Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova ndi Woyenera Kutamandidwa ndi Tonsefe

Yehova ndi Woyenera Kutamandidwa ndi Tonsefe

Yehova ndi Woyenera Kutamandidwa ndi Tonsefe

“Haleluya.”​—SAL. 111:1.

1, 2. Kodi mawu akuti “Haleluya” amatanthauza chiyani, ndipo agwiritsidwa ntchito bwanji m’Malemba Achigiriki Achikhristu?

“HALELUYA!” Amenewa ndi mawu amene anthu amakonda kunena m’Matchalitchi Achikhristu. Anthu ena amagwiritsa ntchito mawu amenewa tsiku ndi tsiku polankhulana. Koma ndi ochepa chabe amene amadziwa kuti mawuwa ali ndi tanthauzo lapadera, ndipo makhalidwe a anthu ambiri amene amawagwiritsa ntchito salemekeza Mulungu. (Tito 1:16) Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo limati: “Haleluya ndi mawu amene anthu omwe analemba masalmo osiyanasiyana anagwiritsa ntchito popempha anthu onse kuti agwirizane nawo kutamanda Yehova.” Ndiponso akatswiri ambiri a Baibulo amanena kuti mawu akuti “Haleluya” amatanthauza “‘Inu Tamandani Ya,’ [kutanthauza] Yehova.”

2 Choncho, m’pomveka kuti Baibulo la New World Translation linamasulira mawu opezeka pa Salmo 111:1 kuti “Tamandani Ya, anthu inu!” Mawu a Chigiriki otanthauza zomwezi amapezeka kanayi pa Chivumbulutso 19:1-6, pomwe agwiritsidwa ntchito pokondwerera kutha kwa chipembedzo chonyenga. Chipembedzo chonyenga chikadzawonongedwa, olambira oona adzakhala ndi chifukwa chomveka chogwiritsira ntchito mawu akuti “Haleluya!” mwaulemu.

Ntchito Zake Zazikulu

3. Kodi cholinga chachikulu chopezekera pamisonkhano yathu nthawi zonse n’chiyani?

3 Wolemba Salmo 111 akupereka zifukwa zambiri zosonyeza kuti Yehova ndi woyenera kutamandidwa ndi tonsefe. Vesi 1 limati: “Ndidzayamika Yehova ndi mtima wonse, mu upo wa oongoka mtima, ndi mumsonkhano.” Masiku ano, ife Mboni za Yehova tilinso ndi maganizo otero. Cholinga chachikulu chopezekera pamisonkhano yathu, yampingo ndiponso ikuluikulu, ndi kutamanda Yehova.

4. Kodi anthufe tingafufuze bwanji ntchito za Yehova?

4 “Ntchito za Yehova n’zazikulu, zofunika ndi onse akukondwera nazo.” (Sal. 111:2) Taonani palembali mawu akuti “zofunika,” kapena kuti zofufuzidwa. Malinga ndi buku lina, vesili limanena za anthu amene “amakonda kuphunzira mwakhama ndi kusinkhasinkha” ntchito za Mulungu. Zinthu zimene Yehova analenga zimasonyeza kuti iye anali ndi cholinga chapadera. Iye anaika dzuwa, dziko lapansi ndi mwezi pamalo oyenerera. Zimenezi zimathandiza kuti dziko lapansi lizilandira kutentha ndi kuwala, ndiponso kuti kuzikhala usana ndi usiku. Zimathandizanso kuti kukhale nyengo zosiyanasiyana ndiponso kuti madzi m’nyanja azichuluka kapena kuphwera.

5. Kodi kudziwa zambiri zokhudza chilengedwe kwasonyeza chiyani?

5 Asayansi aphunzira zambiri zokhudza malo amene dziko lapansili lili. Ndiponso aphunzira zambiri zokhudza mwezi, monga mmene umazungulirira dziko, kukula kwake ndi kulemera kwake, zimene zimathandiza kwambiri dziko lapansi. Malo amene dziko lapansi ndi mwezi zili, ndiponso mmene zimagwirira ntchito, zimathandiza kuti pazikhala kusintha kwa nyengo kosangalatsa. Ndiponso asayansi aphunzira zambiri zokhudza mphamvu za m’chilengedwe ndipo apeza kuti zinalinganizidwa bwino. Ndiye chifukwa chake m’nkhani yakuti “Chilengedwe Chinapangidwa ‘Moyenerera,’” pulofesa wina wa luso lopanga zinthu anati: “N’zosavuta kuona chifukwa chimene asayansi ambiri asinthira maganizo awo zaka 30 zapitazi, n’kuyamba kuvomereza kuti m’pofunika chikhulupiriro champhamvu kuti munthu anene kuti zinthu zonsezi zinakhalako zokha, popanda wozipanga. Umboni wosatsutsika wakuti kuli wina wanzeru amene anapanga zonsezi, umachulukirachulukira tikamadziwa zambiri zokhudza dziko lathuli lomwe linapangidwa mwaluso.”

6. Kodi mumamva bwanji mukaganizira mmene Mulungu anapangira munthu?

6 Njira inanso imene imasonyeza bwino kuti zinthu zinachita kulengedwa, ndi mmene Mulungu anatilengera anthufe. (Sal. 139:14) Mulungu anapatsa anthu ubongo, thupi lokhala ndi ziwalo zonse zofunikira ndiponso luso ndi mphamvu zogwirira ntchito. Iye anapatsanso anthu luso lodabwitsa lolankhula ndi kumvetsera komanso lolemba ndi kuwerenga. Anthu ambiri ali ndi luso limeneli. Mulinso ndi thupi lopangidwa modabwitsa ndipo n’chifukwa chake mumatha kuimirira bwinobwino. Mmene thupi lanu linapangidwira, komanso mmene limagwirira ntchito zosiyanasiyana, n’zochititsa chidwi kwambiri. Kuwonjezera pa zimenezi, kalumikizidwe kodabwitsa ka minyewa imene imathandiza kuti ubongo ndi ziwalo zina zizigwira ntchito, kamaposa chilichonse chimene asayansi apanga. Ndipotu, zimene anthu amapanga zimatheka chifukwa chakuti anapatsidwa ubongo ndiponso mphamvu zosiyanasiyana. Ngakhale munthu wopanga zinthu waluso kwambiri komanso wophunzitsidwa bwino, sakanatha kupanga zinthu zokongola ndi zothandiza kwambiri ngati chala chanu chamanthu ndi zala zinazo, zomwe zimakuthandizani kunyamula zinthu. Dzifunseni kuti, ‘Kodi ntchito zaluso ndi zomangamanga zochititsa chidwi zikanatheka popanda kugwiritsa ntchito mwaluso zala zimene Mulungu anatipatsa?’

Ntchito Zazikulu za Yehova Ndiponso Makhalidwe Ake

7. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuona kuti Baibulo ndi imodzi mwa ntchito zazikulu za Mulungu?

7 Ntchito zazikulu za Yehova zikuphatikizapo zinthu zina zodabwitsa zimene iye wachitira anthu, zimene zimafotokozedwa m’Baibulo. Ndipo Baibulo lenilenilo ndi lodabwitsa kwambiri chifukwa mabuku ake amagwirizana. Mosiyana ndi mabuku ena onse, Baibulo ‘analiuzira ndi Mulungu, ndipo ndi lopindulitsa pa kuphunzitsa.’ (2 Tim. 3:16) Mwachitsanzo, buku loyamba la m’Baibulo, Genesis, limafotokoza mmene Mulungu anachotsera kuipa padziko lapansi m’nthawi ya Nowa. Buku lachiwiri la Eksodo, limafotokoza mmene Yehova anasonyezera Umulungu wake mwa kupulumutsa Aisiraeli ku ukapolo wa ku Iguputo. Wamasalmo ayenera kuti ankaganizira zinthu zimenezi pamene anati: “Chochita [Yehova] n’cha ulemu, ndi ukulu: Ndi chilungamo chake chikhalitsa kosatha. Anachita chokumbukitsa zodabwiza zake; Yehova ndiye wa chisomo ndi nsoni zokoma.” (Sal. 111:3, 4) Kodi inuyo simukuvomereza kuti zochita za Yehova kuyambira kalekale, kuphatikizapo zimene wachita inuyo muli ndi moyo, ndi chikumbutso cha ‘ulemu ndi ukulu’ wake?

8, 9. (a) Kodi ntchito za Mulungu n’zosiyana bwanji ndi ntchito zambiri za anthu? (b) Kodi ndi makhalidwe ati a Mulungu amene inuyo mumawakonda kwambiri?

8 Onani kuti wamasalmo anatsindikanso makhalidwe apamwamba a Yehova, monga chilungamo, chisomo ndi nsoni zokoma kapena kuti chifundo. Inu mukudziwa kuti nthawi zambiri anthu sachita zinthu chifukwa chotsatira chilungamo. Iwo nthawi zambiri amachita zinthu chifukwa cha dyera, nsanje ndi kudzikuza. Umboni wa zimenezi ndi zida zoopsa zimene anthu amapanga kuti alemere ndiponso kuti amenyere nkhondo zimene iwo amayambitsa. Zimenezi zimabweretsa mavuto osaneneka kwa anthu ambirimbiri osalakwa. Ndiponso ntchito zambiri za anthu zimapondereza osauka. Chitsanzo chimene anthu ambiri angapereke ndi kugwiritsa ntchito akapolo pomanga mapiramidi. Mapiramidiwa ankagwiritsidwa ntchito ngati manda a Afarao a ku Iguputo, omwe anali mafumu odzikuza. Ndipo ntchito zambiri za anthu masiku ano sikuti zangokhala zopondereza, koma ‘zimawononganso dziko lapansi.’​—Werengani Chivumbulutso 11:18.

9 Zimenezitu n’zosiyana kwambiri ndi ntchito za Yehova, zomwe nthawi zonse amazichita chifukwa chotsatira chilungamo. Ntchitozo zimaphatikizapo mphatso yachifundo yopulumutsira ochimwa. Popereka dipo, Mulungu ‘anaonetsa chilungamo chake.’ (Aroma 3:25, 26) Indedi, “chilungamo chake chikhalitsa kosatha.” Mulungu wasonyeza chisomo chake pochita zinthu moleza mtima ndi anthu ochimwa. Nthawi zina, iye ankachita kuwachonderera mokoma mtima kuti anthuwo asiye njira zawo zoipa n’kuyamba kuchita zabwino.​—Werengani Ezekieli 18:25.

Amakwaniritsa Malonjezo Ake

10. Kodi Yehova anapereka chitsanzo cha kukhulupirika chotani pankhani ya chipangano chake ndi Abulahamu?

10 “Anapatsa akumuopa Iye chakudya; adzakumbukira chipangano chake kosatha.” (Sal. 111:5) Zikuoneka kuti wamasalmo palembali anali kunena za chipangano cha Abulahamu. Yehova analonjeza kuti adzadalitsa mbewu ya Abulahamu ndipo anati iwo adzagonjetsa chipata cha adani awo. (Gen. 22:17, 18; Sal. 105:8, 9) Pa kukwaniritsidwa koyamba kwa malonjezo amenewa, mbewu ya Abulahamu inadzakhala mtundu wa Isiraeli. Kwa nthawi yaitali, mtunduwu unakhala mu ukapolo ku Iguputo, koma kenako “Mulungu anakumbukira chipangano chake ndi Abrahamu” ndipo anaupulumutsa. (Eks. 2:24) Zimene Yehova anawachitira Aisiraeli atawapulumutsa, zimasonyeza kuti iye ndi wowolowa manja. Iye anawapatsa chakudya chakuthupi kuti akhale ndi moyo ndiponso chakudya chauzimu kuti maganizo awo azigwirizana ndi mfundo zake. (Deut. 6:1-3; 8:4; Neh. 9:21) Koma kwa zaka zambiri kuyambira panthawi imeneyi, mtunduwu nthawi zambiri unkapandukira Mulungu, ngakhale kuti iye ankawatumizira aneneri kuti awapemphe kubwerera kwa iye. Patapita zaka zoposa 1,500 atapulumutsa Aisiraeli ku Iguputo, Mulungu anatumiza Mwana wake wobadwa yekha padziko lapansi. Ayuda ambiri anakana Yesu ndipo analolera kuti iye aphedwe. Choncho, Yehova anapanga mtundu watsopano wauzimu, “Isiraeli wa Mulungu.” Pamodzi ndi Khristu, mtundu umenewu ndiwo mbewu yauzimu ya Abulahamu, imene Yehova analosera kuti adzaigwiritsa ntchito podalitsa anthu onse.​—Agal. 3:16, 29; 6:16.

11. Kodi Yehova akupitiriza bwanji ‘kukumbukira chipangano chake’ ndi Abulahamu?

11 Yehova akupitirizabe ‘kukumbukira chipangano chake’ ndiponso madalitso amene analonjeza kudzera mu chipanganochi. Masiku ano, iye akupereka chakudya chauzimu chochuluka, m’zilankhulo zoposa 400. Ndiponso akupitirizabe kuyankha mapemphero athu okhudza zinthu zakuthupi zimene timafunikira, mogwirizana ndi mawu akuti: “Mutipatse ife chakudya chathu cha lero malinga ndi chakudya chofunika pa tsikuli.”​—Luka 11:3; Sal. 72:16, 17; Yes. 25:6-8.

Mphamvu Zodabwitsa za Yehova

12. Kodi mtundu wa Isiraeli unapatsidwa bwanji “cholowa cha amitundu”?

12 “Anaonetsera anthu ake mphamvu ya ntchito zake, pakuwapatsa cholowa cha amitundu.” (Sal. 111:6) Chinthu chimodzi chosaiwalika m’mbiri ya Aisiraeli chimene wamasalmo ayenera kuti ankachiganizira, chinali kupulumutsidwa kwawo mozizwitsa pochoka ku Iguputo. Yehova atalola Aisiraeli kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, iwo anagonjetsa maufumu a kum’mawa ndi kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodano. (Werengani Nehemiya 9:22-25.) Inde, Yehova anapatsa Aisiraeli “cholowa cha amitundu.” Pamenepatu Mulungu anaonetsa mphamvu zake zazikulu.

13, 14. (a) Kodi wamasalmo ayenera kuti ankaganizira zinthu zotani zimene Mulungu anachita ndi Babulo posonyeza mphamvu zake? (b) Kodi Yehova wachitanso ntchito zazikulu zotani zopulumutsa anthu?

13 Ngakhale kuti Yehova anawachitira zambiri Aisiraeli, tonsefe tikudziwa kuti iwo sanamulemekeze ndiponso sanalemekeze makolo awo Abulahamu, Isake ndi Yakobo. Aisiraeli anapitirizabe kupanduka, mpaka Mulungu anagwiritsa ntchito Ababulo kuwachotsa m’dziko lawo, n’kuwatengera ku ukapolo. (2 Mbiri 36:15-17; Neh. 9:28-30) Akatswiri ena a Baibulo amanena kuti wolemba Salmo 111 anakhala ndi moyo Aisiraeli atabwerako ku Babulo. Ngati zimenezi zili zoona, ndiye kuti iye anali ndi chifukwa chinanso chotamandira Yehova chifukwa cha kukhulupirika ndi mphamvu zake. Mulungu anasonyeza zimenezi populumutsa Ayudawo ku Babulo, ufumu umene unali ndi lamulo losamasula akapolo ake.​—Yes. 14:4, 17.

14 Patatha zaka pafupifupi 500, Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu zake m’njira yapamwamba kwambiri. Iye anapulumutsa anthu olapa ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Chinthu chimodzi chimene chinatheka chifukwa cha zimenezi, ndi mwayi wakuti anthu otsatira Khristu okwana 144,000 adzozedwe ndi mzimu. Mu 1919, Yehova anagwiritsa ntchito mphamvu zake kupulumutsa kagulu kochepa ka otsalira odzozedwa ku ukapolo wa chipembedzo chonyenga. Zinthu zazikulu zimene odzozedwa amenewa akuchita nthawi yamapeto ino zikutheka chifukwa cha mphamvu za Mulungu. Ndipo iwo akakhalabe okhulupirika mpaka imfa, adzalamulira dziko lapansi limodzi ndi Yesu Khristu ali kumwamba, kuti athandize anthu olapa. (Chiv. 2:26, 27; 5:9, 10) Iwo adzalandira dziko lonse lapansi, kuposa mmene zinalili ndi Aisiraeli.​—Mat. 5:5.

Mfundo Zosasintha Ndiponso Zodalirika

15, 16. (a) Kodi zina mwa ntchito za manja a Mulungu ndi ziti? (b) Kodi Mulungu anapereka malamulo otani ku mtundu wa Isiraeli?

15 “Ntchito za manja ake ndizo choonadi ndi chiweruzo; malangizo ake onse ndiwo okhulupirika. Achirikizika ku nthawi za nthawi, achitika m’choonadi ndi chilunjiko.” (Sal. 111:7, 8) Zina mwa “ntchito za manja [a Yehova]” ndi magome awiri amiyala amene panalembedwa malamulo ofunika  10 kuti Aisiraeli aziwatsatira. (Eks. 31:18) Malamulo amenewa ndiponso ena omwe anadzakhala mbali ya chipangano cha Chilamulo cha Mose, ndi ogwirizana ndi mfundo za Mulungu zosasintha ndiponso zodalirika.

16 Mwachitsanzo, limodzi mwa malamulo olembedwa pa magomepo limati: “Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.” Ndipo limapitiriza kunena kuti Yehova ‘amachitira chifundo anthu zikwizikwi amene akondana ndi iye, nasunga malamulo ake.’ Magome amiyala amenewa analinso ndi mfundo zosasintha ndiponso zothandiza monga yakuti, “uzilemekeza atate wako ndi amako” ndi yakuti, “usabe.” Komanso anali ndi lamulo losonyeza nzeru zapamwamba loletsa kusirira zinthu za ena.​—Eks. 20:5, 6, 12, 15, 17.

Mpulumutsi Wathu Woyera Ndiponso Wochititsa Mantha

17. Kodi Aisiraeli anali ndi zifukwa zotani zochitira zinthu mosonyeza kuti dzina la Mulungu ndi loyera?

17 “Anatumizira anthu ake chipulumutso; analamulira chipangano chake kosatha; dzina lake ndilo loyera ndi loopedwa.” (Sal. 111:9) Apanso wamasalmo ayenera kuti ankaganizira za kukhulupirika kwa Yehova pa zimene analonjeza m’chipangano chake kwa Abulahamu. Mogwirizana ndi zimene analonjeza, Yehova sanataye anthu ake, choyamba pamene anali akapolo ku Iguputo ndipo kenako pamene anali andende ku Babulo. Panthawi ziwiri zonsezi, Mulungu anapulumutsa anthu ake. Ndipotu ngakhale zinthu ziwiri zokhazi, zinali zokwanira kupangitsa Aisiraeli kuona kuti dzina la Mulungu ndi loyera.​—Werengani Eksodo 20:7; Aroma 2:23, 24.

18. Kodi n’chifukwa chiyani inuyo mukuona kuti ndi mwayi wapadera kudziwika ndi dzina la Mulungu?

18 N’chimodzimodzinso ndi Akhristu masiku ano, amene apulumutsidwa ku ukapolo wowawa wa uchimo ndi imfa. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti moyo wathu uzigwirizana ndi pempho loyamba m’pemphero la chitsanzo, lomwe limati: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mat. 6:9) Kusinkhasinkha dzina lokwezeka limeneli kuyenera kutithandiza kukhala ndi mantha aumulungu. Wolemba Salmo 111 anali kuwadziwa bwino mantha aumulungu ndipo anati: “Kumuopa Yehova ndiko chiyambi cha nzeru; onse akuchita chotero [kusunga malamulo ake] ali nacho chidziwitso chokoma.”​Sal. 111:10.

19. Kodi mu nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

19 Kuopa Mulungu moyenera kungatithandize kudana ndi zoipa. Kungatithandizenso kutengera makhalidwe apamwamba a Mulungu amene afotokozedwa mu Salmo 112, limene tidzakambirane mu nkhani yotsatira. Salmo limeneli limasonyeza zimene tingachite kuti tikhale m’gulu la anthu mamiliyoni ambiri amene adzatamande Mulungu kosatha. Iye ndi woyeneradi kutamandidwa. “Chilemekezo chake chikhalitsa kosatha.”​Sal. 111:10.

Mafunso Owasinkhasinkha

• N’chifukwa chiyani Yehova ndi woyenera kutamandidwa ndi tonsefe?

• Kodi ntchito za Yehova zimasonyeza makhalidwe ake ati?

• Kodi inuyo mumauona bwanji mwayi womwe muli nawo wodziwika ndi dzina la Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 20]

Cholinga chachikulu chopezekera pamisonkhano yathu nthawi zonse n’kutamanda Yehova

[Chithunzi patsamba 23]

Malamulo onse a Yehova ndi ogwirizana ndi mfundo zake zosasintha ndiponso zodalirika