Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuzindikira Mose Wamkulu

Kuzindikira Mose Wamkulu

Kuzindikira Mose Wamkulu

“Yehova Mulungu adzakuutsirani mneneri ngati ine kuchokera mwa abale anu. Mudzam’mvere iye.”​—MAC. 3:22.

1. Kodi Yesu Khristu wakhudza bwanji mbiri ya anthu?

ZAKA 2,000 zapitazo, kunabadwa mwana wamwamuna. Mwanayu atabadwa, khamu la angelo kumwamba linatamanda Mulungu, ndipo abusa ena anamva zimenezi. (Luka 2:8-14) Mwanayu atakwanitsa zaka 30, anayamba ntchito imene anaigwira kwa zaka zitatu ndi theka basi, koma inasintha kwambiri mbiri yonse ya anthu. Wolemba mbiri wina wotchuka wa m’zaka za m’ma 1800, dzina lake Philip Schaff, anagoma ndi mnyamata ameneyu ndipo anati: “Mnyamatayu sanalembe chilichonse, koma chifukwa cha zimene analankhula ndi kuchita, anthu ambiri anapeza zolemba m’mabuku awo, zoimba m’nyimbo zawo, zolankhula m’maulaliki awo, ndiponso zojambula. Kuyambira kale mpaka masiku ano palibe munthu wotchuka aliyense amene anachita zimenezi.” Mnyamata wochititsa chidwi ameneyu si wina ayi koma Yesu Khristu.

2. Kodi mtumwi Yohane anati chiyani za Yesu ndi utumiki Wake?

2 Mtumwi Yohane analemba nkhani ya utumiki wa Yesu ndipo pomaliza nkhaniyo anati: “Pali zinthu zinanso zambiri zimene Yesu anachita, chikhala kuti zinalembedwa zonse mwa tsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana m’dzikoli.” (Yoh. 21:25) Yohane anadziwa kuti sakanatha kulemba zonse zimene Yesu analankhula ndi kuchita m’zaka zitatu ndi theka zosaiwalika zimenezi. Komabe zochitika zimene Yohane analemba mu Uthenga Wabwino n’zopindulitsa kwambiri.

3. Kodi n’chiyani chingatithandize kumvetsa udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu?

3 Kuwonjezera pa nkhani za m’mabuku anayi a Uthenga Wabwino, mabuku enanso a m’Baibulo amafotokoza mfundo zolimbitsa chikhulupiriro zokhudza moyo wa Yesu. Mwachitsanzo, nkhani za m’Baibulo zofotokoza za amuna okhulupirika amene anakhalapo Yesu asanabadwe, zili ndi mfundo zimene zimatithandiza kumvetsa udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Tiyeni tikambirane zina mwa nkhani zimenezi.

Anthu a Mulungu Amene Anachitira Chithunzi Khristu

4, 5. Kodi ndi anthu ati amene anachitira chithunzi Yesu, ndipo anachita bwanji zimenezi?

4 Yohane ndi anzake ena atatu amene analemba Mauthenga Abwino anasonyeza kuti Mose, Davide ndi Solomo anachitira chithunzi Yesu monga Wodzozedwa wa Mulungu komanso Mfumu Yam’tsogolo. Kodi atumiki a Mulungu akale amenewa anakhala bwanji akalambula bwalo a Yesu, ndipo tingaphunzire chiyani pa nkhani za anthu amenewa?

5 Kunena mwachidule, Baibulo limatiuza kuti Mose anali mneneri, mkhalapakati komanso mpulumutsi. N’chimodzimodzinso ndi Yesu. Davide anali mbusa komanso mfumu imene inagonjetsa adani a Isiraeli. Nayenso Yesu ndi mbusa komanso mfumu imene ikugonjetsa adani ake. (Ezek. 37:24, 25) Pamene Solomo anali wokhulupirika, iye anali wolamulira wanzeru, ndipo mu ufumu wake Aisiraeli anali pa mtendere. (1 Maf. 4:25, 29) Nayenso Yesu ndi wanzeru kwambiri ndipo amatchedwa “Kalonga wa mtendere.” (Yes. 9:6) Izi zikusonyeza kuti udindo wa Khristu Yesu ndi wofanana ndi wa amuna akale amenewa, ngakhale kuti udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu ndi waukulu kwambiri. Choyamba, tiyeni tione kufanana kwa Yesu ndi Mose, kumene kudzatithandiza kumvetsa kwambiri udindo wa Yesu pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.

Mose Anali Kalambula Bwalo wa Yesu

6. Kodi mtumwi Petulo anafotokoza bwanji kufunika komvera Yesu?

6 Tsiku lina Pentekosite wa mu 33 C.E. atachitika, mtumwi Petulo ananena mawu a mu ulosi wa Mose umene unakwaniritsidwa ndi Yesu Khristu. Apa Petulo anali ataimirira pamaso pa gulu la anthu amene ankalambira m’kachisi. Anthuwa anali “odabwa kwambiri” pamene Petulo ndi Yohane anachiritsa munthu wopemphapempha amene anali wolemala chibadwire, ndipo iwo anathamanga kuti akaone zimene zinachitika. Petulo anawafotokozera kuti zodabwitsa zimenezo zinachitika chifukwa cha mphamvu ya mzimu woyera wa Yehova umene unagwira ntchito kudzera mwa Yesu Khristu. Kenako iye ananena mawu a m’Malemba a Chiheberi ndipo anati: “Mose anati, ‘Yehova Mulungu adzakuutsirani mneneri ngati ine kuchokera mwa abale anu. Mudzam’mvere iye pa zinthu zonse zimene adzalankhula kwa inu.’”​—Mac. 3:11, 22, 23; werengani Deuteronomo 18:15, 18, 19.

7. Kodi n’chifukwa chiyani anthu amene Petulo anali kulankhula nawo anatha kumvetsa za mneneri wamkulu woposa Mose?

7 Anthu amene Petulo anali kulankhula nawo ayenera kuti ankadziwa mawu a Mose amenewa. Monga Ayuda, iwo ankamulemekeza kwambiri Mose. (Deut. 34:10) Iwo ankayembekezera mwachidwi kubwera kwa mneneri wamkulu woposa Mose. Mneneri ameneyo sanali mesiya wina aliyense kapena wodzozedwa wa Mulungu monga Mose, koma anali Mesiya weniweni, “Khristu wa Mulungu, Wosankhika” wa Yehova.​—Luka 23:35; Aheb. 11:26.

Kufanana kwa Yesu ndi Mose

8. Kodi moyo wa Yesu ndi wa Mose unali wofanana motani?

8 Moyo wapadziko lapansi wa Yesu unali wofanana ndi wa Mose m’mbali zina. Mwachitsanzo, Mose ndi Yesu ali ana anapulumuka, mafumu ankhanza atafuna kuwapha. (Eks. 1:22–2:10; Mat. 2:7-14) Kuwonjezera pamenepo, onse ‘anaitanidwa ali m’Aigupto.’ Mneneri Hoseya ananena kuti: “Pamene Israyeli anali mwana, ndinam’konda, ndinaitana mwana wanga ali m’Aigupto.” (Hos. 11:1) Hoseya ankanena za nthawi imene mtundu wa Isiraeli unatulutsidwa ku Iguputo, motsogoleredwa ndi mtsogoleri wawo wosankhidwa ndi Mulungu, Mose. (Eks. 4:22, 23; 12:29-37) Komabe Hoseya sankangonena zinthu zakale zokha koma ankaloseranso zam’tsogolo. Ulosi wakewu unakwaniritsidwa pamene Yosefe ndi Mariya anachoka ku Iguputo ndi Yesu kubwerera kwawo, Mfumu Herode atafa.​—Mat. 2:15, 19-23.

9. (a) Kodi Mose ndi Yesu anachita zozizwitsa zotani? (b) Nenani kufanana kwina kwa Yesu ndi Mose. (Onani bokosi lakuti  “Kufanana Kwinanso kwa Yesu ndi Mose,” patsamba 26.)

9 Onse awiri, Mose ndi Yesu, anachita zozizwitsa zimene zinasonyeza kuti Yehova anali nawo. Baibulo limasonyeza kuti Mose ndiye anali munthu woyamba kuchita zozizwitsa. (Eks. 4:1-9) Mwachitsanzo, Mose anachita zozizwitsa ndi madzi. Iye analamula kuti madzi a mtsinje wa Nile ndi matamanda ake asanduke magazi, kuti Nyanja Yofiira igawanike, ndiponso kuti madzi atuluke m’thanthwe la m’chipululu. (Eks. 7:19-21; 14:21; 17:5-7) Nayenso Yesu anachita zozizwitsa ndi madzi. Chozizwitsa choyamba chimene iye anachita chinali kusandutsa madzi kukhala vinyo paphwando la ukwati. (Yoh. 2:1-11) Kenako, iye anatontholetsa namondwe wamphamvu panyanja ya Galileya. Ndipo nthawi ina iye anachita kuyenda pamadzi. (Mat. 8:23-27; 14:23-25) Kuti mudziwe kufanana kwina kwa Mose ndi Yesu, yemwe ndi Mose Wamkulu, onani  bokosi patsamba 26.

Dziwani Kuti Khristu Ndi Mneneri

10. Kodi mneneri weniweni ndi munthu wotani, ndipo n’chifukwa chiyani Mose anali mneneri weniweni?

10 Anthu ambiri amaganiza kuti mneneri ndi munthu amene amalosera zam’tsogolo basi, koma imeneyi ndi ntchito imodzi chabe ya mneneri. Mneneri weniweni ndi munthu wouziridwa amene amalankhulira Yehova. Iye amalengeza “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Mac. 2:11, 16, 17) Zinthu zina zimene iye amachita pa ntchito yake ya uneneri ndi kulosera zinthu zam’tsogolo, kudziwitsa anthu mbali zokhudza cholinga cha Yehova, kapena kulengeza ziweruzo za Mulungu. Mose anali mneneri wotero. Iye analosera uliwonse wa Milili Khumi imene inagwera dziko la Iguputo. Anadziwitsa Aisiraeli za pangano la Chilamulo paphiri la Sinai. Ndipo anaphunzitsa mtunduwo chifuniro cha Mulungu. Koma m’kupita kwa nthawi, panali kudzabwera mneneri wamkulu kuposa Mose.

11. Kodi Yesu anakwaniritsa bwanji udindo wake monga mneneri wamkulu kuposa Mose?

11 Patapita zaka zambirimbiri, Zekariya anakhala mneneri pamene anadziwitsa anthu cholinga cha Mulungu chokhudza mwana wake, Yohane. (Luka 1:76) Mwana ameneyo anadzakhala Yohane Mbatizi, ndipo iye analengeza za kubwera kwa mneneri wamkulu kuposa Mose, Yesu Khristu, amene anthu anamuyembekezera kwa nthawi yaitali. (Yoh. 1:23-36) Monga mneneri, Yesu analosera zinthu zambiri. Mwachitsanzo, iye analosera za imfa yake, ndipo anafotokoza mmene adzafera, komwe adzafera ndiponso anthu amene adzamupha. (Mat. 20:17-19) Yesu analoseranso za kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi kachisi wake, zimene zinadabwitsa kwambiri omvera ake. (Maliko 13:1, 2) Ndipo zinthu zimene iye analosera zikuchitika masiku ano.​—Mat. 24:3-41.

12. (a) Kodi Yesu anayala bwanji maziko a ntchito yapadziko lonse yolalikira? (b) N’chifukwa chiyani timatsatira chitsanzo cha Yesu masiku ano?

12 Kuwonjezera pa kukhala mneneri, Yesu analinso mlaliki ndi mphunzitsi. Iye analalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ndipo ankalankhula molimba mtima kwambiri kuposa wina aliyense. (Luka 4:16-21, 43) Komanso iye anali mphunzitsi wopanda wina wofanana naye. Anthu ena amene anamva Yesu akuphunzitsa anati: “Palibe munthu analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” (Yoh. 7:46) Yesu anali wachangu pa ntchito yake yolalikira uthenga wabwino, ndipo zimenezi zinalimbikitsanso otsatira ake kuti akhale achangu pa ntchito ya Ufumu. Choncho, iye anayala maziko a ntchito yapadziko lonse yolalikira ndi kuphunzitsa imene ikuchitikabe masiku ano. (Mat. 28:18-20; Mac. 5:42) Mwachitsanzo, chaka chatha otsatira a Khristu oposa 7 miliyoni anathera maola pafupipafupi 1.5 biliyoni akulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kuphunzitsa anthu achidwi choonadi cha m’Baibulo. Kodi inuyo mukugwira nawo ntchito imeneyi mwakhama?

13. Kodi n’chiyani chimene chingatithandize ‘kukhalabe maso’?

13 Palibe amene angatsutse kuti Yehova anakwaniritsa ulosi wakuti adzautsa mneneri ngati Mose. Kodi kudziwa zimenezi kwakukhudzani bwanji? Kodi kwalimbitsa chikhulupiriro chanu chakuti maulosi ouziridwa onena za zimene zichitike posachedwa adzakwaniritsidwa? Zoonadi, kusinkhasinkha chitsanzo cha Mose Wamkulu kungatithandize kuti “tikhalebe maso ndi kusunga maganizo athu” pa zinthu zimene Mulungu achite posachedwapa.​—1 Ates. 5:2, 6.

Khristu Ndi Mkhalapakati Wofunika

14. Kodi Mose anakhala bwanji mkhalapakati wa Aisiraeli ndi Mulungu?

14 Mofanana ndi Mose, Yesu anali mkhalapakati. Mkhalapakati amagwirizanitsa mbali ziwiri. Yehova anagwiritsa ntchito Mose monga mkhalapakati wake ndi Aisiraeli pokhazikitsa pangano la Chilamulo. Ana a Yakobo akanamvera malamulo a Mulungu, akanakhalabe chuma chapadera cha Mulungu, mpingo wake. (Eks. 19:3-8) Pangano limenelo linagwira ntchito kuyambira mu 1513 B.C.E. mpaka m’zaka zoyambirira za m’ma C.E.

15. N’chifukwa chiyani Yesu ali mkhalapakati wamkulu?

15 Mu 33 C.E., Yehova anakhazikitsa pangano ndi Isiraeli watsopano, “Isiraeli wa Mulungu,” yemwe anakhala mpingo wapadziko lonse wa Akhristu odzozedwa. Pangano limeneli ndi loposa loyamba lija. (Agal. 6:16) Ngakhale kuti pangano limene Mose anali mkhalapakati wake linali ndi malamulo olembedwa ndi Mulungu pamiyala, pangano limene mkhalapakati wake ndi Yesu, ndilo lapamwamba kwambiri. Malamulo ake ndi olembedwa ndi Mulungu m’mitima ya anthu. (Werengani 1 Timoteyo 2:5; Aheberi 8:10.) Choncho, “Isiraeli wa Mulungu” tsopano ndiye chuma chapadera cha Mulungu, “mtundu wobala zipatso” za Ufumu wa Mesiya. (Mat. 21:43) Anthu a mtundu wauzimu umenewu ndi amene ali m’pangano latsopano limeneli. Koma sikuti ndi iwo okha amene adzapeza madalitso a panganoli. Gulu la anthu osawerengeka, kuphatikizapo ambiri amene akugona mu imfa, adzalandira madalitso osatha chifukwa cha pangano lapamwamba limeneli.

Lemekezani Khristu Yemwe Ndi Mpulumutsi

16. (a) Kodi Yehova anamugwiritsa ntchito bwanji Mose populumutsa Aisiraeli? (b) Malinga ndi Eksodo 14:13, kodi Mpulumutsi weniweni ndani?

16 Usiku womaliza Aisiraeli asanachoke ku Iguputo, moyo wa ena mwa ana awo unali pa ngozi. Mngelo wa Mulungu anali atatsala pang’ono kudutsa m’dziko la Iguputo ndi kupha ana onse oyamba kubadwa. Yehova anauza Mose kuti Aisiraeli atenge magazi a mwana wa nkhosa wa Pasika ndi kuwawaza pamphuthu za makomo a nyumba zawo, kuti ana awo oyamba kubadwa apulumuke. (Eks. 12:1-13, 21-23) Ndipo iwo anachita zimenezi. Pambuyo pake, mtundu wonsewo unakhala pa ngozi. Iwo anasowa kolowera atafika pa Nyanja Yofiira chifukwa kumbuyo kwawo kunali kubwera magaleta a nkhondo a ku Iguputo. Apanso Yehova anawapulumutsa kudzera mwa Mose, amene anagawanitsa madzi a m’nyanjayo mozizwitsa.​—Eks. 14:13, 21.

17, 18. N’chifukwa chiyani Yesu ali mpulumutsi wamkulu kuposa Mose?

17 Ngakhale kuti Yehova anachita zazikulu populumutsa anthu ake, chipulumutso chimene iye wapereka kudzera mwa Yesu n’chachikulu koposa. Yesu ndiye njira imene anthu omvera amapulumutsidwira ku ukapolo wa uchimo. (Aroma 5:12, 18) Ndipo chipulumutso chimenechi ndi “chilanditso chosatha.” (Aheb. 9:11, 12) Dzina lakuti Yesu limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Chipulumutso.” Yesu Mpulumutsi wathu, samangotilanditsa ku machimo athu akale, komanso amatitsegulira njira yopezera tsogolo labwino kwambiri. Mwa kulanditsa otsatira ake ku ukapolo wa uchimo, Yesu amawapulumutsa ku mkwiyo wa Mulungu ndipo amawathandiza kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.​—Mat. 1:21.

18 Yesu amatipulumutsa ku uchimo, koma pa nthawi yake adzatipulumutsanso ku matenda ndi imfa, zobwera chifukwa cha uchimowo. Kuti tione mmene zinthu zidzakhalira, tiyeni tiganizire zimene zinachitika pamene Yesu anapita kunyumba ya munthu wina, dzina lake Yairo, amene mwana wake wazaka 12 anamwalira. Yesu anamutsimikizira Yairo kuti: “Usaope, ingokhala ndi chikhulupiriro basi, ndipo mwana wako apulumuka.” (Luka 8:41, 42, 49, 50) Mawu amenewa anali oona chifukwa mtsikanayo anauka. Kodi mukuganiza kuti makolo a mwanayu anasangalala motani? Kuganizira zimenezi kungatithandize kumvetsa mmene tidzasangalalire pamene “onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka” pa nthawi ya kuuka kwa akufa. (Yoh. 5:28, 29) Zoonadi, Yesu ndi Mpulumutsi wathu.​—Werengani Machitidwe 5:31; Tito 1:4; Chiv. 7:10.

19, 20. (a) Kodi kusinkhasinkha za udindo wa Yesu monga Mose Wamkulu kumatikhudza bwanji? (b) Kodi nkhani yotsatira ikufotokoza chiyani?

19 Tadziwa kuti tingathe kuthandiza kwambiri anthu kupindula ndi ntchito ya Yesu yopulumutsa. Zimenezi zikutilimbikitsa kugwira nawo ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa anthu. (Yes. 61:1-3) Komanso kusinkhasinkha za udindo wa Yesu monga Mose Wamkulu kumalimbitsa chikhulupiriro chathu chakuti iye adzapulumutsa otsatira ake akamadzapereka chiweruzo kwa anthu oipa.​—Mat. 25:31-34, 41, 46; Chiv. 7:9, 14.

20 Zoonadi, Yesu ndi Mose Wamkulu. Iye anachita zinthu zambiri zazikulu zimene Mose sakanatha kuchita. Zimene Yesu ananena monga mneneri komanso zimene anachita monga mkhalapakati zimakhudza mtundu wonse wa anthu. Monga Mpulumutsi, Yesu adzabweretsa chipulumutso osati cha kanthawi kochepa chabe, koma chosatha kwa anthu otheka kuwapulumutsa. Komabe pali zinthu zambiri zokhudza Yesu zimene tingaphunzire kwa anthu okhulupirika akale. Nkhani yotsatirayi ikufotokoza mmene Yesu analili Davide Wamkulu komanso Solomo Wamkulu.

Kodi Mungafotokoze?

Kodi n’chifukwa chiyani Yesu ali wamkulu kuposa Mose monga

• mneneri?

• mkhalapakati?

• mpulumutsi?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 26]

  Kufanana Kwinanso kwa Yesu ndi Mose

□ Onse awiri anasiya malo apamwamba pofuna kutumikira Yehova ndi anthu ake.​—2 Akor. 8:9; Afil. 2:5-8; Aheb. 11:24-26.

□ Onse awiri anali odzozedwa, kapena kuti ‘khristu.’​—Maliko 14:61, 62; Yoh. 4:25, 26; Aheb. 11:26.

□ Onse awiri anabwera m’dzina la Yehova.​—Eks. 3:13-16; Yoh. 5:43; 17:4, 6, 26.

□ Onse awiri anali ofatsa.​—Num. 12:3; Mat. 11:28-30.

□ Onse awiri anadyetsa anthu ambirimbiri chakudya.​—Eks. 16:12; Yoh. 6:48-51.

□ Onse awiri anali oweruza ndiponso opereka malamulo.​—Eks. 18:13; Mal. 4:4; Yoh. 5:22, 23; 15:10.

□ Onse awiri anali mutu wa panyumba ya Mulungu.​—Num. 12:7; Aheb. 3:2-6.

□ Onse awiri akufotokozedwa kuti ndi mboni zokhulupirika za Yehova.​—Aheb. 11:24-29; 12:1; Chiv. 1:5.

□ Mose ndi Yesu atamwalira, Mulungu anaonetsetsa kuti mitembo yawo isapezeke.​—Deut. 34:5, 6; Luka 24:1-3; Mac. 2:31; 1 Akor. 15:50; Yuda 9.