Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumatsatira “Njira Yopambana” ya Chikondi?

Kodi Mumatsatira “Njira Yopambana” ya Chikondi?

Kodi Mumatsatira “Njira Yopambana” ya Chikondi?

“MULUNGU ndiye chikondi.” Mawu a mtumwi Yohane amenewa amasonyeza khalidwe lalikulu kwambiri la Mulungu. (1 Yoh. 4:8) Chikondi chimene Mulungu ali nacho pa anthufe, n’chimene chimatheketsa kuti timuyandikire ndi kukhala naye pa ubwenzi. Kodi chikondi cha Mulungu chimatikhudzanso m’njira ina iti? Pali mawu akuti: “Khalidwe lathu limayenderana ndi zokonda zathu.” Izitu n’zoona. Komabe, n’zoonanso kuti timatengera khalidwe la anthu amene timakondana nawo. Popeza tinalengedwa m’chifanizo cha Mulungu, timatha kusonyeza chikondi ngati Mulungu. (Gen. 1:27) N’chifukwa chake mtumwi Yohane analemba kuti timakonda Mulungu “chifukwa anayamba ndi iye kutikonda.”​—1 Yoh. 4:19.

Mawu Anayi Ofotokozera Chikondi

Mtumwi Paulo ananena kuti chikondi ndi “njira yopambana.” (1 Akor. 12:31) N’chifukwa chiyani chikondi anachifotokoza motero? Kodi Paulo ankanena za chikondi chotani? Kuti tiyankhe mafunso amenewa, tiyeni tione bwinobwino tanthauzo la mawu akuti “chikondi.”

Agiriki akale anali ndi mawu anayi ofotokoza chikondi. Mawu ake ndi awa: stor·geʹ, eʹros, phi·liʹa ndi a·gaʹpe. Pa mawu amenewa, mawu oti a·gaʹpe ndi amene anawagwiritsa ntchito pofotokoza Mulungu yemwe “ndiye chikondi.” * Ponena za chikondi chimenechi, Pulofesa William Barclay ananena m’buku lake kuti: “Agapē ndi chikondi chimene munthu amachisonyeza chifukwa chakuti m’maganizo mwake akufuna kuchita zimenezo. Si khalidwe limene ungangolisonyeza chifukwa chotengeka mtima. Ndi khalidwe limene munthu umasonyeza pofuna kutsatira mfundo zinazake. Agapē ndi chikondi chimene munthu amachisonyeza chifukwa chakuti watsimikiza kuchita zimenezo.” (New Testament Words) Izi zikusonyeza kuti chikondi cha a·gaʹpe chili ndi mfundo zimene chimayendera, koma pochisonyeza nthawi zambiri munthu amakhudzidwa kwambiri mumtima. Popeza kuti pamakhala mfundo zabwino ndi zoipa, n’zodziwikiratu kuti Akhristu ayenera kutsatira mfundo zabwino zimene Yehova Mulungu wapereka m’Baibulo. Kuyerekezera zimene Baibulo limanena pofotokoza chikondi cha a·gaʹpe ndi mawu ena a m’Baibulo ofotokoza chikondi, kungatithandize kumvetsa bwino chikondi chimene tiyenera kusonyeza.

Chikondi cha M’banja

Zimakhala zosangalatsa kwambiri kukhala m’banja logwirizana ndiponso lokondana kwambiri. Mawu a Chigiriki akuti stor·geʹ nthawi zambiri ankagwiritsidwa ntchito pofotokoza chikondi chimene anthu a banja limodzi amasonyezana mwachibadwa. Akhristu amayesetsa kusonyeza chikondi kwa anthu a m’banja lawo. Paulo analosera kuti m’masiku otsiriza, anthu adzakhala “opanda chikondi chachibadwa.” *​—2 Tim. 3:1, 3.

N’zomvetsa chisoni kuti masiku ano anthu m’banja alibe chikondi chachibadwa. N’chifukwa chiyani amayi ambiri oyembekezera amachotsa mimba? N’chifukwa chiyani mabanja ambiri safuna kusamalira makolo awo okalamba? N’chifukwa chiyani chiwerengero cha anthu osudzulana chikukwera? Chifukwa chake n’chakuti anthu alibe chikondi chachibadwa.

Komanso Baibulo limaphunzitsa kuti “mtima ndiwo wonyenga koposa.” (Yer. 17:9) Chikondi cha m’banja chimadalira mtima wa munthu. N’zochititsa chidwi kuti Paulo anagwiritsa ntchito mawu oti a·gaʹpe pofotokoza chikondi chimene mwamuna ayenera kusonyeza mkazi wake. Iye anayerekezera chikondi chimenechi ndi chimene Khristu amasonyeza mpingo. (Aef. 5:28, 29) Chikondi chimenechi chimayendera mfundo zimene Yehova, yemwe anayambitsa banja, anakhazikitsa.

Chikondi chenicheni kwa anthu a m’banja mwathu chimatilimbikitsa kuthandiza makolo athu okalamba komanso kusamalira ana athu. Chimathandizanso makolo kuti azilanga ana awo mwachikondi pakafunika kutero ndiponso kuti asamachite zinthu mongotengeka maganizo, zimene zingapangitse kuti azingolekerera ana awo.​—Aef. 6:1-4.

Mfundo za m’Baibulo N’zothandiza pa Nkhani ya Chikondi cha Pakati pa Mwamuna ndi Mkazi

Chikondi chimene mwamuna ndi mkazi wake amasonyezana ndi mphatso yochokera Mulungu. (Miy. 5:15-17) Koma mawu oti eʹros, amene amatanthauza chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi, sanagwiritsidwe ntchito ndi anthu amene anauziridwa kulemba Baibulo. N’chifukwa chiyani sanatero? M’mbuyomo, Nsanja ya Olonda inanena kuti: “Masiku ano anthu padziko lonse ali ndi vuto limene Agiriki anali nalo. Iwo ankalambira Eros ngati mulungu, ankagwadira guwa lake ndipo ankapereka nsembe kwa iye. . . . Koma umboni umasonyeza kuti kulambira chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi kumeneku, kunachititsa kuti anthu akhale ndi makhalidwe otayirira, onyansa komanso autchisi. Mwina n’chifukwa chake olemba Baibulo sanagwiritse ntchito mawu amenewa.” Kuti tipewe kuyamba chibwenzi chifukwa chongokopeka ndi maonekedwe a munthu, tiyenera kulola kuti mfundo za m’Baibulo zizititsogolera posonyeza chikondi. Choncho tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi chikondi chimene ndili nacho pa munthuyu ndi chenicheni?’

Munthu akafika “pachimake pa unyamata,” amakhala ndi chilakolako champhamvu chofuna kugonana. Pa nthawi imeneyi achinyamata amene amachita khama kutsatira mfundo za m’Baibulo amakhalabe oyera. (1 Akor. 7:36; Akol. 3:5) Timaona kuti ukwati ndi mphatso yopatulika yochokera kwa Yehova. Ponena za anthu okwatirana, Yesu anati: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:6) M’malo mokhala m’banja chifukwa chongosangalatsidwa ndi mnzathuyo, timaona kuti ukwati ndi nkhani yaikulu. M’banja mukabuka mavuto, sitiyesa kupeza njira yothetsera banjalo, koma timayesetsa kusonyeza makhalidwe abwino amene angathandize kuti banja lathu likhale losangalala. Kuchita zimenezo kumathandiza kuti banja likhale losangalala mpaka kalekale.​—Aef. 5:33; Aheb. 13:4.

Chikondi cha Pakati pa Munthu ndi Mnzake

Popanda mabwenzi, moyo sungakhale wosangalatsa. Mwambi wina wa m’Baibulo umati: “Lilipo bwenzi lipambana ndi m’bale kuumirira.” (Miy. 18:24) Yehova amafuna kuti tikhale ndi mabwenzi apamtima. Tonsefe timadziwa kuti Davide ndi Jonatani anali pa ubwenzi wa ponda apa m’pondepo. (1 Sam. 18:1) Ndiponso Baibulo limati Yesu “anali kum’konda” kwambiri mtumwi Yohane. (Yoh. 20:2) Apa, mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kum’konda” ndi phi·liʹa, ndipo amatanthauzanso ubale pakati pa mabwenzi. Motero, sikulakwa kukhala ndi mnzathu amene timakondana naye kwambiri mumpingo. Komabe pa lemba la 2 Petulo 1:7, timalimbikitsidwa kuwonjezera chikondi (a·gaʹpe) pa “chikondi cha pa abale” (phi·la·del·phiʹa, omwe ndi mawu amene anapangidwa pophatikiza mawu awiri a Chigiriki, phiʹlos, kutanthauza “bwenzi” ndi a·del·phosʹ, kutanthauza “m’bale”). Ngati tikufuna kuti ubwenzi umene tili nawo ndi anzathu upitirire, tiyenera kutsatira malangizo amenewa. Choncho ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi mtima waubwenzi umene ndili nawo kwa anzanga umagwirizana ndi mfundo za m’Baibulo?’

Mawu a Mulungu amatithandiza kuti tisakhale atsankho pochita zinthu ndi anzathu. Sitikhala olekerera ngati mnzathu wapamtima walakwitsa chinachake, n’kumakhwimitsa kwambiri zinthu akakhala kuti yemwe walakwayo si mnzathu wapamtima. Komanso sitilankhula mawu osyasyalika n’cholinga choti tipeze mabwenzi. Ndiponso chofunika kwambiri n’chakuti kutsatira mfundo za m’Baibulo kumatithandiza kusankha mwanzeru mabwenzi ndiponso kupewa ‘mayanjano oipa amene amawononga makhalidwe abwino.’​—1 Akor. 15:33.

Chikondi Chimalimbikitsa Mgwirizano

Mgwirizano umene umakhala pakati pa Akhristu ndi wapadera kwambiri. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chikondi chanu chisakhale cha chiphamaso. . . . Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake.” (Aroma 12:9, 10) Chikondi cha a·gaʹpe chimene Akhristu amasonyezana si “cha chiphamaso.” Chikondi chimenechi sichimangochokera mumtima mwathu. M’malomwake chimayendera kwambiri mfundo za m’Baibulo. Koma Paulo ananenanso za “chikondi chaubale” (phi·la·del·phiʹa) ndi “chikondi chenicheni”(phi·loʹstor·gos, mawu amene anapangidwa kuchokera ku mawu akuti phiʹlos ndi stor·geʹ). Katswiri wina anati mawu akuti “chikondi chaubale” amatanthauza “chikondi chochokera pansi pa mtima, kukomerana mtima, kuchitirana chifundo komanso kuthandizana.” Chikondi cha a·gaʹpe limodzi ndi chikondi chaubale zimathandiza kuti anthu olambira Yehova azigwirizana. (1 Ates. 4:9, 10) Mawu ena amene anamasuliridwa kuti “chikondi chenicheni,” anagwiritsidwa ntchito malo amodzi okha m’Baibulo ndipo amatanthauza kugwirizana kwambiri ndi munthu ngati kuti ndi m’bale wako.

Mgwirizano umene umakhala pakati pa Akhristu umatheka chifukwa choti amasonyezana chikondi cha m’banja, chikondi cha munthu ndi mnzake wapamtima, komanso mitundu ina yonse ya chikondi, ndipo amachita zimenezi motsatira chikondi chimene chimayendera mfundo za m’Baibulo. Mpingo wachikhristu si malo ochezera kumene anthu amangopita kukasangalala ndipo suli ngati bungwe, koma ndi banja la anthu ogwirizana kwambiri polambira Yehova Mulungu. Timanena Akhristu anzathu kuti abale ndi alongo ndipo umu ndi mmene timawaoneradi. Iwo ndi abale ndi alongo athu auzimu, ndi anzathu amene timawakonda, ndipo nthawi zonse timayesetsa kuti khalidwe lathu lizigwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Tiyeni tonse tipitirize kulimbikitsa chikondi chimene chimagwirizanitsa komanso kudziwikitsa Akhristu oona.​—Yoh. 13:35.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 Chikondi cha a·gaʹpe chimagwiritsidwanso ntchito pofotokoza zinthu zimene sitiyenera kuchita.​—Yoh 3:19; 12:43; 2 Tim. 4:10; 1 Yoh. 2:15-17.

^ ndime 7 Mawu akuti “opanda chikondi chachibadwa” amasuliridwa kuchokera ku mawu akuti aʹstor·goi. Mawuwa achokera ku mawu akuti stor·geʹ, koma ali ndi mphatikira kutsogolo a-, wotanthauza “opanda.”​—Onaninso Aroma 1:31.

[Mawu Otsindika patsamba 12]

Kodi mungalimbikitse bwanji chikondi chimene chimatigwirizanitsa?