri chifukwa chakuti ankakonda kwambiri Yehova komanso anali wolimba mwauzimu.” (Yer. 1:17) Nayenso Rafał amalimbikitsidwa kwambiri ndi chitsanzo cha Yeremiya. Iye anati: “M’malo moganizira kwambiri za moyo wake ndi zofuna zake, Yeremiya ankadalira kwambiri Mulungu. Iye anagwirabe ntchito yake mopanda mantha ngakhale kuti ambiri ankamuda. Ndimayesetsa kukumbukira zimenezi.”

Mneneri wina amene chitsanzo chake chimathandiza ambiri kupirira muutumiki ndi Yesaya. Mulungu anamuuza kuti anthu a mtundu wake sadzamvetsera uthenga wake. Yehova anati: “Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu awo.” Kodi izi zinatanthauza kuti Yesaya alephera ntchito yake? Mulungu sanaganize choncho. Ndipo pamene Yesaya anasankhidwa kukhala mneneri, iye anati: “Ndine pano; munditumize ine.” (Yes. 6:8-10) Yesaya sanasiye ntchito yake. Kodi inunso mumamvera lamulo lolalikira?

Kuti tipitirizebe kulalikira tikamakumana ndi anthu opanda chidwi, monga mmene Yesaya anachitira, tifunikira kupewa kuganizira kwambiri za anthu amene amakana uthenga wathu. Rafał amachita zimenezi akakumana ndi anthu otero. Iye anati: “Ndimayesetsa kuti ndisamaganizire kwambiri zinthu zogwetsa ulesi zimene anthu amanena. Anthu a m’gawo langa ali ndi ufulu woyankha mmene akufunira.” Anna akunenanso kuti: “Sindilola kumangoganizira zinthu zosalimbikitsa kapena zokhumudwitsa. Chimene chimandithandiza ndi pemphero ndiponso kuwerenga lemba la tsiku ndisanapite muutumiki wa kumunda. Choncho, maganizo onse ofooketsa amatha msanga.”

Mneneri Ezekieli ankatumikira pakati pa Ayuda ouma khosi amene anali kuukapolo ku Babulo. (Ezek. 2:6) Mneneriyu akanati asawauze anthuwo mawu a Mulungu, ndipo ngati munthu wina woipa akanafa wosachenjezedwa, Ezekieli akanakhala ndi mlandu. Yehova anauza Ezekieli kuti: “Mwazi wake ndidzaufuna pa dzanja lako.”​—Ezek. 3:17, 18.

Henryk amayesetsa kukhala ndi maganizo ngati a Ezekieli. Iye anati: “Ndikufuna kupewa mlandu wa magazi a anthu onse. Miyoyo ya anthu yamtengo wapatali ili pangozi.” (Mac. 20:26, 27) Nayenso Zbigniew amaganiza chimodzimodzi. Iye anati: “Ezekieli anapitirizabe ntchito yake ngakhale kuti anthu ankamuona ngati woipa. Kuganizira zimenezi kumandithandiza kuti ndiziona ntchito yolalikira monga mmenenso Mlengi wathu amaionera.”

Simuli Nokha

Mukamalalikira, sikuti mumakhala nokha. Mtumwi Paulo ananena kuti: “Ndife antchito anzake a Mulungu,” ndipo zimenezi ndi zoona. (1 Akor. 3:9) Krystyna, amene anati nthawi zina amakhumudwa, akunena kuti: “N’chifukwa chake ndimapitirizabe kupempha Yehova kuti andipatse mphamvu. Ndipo nthawi zonse amandithandiza.” Zoonadi, timafunikira mzimu wa Mulungu kuti utithandize muutumiki.​—Zek. 4:6.

Tikamalalikira, mzimu woyera umatithandiza kukhala ndi makhalidwe amene ndi “zipatso za mzimu.” (Agal. 5:22, 23) Ndiyeno makhalidwe amenewa amatithandiza kulimbikira kulalikira, zivute zitani. Henryk anati: “Ntchito yolalikira imandithandiza kukonza umunthu wanga. Ndimakhala woleza mtima, woganizira ena ndiponso wakhama.” Mukamapirira muutumiki pokumana ndi mavuto osiyanasiyana, zimakuthandizani kukhala ndi zipatso za mzimu mokulira.

Yehova amagwiritsa ntchito angelo kutsogolera ntchito yapadera imeneyi. (Chiv. 14:6) Baibulo limasonyeza kuti zolengedwa zauzimu zimenezi zilipo “miyanda kuchulukitsa ndi miyanda ndiponso masauzande kuchulukitsa ndi masauzande.” (Chiv. 5:11) Motsogoleredwa ndi Yesu, angelo amenewa amathandiza atumiki a Mulungu padziko lapansi. Kodi inuyo mumakumbukira zimenezi nthawi zonse mukakhala muutumiki?

“Kusinkhasinkha mfundo yakuti angelo amakhala nafe muutumiki kumandilimbikitsa kwambiri,” anatero Anna. Iye anapitiriza kuti: “Ndimayamikira thandizo limene iwo amapereka motsogoleredwa ndi Yehova ndiponso Yesu.” Kunena zoona, ndi mwayi waukulu kugwira ntchito limodzi ndi angelo okhulupirika amenewa.

Nanga bwanji za ofalitsa Ufumu anzathu? Ndi dalitso lalikulu kudziwana ndi gulu lalikulu la Mboni zokhulupirika. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” Mosakayika, inu mwaona kuti mwambi umenewu ndi woona.​—Miy. 27:17.

Tikamagwira ntchito limodzi ndi ena muutumiki, timakhala ndi mpata wabwino wophunzira njira zolalikira zatsopano komanso zogwira mtima. Elżbieta anati: “Kulalikira limodzi ndi ofalitsa osiyanasiyana kumandipatsa mpata wosonyeza chikondi kwa okhulupirira anzanga komanso kwa anthu amene timakumana nawo.” Yesetsani kulalikira ndi ofalitsa osiyanasiyana. Zimenezi zingathandize kuti utumiki wanu ukhale wosangalatsa.

Dzisamalireni

Kuti changu chathu muutumiki chisathe, timafunikira dongosolo labwino, chizolowezi chabwino cha phunziro laumwini ndiponso kupuma mokwanira. M’mawu ena, tinganene kuti tiyenera kudzisamalira mwauzimu ndi mwakuthupi.

Baibulo limati: “Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu.” (Miy. 21:5) Zygmunt, yemwe ali ndi zaka 88, anati: “Kukhala ndi pulogalamu yabwino muutumiki kumandithandiza kukwaniritsa zolinga zanga. Ndimagawa nthawi yanga bwinobwino kuti ndikhale ndi nthawi yokwanira yolalikirira.”

Kudziwa bwino Malemba kumatipatsa mphamvu ndipo kumatithandiza kukhala okonzeka kulalikira. Monga mmene timafunikira chakudya chakuthupi kuti tikhale ndi moyo, timafunikiranso chakudya chauzimu nthawi zonse kuti tipitirizebe ntchito yolalikira. Kudya Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku ndiponso ‘chakudya cha panthawi yoyenera,’ kungatipatse mphamvu kuti tipitirizebe kulalikira.​—Mat. 24:45-47.

Elżbieta anasintha kwambiri zinthu pamoyo wake kuti awongolere luso lake muutumiki. Iye ananena kuti: “Ndachepetsa kwambiri nthawi imene ndimaonera TV kuti ndikhale ndi nthawi yokwanira yokonzekera utumiki. Ndikamawerenga Baibulo madzulo alionse, ndimaganizira za anthu amene ndinakumana nawo m’gawo. Ndimayang’ana malemba ndi nkhani zimene zingawathandize.”

Kupuma mokwanira kungakuthandizeni kukhalabe ndi mphamvu ndipo mungathe kuchita zambiri muutumiki. Koma kuthera nthawi yambiri pa zinthu zosangalatsa kungasokoneze kwambiri utumiki wanu. Andrzej, yemwe ndi wofalitsa wachangu, anati: “Ngati supuma mokwanira, umakhala wotopa kwambiri, ndipo suchedwa kukhumudwa. Ndimayesetsa mmene ndingathere kupewa zimenezi.”​—Mlal. 4:6.

Ngakhale tingachite khama kwambiri, ndi anthu ochepa amene amalabadira uthenga wabwino. Komabe, Yehova sadzaiwala ntchito yathu. (Aheb. 6:10) Ngakhale kuti anthu ambiri safuna kulankhula nafe, amalankhulabe za ife tikachoka pakhomo pawo. Zotsatira zake zimakhala ngati zimene timawerenga zokhudza Ezekieli. Anthu “adzadziwa kuti panali mneneri pakati pawo.” (Ezek. 2:5) Kunena zoona, utumiki wathu ndi wovuta, koma umatithandiza kwambiri ifeyo komanso anthu amene amamvetsera.

Zygmunt anati: “Kulalikira kumatithandiza kuvala umunthu watsopano ndi kusonyeza chikondi kwa Mulungu komanso anthu anzathu.” Andrzej akuwonjezera kuti: “Ndi mwayi waukulu kuchita nawo ntchito yopulumutsa miyoyo imeneyi. M’tsogolomu sitidzagwiranso ntchito imeneyi ngati mmene tikuigwirira pano kapenanso movutikira ngati mmene tikuchitira.” Inunso mungapeze madalitso ochuluka masiku ano ngati mukupirirabe muutumiki.​—2 Akor. 4:1, 2.

[Zithunzi patsamba 31]

Kudzisamalira mwauzimu ndi mwakuthupi kumatithandiza kupirira muutumiki