Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Anapeza Chuma Chobisika

Anapeza Chuma Chobisika

Anapeza Chuma Chobisika

KODI munayamba mwapeza chuma chobisika pamalo osayembekezereka? Izi n’zimene zinachitikira Ivo Laud wa ku Estonia, pa March 27, 2005. Iye ndi wa Mboni za Yehova, ndipo pa nthawiyi ankathandiza mlongo wina wachikulire dzina lake Alma Vardja kugwetsa nyumba yakale yosungiramo katundu. Pogwetsa khoma lakunja, anapeza chithabwa chimene chinaikidwa mbali ina ya chipilala. Atachotsa chithabwacho anapeza dzenje lalikulu masentimita 120 m’litali, masentimita 10 m’lifupi, ndipo linali lakuya masentimita 10. Linali lovundikiridwa ndi thabwa lofanana ndi kukula kwa dzenjeli. M’dzenjemu munali chuma chobisika. (chithunzi  1) Kodi chuma chimenecho chinali chiyani? Nanga anachibisamo ndani?

M’dzenjeli munali mipukutu yokulungidwa bwino m’mapepala okhuthala. M’mipukutuyi (chithunzi 2), munali zofalitsa za Mboni za Yehova ndipo zambiri mwa izo zinali nkhani zophunzira za mu Nsanja ya Olonda ndipo zina zinali za mu 1947. Zonsezi zinali zolembedwa mwaluso pamanja m’Chiesitoniya. (chithunzi 3) Mipukutu ina inali ndi zinthu zina zothandiza anthu kudziwa amene anabisa chumachi. M’mipukutuyi munalembedwa mafunso amene Villem Vardja, yemwe anali mwamuna wa Alma, anafunsidwa ndi apolisi. Munalembedwanso zaka zimene iye anakhala m’ndende. Kodi n’chifukwa chiyani iye anamangidwa?

Villem Vardja anali ndi udindo mumpingo wa Mboni wa Tartu ndipo kenako anakatumikira kumpingo wa Otepää ku Estonia, dziko lomwe kale linali mbali ya Soviet Union. Zikuoneka kuti iye anaphunzira choonadi cha m’Baibulo, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse isanayambe. Patapita zaka zochepa, pa December 24, 1948, boma la Chikomyunizimu linamanga M’bale Vardja chifukwa cha chipembedzo chake. Apolisi anamupanikiza ndi mafunso ndiponso anamuzunza pomukakamiza kuti aulule maina a Mboni zinzake. Iye sanapatsidwe mwayi wokadziteteza kukhoti, m’malomwake analamulidwa kukakhala kundende ya ku Russia zaka 10.

Villem Vardja anakhalabe wokhulupirika kwa Yehova mpaka pamene anamwalira pa March 6, 1990. Mkazi wake sankadziwa kuti mabukuwa alipo. N’kutheka kuti M’bale Vardja sanamuuze chifukwa choti ankafuna kumuteteza kuti akadzapanikizidwa ndi mafunso asadzaulule. N’chifukwa chiyani iye anabisa mabukuwa? Iye anachita zimenezi chifukwa chakuti bungwe la chitetezo cha boma lotchedwa Soviet State Security Committee (KGB), linkachita kafukufuku m’nyumba za Mboni za Yehova kuti alande mabuku awo. M’bale Vardja anabisa mabukuwa n’cholinga choti okhulupirira anzake adzakhale ndi chakudya chauzimu poopa kuti mwina a KGB aja akanatha kulanda zonse. Zinthu zina zoterezi anali atazipezanso m’chilimwe m’chaka cha 1990. Zina anazipeza ku Tartu, chakum’mwera kwa dziko la Estonia. Chuma chimenechinso chinabisidwa ndi Villem Vardja.

Kodi n’chifukwa chiyani tikuti chimenechi chinali chuma? Chifukwa chakuti anachita khama polemba zinthuzi pamanja, n’kuzibisa mosamala, zimenezi zimasonyeza kuti Mboni zinkaona kuti chakudya chauzimu chimene zinkapeza pa nthawiyi chinali chamtengo wapatali. (Mat. 24:45) Kodi inuyo mumaona kuti chakudya chauzimu chimene mumalandira n’chamtengo wapatali? China mwa chakudya chimenechi ndi magazini a Nsanja ya Olonda amene amapezeka m’Chiesitoniya ndiponso m’zinenero zina zoposa 170.