“Mngelo wa Yehova Azinga” Anthu Ake
“Mngelo wa Yehova Azinga” Anthu Ake
Yosimbidwa ndi Christabel Connell
Tinali titatanganidwa kwambiri ndi kuyankha mafunso okhudza Baibulo amene Christopher anali nawo, moti sitinadziwe kuti kunja kwada. Sitinadziwenso kuti panthawi yonseyi Christopher ankayang’ana pa windo. Kenako, iye anatiuza kuti, “Tsopano zili bwino, mungathe kumapita.” Atanena zimenezi, anatiperekeza pomwe panali njinga zathu ndipo tinatsanzikana. Kodi iye anaona chiyani chomwe chinali choopsa kwambiri?
NDINABADWIRA mu mzinda wa Sheffield, ku England, m’chaka cha 1927. Bambo anga dzina lawo anali a Earl. Panthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, nyumba yathu inaphulitsidwa ndi bomba, choncho anandipititsa kwa agogo aakazi kuti ndikamalize sukulu. Pasukulu ina ya Katolika yomwe ndinkaphunzira, ndinkakonda kufunsa masisitere kuti andiuze chifukwa chake padzikoli pamachitika zinthu zoipa kwambiri ndi zachiwawa. Koma iwo ndiponso anthu ena achipembedzo amene ndinkawafunsa, sankandiyankha zogwira mtima.
Nkhondoyo itatha, ndinachita maphunziro a unamwino. Kenako ndinasamukira ku London kukagwira ntchito pachipatala cha Paddington Genral Hospital. Koma mumzinda umenewu ndinkaona zachiwawa zambiri zikuchitika. Mchimwene wanga atangopita kukamenya nawo Nkhondo ya ku Korea, ndinaona ndewu yoopsa kwambiri panja pa chipatala. Panalibe aliyense amene anathandiza munthu womenyedwayo moti anavulala kwambiri mpaka anasiya kuona. Panthawi yomwe ndinkagwira ntchito pachipatalachi, ndinkapita ndi mayi anga ku misonkhano ya anthu okhulupirira zamizimu, koma zimenezi sizinandithandize ngakhale pang’ono kudziwa chifukwa chake zinthu zoipa zimachitika.
Anandilimbikitsa Kuphunzira Baibulo
Tsiku lina, mchimwene wanga wamkulu dzina lake John, yemwe anali atakhala wa Mboni za Yehova, anabwera kudzatichezera. Iye anandifunsa kuti: “Kodi ukudziwa chimene chimachititsa zinthu zoipa zonsezi?” Ndinamuyankha kuti: “Ayi.” Iye anatsegula Baibulo lake n’kuwerenga lemba la Chivumbulutso 12:7-12. Tsopano ndinadziwa kuti Satana ndi ziwanda zake ndi amene amachititsa mavuto ambiri padzikoli. Kenako John anandilimbikitsa kuti ndiyambe kuphunzira Baibulo, ndipo posapita nthawi ndinayambadi kuphunzira. Komabe, panthawi imeneyi ndinkalephera kubatizidwa chifukwa choopa anthu.—Miy. 29:25.
Mchemwali wanga Dorothy anali atakhalanso wa Mboni. Iye pamodzi ndi m’bale yemwe anali naye pachibwenzi, dzina lake Bill Roberts, anabwera kunyumba kuchokera kumsonkhano wamayiko womwe unachitikira ku New York (mu 1953).
Ndinawauza kuti ndinaphunzira Baibulo ndi munthu wina. Bill anandifunsa kuti: “Kodi unkawerenga malemba onse? Nanga unkadula mizere kunsi kwa mayankho a m’bukulo?” Nditamuuza kuti ayi, anayankha kuti: “Ndiye sunaphunziretu! Ukumane ndi mlongoyo kuti muyambirenso.” Panthawi imeneyi ziwanda zinayamba kundivutitsa. Ndimakumbukirabe kuti ndinkapempha Yehova kuti anditeteze ndiponso ndimasuke ku mphamvu ya ziwanda.Kuchita Upainiya ku Scotland ndi ku Ireland
Ndinabatizidwa pa January 16, 1954. Ndinasiya ntchito yanga ya unamwino mu May chaka chomwecho ndipo mu June ndinayamba upainiya. Patatha miyezi 8 ndinatumizidwa kukachita upainiya wapadera ku Grangemouth, Scotland. Ndikulalikira kudera lakutali limeneli, ndinaona kuti angelo a Yehova ‘akundizinga.’—Sal. 34:7.
Mu 1956, anandipempha kuti ndikatumikire ku Ireland. Ine pamodzi ndi alongo ena awiri tinayamba kutumikira mumzinda wa Galway. Tsiku loyamba kulalikira mumzindawu, ndinafika panyumba ya wansembe. Pasanapite nthawi, panafika wapolisi, ndipo ine ndi mnzanga anatitenga n’kupita nafe kupolisi. Wapolisiyu atalemba mayina athu ndi kumene tinkakhala, msangamsanga anapita pomwe panali telefoni. Kenako tinamumva akunena kuti, “Ee, Abambo, ndikudziwa bwino kumene akukhala.” Wapolisiyu anatumidwa ndi wansembeyo. Eni nyumba imene tinkakhala anakakamizidwa kuti atithamangitse m’nyumba yawo, choncho ofesi ya nthambi inanena kuti ndi bwino kuti tisamuke m’derali. Tinachedwa kufika pamalo okwerera sitima ndi mphindi 10. Komabe tinapeza sitima isananyamuke ndipo panali munthu amene ankatidikirira pofuna kuonetsetsa kuti takwera. Apatu n’kuti titangokhala milungu itatu yokha ku Galway.
Tinauzidwa kuti tikatumikire ku Limerick, mzinda winanso kumene Tchalitchi cha Katolika chinali ndi mphamvu kwambiri. Nthawi zambiri magulu achiwawa ankatikuwiza. Anthu ambiri ankachita mantha kutilandira m’nyumba zawo kuti tiwalalikire. Panali patangotha chaka pamene m’bale wina anamenyedwa ku Cloonlara, tawuni yaing’ono yapafupi ndi kumene tinkakhala. Choncho tinasangalala kukumana ndi Christopher amene ndamutchula poyamba paja. Iye anatipempha kuti tidzapitenso kunyumba kwake kuti tikakambirane mafunso omwe anali nawo okhudza Baibulo. Titapitako, wansembe wina anangolowa m’nyumbayo ndi kumuuza Christopher kuti atitulutse. Christopher sanagwirizane ndi zimenezi ndipo anati: “Amayi awa ndachita kuwaitana ndipo anagogoda asanalowe. Koma inu sindinakuitaneni ndiponso simunagogode.” Wansembeyo anatuluka atakwiya n’kumapita.
Sitinadziwe kuti wansembeyo anasonkhanitsa gulu lalikulu la amuna amene ankatidikirira panja pa nyumba ya Christopher. Podziwa kuti amunawa anali ankhanza ndi okwiya, Christopher anachita zomwe ndafotokoza poyamba paja. Anaonetsetsa kuti tisanyamuke mpaka anthuwo atachoka. Kenako tinadzamva kuti iye ndi banja lake anathamangitsidwa m’derali ndipo anapita kukakhala ku England.
Ndinaitanidwa ku Gileadi
Ndikukonzekera kukapezeka ku New York kumsonkhano wa mayiko wa mu 1958 wa mutu wakuti “Chifuniro cha Mulungu,” ndinalandira kalata yondiitana kuti ndikakhale nawo m’kalasi la nambala 33 ku Sukulu ya Gileadi. Msonkhanowu utatha sindinabwerere kunyumba. M’malomwake ndinakatumikira ku Collingwood, ku Ontario, m’dziko la Canada, ndipo ndinatumikira kumeneko mpaka pamene Sukulu ya Gileadi inayamba mu 1959. Koma panthawi ya msonkhano ija, ndinakumana ndi Eric Connell. Iye anaphunzira choonadi mu 1957 ndipo anayamba upainiya mu 1958. Msonkhano utatha, Eric ankandilembera kalata tsiku lililonse panthawi imene ndinali ku Canada ndiponso panthawi yonse yomwe ndinali ku Sukulu ya Gileadi. Sindinkadziwa kuti zitha bwanji ndikamaliza sukulu.
Kupita ku Sukulu ya Gileadi chinali chinthu chosaiwalika pamoyo wanga. Kusukuluyi, ndinali limodzi ndi mchemwali wanga Dorothy ndi mwamuna wake. Iwo anatumizidwa kukachita umishonale ku Portugal. Ndinadabwa kumva kuti anditumiza ku Ireland. Ndinakhumudwa kwambiri kudziwa kuti ndisiyana ndi mchemwali wanga. Ndinafunsa mmodzi wa alangizi kuti andiuze ngati panali chinachake chomwe ndinalakwitsa. Iye anayankha kuti, “Ayi. Iwe ndi mnzako Eileen Mahoney munavomereza kuti mudzapita kulikonse
padziko lapansi.” Indedi, mawu akuti “kulikonse” anaphatikizapo dziko la Ireland.Ndinabwereranso ku Ireland
Ndinabwerera ku Ireland mu August 1959, ndipo ndinkasonkhana mumpingo wa Dun Laoghaire. Panthawiyi n’kuti Eric atabwerera ku England, ndipo anasangalala kwambiri kuona kuti ndili pafupi. Nayenso ankafuna kukhala mmishonale. Eric anaganiza kuti popeza ku Ireland kunkafunika amishonale, angakachite upainiya kumeneko. Iye anasamukira mumpingo wa Dun Laoghaire, ndipo tinakwatirana mu 1961.
Patatha miyezi 6, Eric anachita ngozi ya njinga yamoto. Iye anavulala kwambiri m’mutu ndipo madokotala ankakayikira zoti angam’pulumutse. Atakhala milungu itatu m’chipatala, ndinamusamalira kunyumba kwa miyezi 5 mpaka atachira. Ndinapitirizabe utumiki wanga malinga ndi zomwe ndikanatha kuchita.
Mu 1965, tinatumizidwa mumpingo womwe unali ndi ofalitsa 8, ku Sligo, doko la kumpoto chakumadzulo kwa Ireland. Patatha zaka zitatu, tinasamukira mumpingo wina waung’ono ku Londonderry, kumpoto kwenikweni. Tsiku lina titafika kunyumba kuchokera muutumiki, tinapeza atatseka msewu wathu ndi waya wamingaminga. Uku kunali kuyamba kwa Mavuto a ku Northern Ireland. Magulu a achinyamata ankayatsa magalimoto. Mzindawo unali utagawikana, kwina Apolotesitanti ndipo kwina Akatolika. Zinali zoopsa kuti munthu achoke dera ili kupita dera lina mumzindawo.
Moyo Ndiponso Kulalikira Nthawi ya Mavuto
Ngakhale kuti kuyenda kunali koopsa, tinkalalikira kulikonse. Panthawi imeneyinso tinkaona kuti angelo akutizinga. Tikaona kuti kudera limene tikulalikira kwayambika zipolowe, tinkachoka msangamsanga ndipo tinkabwereranso zipolowe zikatha. Tsiku lina zipolowe zikuchitika pafupi ndi nyumba yathu, zidutswa za zinthu zakupsa za pasitolo ina yogulitsira penti zinafika pawindo la nyumba yathu. Sitinagone poopa kuti nyumba yathu ingayambe kupsa ife tili m’tulo. Titasamukira ku Belfast mu 1970, tinamva kuti sitolo yogulitsira penti ija inapsa chifukwa cha bomba limene linaphulika, ndipo nyumba yomwe tinkakhala ija inapsanso.
Tsiku lina ine ndi mlongo wina tili muutumiki, tinaona paipi yokayikitsa pawindo la nyumba ina. Tinangopitirira. Patangotha mphindi zochepa, paipi ija inaphulika. Anthu a m’derali anaganiza kuti bombalo, limene linkaoneka ngati paipi, tinatchera ndi ifeyo. Koma panthawi yomweyi mlongo wina yemwe ankakhala m’dera lomweli anatiitana kunyumba kwake. Ndipo anthu apafupi ataona zimenezi, anadziwa kuti sindife tinatchera bombalo.
Mu 1971, tinabwerera ku Londonderry kukacheza ndi mlongo wina. Titamuuza mmene tayendera komanso msewu umene tadutsa, anatifunsa kuti, “Simunapeze paliponse pamene atchinga msewu?” Tinamuyankha kuti, “Tinapeza, koma sanatipange chilichonse.” Iye sanamvetse zimenezi chifukwa masiku ena m’mbuyomo, dokotala wina ndiponso wapolisi, analandidwa magalimoto awo n’kuwaotcha.
Mu 1972 tinasamukira ku Cork. Ndiyeno tinakatumikira ku Naas, ndipo kenako ku Arklow. Pomaliza, mu 1987 anatitumiza ku Castlebar ndipo n’komwe tili mpaka pano. Kunoko tinali ndi mwayi wapadera kwambiri womanga nawo Nyumba ya Ufumu. Mu 1999, Eric anadwala kwambiri. Koma ndi thandizo la Yehova ndiponso la anthu mumpingo, ndinathanso kupirira ndi kum’samalira mpaka atachira.
Ine ndi Eric talowa Sukulu ya Utumiki Waupainiya maulendo awiri. Iye akutumikirabe monga mkulu. Ine ndimadwala nyamakazi ndipo anandipanga opaleshoni ya m’maondo ndi m’chiuno. Ndinakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cha anthu achipembedzo komanso ndakhala ndi moyo m’nthawi ya mavuto andale ndi mavuto ena. Komabe, vuto limodzi mwa mavuto akuluakulu amene ndinakumana nawo ndi kusiya kuyendetsa galimoto. Zimenezi zinali zovuta chifukwa zinandilanda ufulu woyenda. Anthu mumpingo akhala akundithandiza kwambiri. Panopa ndimayenda ndi ndodo, koma ukakhala ulendo wautali, ndimagwiritsa ntchito njinga ya olemala yoyendera batire.
Tikaphatikiza zaka zomwe ine ndi Eric tatumikira ngati apainiya apadera zikukwana 100, ndipo 98 pazaka zimenezi takhala tili kuno ku Ireland. Sitikufuna kusiya ntchito yathu. Sitidalira zozizwitsa, koma timakhulupirira kuti angelo amphamvu a Yehova ‘amazinga’ anthu onse amene akumuopa ndi kum’tumikira mokhulupirika.