Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuzindikira Yesu Monga Davide Wamkulu Ndiponso Solomo Wamkulu

Kuzindikira Yesu Monga Davide Wamkulu Ndiponso Solomo Wamkulu

Kuzindikira Yesu Monga Davide Wamkulu Ndiponso Solomo Wamkulu

“Tsopano wina woposa Solomo ali pano.”​—MAT. 12:42.

1, 2. Kodi n’chifukwa chiyani zingakhale zodabwitsa kwa anthu kuti Yehova anauza Samueli kuti adzoze Davide kukhala mfumu?

IYE sanaoneke ngati angakhale mfumu. Mneneri Samueli anangomuona ngati kamnyamata komanso kambusa wamba. Ndiponso kwawo ku Betelehemu kunali kosatchuka. Baibulo limati mudziwu unali ‘waung’ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda.’ (Mika 5:2) Komabe kamnyamata kosadziwika bwino kameneka ka m’mudzi waung’ono umenewu, kanali pafupi kudzozedwa ndi mneneri Samueli kuti kadzakhale mfumu ya Isiraeli.

2 Samueli atabwera kunyumba kwa Jese kuti adzadzoze mmodzi wa ana ake, Jese sanaganizire n’komwe kuti angamusonyeze mwana wake wamng’ono Davide. Davide anali mwana womaliza pa ana aamuna 8 a Jese. Ndipo pamene Samueli anabwera kunyumba kwa Jese kudzadzoza mmodzi wa ana aamuna a munthu wokhulupirika ameneyu kuti adzakhale mfumu, Davide panalibepo. Koma zonsezi zinalibe kanthu chifukwa Yehova anafuna kusankha Davide.​—1 Sam. 16:1-10.

3. (a) Kodi Yehova akamayang’ana munthu, amaona kuti chofunika kwambiri n’chiyani? (b) Kodi Davide atadzozedwa, n’chiyani chinalimbika pa iye?

3 Yehova anaona zimene Samueli sakanatha kuona. Mulungu ankadziwa mtima wa Davide ndipo unali kumusangalatsa. Chofunika kwa Mulungu si maonekedwe, koma mtima wa munthu. (Werengani 1 Samueli 16:7.) Samueli atadziwa kuti Yehova sanasankhe wina aliyense wa ana 7 a Jese, iye anawauza kuti am’bweretsere mnyamata wamng’ono pa onsewo amene anali kodyetsa ziweto. Nkhaniyo imati: “Ndipo [Jese] anatumiza munthu, nabwera naye [Davide]. Tsono iye anali wofiirira, ndi wankhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka um’dzoze, pakuti ndi ameneyu. Pamenepo Samueli anatenga nyanga ya mafuta, nam’dzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli.”​—1 Sam. 16:12, 13.

Davide Anachitira Chithunzi Khristu

4, 5. (a) Fotokozani kufanana kwina kwa Davide ndi Yesu. (b) N’chifukwa chiyani Yesu akutchedwa kuti Davide Wamkulu?

4 Yesu nayenso anabadwira ku Betelehemu patapita zaka ngati 1,100 kuchokera m’nthawi ya Davide. Kwa anthu ambiri, Yesu nayenso sankaoneka ngati angakhale mfumu. Zili choncho chifukwa chakuti Aisiraeli ambiri ankaganiza kuti iye sanali mfumu imene iwo ankaiyembekezera. Komabe mofanana ndi Davide, iye anasankhidwa ndi Yehova. Ndiponso monga Davide, iye anakondedwa ndi Yehova. * (Luka 3:22) Komanso ‘mzimu wa Yehova unalimbika’ pa Yesu.

5 Davide ndi Yesu akufanana m’njira zinanso. Mwachitsanzo, Davide anachitiridwa chiwembu ndi phungu wake Ahitofeli, ndipo Yesu anachitiridwanso chiwembu ndi mtumwi wake Yudasi Isikariyoti. (Sal. 41:9; Yoh. 13:18) Davide ndi Yesu onse anali ndi changu cha panyumba ya Yehova yolambirira. (Sal. 27:4; 69:9; Yoh. 2:17) Yesu analinso wolowa nyumba wa Davide ndipo iye asanabadwe, mngelo anauza mayi wake kuti: “Yehova Mulungu adzam’patsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.” (Luka 1:32; Mat. 1:1) Komabe chifukwa chakuti malonjezo onse okhudza Mesiya adzakwaniritsidwa mwa Yesu, iye ndi woposa Davide. Zoonadi, Yesu ndi Davide Wamkulu ndiponso Mfumu Mesiya imene anthu anakhala akuiyembekezera kwa nthawi yaitali.​—Yoh. 7:42.

Tsatirani Mfumu Imenenso Ndi Mbusa Wathu

6. Kodi n’chifukwa chiyani Davide anali mbusa wabwino?

6 Yesu nayenso ndi mbusa. Kodi mbusa wabwino ndi wotani? Mbusa wabwino ndi amene amasamala, kudyetsa ndi kuteteza ziweto zake mokhulupirika ndiponso molimba mtima. (Sal. 23:2-4) Davide ali mnyamata, anali mbusa ndipo ankasamalira bwino nkhosa za bambo ake. Iye anasonyeza kulimba mtima pamene anaika moyo wake pa ngozi poteteza nkhosazo kwa mkango komanso chimbalangondo.​—1 Sam. 17:34, 35.

7. (a) Kodi chinathandiza Davide kukonzekera udindo wa ufumu n’chiyani? (b) Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi Mbusa Wabwino?

7 Zaka zimene Davide anagwira ntchito yoweta nkhosa m’mapiri ndi malo ena, zinamuthandiza kukonzekera ntchito komanso udindo wovuta woweta mtundu wa Isiraeli. * (Sal. 78:70, 71) Yesu nayenso wasonyeza kuti ndi mbusa wachitsanzo chabwino. Yehova amam’patsa mphamvu komanso amam’tsogolera pamene akuweta “kagulu ka nkhosa” ndiponso “nkhosa zina.” (Luka 12:32; Yoh. 10:16) Choncho, Yesu ndi Mbusa Wabwino. Iye amadziwa bwino nkhosa zake, moti nkhosa iliyonse amaitchula dzina lake. Ndiponso iye amazikonda kwambiri nkhosa zake, moti ali padziko lapansi, analolera kupereka moyo wake m’malo mwa nkhosazo. (Yoh. 10:3, 11, 14, 15) Monga Mbusa Wabwino, Yesu akuchita zazikulu zimene Davide sakanatha kuchita. Nsembe yake ya dipo inapereka njira yopulumutsira anthu ku imfa. Palibe chimene chingamulepheretse kuweta “kagulu ka nkhosa” kuti kadzalandire moyo wosakhoza kufa kumwamba, komanso kutsogolera “nkhosa zina” ku moyo wosatha m’dziko latsopano lolungama momwe simudzapezeka anthu onga mimbulu.​—Werengani Yohane 10:27-29.

Tsatirani Mfumu Yogonjetsa Adani Ake

8. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti anali mfumu yogonjetsa adani ake?

8 Mfumu Davide anali msilikali wolimba mtima ndipo anateteza dziko la anthu a Mulungu, ndiponso “Yehova anasunga Davide kulikonse anamukako.” Mu ulamuliro wa Davide, malire a dziko la Isiraeli anayambira kumtsinje wa ku Iguputo kukafika kumtsinje wa Firate. (2 Sam. 8:1-14) Ndi mphamvu ya Yehova, iye anakhala wolamulira wamphamvu kwambiri. Baibulo limati: “Mbiri ya Davide inabuka m’mayiko onse, nafikitsira Yehova kuopsa kwake pa amitundu onse.”​—1 Mbiri 14:17.

9. Fotokozani mmene Yesu, monga Mfumu Yam’tsogolo, anagonjetsera adani ake.

9 Mofanana ndi Mfumu Davide, Yesu anali wolimba mtima. Monga Mfumu Yam’tsogolo, iye anasonyeza kuti anali ndi mphamvu pa ziwanda ndipo anapulumutsa anthu amene ankazunzidwa ndi ziwandazo. (Maliko 5:2, 6-13; Luka 4:36) Ngakhale mdani wamkulu, Satana Mdyerekezi, alibe mphamvu pa iye. Mwa mphamvu ya Yehova, Yesu anagonjetsa dzikoli, limene lili m’manja mwa Satana.​—Yoh. 14:30; 16:33; 1 Yoh. 5:19.

10, 11. Kodi udindo wa Yesu monga Mfumu Yankhondo kumwamba ndi wotani?

10 Patadutsa zaka pafupifupi 60 kuchokera pamene Yesu anafa ndi kuukitsidwa kupita kumwamba, mtumwi Yohane anaona masomphenya olosera za m’tsogolo. M’masomphenyawo anaona Yesu kumwamba monga Mfumu Yankhondo. Yohane analemba kuti: “Ndipo nditayang’ana, ndinaona kavalo woyera. Wokwerapo wake, ananyamula uta. Ndipo anapatsidwa kolona wachifumu, napita kukagonjetsa ndi kukatsiriza kugonjetsa kwake.” (Chiv. 6:2) Amene anakwera pakavalo woyera ndi Yesu. Iye “anapatsidwa kolona wachifumu” mu 1914 pamene anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wakumwamba. Kenako ‘anapita kukagonjetsa.’ Zoonadi, mofanana ndi Davide, Yesu ndi mfumu yogonjetsa adani ake. Atangoikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, anamenya nkhondo ndi kugonjetsa Satana ndipo anam’gwetsera kudziko lapansi limodzi ndi ziwanda zake. (Chiv. 12:7-9) Iye adzapitirizabe ulendo wogonjetsa adani ake mpaka ‘atatsiriza kugonjetsa kwake,’ pamene adzawonongeratu dongosolo loipa la Satanali.​—Werengani Chivumbulutso 19:11, 19-21.

11 Komabe mofanana ndi Davide, Yesu ndi mfumu yachifundo ndipo adzateteza “khamu lalikulu” pa Aramagedo. (Chiv. 7:9, 14) Ndiponso mu ulamuliro wa Yesu limodzi ndi olamulira anzake a 144,000 oukitsidwa, mudzakhala “kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Mac. 24:15) Anthu amene adzauka padziko lapansi adzakhala ndi chiyembekezo cholandira moyo wosatha. Koma ndiye ali ndi tsogolo labwino bwanji! Tiyeni tonsefe tisasiye ‘kuchita chokoma’ kuti tidzakhalepo pamene dziko lapansi lidzadzala ndi anthu olungama, osangalala komanso ogonjera Davide Wamkulu.​—Sal. 37:27-29.

Solomo Anayankhidwa Atapempha Nzeru

12. Kodi Solomo anapempha chiyani?

12 Nayenso Solomo mwana wa Davide anachitira chithunzi Yesu. * Solomo atakhala mfumu, Yehova anaonekera kwa iye m’maloto ndipo anamulonjeza kuti am’patsa chilichonse chimene angapemphe. Solomo akanatha kupempha chuma chambiri, mphamvu kapenanso moyo wautali. Koma m’malomwake, iye mopanda dyera anapempha Yehova kuti: “Mundipatse tsono nzeru ndi chidziwitso, kuti ndituluke ndi kulowa pamaso pa anthu awa; pakuti angathe ndani kuweruza anthu anu awa ambiri?” (2 Mbiri 1:7-10) Yehova anayankha pemphero la Solomo.​—Werengani 2 Mbiri 1:11, 12.

13. Kodi n’chifukwa chiyani kunalibe munthu wanzeru ngati Solomo, nanga nzeru zakezo zinachokera kuti?

13 Pamene Solomo anali wokhulupirika kwa Yehova, panalibe munthu aliyense wonena mawu anzeru mofanana naye. Solomo ananena ‘miyambi zikwi zitatu.’ (1 Maf. 4:30, 32, 34) Yambiri mwa miyambi imeneyi inalembedwa, ndipo anthu amene amafuna nzeru amaikonda kwambiri. Mfumukazi ya ku Seba inayenda mtunda wa makilomita pafupifupi 2,400 kuti idzayese nzeru za Solomo ndi “miyambi yododometsa.” Koma iyo inagoma ndi zimene Solomo ananena ndiponso ndi ulemelero wa ufumu wake. (1 Maf. 10:1-9) Baibulo limatchula kumene nzeru ya Solomo inachokera. Limati: “Anthu onse apadziko anafuna nkhope ya Solomo, kudzamva nzeru zake zimene Mulungu analonga m’mtima mwake.”​—1 Maf. 10:24.

Tsatirani Mfumu Yanzeru

14. Kodi Yesu anali “wina woposa Solomo” m’njira ziti?

14 Ndi munthu mmodzi yekha amene anali ndi nzeru kuposa Solomo. Munthu ameneyu anali Yesu Khristu. Iye anadzitcha kuti “wina woposa Solomo.” (Mat. 12:42) Mawu a Yesu anali “mawu amoyo wosatha.” (Yoh. 6:68) Chitsanzo cha zimenezi ndi mfundo zimene iye ananena mu ulaliki wapaphiri. Mfundo zimenezi zimafotokoza bwino lomwe zinthu zimene Solomo ananena m’miyambi yake ndipo zimatithandiza kumvetsa miyambiyo. Solomo anafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zingawathandize atumiki a Yehova kukhala osangalala. (Miy. 3:13; 8:32, 33; 14:21; 16:20) Yesu anatsindika mfundo yakuti zimene zimabweretsa chisangalalo chenicheni ndi zinthu zokhudza kulambira Yehova komanso kukwaniritsidwa kwa malonjezo ake. Iye ananena kuti: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu, popeza ufumu wa kumwamba ndi wawo.” (Mat. 5:3) Anthu amene amagwiritsa ntchito mfundo zimene Yesu anaphunzitsa amakhala pa ubwenzi ndi Yehova, yemwe ndi “chitsime cha moyo.” (Sal. 36:9; Miy. 22:11; Mat. 5:8) Zoonadi, Khristu ndi “nzeru za Mulungu.” (1 Akor. 1:24, 30) Monga Mfumu Mesiya, Yesu Khristu ali ndi “mzimu wanzeru.”​—Yes. 11:2.

15. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipindule ndi nzeru ya Mulungu?

15 Kodi ife monga otsatira a Solomo Wamkulu, tingachite chiyani kuti tipindule ndi nzeru ya Mulungu? Nzeru ya Yehova imapezeka m’Mawu ake, choncho tiyenera kuyesetsa kuipeza mwa kuphunzira Baibulo mosamalitsa, makamaka mawu a Yesu olembedwa, ndiponso kusinkhasinkha zimene tikuwerenga. (Miy. 2:1-5) Komanso tiyenera kulimbikira kupempha nzeru kwa Mulungu. Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti mapemphero athu ochokera pansi pa mtima, opempha thandizo, adzayankhidwa. (Yak. 1:5) Mzimu woyera udzatithandiza kupeza nzeru yamtengo wapatali m’Mawu a Mulungu, imene ingatithandize kulimbana ndi mavuto ndiponso kusankha zinthu mwanzeru. (Luka 11:13) Solomo ankatchedwanso kuti “Mlaliki” kapena kuti wosonkhanitsa ndipo “anaphunzitsabe anthu nzeru.” (Mlal. 12:9, 10) Nayenso Yesu, monga Mutu wa mpingo wachikhristu, amasonkhanitsa anthu ake. (Yoh. 10:16; Akol. 1:18) Motero ndi bwino kuti tizipezeka kumisonkhano ya mpingo kumene ‘timaphunzitsidwabe.’

16. Kodi Solomo akufanana bwanji ndi Yesu?

16 Solomo anali mfumu yolimbikira ntchito. Iye anakhazikitsa ntchito yomanga m’dziko lake lonse. Ndipo ankayang’anira ntchito yomanga nyumba zachifumu, misewu, matamanda a madzi, mizinda yosungiramo katundu, mizinda yosungirako magaleta komanso mizinda yokhalamo okwera pa akavalo. (1 Maf. 9:17-19) Ufumu wake wonse unapindula ndi ntchito yake yomangayi. Nayenso Yesu ndi mmisiri. Iye anamanga mpingo wake pa “thanthwe.” (Mat. 16:18) Ndiponso iye adzayang’anira ntchito yomanga imene idzachitika m’dziko latsopano.​—Yes. 65:21, 22.

Tsatirani Mfumu Yamtendere

17. (a) Kodi n’chiyani chimene chinali chochititsa chidwi ndi ulamuliro wa Solomo? (b) Kodi Solomo sakanatha kuchita chiyani?

17 Dzina lakuti Solomo limachokera ku tsinde la mawu amene amatanthauza kuti “mtendere.” Ndiponso likulu la ufumu wa Solomo linali Yerusalemu, ndipo dzina limeneli limatanthauza “Mwini Mtendere Wamitundu Iwiri.” Pa zaka 40 zimene iye analamulira, dziko la Isiraeli linali pa mtendere wokhawokha. Ponena za nthawi imeneyi, Baibulo limati: “Ayuda ndi Aisrayeli anakhala mosatekeseka, munthu yense patsinde pa mpesa wake ndi mkuyu wake, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba, masiku onse a Solomo.” (1 Maf. 4:25) Ngakhale zinali choncho, Solomo ndi nzeru zake zonse sakanatha kumasula anthu ake ku ukapolo wa matenda, uchimo ndi imfa. Koma Solomo Wamkulu adzamasula anthu ake ku zinthu zonsezi.​—Werengani Aroma 8:19-21.

18. Kodi tikusangalala ndi chiyani mumpingo wachikhristu?

18 Ngakhale panopa, tili pa mtendere mumpingo wachikhristu. Zoonadi, tikusangalala ndi paradaiso weniweni wauzimu. Tili pa mtendere ndi Mulungu komanso anthu anzathu. Taonani zimene Yesaya analosera za madalitso amene tili nawo masiku ano. Iye anati: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.” (Yes. 2:3, 4) Tikamachita zinthu mogwirizana ndi mzimu wa Mulungu, timawonjezera kukongola kwa paradaiso wauzimu ameneyu.

19, 20. Kodi tiyenera kusangalala pa zifukwa zotani?

19 Komatu m’tsogolomu zinthu zidzaposa pamenepa kukoma. Pamene anthu omvera azidzasangalala ndi mtendere wosaneneka mu ulamuliro wa Yesu, iwo pang’onopang’ono ‘adzamasulidwa ku ukapolo wa kuvunda’ mpaka atakhala angwiro. (Aroma 8:21) Akadzapambana chiyeso chomaliza pamapeto pa Ulamuliro wa Zaka 1,000, “ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Sal. 37:11; Chiv. 20:7-10) Kunena zoona, ulamuliro wa Khristu Yesu udzaposeratu wa Solomo m’njira zosatheka kuziganizira panopa.

20 Mofanana ndi Aisiraeli amene anasangalala ndi uyang’aniro wa Mose, Davide ndi Solomo, nafenso tidzasangalalatu kwambiri mu ulamuliro wa Khristu. (1 Maf. 8:66) Tikuthokoza kwambiri Yehova potipatsa Mwana wake wobadwa yekha, yemwe ndi Mose, Davide komanso Solomo Wamkulu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Zikuoneka kuti dzina lakuti Davide limatanthauza kuti “Wokondedwa.” Ndipo pa ubatizo wa Yesu komanso atasandulika, Yehova analankhula kuchokera kumwamba ndipo anamutcha kuti, “mwana wanga wokondedwa.”​—Mat. 3:17; 17:5.

^ ndime 7 Davide analinso ngati mwana wa nkhosa amene amakhulupirira mbusa wake. Iye ankadalira Mbusa Wamkulu, Yehova, kuti amuteteze ndi kumutsogolera. Ndi chidaliro chonse, iye anati: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasowa” kanthu. (Sal. 23:1) Yohane Mbatizi ananena kuti Yesu ndi “Mwanawankhosa wa Mulungu.”​—Yoh. 1:29.

^ ndime 12 N’zochititsa chidwi kuti dzina lina la Solomo linali Yedediya, lomwe limatanthauza kuti “Wokondedwa wa Ya.”​—2 Sam. 12:24, 25.

Kodi Mungafotokoze?

• N’chifukwa chiyani Yesu ali Davide Wamkulu?

• N’chifukwa chiyani Yesu ali Solomo Wamkulu?

• Kodi n’chiyani chikukusangalatsani ndi Davide Wamkulu, yemwenso ndi Solomo Wamkulu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 31]

Nzeru ya Solomo imene Mulungu anam’patsa inachitira chithunzi nzeru ya Solomo Wamkulu

[Chithunzi patsamba 32]

Ulamuliro wa Yesu udzaposeratu wa Solomo ndi wa Davide m’njira zosatheka kuziganizira panopa