Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru za Yehova

Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru za Yehova

Chilengedwe Chimasonyeza Nzeru za Yehova

‘Makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso . . . akuonekera m’zinthu zimene anapanga.’​—AROMA 1:20.

1. Kodi n’chiyani chimene chimachitikira anthu ambiri masiku ano amene amatsatira nzeru za dzikoli?

NTHAWI zambiri anthu amagwiritsa ntchito mawu akuti “nzeru” mwachisawawa. Ena amanena kuti ngati munthu akudziwa zinthu zambiri ndiye kuti basi ndi wanzeru. Komabe, anthu amene dzikoli limati ndi anzeru kwambiri sapereka malangizo odalirika othandiza anthu kudziwa cholinga chenicheni cha moyo. M’malomwake, anthu amene amatsatira malangizo a anthu anzeruwa ‘amatengekatengeka ngati kuti akukankhidwa ndi mafunde, ndiponso amangotengeka uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso.’​—Aef. 4:14.

2, 3. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ndiye “wanzeru yekhayo”? (b) Kodi nzeru yochokera kwa Mulungu imasiyana bwanji ndi nzeru ya dzikoli?

2 Zimenezi ndi zosiyana kwambiri ndi anthu amene amapeza nzeru yeniyeni, yochokera kwa Yehova Mulungu. Baibulo limatiuza kuti Yehova ndiye “wanzeru yekhayo.” (Aroma 16:27) Iye amadziwa zonse zokhudza chilengedwe chonse, kuphatikizapo kapangidwe kake ndi mbiri yake. Malamulo onse a m’chilengedwe, amene anthu amadalira akamachita ntchito yawo yakafukufuku, ndi opangidwa ndi Yehova. Choncho, iye sachita chidwi ndi ntchito zaluso za manja a anthu ndiponso sadabwa ndi nzeru za anthu zimene anthu amati n’zapamwamba. “Kwa Mulungu nzeru za m’dzikoli n’zopusa.”​—1 Akor. 3:19.

3 Baibulo limatiuza kuti Yehova ‘amapatsa nzeru’ atumiki ake. (Miy. 2:6) Mosiyana ndi nzeru za anthu, nzeru yochokera kwa Mulungu si yosokoneza. M’malomwake, imathandiza munthu kuganiza bwino ndipo kuti munthu aipeze afunika kumvetsa ndi kudziwa zinthu molondola. (Werengani Yakobe 3:17.) Mtumwi Paulo anazizwa ndi nzeru za Yehova. Iye analemba kuti: “Ha, kuchuluka kwa chuma cha Mulungu! Nzeru zake n’zozama, ndipo kudziwa kwake zinthu n’kozamanso zedi! Ziweruzo zake ndi zosasanthulika.” (Aroma 11:33) Chifukwa chakuti Yehova ndiye mwini nzeru, tili ndi chidaliro chakuti malamulo ake angatithandize kukhala ndi moyo wabwino koposa. Komanso kuposa wina aliyense, Yehova ndiye amadziwa bwino kwambiri zimene timafunikira kuti tikhale osangalala.​—Miy. 3:5, 6.

Yesu Ndi “Mmisiri”

4. Kodi ndi njira imodzi iti imene tingadziwire nzeru za Yehova?

4 Nzeru za Yehova komanso makhalidwe ake ena osayerekezereka, zimaonekera mu zinthu zimene iye anapanga. (Werengani Aroma 1:20.) Kuyambira pa zinthu zazikulu mpaka zinthu zazing’ono, ntchito za Yehova zimasonyeza makhalidwe ake. Kulikonse kumene tingayang’ane, kaya ndi kumwamba kapena m’nthaka, timapeza umboni wochuluka wakuti kuli Mlengi wachikondi ndiponso wanzeru zonse. Tingaphunzire zambiri za iye mwa kuona zinthu zimene anapanga.​—Sal. 19:1; Yes. 40:26.

5, 6. (a) Kodi Yehova anagwira ndi ndani ntchito yolenga? (b) Kodi tikambirana chiyani, ndipo chifukwa chiyani?

5 Yehova sanali yekha ‘polenga kumwamba ndi dziko lapansi.’ (Gen. 1:1) Baibulo limasonyeza kuti kalekale Mulungu asanalenge zinthu zooneka ndi maso, iye analenga munthu wauzimu amene kudzera mwa iye anapanga “zinthu zina zonse.” Ameneyu ndi Mwana wake wobadwa yekha, “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse,” amene pambuyo pake anadzakhala padziko lapansi monga munthu, dzina lake Yesu. (Akol. 1:15-17) Mofanana ndi Yehova, Yesu ali ndi nzeru. Ndipotu lemba la Miyambo chaputala 8 limamufotokoza ngati kuti ndi nzeru imene ikulankhula. Chaputala chimenechi chimatchulanso Yesu kuti “mmisiri” wa Mulungu.​—Miy. 8:12, 22-31.

6 Choncho, zinthu zolengedwa zimene timaona ndi maso zimasonyeza nzeru za Yehova ndiponso za Mmisiri wake, Yesu. Zinthu zimenezi zingatiphunzitse mfundo zofunika kwambiri. Tiyeni tikambirane zitsanzo zinayi za zolengedwa zimene zikufotokozedwa pa Miyambo 30:24-28 kuti ndi ‘zopambana kukhala zanzeru,’ kapena kuti ndi zanzeru mwachibadwa. *

Nyerere Zingatiphunzitse Kugwira Ntchito Mwakhama

7, 8. Kodi inuyo mwachita chidwi ndi chiyani pa nkhani ya nyerere?

7 Tikamaganizira mmene zinthu “zazing’ono” zinalengedwera komanso zimene zimachita, tingaphunzire zambiri. Mwachitsanzo, taganizirani za nzeru zachibadwa za nyerere.​—Werengani Miyambo 30:24, 25.

8 Akatswiri ena amaganiza kuti nyerere ndi zochuluka kwambiri kuposa anthu kuwirikiza 200,000 kapena kuposerapo, ndipo zonse zimakhala kalikiliki kugwira ntchito panthaka komanso pansi pa nthaka. Nyerere zili ndi midzi yawo, ndipo m’midzi yambiri muli mitundu itatu ya nyerere. Mitunduyi ndi manthu, nyerere zazimuna ndi zina zogwira ntchito. Gulu lililonse limathandiza m’njira yakeyake kusamalira zofunika pamudzi wawo. Mtundu wina wa nyerere imene imapezeka ku South America imadula masamba. Tingati nyerere imeneyi ndi katswiri wa zaulimi. Nyerere yaing’ono imeneyi imathira manyowa m’minda yake ya nkhungu, imaokera mbewu ndi kudulira mbeuzo, ndipo zimenezi zimathandiza kuti nyerereyi ikolole chakudya chambiri. Akatswiri apeza kuti katswiri wa “zaulimi” ameneyu amachita khama paulimi wakewo, malinga ndi kuchuluka kwa chakudya chimene chingafunikire pamudzipo. *

9, 10. Kodi tingatani kuti tikhale akhama ngati nyerere?

9 Nyerere zikutiphunzitsa kanthu kena. Zikutiphunzitsa kuti tiyenera kuchita khama ngati tikufuna kuti zinthu zitiyendere bwino. Baibulo limatiuza kuti: “Pita kunyerere, wolesi iwe, penya njira zawo nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitawo, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zawo m’malimwe; nizituta dzinthu zawo m’masika.” (Miy. 6:6-8) Yehova ndi Mmisiri wake, Yesu, ndi akhama pantchito. Yesu anati: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.”​—Yoh. 5:17.

10 Popeza timatsanzira Mulungu ndi Khristu, ifenso tiyenera kukhala akhama pantchito. Kaya tili ndi mbali yotani m’gulu la Mulungu, tonsefe tiyenera ‘kukhala ndi zochita zochuluka m’ntchito ya Ambuye.’ (1 Akor. 15:58) Choncho, ndi bwino kutsatira malangizo amene Paulo anapereka kwa Akhristu a ku Roma. Iye anati: “Musakhale aulesi pantchito yanu. Yakani ndi mzimu. Tumikirani Yehova monga akapolo.” (Aroma 12:11) Khama lathu pochita chifuniro cha Yehova silipita pachabe, chifukwa Baibulo limatitsimikizira kuti: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”​—Aheb. 6:10.

Chitetezo Chauzimu

11. Fotokozani makhalidwe ena a mbira.

11 Mbira ndi mtundu wina wa zolengedwa zazing’ono zimene zingatiphunzitse mfundo zofunika kwambiri. (Werengani Miyambo 30:26.) Nyamayi imaoneka ngati kalulu ndipo ili ndi makutu aafupi koma ozungulira, komanso miyendo yake ndi yaifupi. Nyama yaing’ono imeneyi imakhala m’matanthwe. Iyo ili ndi maso akuthwa kwambiri ndipo amaithandiza kuona msanga adani. Komanso m’matanthwe amene imakhala muli maenje ndi mphako zimene zimaiteteza kwa adani. Mwachibadwa, mbira zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, ndipo zimenezi zimapereka chitetezo komanso zimathandiza nyamazi kukhala zofunda m’nyengo yozizira. *

12, 13. Kodi tikuphunzira chiyani kwa mbira?

12 Kodi tikuphunzira chiyani kwa mbira? Choyamba, onani kuti nyamayi imasamala kuti isagwidwe. Imagwiritsa ntchito maso ake akuthwa kuonera msanga adani ngakhale ali kutali, ndipo imakhala pafupi ndi dzenje kapena mphako, zimene zingathandize kupulumutsa moyo wake. Ifenso tiyenera kukhala ndi maso auzimu akuthwa kuti tizitha kuona zinthu zobisika zangozi zimene zili m’dziko la Satanali. Mtumwi Petulo analangiza Akhristu kuti: “Sungani maganizo anu, khalani maso. Mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti wina umudye.” (1 Pet. 5:8) Yesu ali padziko lapansi, anakhalabe maso, inde watcheru, pamene Satana ankayesetsa kufuna kuswa umphumphu Wake. (Mat. 4:1-11) Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino kwa otsatira ake.

13 Njira imodzi imene tingakhalire maso ndiyo kuyesetsa kugwiritsa ntchito chitetezo chauzimu chimene Yehova wapereka kwa ife. Sitiyenera kunyalanyaza kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kupezeka pamisonkhano yachikhristu. (Luka 4:4; Aheb. 10:24, 25) Ndiponso mofanana ndi mbira zimene zimakula bwino chifukwa chokhala pagulu, tifunikira kukhala pafupi kwambiri ndi Akhristu anzathu kuti ‘tizilimbikitsana.’ (Aroma 1:12) Tikamagwiritsa ntchito chitetezo chimene Yehova wapereka, timasonyeza kuti tikugwirizana ndi zimene wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova ndiye thanthwe langa, ndi linga langa, ndi mpulumutsi wanga; Mulungu wanga, ngaka yanga, ndidzakhulupirira Iye.”​—Sal. 18:2.

Musagonje Potsutsidwa

14. Ngakhale kuti dzombe limodzi silingachititse mantha, kodi tinganene chiyani za dzombe lambiri?

14 Nalonso dzombe lingatiphunzitse kanthu kena. Dzombe limodzi, limene lingatalike pafupifupi masentimita asanu, mwina silingachititse mantha. Koma limachititsa mantha likakhala lambiri. (Werengani Miyambo 30:27.) Popeza dzombe limakhala lanjala kwambiri, gulu losatopa limeneli pa nthawi yochepa lingawononge munda wa mbewu zimene zacha kale. Baibulo limayerekezera mkokomo wa kubwera kwa tizilombo tambiri, kuphatikizapo dzombe, ndi phokoso la magaleta komanso kuthetheka kwa moto umene ukupsereza ziputu. (Yow. 2:3, 5) Anthu amayatsa moto kuti aletse dzombe limene likubwera, koma zimenezi nthawi zambiri sizithandiza. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti matupi a dzombe limene lafa amazimitsa motowo, kenako dzombe lotsalalo limapitirizabe ulendo wake popanda choletsa. Ngakhale kuti lilibe mfumu kapena mtsogoleri, gulu la dzombe limakhala ladongosolo ngati gulu la nkhondo, ndipo limagonjetsa zopinga zamtundu uliwonse. *​—Yow. 2:25.

15, 16. Kodi olengeza Ufumu a masiku ano ali ngati dzombe motani?

15 Mneneri Yoweli anayerekezera ntchito ya atumiki a Yehova ndi mmene dzombe limachitira. Iye analemba kuti: “Athamanga ngati amphamvu; akwera linga ngati anthu a nkhondo; niliyenda lililonse njira yake, osasokonezeka m’mabande awo. Sakankhana, ayenda lililonse m’mopita mwake; akagwa m’zida, siithyoka nkhondo yawo.”​—Yow. 2:7, 8.

16 Ulosi umenewu ukufotokoza bwino za olengeza Ufumu wa Mulungu a masiku ano. Palibe “linga” la chitsutso limene latha kuletsa ntchito yawo yolalikira. M’malomwake, iwo amatsanzira Yesu, amene analimbikira kuchita chifuniro cha Mulungu ngakhale kuti ankanyozedwa ndi anthu ambiri. (Yes. 53:3) Ndi zoona kuti Akhristu ena ‘agwa m’zida’ pophedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Koma ntchito yolalikira yapitabe patsogolo, ndipo chiwerengero cha olengeza Ufumu chikuchulukirabe. Ndipotu nthawi zambiri, chizunzo chathandiza kufalitsa uthenga wabwino kwa anthu amene popanda chizunzocho, sakanamva uthenga wa Ufumu. (Mac. 8:1, 4) Kodi inuyo pa utumiki wanu, mwasonyeza mtima wosagonja ngati dzombe, ngakhale mutakumana ndi chitsutso kapena anthu opanda chidwi?​—Aheb. 10:39.

“Gwiritsitsani Chabwino”

17. N’chifukwa chiyani mapazi a nalimata amatha kugwira pamalo osalala?

17 Kabuluzi kakang’ono kotchedwa nalimata kamakhala ngati sikakhudzidwa ndi mphamvu yokoka ya dziko lapansi. (Werengani Miyambo 30:28.) Ndipo m’pake kuti asayansi amadabwa ndi luso la kacholengedwa kameneka. Iko kamatha kukwera khoma mothamanga ndipo nthawi zina kamatha kuthamanga kudenga losalala la nyumba chagada koma osagwa. Kodi nalimata amatha bwanji kuchita zimenezi? Chinsinsi chake sichinagone pa zida zomatira kapena mtundu wa guluu. M’malomwake, chala chilichonse cha nalimata n’chophwatalala ndipo chili ndi timizere, ndipo m’timizere timeneti muli tinthu masauzande ambirimbiri tokhala ngati tsitsi. Nakonso katsitsi kamodzi kali ndi timphanda mazana ambiri timene kunsonga kwake ndi kozungulira ngati sosala. M’timphanda timeneti muli mphamvu yokwanira kapena yoposerapo yothandiza nalimatayo kuti asagwe, ngakhale pamene akuthamanga chagada pagalasi. Pochita chidwi ndi luso la nalimata, akatswiri amanena kuti ngati angapange zinthu potengera mapangidwe a mapazi a nalimata, zinthuzo zingathe kukhala zomatira zamphamvu kwambiri. *

18. Kodi tingachite bwanji kuti nthawi zonse ‘tizigwiritsitsa chabwino’?

18 Kodi nalimata akutiphunzitsa chiyani? Baibulo limatilangiza kuti: “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.” (Aroma 12:9) M’dziko la Satanali muli zinthu zosayenera zambirimbiri zimene zingatilepheretse kugwiritsitsa mfundo zochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, tingakhale ndi mtima wosafuna kuchita chabwino ngati ticheza ndi anthu amene samamatira malamulo a Mulungu kaya kusukulu, kuntchito kapena kudzera m’zosangalatsa zosayenera. Musalole zimenezo kukuchitikirani. Mawu a Mulungu amachenjeza kuti: “Usadziyese wekha wanzeru.” (Miy. 3:7) M’malomwake, tsatirani uphungu wanzeru umene Mose anapereka kwa anthu a Mulungu a m’nthawi yakale, wakuti: “Muziopa Yehova Mulungu wanu; mum’tumikire iyeyo; mum’mamatire iye.” (Deut. 10:20) Tikamumamatira Yehova, ndiye kuti tikutsanzira Yesu, amene ponena za iye, Baibulo limati: “Unakonda chilungamo, unadana ndi kusamvera malamulo.”​—Aheb. 1:9.

Zimene Chilengedwe Chimatiphunzitsa

19. (a) Kodi ndi makhalidwe ati a Yehova amene inuyo mumaona m’chilengedwe? (b) Kodi tingapindule bwanji ndi nzeru yochokera kwa Mulungu?

19 Monga taonera, makhalidwe a Yehova amaonekera bwino lomwe m’zinthu zimene anapanga, ndiponso zinthu zimene iye analenga zimatiphunzitsa mfundo zofunika kwambiri. Tikamaphunzira kwambiri ntchito za Yehova, m’pamenenso timadabwa kwambiri ndi nzeru zake. Ngati tipitirizabe kuphunzira za nzeru za Mulungu, tingakhale osangalala kwambiri panopa ndiponso nzeruyo idzatiteteza m’tsogolo. (Mlal. 7:12) Inde, tidzaona kuti lonjezo la pa Miyambo 3:13, 18 ndi loona. Mawu ake amati: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira n’ngodala.”

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Makamaka ana komanso achinyamata angachite bwino kuwerenga zimene zasonyezedwa m’mawu a m’munsi a munkhani ino, ndipo adzafotokoze zimene apeza podzakambirana nkhaniyi kumpingo pa Phunziro la Nsanja ya Olonda.

^ ndime 8 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya nyerere yodula masamba, onani Galamukani! ya Chingelezi ya March 22, 1997, tsamba  31, ndi ya Chichewa ya June 8, 2002, tsamba 31.

^ ndime 11 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya mbira, onani Galamukani! ya Chingelezi ya September 8, 1990, masamba 15-16.

^ ndime 14 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya dzombe, onani Insight on the Scriptures, Vol. 2, masamba 260-261.

^ ndime 17 Kuti mudziwe zambiri pa nkhani ya nalimata, onani Galamukani! ya April 2008, tsamba 26.

Kodi Mukukumbukira?

Kodi ndi mfundo zothandiza zotani zimene tikuphunzira kwa . . .

• nyerere?

• mbira?

• dzombe?

• nalimata?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 16]

Kodi ndinu wakhama ngati nyerere imene imadula masamba?

[Zithunzi patsamba 17]

Mbira imapeza chitetezo mwa kukhala pagulu. Kodi inunso mumatero?

[Zithunzi patsamba 18]

Monga dzombe, Akhristu amasonyeza mtima wosagonja

[Chithunzi patsamba 18]

Monga mmene nalimata amamatirira pamalo, Akhristu amamatirira chabwino

[Mawu a Chithunzi]

Stockbyte/​Getty Images