Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Mabanja Achikhristu, Tsatirani Chitsanzo cha Yesu

Mabanja Achikhristu, Tsatirani Chitsanzo cha Yesu

Mabanja Achikhristu, Tsatirani Chitsanzo cha Yesu

“Khristu . . . [anakusiyirani] chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa.”​—1 PET. 2:21.

1. (a) Kodi Mwana wa Mulungu anagwira ntchito yotani pa nthawi yolenga zinthu? (b) Kodi Yesu amamva bwanji ndi anthu?

PA NTHAWI imene Mulungu anali kupanga kumwamba ndi dziko lapansi, Mwana wake woyamba kubadwa anali pambali pake “ngati mmisiri.” Mwana wa Mulunguyo anagwira ntchito mogwirizana ndi Atate wake Yehova pamene Atate wakewo anakonza mapulani ndi kulenga nyama ndiponso zomera zambirimbiri padziko pano, komanso pamene Iye ankakonza Paradaiso woti muzidzakhala anthu, amene analengedwa m’chifanizo cha Yehova. Mwana wa Mulungu, yemwe patsogolo pake anadzadziwika ndi dzina loti Yesu, ankakonda anthu kwambiri. Iye anali “kusekerera [kapena kuti kusangalala] ndi ana a anthu.”​—Miy. 8:27-31; Gen. 1:26, 27.

2. (a) Kodi Yehova wapereka chiyani pofuna kuthandiza anthu opanda ungwiro? (b) Kodi Baibulo limathandizanso pa nkhani iti?

2 Anthu awiri oyambirira atachimwa, kuwombola anthu ochimwa kunakhala mbali yofunika kwambiri ya cholinga cha Yehova. Kuti zimenezi zitheke, Yehova anapereka nsembe ya dipo ya Khristu. (Aroma 5:8) Ndiponso Yehova anapereka Mawu ake, Baibulo, omwe amapatsa anthu malangizo ofunikira kuti zinthu ziziwayendera bwino ngakhale ali opanda ungwiro. (Sal. 119:105) M’Mawu akewo, Yehova wapereka malangizo othandiza anthu kukhala ndi mabanja olimba komanso achimwemwe. Pa nkhani ya ukwati, buku la Genesis limati mwamuna ayenera ‘kudziphatika kwa mkazi wake n’kukhala thupi limodzi.’​—Gen. 2:24.

3. (a) Kodi Yesu anaphunzitsa zotani pa nkhani ya ukwati? (b) Kodi nkhani ino ifotokoza chiyani?

3 Pa nthawi ya utumiki wake padziko lapansi, Yesu anagogomezera kuti ukwati suyenera kutha. Iye anaphunzitsa mfundo zimene zingathandize anthu kupewa maganizo ndi makhalidwe amene angasokoneze ukwati wawo kapena kuchititsa kuti banja lawo likhale losasangalala. (Mat. 5:27-37; 7:12) Nkhani ino ifotokoza mmene ziphunzitso za Yesu ndi chitsanzo chimene anapereka ali padziko lapansi zingathandizire amuna, akazi, makolo, ndiponso ana kukhala osangalala pa moyo wawo.

Mmene Mwamuna Wachikhristu Angalemekezere Mkazi Wake

4. Kodi udindo wa Yesu ndi wofanana bwanji ndi udindo wa amuna achikhristu?

4 Mulungu anaika mwamuna kukhala mutu wa banja, monga mmene Yesu alili Mutu wa mpingo. Mtumwi Paulo anati: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi wake monganso Khristu alili mutu wa mpingo, pokhala iye mpulumutsi wa thupilo. Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu, monga Khristu anakonda mpingo nadzipereka yekha chifukwa cha mpingowo.” (Aef. 5:23, 25) Pochita zinthu ndi akazi awo, amuna achikhristu ayenera kutsanzira mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake. Tiyeni tikambirane njira zingapo kuti tione mmene Yesu ankagwiritsira ntchito mphamvu zimene Mulungu anam’patsa.

5. Kodi Yesu ankagwiritsa ntchito motani mphamvu zake pochita zinthu ndi ophunzira ake?

5 Yesu anali “wofatsa ndi wodzichepetsa.” (Mat. 11:29) Analinso wachangu pochita zinthu. Sankanyalanyaza udindo wake ayi. (Maliko 6:34; Yoh. 2:14-17) Iye ankapereka uphungu kwa ophunzira ake mokoma mtima, ndipo ankatha kubwereza uphunguwo ngati pakufunikira kutero. (Mat. 20:21-28; Maliko 9:33-37; Luka 22:24-27) Komabe, sankachita zimenezi mowanyoza kapena mowachititsa manyazi. Komanso sankawapangitsa kuona kuti sawakonda kapena kuti iwowo sangakwanitse kuchita zimene iye ankawaphunzitsa. M’malomwake, iye ankawayamikira ndi kuwalimbikitsa. (Luka 10:17-21) Yesu ankachita zinthu mwachikondi ndiponso mwachifundo. N’chifukwa chake ophunzira ake ankamulemekeza kwambiri.

6. (a) Kodi mwamuna angaphunzire chiyani kwa Yesu poona mmene iye ankachitira zinthu ndi ophunzira ake? (b) Kodi Petulo akulimbikitsa amuna kuchita chiyani?

6 Chitsanzo cha Yesu chimaphunzitsa amuna kuti Mkhristu sayenera kugwiritsa ntchito umutu wake mopondereza. M’malomwake, umutu wakewo uyenera kukhala waulemu ndiponso wololera kuvutikira ena. Mtumwi Petulo analimbikitsa amuna kuti azitsanzira chikondi cha Yesu pochita zinthu ndi akazi awo, ‘n’kumawapatsa ulemu.’ (Werengani 1 Petulo 3:7.) Ndiyeno kodi mwamuna angagwiritse ntchito bwanji mphamvu zake kwinako akusonyezabe kuti amalemekeza mkazi wake?

7. Kodi mwamuna angalemekeze bwanji mkazi wake? Perekani chitsanzo.

7 Njira imodzi imene mwamuna angalemekezere mkazi wake ndiyo kukambirana naye kuti adziwe maganizo a mkaziyo asanasankhe zochita pa nkhani zokhudza banja. Mwachitsanzo, angafunikire kupanga chosankha pa nkhani ya kusamuka, kusintha ntchito kapena pa nkhani za tsiku ndi tsiku monga kokachitira tchuthi ndi kukonzanso bajeti mogwirizana ndi kukwera mtengo kwa zinthu. Popeza nkhani zimenezi zimakhudza banja lonse, zingakhale bwino ngati mwamuna angakomere mtima mkazi wake mwa kukambirana naye kaye kuti amve maganizo ake. Zimenezi zingathandize mwamunayo kusankha zinthu mwanzeru ndipo mkazi wakeyo sangavutike kumuchirikiza kuti mfundo agwirizanazo zitheke. (Miy. 15:22) Amuna achikhristu amene amalemekeza akazi awo amapatsidwa ulemu ndi akaziwo, ndipo chofunika kwambiri n’chakuti iwo amasangalatsa Yehova.​—Aef. 5:28, 29.

Mmene Mkazi Angasonyezere Ulemu Waukulu kwa Mwamuna Wake

8. N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa chitsanzo cha Hava?

8 Yesu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa akazi achikhristu pa nkhani ya kugonjera. Pa nkhani yolemekeza ulamuliro, maganizo a Yesu anali osiyana kwambiri ndi maganizo a mkazi woyamba. Hava sanapereke chitsanzo chabwino kwa akazi. Iye anali ndi mutu wake woikidwa ndi Yehova umene Yehovayo ankagwiritsa ntchito popereka malangizo. Koma Hava sanalemekeze dongosolo limeneli. Iye analephera kutsatira malangizo amene Adamu anamuuza. (Gen. 2:16, 17; 3:3; 1 Akor. 11:3) N’zoona kuti Hava anachita kunyengedwa, koma akanatha kufunsa kaye mwamuna wake kuti adziwe ngati anayenera kutsatira mawu amene anaoneka ngati akumuuza zimene ‘Mulungu akudziwa.’ M’malomwake, iye anauza mwamuna wake zoti achite, ndipo kumeneku kunali kudzikuza mapeto.​—Gen. 3:5, 6; 1 Tim. 2:14.

9. Kodi Yesu amapereka chitsanzo chotani pa nkhani ya kugonjera?

9 Mosiyana ndi Hava, Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri chogonjera Mutu wake. Maganizo ake ndiponso moyo wake wonse umasonyeza kuti “kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizirepo ngati chinthu choti angalande.” M’malomwake, iye “anakhuthula zonse za mwa iye n’kukhala ngati kapolo.” (Afil. 2:5-7) Panopo Yesu ndi Mfumu imene ikulamulira, ndipo maganizo ake ndi omwewa. Modzichepetsa, amagonjera Atate wake m’zinthu zonse ndipo amachirikiza umutu Wake.​—Mat. 20:23; Yoh. 5:30; 1 Akor. 15:28.

10. Kodi mkazi angachirikize bwanji umutu wa mwamuna wake?

10 Mkazi wachikhristu ayenera kutsanzira Yesu pochirikiza umutu wa mwamuna wake. (Werengani 1 Petulo 2:21; 3:1, 2.) Tiyeni tione nkhani imene ingapatse mkazi mpata wochita zimenezi. Tiyerekerezere kuti mwana wamwamuna akufuna kukachita zinazake zimene sangachite popanda chilolezo cha makolo. Kenako akupempha mayi ake. Koma popeza nkhaniyo ndi yoti mkaziyo sanakambiranepo ndi mwamuna wake, iye angachite bwino kufunsa mwanayo kuti, “Kodi bambo ako wawafunsa kale?” Ngati sanawafunse, mayiyo ayenera kukambirana kaye ndi mwamuna wake asanamulole mwanayo. Komanso mkazi wachikhristu ayenera kupewa kutsutsa mwamuna wake kapena kukana maganizo ake pamaso pa ana. Ngati sakugwirizana ndi mwamuna wakeyo pa nkhani inayake, ayenera kukambirana naye nkhaniyo ali awiri.​—Aef. 6:4.

Yesu Anapereka Chitsanzo kwa Makolo

11. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani kwa makolo?

11 Ngakhale kuti Yesu sanakwatire n’kukhala ndi ana, iye ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa makolo achikhristu. Kodi anapereka chitsanzo chotani? Iye moleza mtima ankaphunzitsa ophunzira ake mwachikondi, ndipo ankachita zimenezi mwa zolankhula ndi zochita zake. Iye anawasonyeza mmene angachitire ntchito imene anawapatsa. (Luka 8:1) Zimene Yesu ankachitira ophunzira ake ndiponso mmene ankawaonera, zinali chitsanzo cha zimene iwonso anayenera kuchita.​—Werengani Yohane 13:14-17.

12, 13. Kodi makolo angatani kuti ana awo akhale oopa Mulungu?

12 Ana amatsanzira makolo awo pa zilizonse, kaya zabwino kapena zoipa. Choncho, makolo ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi timapereka chitsanzo chotani kwa ana athu tikayerekezera nthawi imene timakhala tikuonera TV ndiponso kuchita zosangalatsa ndi nthawi imene timagwiritsa ntchito pophunzira Baibulo komanso polalikira? Kodi kwenikweni ndi zinthu ziti zimene timaika patsogolo m’banja mwathu? Kodi tikupereka chitsanzo chabwino chosonyeza kuti timaika kulambira koona patsogolo mwa zimene timachita pa moyo wathu komanso zosankha zathu?’ Kuti athe kuphunzitsa ana awo kukhala anthu oopa Mulungu, malamulo Mulungu choyamba ayenera kukhala mumtima mwa makolo.​—Deut. 6:6.

13 Ngati makolo amayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo, ana amaona zimenezo. Iwo amamvera zimene makolo awo amawaphunzitsa ndi kuwauza. Koma ana akaona kuti makolo amachita zosiyana ndi zimene amaphunzitsazo, angaganize kuti mfundo za m’Baibulo si zofunikira kwenikweni ndipo ndi zoti makolo amangozilankhula basi. Zimenezi zingachititse kuti anawo azigonja mosavuta akakumana ndi ziyeso za m’dzikoli.

14, 15. Kodi makolo ayenera kulimbikitsa ana awo kuchita chiyani, ndipo kodi ndi njira ina iti imene makolo angachitire zimenezi?

14 Makolo achikhristu amazindikira kuti kulera ana sikungowapezera zofunika zakuthupi zokha. Choncho si nzeru ngakhale pang’ono kuti makolo azingolimbikitsa ana awo kufuna zinthu zakuthupi. (Mlal. 7:12) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti aziika zinthu zauzimu patsogolo. (Mat. 6:33) Choncho makolo achikhristu ayenera kutsanzira Yesu mwa kuyesetsa kulimbikitsa ana awo kukhala ndi zolinga zauzimu.

15 Njira imodzi imene makolo angachitire zimenezi ndiyo kuyesetsa kupeza mpata woti ana awo azicheza ndi anthu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse. Tangoganizirani mmene achinyamata angalimbikitsidwire ngati atadziwana bwino ndi apainiya kapena woyang’anira dera ndiponso mkazi wake. Amishonale, anthu amene ali pa Beteli, ndiponso atumiki ochokera kunja ogwira ntchito yomanga, amanena zinthu zambiri zolimbikitsa zokhudza chimwemwe chimene munthu amapeza potumikira Yehova. Mosakayikira anthu amenewa amakhala ndi nkhani zambiri zolimbikitsa zimene angatisimbire. Chitsanzo chawo cha kutumikira ndi mtima wonse chingathandize kwambiri ana anu kusankha zinthu mwanzeru, kukhala ndi zolinga zabwino zotumikira Mulungu, ndiponso kusankha maphunziro amene angadzawathandize kudzisamalira pochita utumiki wa nthawi zonse.

Ananu, Kodi N’chiyani Chingakuthandizeni Kutsatira Chitsanzo cha Yesu?

16. Kodi Yesu ankalemekeza bwanji makolo ake a padziko lapansi komanso Atate wake wakumwamba?

16 Ananu, dziwani kuti inunso Yesu anakusiyirani chitsanzo chabwino kwambiri. Iye analeredwa ndi Yosefe ndi Mariya, ndipo ankawamvera. (Werengani Luka 2:51.) Yesu ankadziwa kuti ngakhale kuti iwo ankalakwitsa zinthu zina ndi zina, Mulungu anawapatsa udindo womulera. Motero anayenera kuwapatsa ulemu. (Deut. 5:16; Mat. 15:4) Atakula, nthawi zonse Yesu ankachita zinthu zosangalatsa Atate wake wakumwamba. Kuti athe kutero, iye anayenera kusagonja pokumana ndi mayesero. (Mat. 4:1-10) Nthawi zina inunso achinyamata mungayesedwe kuti muchite zinthu zosamvera makolo anu. Ndiyeno kodi n’chiyani chingakuthandizeni kutsatira chitsanzo cha Yesu?

17, 18. (a) Kodi achinyamata amakumana ndi mayesero otani kusukulu? (b) Kodi achinyamata sayenera kuiwala chiyani kuti apirire ziyeso?

17 N’kutheka kuti anzanu ambiri akusukulu saganizira kwambiri mfundo za m’Baibulo ndipo mwina safuna n’komwe kuzitsatira. N’kuthekanso kuti amayesa kukunyengererani kuti muchite nawo zinthu zoipa ndipo mwina amakusekani mukakana. Kodi anzanu akusukulu amakupatsani mayina ena ake chifukwa chokana kuchita nawo zinthu zina? Ndiye kodi mumatani? Inuyo mukudziwa kuti ngati mungatsatire zochita za anzanu chifukwa cha mantha, mungakhumudwitse makolo anu komanso Yehova. Kodi zochita za anzanu zingakufikitseni kuti? Mwina muli ndi zolinga monga kudzakhala mpainiya, mtumiki wothandiza, kutumikira gawo losowa ofalitsa Ufumu kapena kutumikira pa Beteli. Kodi kucheza kwambiri ndi anzanu akusukulu kungakuthandizeni kukwaniritsa zolinga zanuzo?

18 Kodi achinyamatanu amene muli mumpingo wachikhristu, nthawi zina mumakumana ndi zinthu zimene zimayesa chikhulupiriro chanu? Nanga zikatero mumatani? Taganizirani za Yesu, yemwe ndi chitsanzo chanu. Iye sanalole kugonja pamene ankayesedwa ndipo sanalole ngakhale pang’ono kusiya kuchita zimene ankadziwa kuti n’zoyenera. Mukamayesetsa kusaiwala mfundo zimenezi, mungathe kulimba mtima n’kuwauza anzanuwo mosapita m’mbali kuti simungalole kuchita nawo zinthu zimene mukudziwa kuti n’zoipa. Monga Yesu, maganizo anu azikhala pa cholinga chanu chotumikira Yehova mwachimwemwe ndiponso kumumvera kwa moyo wanu wonse.​—Aheb. 12:2.

Chinthu Chofunika Kwambiri Kuti Banja Lizisangalala

19. N’chiyani chingathandize anthu kukhala osangalala pa moyo wawo?

19 Yehova Mulungu ndi Yesu Khristu amatifunira zabwino anthufe. Ngakhale ndife opanda ungwiro, n’zotheka kukhala osangalala ndithu. (Yes. 48:17, 18; Mat. 5:3) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake mfundo za choonadi zimene zingathandize munthu kukhala wosangalala. Komatu si zokhazi zimene anawaphunzitsa. Iye anaphunzitsanso zimene munthu ayenera kuchita pa moyo wake kuti akhale wosangalala. Anatisiyiranso chitsanzo chabwino cha mmene tingakhalire ndi moyo wabwino ndiponso maganizo oyenera. Aliyense m’banja, kaya ali ndi udindo wotani, angapindule ngati atatsatira chitsanzo cha Yesu. Motero inu amuna, akazi, makolo komanso ana, tsatirani chitsanzo cha Yesu. Kumvera zimene Yesu anaphunzitsa komanso kutsatira chitsanzo chake, ndi kumene kungathandize kuti banja likhale losangalala.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi amuna ayenera kugwiritsa ntchito bwanji mphamvu zimene Mulungu wawapatsa?

• Kodi mkazi angatsatire bwanji chitsanzo cha Yesu?

• Kodi makolo angaphunzire chiyani poona mmene Yesu ankachitira zinthu ndi ophunzira ake?

• Kodi ana angaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Yesu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Kodi mwamuna amene amakonda mkazi wake amatani asanasankhe zochita pa nkhani zokhudza banja?

[Chithunzi patsamba 9]

Kodi ndi nkhani iti imene imapereka mpata kwa mkazi, wosonyeza kuti iye amalemekeza mutu wake?

[Chithunzi patsamba 10]

Ana amatengera zinthu zabwino zimene makolo amachita