Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Yesetsani Kukula Mwauzimu Chifukwa “Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi”

Yesetsani Kukula Mwauzimu Chifukwa “Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi”

Yesetsani Kukula Mwauzimu Chifukwa “Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi”

“Tiyeni tiyesetse mwakhama kufika pa uchikulire.”​—AHEB. 6:1.

1, 2. Kodi ndi mpata wotani ‘wothawira kumapiri’ umene Akhristu oyambirira a ku Yerusalemu ndi Yudeya anali nawo?

PAMENE Yesu anali padziko pano, ophunzira ake anamufunsa kuti: “Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo kwanu ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?” Ulosi umene Yesu ananena poyankha funso limeneli unakwaniritsidwa koyamba m’nthawi ya atumwi. Yesu anafotokoza kuti padzachitika zinthu zomwe zinali zisanachitikepo, zosonyeza kuti mapeto ayandikira. Iye anati anthu akadzaona zimenezi, “amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira ku mapiri.” (Mat. 24:1-3, 15-22) Kodi zinthuzo zitayamba kuchitika, ophunzirawo anazindikira kuti n’zimene Yesu ananena, ndipo kodi anatsatira malangizo amene iye anawapatsa?

2 Patatha pafupifupi zaka 30, m’chaka cha 61 C.E., mtumwi Paulo analemba kalata yopita kwa Akhristu Achiheberi, omwe ankakhala ku Yerusalemu ndi m’madera ozungulira mzindawo. M’kalatayo munali uthenga wosapita m’mbali. Paulo, ngakhalenso Akhristu anzakewo, sankadziwa kuti panali patangotsala zaka zisanu zokha kuti chizindikiro chosonyeza mbali yoyamba ya “chisautso chachikulu” chioneke. (Mat. 24:21) M’chaka cha 66 C.E., mzinda wa Yerusalemu unangotsala pang’ono kugonjetsedwa ndi asilikali Achiroma otsogoleredwa ndi Cestius Gallus. Koma mwadzidzidzi, iye ndi asilikali akewo anabwerera ndipo zimenezi zinapereka mpata woti anthu athawe.

3. Kodi Paulo anawalimbikitsa chiyani Akhristu Achiheberi, ndipo n’chifukwa chiyani?

3 Akhristu amenewo anafunikira kuona zinthu mwauzimu. Anafunikanso kuzindikira kuti zimene zinali kuchitikazo zinali kukwaniritsa mawu a Yesu, motero anayenera kuthawa. Tsoka ilo, ena anali ‘atagontha m’kumva kwawo.’ Mwauzimu, iwo anali ngati ana ofunikira “mkaka.” (Werengani Aheberi 5:11-13.) Ngakhale ena amene anali atayenda m’njira ya choonadi kwa zaka zambirimbiri anasonyeza kuti ‘akukanganuka kwa Mulungu wa moyo.’ (Aheb. 3:12) Anthu ena anali ndi “chizolowezi” chojomba kumisonkhano yachikhristu pa nthawi imene ‘tsiku loopsa limeneli linkayandikira.’ (Aheb. 10:24, 25) Mpake kuti Paulo anawalimbikitsa kuti: “Pamene tasiya chiphunzitso choyambirira cha Khristu tsopano, tiyeni tiyesetse mwakhama kufika pa uchikulire.”​—Aheb. 6:1.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala atcheru mwauzimu, ndipo n’chiyani chingatithandize kuchita zimenezo?

4 Tikukhala m’nthawi imene ulosi wa Yesu ukukwaniritsidwa komaliza. “Tsiku lalikulu la Yehova,” pamene Iye adzawononge dongosolo lonse la Satana, “lili pafupi.” (Zef. 1:14) Kuposa kale lonse, panopo m’pamene tiyenera kukhala tcheru kwambiri mwauzimu. (1 Pet. 5:8) Kodi tikutero? Kukula mwauzimu kumatithandiza kusaiwala nthawi imene tikukhalamo.

Tanthauzo la Kukula Mwauzimu

5, 6. (a) Kodi kukula mwauzimu kumatanthauza chiyani? (b) Ndi zinthu ziwiri ziti zimene tiyenera kuyesetsa kuchita kuti tikule mwauzimu?

5 M’kalata yake yopita kwa Aheberi, sikuti Paulo anangolimbikitsa Akhristuwo kuchita khama kuti akule mwauzimu koma anawauzanso tanthauzo la kukula mwauzimuko. (Werengani Aheberi 5:14.) “Anthu okhwima” mwauzimu sakhutitsidwa ndi “mkaka” wokha. Iwo amadya “chakudya chotafuna.” Motero amadziwa “mfundo zoyambirira” komanso “zinthu zozama” za choonadi. (1 Akor. 2:10) Ndiponso amadziwa kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika chifukwa choti amaphunzitsa luntha lawo la kulingalira mwa kuchita zimene aphunzira. Akafuna kusankha zochita, zimenezi zimawathandiza kudziwa mfundo za m’Malemba zogwirizana ndi nkhaniyo ndipo amaona mmene angazigwiritsire ntchito.

6 Paulo analemba kuti: “Tisamalire mwapadera, koposa mwa nthawi zonse, zinthu zimene tinamva, kuti tisatengeke konse pang’onopang’ono kusiya chikhulupiriro.” (Aheb. 2:1) Mosazindikira, tingathe kutengeka pang’onopang’ono n’kusiya chikhulupiriro. Tingapewe zimenezi mwa “kusamalira mwapadera” zimene timamva tikamaphunzira zinthu zauzimu. Motero aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndidakali pa mfundo zoyambirira? Kodi ndimangochita zinthu mwamwambo popanda kukhudzidwa mumtima ndi choonadi? Kodi ndingatani kuti ndipitedi patsogolo mwauzimu?’ Kuti tikule mwauzimu tiyenera kuyesetsa kuchita zinthu ziwiri. Tiyenera kudziwa bwino Mawu a Mulungu ndipo tiyenera kuphunzira kumvera.

Dziwani Bwino Mawu

7. Kodi tingapindule bwanji chifukwa chodziwa bwino Mawu a Mulungu?

7 Paulo anati: “Pakuti aliyense woyamwa mkaka sadziwa mawu a chilungamo, popeza ali kamwana.” (Aheb. 5:13) Kuti tikule mwauzimu, tiyenera kudziwa bwino Mawu a Mulungu, omwe ndi uthenga umene Mulunguyo watipatsa. Popeza kuti uthenga umenewu uli m’Mawu ake, Baibulo, tiyenera kuchita khama pophunzira Malemba ndi mabuku a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Kuphunzira mwakhama kungatithandize kudziwa kaganizidwe ka Mulungu n’kunola luntha lathu la kuzindikira. Taganizirani chitsanzo cha mlongo wina dzina lake Orchid. * Iye anati: “Malangizo amene akhudza kwambiri moyo wanga ndi akuti tiyenera kumawerenga Baibulo nthawi zonse. Zinanditengera zaka ziwiri kuti ndimalize kuwerenga Baibulo lonse. Koma nditamaliza ndinamva ngati kuti ndangomudziwa kumene Mlengi. Ndinadziwa zochita zake, zimene amakonda, zimene amadana nazo, kuchuluka kwa mphamvu zake, ndiponso kuya kwa nzeru zake. Kuwerenga Baibulo tsiku lililonse kunandithandiza pa nthawi imene ndinali pamavuto aakulu kwambiri pa moyo wanga.”

8. Kodi mphamvu ya Mawu a Mulungu ingatithandize motani?

8 Tikamawerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse, uthenga wake umakhala ndi ‘mphamvu’ yokhudza mtima wathu. (Werengani Aheberi 4:12.) Zimenezi zingaumbe umunthu wathu wamkati n’kutithandiza kuti tizisangalatsa kwambiri Yehova. Kodi inuyo panokha mukuona kuti mungatani kuti muzikhala ndi nthawi yokwanira yowerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene limanena?

9, 10. Kodi kudziwa bwino Mawu a Mulungu kumatanthauza chiyani? Perekani chitsanzo.

9 Kudziwa bwino Baibulo si kungodziwa zimene limanena. M’nthawi ya Paulo, sikuti anthu amene anali ngati ana mwauzimu sankadziwa ngakhale pang’ono zimene Mawu ouziridwa a Mulungu amanena. Vuto lawo linali lakuti sanagwiritse ntchito zimenezi n’kuona ubwino wake. Iwo sanalole kuti mawuwo aziwatsogolera posankha zinthu mwanzeru pa moyo wawo choncho tingati sankawadziwa bwino mawu.

10 Kudziwa bwino Mawu a Mulungu kumatanthauza kumvetsa zimene amanena n’kumazitsatira. Zimene mlongo wina wotchedwa Kyle anakumana nazo zimasonyeza mmene tingachitire zimenezi. Kyle anayambana ndi mnzake kuntchito. Kodi anatani kuti athetse vutoli? Iye anati: “Lemba lomwe ndinalikumbukira mwamsanga ndi la Aroma 12:18, lomwe limati: ‘Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse.’ Choncho ndinamupempha kuti tionane poweruka kuti tikambirane.” Zokambirana zawo zinayenda bwino kwambiri ndipo mnzakeyo anasangalala kwambiri chifukwa cha zimene Kyle anachita. Kyle anati: “Ndinaphunzira kuti ngati munthu atatsatira mfundo za m’Baibulo, chilichonse chimene angachite chimakhala cholondola.”

Phunzirani Kumvera

11. N’chiyani chikusonyeza kuti kumvera pa nthawi imene tili pa mavuto si kophweka?

11 Kugwiritsa ntchito zimene taphunzira m’Malemba kungakhale kovuta nthawi zina makamaka pamene zinthu zavuta. Mwachitsanzo, Yehova atangopulumutsa kumene Aisiraeli ku Iguputo komwe anali akapolo, iwo “anatsutsana ndi Mose” ndipo anapitiriza ‘kuyesa Yehova.’ Iwo anachita zimenezi pa nthawi imene anasowa madzi akumwa. (Eks. 17:1-4) Pasanathe miyezi iwiri iwo atachita pangano ndi Mulungu n’kuvomereza kuti azichita ‘mawu onse amene Yehova analankhula,’ iwo anaphwanya lamulo loletsa kulambira mafano. (Eks. 24:3, 12-18; 32:1, 2, 7-9) Kodi Aisiraeli anachita zimenezi chifukwa cha mantha ataona kuti Mose akuchedwa ku phiri la Horebe kumene ankalandira malangizo? Kapena kodi ankaopa kuti Aamaleki akawaukiranso Mose kulibe asowa chochita? Pajatu Mose ndi amene anawathandiza kuti apambane pa nkhondo ina chifukwa chokweza manja ake. (Eks. 17:8-16) Kaya chinawachititsa ndi chiyani, koma mfundo ndi yakuti Aisiraeli ‘anakana kumvera.’ (Mac. 7:39-41) Paulo analimbikitsa Akhristu kuti ‘achite chilichonse chotheka’ kuti apewe ‘kugwera m’kusamvera’ kumene Aisiraeli anasonyeza pochita mantha kulowa m’dziko lolonjezedwa.​—Aheb. 4:3, 11.

12. Kodi Yesu anaphunzira bwanji kumvera ndipo zotsatira zake zinali zotani?

12 Kuti tikule mwauzimu, tifunika kuyesetsa kumvera Yehova pa chilichonse. Monga Yesu Khristu anachitira, nthawi zambiri timaphunzira kumvera tikamakumana ndi mavuto osiyanasiyana. (Werengani Aheberi 5:8, 9.) Asanabwere padziko lapansi, Yesu ankamvera Atate wake. Komano kuti achite chifuniro cha Atate wake padziko lapansi pano, Yesu anafunika kukumana ndi mavuto osiyanasiyana komanso panali zinthu zina zimene zinkamudetsa nkhawa. Yesu anakhala womvera pa nthawi imene ankakumana ndi mikwingwirima. Zimenezi zinachititsa kuti Yesu ‘apangidwe kukhala wangwiro,’ kapena kuti woyenerera kwambiri udindo umene Mulungu anali atamukonzera, woti akhale Mfumu ndiponso Mkulu wa Ansembe.

13. N’chiyani chingasonyeze kuti taphunzira kumvera?

13 Kodi nafenso tili ndi mtima wofunitsitsa kumvera Yehova ngakhale pamene takumana ndi mikwingwirima? (Werengani 1 Petulo 1:6, 7.) Mulungu amapereka malangizo omveka bwino pa nkhani ya makhalidwe, kuona mtima, kalankhulidwe, kuphunzira Baibulo patokha, kupezeka pamisonkhano yachikhristu komanso kugwira nawo ntchito yolalikira. (Yos. 1:8; Mat. 28: 19, 20; Aef. 4:25, 28, 29; 5:3-5; Aheb. 10:24, 25) Kodi timamvera malangizo a Yehova amenewa ngakhale pamene zinthu zavuta kwambiri? Ngati timamvera ndiye kuti tikuyesetsa kukula mwauzimu.

Ubwino wa Kukula Mwauzimu

14. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti munthu amene akuyesetsa kukula mwauzimu amakhala wotetezeka.

14 M’dziko lino anthu afika poti “sangathenso kuzindikira makhalidwe abwino.” (Aef. 4:19) Koma Mkhristu amatetezedwa akakhala ndi luntha la kuzindikira, limene limamuthandiza kusiyanitsa bwinobwino choyenera ndi cholakwika. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake James, amene nthawi zonse ankachita khama kwambiri kuwerenga mabuku athu, anayamba ntchito pakampani ina ndipo ankagwira ndi atsikana okhaokha. Iye anati: “Atsikana onsewo ankaonekeratu kuti anali ndi makhalidwe oipa, kupatula mmodzi yekha amene ankaoneka kuti amadzisungira ulemu komanso kuti amafuna atadziwa bwino choonadi cha m’Baibulo. Koma tsiku lina tikugwira ntchito awiriwiri m’chipinda china, iye anayamba kundigwiragwira. Poyamba ndimaganiza kuti n’zongocheza koma mtsikanayo anandikakamira kwambiri. Kenako ndinakumbukira nkhani ina imene inalembedwa mu Nsanja ya Olonda. Nkhaniyo inatchula za m’bale wina amene anakumananso ndi vuto ngati lomweli kuntchito kwake. Inafotokozanso nkhani ya Yosefe ndi mkazi wa Potifara. * Nthawi yomweyo ndinamukankha mtsikanayo ndipo anathawa.” (Gen. 39:7-12) James anasangalala kwambiri kuti sanachite tchimo lililonse ndipo anali ndi chikumbumtima choyera.​—1 Tim. 1:5.

15. Kodi kuyesetsa kuti tikule mwauzimu kumalimbitsa bwanji mtima wathu wophiphiritsa?

15 Kukula mwauzimu kumathandizanso kuti tilimbitse mtima wathu wophiphiritsa komanso kuti “tisatengeke ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo.” (Werengani Aheberi 13:9.) Tikamayesetsa kuti tikule mwauzimu, maganizo athu amakhala pa “zinthu zofunika kwambiri.” (Afil. 1:9, 10) Tikatero timakhala oyamikira kwambiri Mulungu ndi zinthu zimene amatipatsa kuti zitithandize. (Aroma 3:24) Mkhristu yemwe ‘ndi wamkulu msinkhu pa luntha la kuzindikira’ amakhala ndi mtima woyamikira ndipo amakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.​—1 Akor. 14:20.

16. Kodi n’chiyani chimene chinathandiza mlongo wina ‘kulimbitsa mtima’ wake wophiphiritsira?

16 Mlongo wina dzina lake Louise anafotokoza kuti kwanthawi ndithu atabatizidwa, cholinga chake chachikulu chinali kusangalatsa anthu. Iye anati: “Sikuti pali chinachake choipa chimene ndinkachita koma kungoti ndinalibe mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova. Ndinazindikira kuti ngati ndikufuna kuti ndizimva kuti ndikutumikira Yehova ndi mtima wonse, ndiyenera kusintha zinthu zina ndi zina. Chinthu chofunika kwambiri pa zinthu zimenezi chinali chakuti ndiyambe kulambira Yehova ndi mtima wanga wonse.” Atachita zimenezi, Louise ‘analimbitsa mtima wake’ wophiphiritsira ndipo izi zinamuthandiza kwambiri pamene anapezeka ndi matenda aakulu. (Yak. 5:8) Louise anati: “Ndinavutika kwambiri ndi matendawo, koma ndinayandikira kwambiri kwa Yehova.”

‘Khalani Omvera Mochokera Pansi pa Mtima’

17. N’chifukwa chiyani kumvera kunali kofunika kwambiri m’nthawi ya atumwi?

17 Malangizo a Paulo onena kuti ‘yesetsani mwakhama kufika pa uchikulire,’ anathandiza Akhristu a ku Yerusalemu ndi Yudeya kuti apulumuke. Anthu amene anamvera malangizowa, anatha kuona zinthu mwauzimu ndipo anazindikira zimene Yesu anawauza kuti zikachitika “adzayambe kuthawira ku mapiri.” Iwo ataona magulu ankhondo a Aroma atazungulira komanso atayamba kulowa mu Yerusalemu, anadziwa kuti akuimira ‘chonyansa chosakaza choimirira m’malo oyera,’ ndipo anayamba kuthawa. (Mat. 24:15, 16) Akhristu anamvera chenjezo limene Yesu anapereka ndipo anathawa mumzinda wa Yerusalemu mzindawo usanawonongedwe. Wolemba mbiri wina dzina lake Eusebius, ananena kuti iwo anakakhala m’tawuni inayake yotchedwa Pella cha kumapiri a ku Gileadi. Izi zinachititsa kuti apulumuke zinthu zoopsa kwambiri zimene zinachitika mu Yerusalemu.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani kumvera kuli kofunika masiku ano? (b) Kodi nkhani yotsatirayi ifotokoza chiyani?

18 Kumvera chifukwa choti takula mwauzimu, kudzatithandizanso kuti tipulumuke panthawi imene ulosi wa Yesu wakuti kudzakhala “chisautso chachikulu” chimene sichinachitikepo chiyambire, udzakwaniritsidwa. (Mat. 24:21) Kodi tidzamvera malangizo alionse amene tidzalandire kuchokera kwa “mdindo wokhulupirika ndi wanzeru”? (Luka 12:42) Ndi bwino kuti tiphunzire ‘kumvera mochokera pansi pa mtima.’​—Aroma 6:17.

19 Choncho kuti tikule mwauzimu tiyenera kuphunzitsa luntha lathu la kulingalira. Tingachite zimenezi poyesetsa kudziwa bwino Mawu a Mulungu ndiponso kuphunzira kukhala omvera. Komatu pali zovuta zambiri zimene achinyamata amakumana nazo akamayesetsa kukula mwauzimu. Nkhani yotsatirayi ifotokoza zimene achinyamata angachite polimbana ndi zovuta zimenezi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Mayina ena tawasintha.

^ ndime 14 Onani nkhani yakuti “Olimba Pokana Kuchita Tchimo,” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 1999.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi kukula mwauzimu kumatanthauza chiyani ndipo tingatani kuti tikule mwauzimu?

• Kodi kudziwa bwino Mawu a Mulungu kumatithandiza bwanji tikamayesetsa kukula mwauzimu?

• Kodi timaphunzira bwanji kukhala omvera?

• Kodi kukula mwauzimu kumatithandiza m’njira zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 10]

Kukhala wachikulire mwauzimu kumathandiza munthu kulimbana ndi mavuto pogwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Akhristu a m’nthawi ya atumwi anapulumuka chifukwa chotsatira malangizo a Yesu