Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Achangu pa Nyumba ya Yehova

Khalani Achangu pa Nyumba ya Yehova

Khalani Achangu pa Nyumba ya Yehova

“Kukangalika kwanga pa nyumba yanu kudzandidya ine.”​—YOHANE 2:17.

1, 2. Fotokozani zimene Yesu anachita kukachisi mu 30 C.E., ndipo kodi anachitiranji zimenezo?

TAGANIZIRANI zimene zinachitika pa nthawi ya Pasika mu 30 C.E. Apa n’kuti Yesu atachita utumiki wake kwa miyezi 6. Tsopano anali pa ulendo wopita ku Yerusalemu. Atafika kukachisi n’kulowa m’Bwalo la Akunja, anapeza “ogulitsa ng’ombe, nkhosa ndi nkhunda komanso osintha ndalama atakhala m’mipando yawo.” Mokalipa, Yesu anatenga mkwapulo wa zingwe n’kuthamangitsa nyama zonse ndi amalonda onse. Iye anakhuthuliranso pansi makobili a osintha ndalama ndi kugubuduza matebulo awo. Anauzanso anthu amene ankagulitsa nkhunda kuti achotse zinthu zawo zonse ndi kutuluka.​—Yoh. 2:13-16.

2 Zimene Yesu anachitazi zimasonyeza kuti ankakonda kwambiri kachisi. Iye anati: “Mulekeretu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!” Ophunzira a Yesu ataona zimenezi, anakumbukira mawu amene Davide analemba zaka zambiri m’mbuyomo. Iye analemba kuti: “Changu cha pa nyumba yanu chandidya.”​—Yoh. 2:16, 17; Sal. 69:9.

3. (a) Kodi mawu akuti changu amatanthauza chiyani? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa funso lotani?

3 Yesu anachita zimenezi chifukwa cha changu chake pa nyumba ya Mulungu. Mawu akuti changu amatanthauza “kukhala ndi mtima wofunitsitsa ndiponso kulakalaka kwambiri kuchita chinachake.” Masiku ano, anthu oposa 7 miliyoni akusonyeza changu pa nyumba ya Mulungu. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo ndingawonjezere bwanji changu changa pa nyumba ya Yehova?’ Kuti tiyankhe funso limeneli tiyeni tione zimene nyumba ya Mulungu imaimira masiku ano. Kenako tiona zitsanzo za m’Baibulo za anthu okhulupirika amene anasonyeza changu pa nyumba ya Mulungu. Zitsanzo zawo zinalembedwa “kuti zitilangize ife” ndipo zingatithandize kuwonjezera changu chathu.​—Aroma 15:4.

Nyumba ya Mulungu Kalelo Komanso Masiku Ano

4. Kodi ntchito ya kachisi amene Solomo anamanga inali yotani?

4 M’nthawi ya Aisiraeli, nyumba ya Mulungu inali kachisi wa ku Yerusalemu. Komabe sikuti Yehova ankakhala m’nyumba imeneyo ayi. Iye anati: “Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga; mudzandimangira Ine nyumba yotani? Ndi malo ondiyenera kupumamo ali kuti?” (Yes. 66:1) Ngakhale zili choncho, kachisi amene anamangidwa mu ulamuliro wa Solomo anali chimake cha kulambira Yehova ndipo anthu ankapemphera kumeneko.​—1 Maf. 8:27-30.

5. Kodi kulambira kumene kunkachitika pakachisi wa Solomo kukuimira chiyani masiku ano?

5 Masiku ano, nyumba ya Yehova si nyumba yeniyeni yomangidwa ku Yerusalemu kapena malo ena alionse. M’malomwake, imatanthauza dongosolo limene Yehova wakonza potithandiza kuti tizimulambira kudzera mu nsembe ya dipo ya Khristu. Atumiki onse okhulupirika a Mulungu amamulambira mogwirizana m’kachisi wauzimu ameneyu.​—Yes. 60:4, 8, 13; Mac. 17:24; Aheb. 8:5; 9:24.

6. Tchulani mafumu a Yuda amene anasonyeza changu chenicheni pa kulambira koona.

6 Ufumu wa Isiraeli unagawikana mu 997 B.C.E. Izi zitachitika, pa mafumu 19 amene analamulira Yuda, mafumu anayi ndiwo anali ndi changu chenicheni pa kulambira koona. Mafumu amenewa anali Asa, Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya. Kodi tingaphunzire chiyani pa zitsanzo zawo?

Munthu Amadalitsidwa Akamatumikira ndi Mtima Wonse

7, 8. (a) Kodi Yehova amatidalitsa tikamam’tumikira motani? (b) Kodi nkhani ya Mfumu Asa ikutiphunzitsa kuti tiyenera kupewa chiyani?

7 Mu ulamuliro wa Mfumu Asa, Yehova anatumiza aneneri kuti athandize mtundu Wake kukhala wokhulupirika. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza kuti Asa anamvera mneneri Azariya yemwe anali mwana wa Odedi. (Werengani 2 Mbiri 15:1-8.) Zimene Asa anachita zinathandiza kuti anthu onse a mu Yuda komanso ena a mu ufumu wa Isiraeli amene anabwera ku Yerusalemu, akhale ogwirizana. Onsewa ananena motsimikiza kuti adzalambira Yehova mokhulupirika. Baibulo limati: “Analumbira kwa Yehova ndi mawu aakulu, ndi kufuula ndi mphalasa ndi malipenga. Ndipo Yuda yense anakondwera nalo lumbirolo; pakuti adalumbira ndi mtima wawo wonse, nam’funafuna ndi chifuno chawo chonse; ndipo anam’peza; ndi Yehova anawapumulitsa pozungulirapo.” (2 Mbiri 15:9-15) Nafenso Yehova adzatidalitsa tikamam’tumikira ndi mtima wonse.​—Maliko 12:30.

8 N’zomvetsa chisoni kuti, Asa anakwiya atadzudzulidwa ndi mlauli wotchedwa Hanani. (2 Mbiri 16:7-10) Kodi ifeyo timatani tikalandira malangizo a Yehova ochokera m’Malemba, kudzera mwa akulu? Kodi timamvera popanda kukwiya?

9. Fotokozani zimene zinachititsa kuti Yehosafati ndi Ayuda achite mantha, ndipo kodi iwo anatani?

9 Yehosafati anali mfumu ya Yuda cha m’ma 900 B.C.E. Iye ndi anthu ake anachita mantha pa nthawi imene mitundu ya Amoni, Moabu ndiponso anthu ena a ku dera la Seiri anafuna kumenyana nawo. Kodi mfumuyo inatani? Iyo limodzi ndi anthu ake, kuphatikizapo akazi ndi ana anasonkhana kunyumba ya Yehova kuti apemphere. (Werengani 2 Mbiri 20:3-6.) Mogwirizana ndi mawu amene Solomo ananena popatulira kachisiyu, Yehosafati anapemphera ndi mtima wonse kwa Yehova. Iye anati: “Mulungu wathu, simudzawaweruza? Pakuti mwa ife mulibe mphamvu yakulimbana nawo aunyinji ambiri awa akutidzera; ndipo sitidziwa ngati tidzatani, koma maso athu ali kwa Inu.” (2 Mbiri 20:12, 13) Yehosafati atamaliza kupemphera “pakati pa msonkhano” mzimu wa Yehova unachititsa kuti Yahazieli Mlevi alankhule mawu okhazika mtima pansi kwa anthuwo.​—Werengani 2 Mbiri 20:14-17.

10. (a) Kodi Yehosafati ndiponso Ayuda analandira malangizo kudzera mwa ndani? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira malangizo amene Yehova amatipatsa?

10 Pa nthawiyo, Yehosafati ndi anthu onse mu ufumu wa Yuda analandira malangizo ochokera kwa Yehova kudzera mwa Yahazieli. Masiku ano kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amatipatsa malangizo komanso amatilimbikitsa. Motero, tiyenera kulandira malangizo amene akulu oikidwa amatipatsa. Iwo amachita maulendo a ubusa komanso amatsatira malangizo a “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”​—Mat. 24:45; 1 Ates. 5:12, 13.

11, 12. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene zinachitikira Yehosafati ndi Ayuda?

11 Yehosafati ndi anthu ake anasonkhana malo amodzi pofuna kupempha kuti Yehova awathandize. Nafenso sitiyenera kuleka kusonkhana nthawi zonse pamodzi ndi abale komanso alongo athu. Tikapanikizika ndi mavuto mpaka kufika posowa chochita, tiyenera kutengera chitsanzo cha Yehosafati ndi anthu a ku Yuda, amene anapemphera kwa Yehova mosakaika ngakhale pang’ono kuti Iye awamvera. (Miy. 3:5, 6; Afil. 4:6, 7) Ngakhale pamene tili kwatokha, kupemphera kwa Yehova kumachititsa kuti tigwirizane ndi ‘gulu lonse la abale athu m’dzikoli.’​—1 Pet. 5:9.

12 Yehosafati ndi anthu ake anatsatira malangizo amene Mulungu anawapatsa kudzera mwa Yahazieli. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Iwo anapambana nkhondoyo ndipo anabwerera ku Yerusalemu “ndi chimwemwe” ndi “zisakasa, ndi azeze, ndi malipenga, ku nyumba ya Yehova.” (2 Mbiri 20:27, 28) Nafenso timamvera malangizo amene Yehova amatipatsa kudzera m’gulu lake ndipo timam’tamanda mogwirizana.

Muzisamalira Bwino Malo Athu Osonkhanira

13. Kodi Hezekiya atangoyamba kulamulira anagwira ntchito yotani?

13 M’mwezi woyamba wa ulamuliro wake, Hezekiya anasonyeza changu chake pa kulambira Yehova. Iye anatsegula ndi kukonzanso kachisi. Anauza ansembe ndi Alevi kuti ayeretse nyumba ya Mulungu ndipo iwo anagwira ntchitoyi masiku 16. (Werengani 2 Mbiri 29:16-18.) Zimene anachitazi zimatikumbutsa kufunika kosamalira ndi kukonza malo athu osonkhanira kuti azioneka bwino. Ndipo malowo akamaoneka bwino amasonyeza kuti ndife achangu pa kulambira Yehova. Mwinanso inuyo mwamvapo anthu akuyamikira kwambiri changu chimene abale ndi alongo amasonyeza pogwira ntchito zoterezi. Abale ndi alongo amenewa amalemekeza Yehova chifukwa cha khama lawoli.

14, 15. Kodi ndi ntchito iti imene ikulemekeza kwambiri Yehova masiku ano? Perekani zitsanzo.

14 Mumzinda wina wa kumpoto kwa England munali munthu wina amene nyumba yake inagundizana ndi Nyumba ya Ufumu. Munthuyu sankafuna kuti Nyumba ya Ufumuyo ikonzedwe. Koma abale a kuderalo sanamukwiyire chifukwa cha zimenezi. Ndipo ataona kuti khoma lolumikiza Nyumba ya Ufumuyi ndi nyumba ya munthuyu likufunika kukonzedwa, abalewo anadzipereka kulikonza popanda kuuza munthuyo kuti apereke chilichonse. Iwo anagwira ntchitoyi mwakhama ndipo anamanganso pafupifupi khoma lonselo. Zimene anachitazi zinathandiza kuti munthu uja asinthe maganizo ake. Panopo iye amaonetsetsa kuti anthu sakuwononga Nyumba ya Ufumuyo.

15 Anthu a Yehova amagwira ntchito ya zomangamanga padziko lonse. Abale ena amatumizidwa kukagwira ntchito zomanga Nyumba za Ufumu, Nyumba za Msonkhano ndi nyumba za Beteli, ndipo amathandizidwa ndi abale ndi alongo odzipereka a m’madera amene ntchitoyo ikuchitikira. Sam ndi katswiri polumikiza zipangizo zothandiza kuti m’nyumba muzitenthera kapena muzizizira bwino. Iye ndi mkazi wake Ruth akhala akuyenda m’mayiko ambiri ku Ulaya ndi ku Africa kukathandiza pa ntchito ya zomangamanga. Iwo amasangalalanso kulalikira limodzi ndi mipingo ya kumene ali. Sam ananena chimene chimamulimbikitsa kugwira nawo ntchito imeneyi. Iye anati: “Abale amene atumikirapo pa Beteli, kwathu kuno komanso m’mayiko ena, ndi amene amandilimbikitsa. Ndikaona changu chawo komanso mmene amasangalalira, zimandichititsa kuti ndizikonda kugwira ntchito imeneyi.”

Muzimvera Malangizo a Mulungu

16, 17. Tchulani ntchito yapadera imene anthu a Mulungu agwira ndipo kodi zotsatira zake n’zotani?

16 Kuwonjezera pa kukonza kachisi, Hezekiya anayambitsanso chikondwerero cha Pasika chimene Yehova analamula kuti chizichitika chaka ndi chaka. (Werengani 2 Mbiri 30:1, 4, 5.) Hezekiya ndiponso anthu amene ankakhala ku Yerusalemu anaitana mtundu wonse kuphatikizapo anthu a mu ufumu wa kumpoto kuti adzakhale nawo pa chikondwererochi. Panali anthu amtokoma amene anakapereka makalata oitanira anthu ku chikondwererochi.​—2 Mbiri 30:6-9.

17 Masiku ano ntchito yofanana ndi imeneyi yakhala ikuchitikanso. Timaitana anthu a m’dera lathu kumwambo wokumbukira Mgonero wa Ambuye pogwiritsa ntchito timapepala tokongola. Timachita zimenezi pomvera lamulo la Yesu. (Luka 22:19, 20) Malangizo amene timalandira pa Msonkhano wa Utumiki, amatithandiza kugwira ntchito imeneyi mwachangu ndipo Yehova waidalitsa kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti chaka chatha ofalitsa pafupifupi 7 miliyoni anagawira timapepala toitanira anthu ku chikumbutso ndipo anthu okwana 17,790,631 anapezeka pa Chikumbutso.

18. Kodi kukhala ndi changu pa kulambira koona kungakuthandizeni motani?

18 Ponena za Hezekiya, Baibulo limati: “Anakhulupirira Yehova Mulungu wa Israyeli; atafa iye panalibe wakunga iye mwa mafumu onse a Yuda, ngakhale mwa iwo okhalapo asanabadwe iye. Pakuti anaumirira Yehova osapambuka pambuyo pake, koma anasunga malamulo amene Yehova adawalamulira Mose.” (2 Maf. 18:5, 6) Nafenso tiyenera kutengera chitsanzo chake. Changu chathu pa nyumba ya Yehova chidzatithandiza ‘kuumirirabe Yehova’ n’kumayembekezera moyo wosatha.​—Deut. 30:16.

Muzitsatira Malangizo Mwamsanga

19. Kodi anthu amayesetsa kuchita zotani pokonzekera Chikumbutso?

19 Yosiya atayamba kulamulira, nayenso anachita zambiri pokonzekera kuti anthu ake achite chikondwerero cha Pasika. (2 Maf. 23:21-23; 2 Mbiri 35:1-19) Nafenso timayesetsa kukonzekera bwino misonkhano yachigawo, misonkhano yadera, masiku a misonkhano yapadera komanso Chikumbutso. M’mayiko ena abale amalolera kuika moyo wawo pachiswe n’cholinga choti akapezeke pa mwambo wokumbukira imfa ya Khristu. Akulu akhama amaonetsetsa kuti sakunyalanyaza munthu wina aliyense mumpingo. Iwo amathandiza okalamba komanso amene akudwala kuti apezeke pa mwambo umenewu.

20. (a) Fotokozani zimene zinachitika mu ulamuliro wa Mfumu Yosiya komanso zimene Yosiyayo anachita. (b) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa nkhani imeneyi?

20 Mfumu Yosiya anauza anthu kuti akonzenso kachisi. Pa ntchito imeneyi, Hilikiya yemwe anali Mkulu wa Ansembe, “anapeza buku la chilamulo la Yehova mwa dzanja la Mose.” Iye anapereka bukulo kwa Safani yemwe anali mlembi ndipo Safaniyo anamuwerengera Yosiya bukulo. (Werengani 2 Mbiri 34:14-18.) Ndiye kodi mfumu Yosiya anatani? Nthawi yomweyo iye anang’amba zovala zake chifukwa cha chisoni ndipo anauza anthu kuti apemphere kwa Yehova. Kudzera mwa mneneri wamkazi, dzina lake Hulida, Mulungu anapereka uthenga wodzudzula miyambo ya chipembedzo imene inkachitika mu Yuda. Ngakhale kuti Yehova analosera za tsoka limene mtundu wonsewo unadzakumana nalo, Iye anaona ndiponso anayamikira khama limene Yosiya anasonyeza pochotsa kulambira mafano. (2 Mbiri 34:19-28) Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Tiyenera kukhala ndi mtima umene Yosiya anali nawo. Tikamva malangizo a Yehova tiyenera kuwatsatira mwamsanga. Tiyeneranso kukumbukira zimene zingachitike ngati mwapang’onopang’ono tikuyamba kuchita za mpatuko kapena zosakhulupirika. Tikamatero sitikayika ngakhale pang’ono kuti Yehova akuona ndipo akuyamikira khama limene tikusonyeza pa kulambira koona, ngati mmene anachitira ndi Yosiya.

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusonyeza changu pa nyumba ya Yehova? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

21 Mafumu anayi a Yuda amenewa omwe ndi Asa, Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya anapereka chitsanzo chabwino kwambiri. Zimene iwo anachita zingatithandize kukhala achangu kwambiri pa nyumba ya Mulungu komanso pa kulambira. Changu chathu chiyenera kutilimbikitsa kukhulupirira Yehova komanso kuchita zonse zimene tingathe pomutumikira. Motero ndi nzeru kumvera ndiponso kutsatira malangizo achikondi amene Mulungu amatipatsa kudzera mumpingo komanso akulu. Tikatero tidzakhala osangalala.

22 Nkhani yotsatira ifotokoza mmene tingakhalire achangu mu utumiki. Iwalimbikitsanso achinyamata kuti azitumikira Atate wathu wachikondi mwachangu. Tikambirananso mmene tingapewere msampha wina woopsa kwambiri umene Satana akugwiritsa ntchito. Tikamachita khama kutsatira malangizo ochokera kwa Yehova amenewa, timakhala tikutsanzira mwana wake Yesu Khristu. Mawu a m’Baibulo akuti “changu cha pa nyumba yanu chandidya,” amanena za iye.​—Sal. 69:9; 119:111, 129; 1 Pet. 2:21.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi Yehova amatidalitsa tikamam’tumikira motani ndipo n’chifukwa chiyani?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakhulupirira Yehova?

• Kodi kukhala achangu kungatithandize bwanji kumvera malangizo a Mulungu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 9]

Kodi Asa, Yehosafati, Hezekiya ndi Yosiya anasonyeza bwanji kuti anali ndi changu pa nyumba ya Yehova?