Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Chikondi cha Khristu Chimatilimbikitsa Kukonda Ena

Chikondi cha Khristu Chimatilimbikitsa Kukonda Ena

Chikondi cha Khristu Chimatilimbikitsa Kukonda Ena

‘Yesu anali kuwakonda akewo amene anali m’dzikoli, anawakonda mpaka mapeto.’​—YOH. 13:1.

1, 2. (a) Kodi n’chifukwa chiyani chikondi cha Yesu chili chapadera kwambiri? (b) Kodi m’nkhani ino tikambirana mbali ziti zosonyezera chikondi?

YESU anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya chikondi. Chilichonse chimene anachita, khalidwe lake ndi kalankhulidwe kake, zimene anaphunzitsa ndiponso imfa yake ya nsembe, zinasonyeza chikondi chake. Mpaka imfa yake, Yesu anasonyeza chikondi kwa anthu amene anakumana nawo, makamaka kwa ophunzira ake.

2 Yesu anaperekadi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya chikondi, ndipo otsatira ake ayenera kumachita zinthu motsatira chikondi chimenecho. Chitsanzo chake chimatilimbikitsanso kusonyeza abale ndi alongo athu ndiponso anthu ena onse chikondi choterocho. M’nkhani ino, tikambirana mmene akulu mumpingo angatsanzirire Yesu, posonyeza chikondi kwa anthu amene achita machimo, ngakhale machimo aakulu. Tikambirananso mmene chikondi cha Yesu chimalimbikitsira Akhristu kuthandiza anthu amene akumana ndi masoka achilengedwe, matenda ndiponso mavuto ena.

3. Ngakhale kuti Petulo analakwa kwambiri, kodi Yesu anatani naye?

3 Usiku woti mawa lake Yesu aphedwa, anakanidwa katatu ndi mtumwi wake weniweni, Petulo. (Maliko 14:66-72) Ngakhale zinatero, Petulo atabwerera, mogwirizana ndi zimene Yesu analosera, Yesuyo anamukhululukira. Kenako Yesu anam’patsa Petulo maudindo akuluakulu. (Luka 22:32; Mac. 2:14; 8:14-17; 10:44, 45) Kodi tikuphunzirapo chiyani pa maganizo a Yesu kwa anthu amene amachita zolakwa zazikulu?

Khalani ndi Maganizo a Khristu Pothandiza Anthu Amene Alakwa

4. Kodi ndi nkhani iti imene makamaka imafuna kusonyeza maganizo a Khristu?

4 Pa nkhani zambiri zimene zimafuna kuti tisonyeze maganizo a Khristu, imene imavuta kwambiri ndi kusamalira nkhani ya munthu amene wachita tchimo lalikulu, kaya ndi m’banja kapena mumpingo. N’zomvetsa chisoni kuti pamene mapeto a dongosolo la Satana akuyandikira, makhalidwe abwino akuloweralowera pansi chifukwa cha mzimu wa dzikoli. Ana ndi akulu omwe angatengere makhalidwe oipa a dzikoli kapena mzimu wake wonyalanyaza makhalidwe abwino, n’kusiya kulimbikira poyenda panjira yopanikiza ya ku moyo. M’nthawi ya atumwi, ena anachotsedwa mumpingo wachikhristu, ndipo ena anadzudzulidwa. N’zimenenso zimachitika masiku ano. (1 Akor. 5:11-13; 1 Tim. 5:20) Ngakhale zili choncho, akulu amene amasamalira nkhani zotere akamasonyeza chikondi ngati cha Khristu, angathandize kwambiri munthu wolakwayo.

5. Kodi akulu angatsanzire bwanji maganizo a Khristu kwa anthu olakwa?

5 Mofanana ndi Yesu, akulu afunikira kuchirikiza mfundo zolungama za Yehova nthawi zonse. Akamatero, amasonyeza kufatsa, kukoma mtima ndiponso chikondi cha Yehova. Ngati munthu walapadi, kutanthauza kuti ali ndi “mtima wosweka” ndi “mzimu wolapadi” chifukwa cha tchimo lake, zingakhale zosavuta kuti akulu ‘awongolere munthu woteroyo ndi mzimu wachifatso.’ (Sal. 34:18; Agal. 6:1) Koma nanga bwanji ngati munthu wolakwayo ali wamwano ndipo sakusonyeza ngakhale pang’ono kuti akumva chisoni ndi zomwe wachitazo?

6. Kodi akulu ayenera kupewa chiyani pothandiza anthu olakwa, nanga n’chifukwa chiyani ayenera kupewa zimenezo?

6 Ngati munthu wolakwa akukana uphungu wa m’Malemba kapena akuloza chala anthu ena kuti ndi amene anamulakwitsa, akulu ndi anthu ena angakwiye. Podziwa kukula kwa zimene munthuyo wasokoneza kale, iwo angafune kuonetsa kuti akwiya ndi zochita zake ndiponso mzimu umene munthuyo akusonyeza. Komatu mkwiyo umawononga zinthu ndipo susonyeza “maganizo a Khristu.” (1 Akor. 2:16; werengani Yakobe 1:19, 20.) Yesu anachenjeza anthu a m’nthawi yake mosapita m’mbali, koma sanagwiritse ntchito mawu okhumudwitsa kapena opweteka ngakhale tsiku limodzi. (1 Pet. 2:23) M’malomwake, iye anapereka mpata wakuti anthu olakwa alape n’kuyamba kuyanjidwanso ndi Yehova. Ndithudi, chifukwa china chachikulu chimene Yesu anabwerera padziko lapansi chinali “kudzapulumutsa ochimwa.”​—1 Tim. 1:15.

7, 8. Kodi akulu ayenera kutsogozedwa ndi chiyani posamalira nkhani zachiweruzo?

7 Kodi chitsanzo cha Yesu pa nkhani imeneyi chiyenera kutithandiza kukhala ndi maganizo otani kwa anthu amene ayenera kulangidwa ndi mpingo? Kumbukirani kuti dongosolo la m’Malemba loweruza anthu olakwa mumpingo limateteza nkhosa ndipo lingathandize kuti munthu wolakwayo alape. (2 Akor. 2:6-8) Zimamvetsa chisoni kuti ena salapa ndipo amayenera kuchotsedwa, komabe n’zolimbikitsa kudziwa kuti ambiri otero amabwerera kwa Yehova ndiponso mumpingo wake. Akulu akamasonyeza maganizo ngati a Khristu, amathandiza kutsegula njira kuti munthuyo asinthe mtima wake ndipo kenako n’kubwerera. Ngakhale kuti ena mwa anthu amenewa sangadzakumbukire uphungu wonse wa m’Malemba umene akulu anawapatsa, adzakumbukirabe kuti akuluwo anawalemekeza ndiponso anawasonyeza chikondi.

8 Choncho, akulu ayenera kusonyeza “zipatso za mzimu,” makamaka chikondi ngati cha Khristu, ngakhale pamene wolakwayo akuvuta. (Agal. 5:22, 23) Iwo sayenera kuthamangira kuchotsa munthu wolakwa mumpingo. Ayenera kusonyeza kuti amafuna kuti anthu olakwa abwerere kwa Yehova. Motero pamene munthu wochimwa wasintha mtima wake, ngati mmene ambiri amachitira, iye angayamikire kwambiri Yehova ndiponso “mphatso za amuna” zomwe zinamuthandiza kwambiri kuti asavutike kubwerera mumpingo.​—Aef. 4:8, 11, 12.

Kusonyeza Chikondi Ngati cha Khristu M’nthawi ya Mapeto Ino

9. Perekani chitsanzo cha mmene Yesu anasonyezera chikondi kwa ophunzira ake.

9 Luka analemba za nkhani imene imasonyeza kuti Yesu ankafuna kuthandiza anthu chifukwa cha chikondi chake chachikulu. Yesu ankadziwa kuti pa nthawi ina, asilikali a Roma adzazinga mzinda wa Yerusalemu utatsala pang’ono kuwonongedwa, ndipo zimenezi zikadzachitika, kuthawa kudzakhala kosatheka. Chifukwa chokonda ophunzira ake, Iye anawachenjeza kuti: “Mukadzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu ankhondo, dziwani kuti chiwonongeko chake chayandikira.” Kodi iwo anayenera kutani? Yesu anaperekeratu malangizo omveka bwino ndi osapita m’mbali, akuti: “Pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira ku mapiri, ndipo amene ali mkati mwa mzindawo adzatulukemo, amene ali m’madera a kumidzi asadzalowe mu mzindawo; chifukwa amenewa ndi masiku obwezera chilango, kuti zonse zimene zinalembedwa zikwaniritsidwe.” (Luka 21:20-22) Magulu ankhondo a Roma atazinga Yerusalemu mu 66 C.E., anthu omvera anatsatira malangizo amenewa.

10, 11. Kodi kuganizira zimene Akhristu oyambirira anachita pothawa ku Yerusalemu, kungatithandize bwanji kukonzekera “chisautso chachikulu”?

10 Pa nthawi imene Akhristu ankathawa kuchoka ku Yerusalemu, iwo anafunika kusonyezana chikondi ngati chimene Khristu anawasonyeza. Mosakayika, iwo anayenera kugawana zimene anali nazo. Koma ulosi wa Yesu sunangokwaniritsidwa pamene mzinda wakalewo unawonongedwa. Unalinso kudzakwaniritsidwa m’tsogolo. Iye analosera kuti: “Kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko kufikira lerolino, ndipo sichidzachitikanso.” (Mat. 24:17, 18, 21) “Chisautso chachikulu” chimenechi chisanayambe ndiponso chili mkati, ifenso tingadzasowe zinthu zofunika pamoyo kapena kukumana ndi mavuto ena. Kukhala ndi maganizo a Khristu kudzatithandiza kupirira.

11 Nthawi imeneyo, tidzafunikira kutsatira chitsanzo cha Yesu posonyezana chikondi chopanda dyera. Pa mfundo imeneyi, Paulo analangiza kuti: “Aliyense wa ife azikondweretsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa. Pakuti ngakhale Khristu sanadzikondweretse yekha . . . Tsopano, Mulungu amene amapatsa anthu mphamvu kuti athe kupirira, achititse nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo.”​—Aroma 15:2, 3, 5.

12. Kodi tifunika kukhala ndi chikondi chotani masiku ano? Perekani chifukwa chake.

12 Petulo, yemwe anasonyezedwa chikondi ndi Yesu, analimbikitsanso Akhristu kukhala ndi “chikondi chaubale chopanda chinyengo” ndiponso kukhala “omvera choonadi.” Iwo ayenera ‘kukondana kwambiri kuchokera mu mtima.’ (1 Pet. 1:22) Masiku ano, tifunika kusonyeza kwambiri makhalidwe a Khristu ngati amenewa kuposa kale lonse. Panopa, mavuto amene anthu onse a Mulungu akukumana nawo akuwonjezeka. Kusokonekera kwa chuma padziko lonse kukusonyezeratu kuti sitiyenera ngakhale pang’ono kudalira mbali iliyonse ya dziko lakaleli. (Werengani 1 Yohane 2:15-17.) M’malomwake, pamene mapeto a dongosolo lino akuyandikira kwambiri, tifunika kuyandikira kwambiri kwa Yehova ndiponso kwa abale athu ndi kukhala ndi mabwenzi enieni mumpingo. Paulo analangiza kuti: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake. Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Ndipo Petulo anatsindikanso kwambiri mfundo imeneyi ponena kuti: “Koposa zonse, khalani okondana kwambiri wina ndi mnzake, pakuti chikondi chimakwirira machimo ochuluka.”​—1 Pet. 4:8.

13-15. Kodi abale ena asonyeza bwanji chikondi ngati cha Khristu patachitika masoka achilengedwe?

13 Padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zimadziwika chifukwa chosonyezana chikondi ngati cha Khristu. Taganizirani za Mboni zimene zinadzipereka kuthandiza anzawo pamene mphepo yamkuntho inasakaza madera ambiri akum’mwera kwa United States mu 2005. Potengera chitsanzo cha Yesu, abale ndi alongo oposa 20,000 anadzipereka, ndipo ambiri anasiya nyumba zabwino ndi ntchito zawo zodalirika kuti akathandize abale awo ovutika.

14 Kudera lina, madzi a m’nyanja anasefukira kufika pamtunda wamakilomita 80 kuchokera kunyanja, ndipo anali akuya mamita 10. Madziwo ataphwa, nyumba imodzi mwa zitatu zilizonse za anthu komanso nyumba zina, zinali zitawonongekeratu. Abale ndi alongo aluso ochokera m’mayiko osiyanasiyana anafika kuderali ndi zida ndiponso katundu womangira ndipo anali okonzeka kugwira ntchito iliyonse imene ingafunike. Alongo awiri amasiye omwe ndi apachibale, analongedza katundu wawo m’galimoto ndi kuyenda ulendo wamakilomita 3,000 kupita kukathandiza kuderali. Mmodzi wa alongo amenewa anakhaliratu komweko, ndipo mpaka pano akuthandizabe komiti yopereka chithandizo komanso akuchita upainiya wokhazikika.

15 M’derali nyumba zoposa 5,600 za Mboni ndiponso za anthu ena zamangidwa kapena kukonzedwa. Kodi Mboni zakumeneko zinamva bwanji zitasonyezedwa chikondi chachikulu ngati chimenechi? Mlongo wina amene nyumba yake inawonongeka anali atasamukira m’kakalavani kodontha ndiponso kokhala ndi sitovu yowonongeka. Abale anamumangira nyumba yaing’ono koma yabwino. Ataimirira kutsogolo kwa nyumba yake yatsopanoyo, analira pothokoza Yehova ndi abale ake. Mboni zambiri zimene nyumba zawo zinawonongeka, zinakhalabe m’malo amene zinasamukira kwa chaka chimodzi kapena kuposerapo, ngakhale kuti anali atazimangira nyumba. Izo zinachita zimenezi pofuna kuti abale ogwira ntchito yopereka chithandizo azikhala m’nyumba zawo zatsopanozo. Kodi chimenechi si chitsanzo chabwino chokhala ndi maganizo a Khristu?

Kusonyeza Maganizo a Khristu kwa Odwala

16, 17. Kodi tingasonyeze maganizo a Khristu kwa odwala m’njira ziti?

16 Ambiri a ife sitinakumanepo ndi masoka akuluakulu achilengedwe. Koma tonse timakumana ndi vuto la matenda, mwina ifeyo kudwala kapena wachibale. Mmene Yesu ankaonera anthu odwala ndi chitsanzo kwa ife. Chifukwa chokonda anthu, iye ankamvera chifundo odwala. Pamene makamu a anthu anamubweretsera odwala, “onse amene sanali kumva bwino m’thupi anawachiritsa.”​—Mat. 8:16; 14:14.

17 Masiku ano, Akhristu alibe mphamvu zochiritsa mozizwitsa zimene Yesu anali nazo. Ngakhale zili choncho, iwo ali ndi mtima wachifundo umene Yesu anali nawo kwa odwala. Kodi amasonyeza bwanji mtima umenewu? Njira ina ndi yakuti akulu amasonyeza maganizo a Khristu mwa kukonza dongosolo loti odwala mumpingo azithandizidwa ndipo amaonetsetsa kuti dongosolo limeneli likutsatiridwa. Amachita izi potsatira mfundo ya pa Mateyo 25:39, 40. * (Werengani.)

18. Kodi alongo awiri anasonyeza bwanji chikondi chenicheni kwa mlongo wina, ndipo zotsatira zake zinali zotani?

18 Komabe, sikuti munthu amafunika kukhala mkulu kuti azichitira ena zabwino. Taganizirani za Charlene wa zaka 44, yemwe anapezeka ndi matenda a khansa ndipo anauzidwa kuti amwalira pakangotha masiku 10. Alongo awiri omwe ndi Sharon ndi Nicolette, poona chisamaliro chimene mlongoyu ankafunika ndi mmene mwamuna wake anali kuvutikira pomusamalira, anadzipereka kumusamalira masiku onse omaliza a moyo wake. Mlongoyu anakhalabe ndi moyo mpaka milungu 6, koma alongowa anapitirizabe kumusamalira ndi kumusonyeza chikondi mpaka pamene anamwalira. Sharon anati: “Zimakhala zovuta ngati ukudziwa kuti munthuyo sachira. Koma Yehova anatipatsa mphamvu. Zimene zinachitikazi zinatithandiza kumukonda kwambiri Yehova ndiponso kukondana ife tonse.” Mwamuna wa Charlene anati: “Sindidzaiwala kukoma mtima kwa alongo awiri okondeka amenewa ndi thandizo limene anapereka. Thandizo lawo lochokera pansi pa mtima ndi chilimbikitso chawo, zinathandiza kuti mkazi wanga wokhulupirika Charlene athe kupirira bwino chiyeso chake chomaliza. Zinandithandizanso kuti ndizipeza mpata wopumula ndiponso kuti maganizo anga azimasukako, zomwe ndinkafunikira kwambiri. Sindidzasiya kuwathokoza. Mtima wawo wodzimana unalimbitsa chikhulupiriro changa mwa Yehova ndi chikondi changa pa gulu lonse la abale.”

19, 20. (a) Kodi takambirana mbali zisanu ziti zosonyezera maganizo a Khristu? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza kuchita chiyani?

19 M’nkhani zitatuzi, takambirana mbali zisanu zosonyezera maganizo a Yesu ndiponso zimene tingachite kuti titengere maganizo ndi zochita zake. Mofanana ndi Yesu, tiyeni tikhale ‘ofatsa ndi odzichepetsa.’ (Mat. 11:29) Tiziyesetsanso kukomera ena mtima, ngakhale pamene zolakwa ndi zofooka zawo zikuonekera kwambiri. Tizimvera malamulo onse a Yehova molimba mtima, ngakhale pamene tikuyesedwa.

20 Ndiponso tizisonyeza chikondi cha Khristu kwa abale athu onse, ngati mmene Khristuyo anachitira “mpaka mapeto.” Chikondi choterechi chimasonyeza kuti ndife otsatira enieni a Yesu. (Yoh. 13:1, 34, 35) Inde, “chikondi chanu chaubale chipitirire.” (Aheb. 13:1) Muzichisonyeza mosaumira. Muzigwiritsa ntchito moyo wanu kutamanda Yehova ndiponso kuthandiza ena. Mukatero, Yehova adzakudalitsani chifukwa cha khama lanu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 17 Onani nkhani yakuti: “Chitani Zoposa Kunena Kuti: ‘Mukafunde ndi Kukhuta,’” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1986.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi akulu angasonyeze bwanji maganizo a Khristu kwa olakwa?

• N’chifukwa chiyani kutengera chikondi cha Khristu kuli kofunika kwambiri masiku otsiriza ano?

• Kodi tingasonyeze bwanji maganizo a Khristu kwa odwala?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 17]

Akulu amafuna kuti anthu olakwa abwerere kwa Yehova

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi Akhristu amene ankathawa ku Yerusalemu anasonyeza bwanji maganizo a Khristu?

[Chithunzi patsamba 19]

Mboni za Yehova zimadziwika chifukwa chosonyezana chikondi ngati cha Khristu