Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Omvera Ndiponso Olimba Mtima Ngati Khristu

Khalani Omvera Ndiponso Olimba Mtima Ngati Khristu

Khalani Omvera Ndiponso Olimba Mtima Ngati Khristu

“Limbani mtima! Ndaligonjetsa dziko ine.”​—YOH. 16:33.

1. Kodi Yesu anamvera Mulungu mpaka pati?

YESU KHRISTU ankachita chifuniro cha Mulungu nthawi zonse. Ngakhale tsiku limodzi, iye sanaganizepo zosamvera Atate wake wakumwamba. (Yoh. 4:34; Aheb. 7:26) Koma padziko lapansi, kumvera sikunali kophweka chifukwa cha zimene anakumana nazo. Kungochokera pamene Yesu anayamba ntchito yolalikira, adani ake, kuphatikizapo Satana, anayesetsa kumunyengerera, kumukakamiza kapena kumupusitsa kuti asiye kukhulupirika kwake. (Mat. 4:1-11; Luka 20:20-25) Adani akewa ankamusowetsa mtendere ndiponso anamuzunza. Pamapeto pake, iwo anamuphera pamtengo wozunzikirapo. (Mat. 26:37, 38; Luka 22:44; Yoh. 19:1, 17, 18) Pa zonsezi, komanso ngakhale kuti iye anavutika kwambiri, Yesu anakhalabe “womvera mpaka imfa.”​—Werengani Afilipi 2:8.

2, 3. Yesu anakhala womvera ngakhale kuti anavutika kwambiri. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

2 Chifukwa cha zimene anakumana nazo ali munthu padziko lapansi, Yesu anaphunzira kumvera m’njira yatsopano. (Aheb. 5:8) Mwina tingaganize kuti palibenso chimene Yesu akanaphunzira pa nkhani yotumikira Yehova. Si uja anali ndi Yehova kwa zaka zambirimbiri komanso anali “mmisiri” wa Mulungu pa nthawi imene ankalenga zinthu? (Miy. 8:30) Ngakhale ndi choncho, kupirira kwake mokhulupirika mavuto amene anakumana nawo ali munthu, kunasonyeza kuti iye anasungadi umphumphu. Yesu, Mwana wa Mulungu, anakula mwauzimu. Kodi zimene zinamuchitikirazi zikutiphunzitsa chiyani?

3 Ngakhale kuti anali munthu wangwiro, Yesu sanaganize kuti payekha angathe kukhalabe womvera, osalakwitsa kalikonse. Iye anapemphera kwa Mulungu kuti amuthandize kukhalabe womvera. (Werengani Aheberi 5:7.) Kuti ifenso tikhale omvera, tifunika kukhala odzichepetsa ndiponso okonda kupemphera. N’chifukwa chake mtumwi Paulo analangiza Akhristu kuti: “Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo.” Iye “anadzichepetsa nakhala womvera mpaka imfa.” (Afil. 2:5-8) Moyo wa Yesu unasonyeza kuti n’zotheka anthu kukhala omvera, ngakhale m’dziko loipali. Yesu anali wangwiro ndipo m’pomveka kuti anali womvera. Koma bwanji anthu opanda ungwirofe?

Tingathe Kukhala Omvera Ngakhale Tili Opanda Ungwiro

4. Kodi mfundo yakuti tinalengedwa ndi ufulu wosankha, imatanthauza chiyani?

4 Polenga Adamu ndi Hava, Mulungu anawapatsa nzeru ndi ufulu wosankha. Popeza ndife mbadwa zawo, ifenso tili ndi ufulu wosankha. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Zikutanthauza kuti tingathe kusankha kuchita zabwino kapena zoipa. Kunena kwina, tingati Mulungu watipatsa ufulu wosankha kumumvera kapena kusamumvera. Koma ufulu waukulu umenewu umatipatsanso udindo. Zosankha zathu, kaya zabwino kapena zoipa, zimakhala ndi zotsatira zake, zimene ndi moyo kapena imfa. Zimakhudzanso anthu ena.

5. Kodi tonsefe tili pa nkhondo iti, ndipo tingatani kuti tipambane?

5 Popeza ndife opanda ungwiro, mwachibadwa si ife omvera. Choncho, kumvera malamulo a Mulungu kumativuta. Ili ndi vuto limenenso Paulo anali nalo. Iye analemba kuti: “Ndimaona chilamulo china m’ziwalo zanga chikumenyana ndi chilamulo cha m’maganizo mwanga ndi kundipanga kapolo wa chilamulo cha uchimo chimene chili m’ziwalo zanga.” (Aroma 7:23) Nthawi zambiri, kumvera kumakhala kosavuta ngati tikuona kuti sitiluza chilichonse, sitimva kupweteka kulikonse kapena ngati tikuona kuti sikusokoneza zimene tikufuna. Koma kodi timatani pamene mtima wathu wofuna kumvera, ukulimbana ndi “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso”? Timakhala ndi zilakolako zoipa zimenezi chifukwa chakuti ndife opanda ungwiro ndiponso chifukwa cha “mzimu wa dziko” limene tikukhalali, ndipo zilakolako zimenezi ndi zamphamvu kwambiri. (1 Yoh. 2:16; 1 Akor. 2:12) Kuti tigonjetse zilakolako zimenezi, tifunika ‘kukonza mtima wathu,’ kapena kuti kuukonzekeretsa tisanakumane ndi mavuto kapena mayesero, ndipo tiyenera kutsimikiza mtima kuti tidzamvera Yehova, zivute zitani. (Sal. 78:8) M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anapambana nkhondoyi chifukwa chakuti iwo anakonzekeretsa mitima yawo.​—Ezara 7:10; Dan. 1:8.

6, 7. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti phunziro laumwini lingatithandize kusankha zinthu mwanzeru.

6 Njira ina imene tingakonzekeretsere mtima wathu, ndiyo kuphunzira mwakhama Malemba ndi mabuku ofotokoza Baibulo. Mwachitsanzo, tinene kuti nthawi yanu yochita phunziro laumwini yakwana. Mwapemphera kuti mzimu wa Yehova ukuthandizeni kugwiritsa ntchito zimene muphunzire m’Mawu ake. Muli ndi pulogalamu yakuti tsiku lotsatira madzulo mudzaonere filimu inayake pa TV. Mwamva kuti anthu ambiri akunena kuti filimuyo ndi yabwino, ngakhale kuti inuyo mukudziwa kuti ili ndi mbali zina zachiwerewere ndi zachiwawa.

7 Kenako mukuganizira malangizo a Paulo a pa Aefeso 5:3, akuti: “Dama ndi chonyansa cha mtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe n’komwe pakati panu, monga kuyenera anthu oyera.” Mukukumbukiranso malangizo a Paulo a pa Afilipi 4:8. (Werengani.) Posinkhasinkha malangizo ouziridwa amenewa, mukudzifunsa kuti, ‘Ngati ndilola zinthu ngati zimenezi kulowa mumtima ndi m’maganizo mwanga, kodi ndidzakhala ndikutsanzira Yesu pa nkhani yomvera Mulungu m’zonse?’ Ndiye kodi mudzatani pamenepa? Kodi mudzangonyalanyaza zonsezi n’kuonera filimuyo?

8. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kutsatira mfundo za Yehova za makhalidwe abwino ndiponso zokhudza moyo wathu wauzimu?

8 Kungakhale kulakwitsa kupeputsa mfundo za Yehova za makhalidwe abwino ndiponso zokhudza moyo wathu wauzimu, mwina chifukwa choganiza kuti ndife olimba mwauzimu ndipo mayanjano oipa, ngakhale atakhala kuonera zosangalatsa zachiwawa ndi zachiwerewere, sangatisokoneze. Koma ife tiyenera kudziteteza ndiponso kuteteza ana athu kuti mzimu wa Satana usapotoze maganizo athu. Anthufe timayesetsa kudziteteza ku matenda opatsirana. Tiyeneranso kuyesetsa kukhala maso kuti tidziteteze ku “machenjera” a Satana.​—Aef. 6:11.

9. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kumvera Yehova tsiku lililonse?

9 Tsiku lililonse timafunika kusankha ndithu kuchita zinthu m’njira ya Yehova kapena ayi. Kuti tidzapulumuke, tiyenera kumvera Mulungu ndi kutsatira mfundo zake zolungama. Mwa kukhala omvera ngati Khristu, mwina “mpaka imfa” kumene, timasonyeza kuti chikhulupiriro chathu ndi chenicheni. Yehova adzatipatsa mphoto chifukwa cha kukhulupirika kwathu. Yesu analonjeza kuti: “Iye amene adzapirira mpaka mapeto, ndiye amene adzapulumuka.” (Mat. 24:13) Apa n’zoonekeratu kuti zimenezi zimafuna kuti tikhaledi olimba mtima ngati Yesu.​—Sal. 31:24.

Yesu Ndi Chitsanzo Chabwino Kwambiri cha Kulimba Mtima

10. Kodi tingakumane ndi mavuto otani, ndipo tiyenera kuchita chiyani?

10 Popeza tikukhala m’dziko limene lili ndi maganizo ndi makhalidwe oipa, tifunika kukhala olimba mtima kuti tisadetsedwe. Akhristu angayesedwe kuchita zoipa, kuchita nawo miyambo yachipembedzo kapena miyambo ina, ndiponso amalimbana ndi mavuto a zachuma. Zinthu zimenezi zingatilepheretse kutsatira njira zolungama za Yehova. Ambiri amatsutsidwa ndi a m’banja mwawo. M’mayiko ena, sukulu zikulimbikitsa kwambiri chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka, ndipo anthu ambiri ayamba kukhulupirira zakuti kulibe Mulungu. Popeza pali mavuto onsewa, ife sitingangokhala phee osachita chilichonse. Tiyenera kulimbana ndi zimenezi kuti tidziteteze. Chitsanzo cha Yesu chimasonyeza mmene tingachitire zimenezi.

11. Kodi kusinkhasinkha chitsanzo cha Yesu kungatithandize bwanji kukhala olimba mtima kwambiri?

11 Yesu anauza ophunzira ake kuti: “M’dzikomu mukumana ndi masautso, koma limbani mtima! Ndaligonjetsa dziko ine.” (Yoh. 16:33) Iye sanalolere kuchita zimene dziko linkafuna. Sanalolenso kuti dziko limulepheretse kugwira ntchito yake yolalikira kapena kumuchititsa kuti apeputse mfundo zokhudza kulambira koona ndiponso za makhalidwe abwino. Nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi. Popempherera ophunzira ake, Yesu anati: “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yoh. 17:16) Kuphunzira ndi kusinkhasinkha chitsanzo cha Khristu cha kulimba mtima kungatithandize kukhala olimba mtima kuti tikhale osiyana ndi dzikoli.

Phunzirani kwa Yesu Kukhala Olimba Mtima

12-14. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yesu anali wolimba mtima.

12 Yesu anasonyeza kuti anali wolimba mtima kwambiri pa nthawi yonse ya utumiki wake. Pogwiritsa ntchito ulamuliro wake monga Mwana wa Mulungu, iye mopanda mantha “analowa m’kachisi ndi kuthamangitsa onse ogulitsa ndi ogula m’kachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mabenchi a ogulitsa nkhunda.” (Mat. 21:12) Asilikali atabwera kudzamugwira usiku womaliza wa moyo wake padziko lapansi, Yesu molimba mtima anachoka pa gulu la ophunzira ake n’kuwayandikira asilikaliwo pofuna kuteteza ophunzira akewo ndipo anati: “Ngati mukufuna ine, alekeni awa apite.” (Yoh. 18:8) Patapita nthawi pang’ono, anauza Petulo kuti abwezere lupanga lake m’chimake, ndipo zimenezi zinasonyeza kuti Yesu ankadalira kwambiri Yehova osati zida za m’dzikoli.​—Yoh. 18:11.

13 Yesu mopanda mantha anatsutsa aphunzitsi onyenga ndiponso opanda chikondi a m’nthawi yake. Iye anatsutsanso ziphunzitso zawo zonyenga. Yesu anawauza kuti: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! chifukwa mukutseka ufumu wa kumwamba kuti anthu asalowemo. Munyalanyaza zinthu zofunika za m’Chilamulo, monga chilungamo, chifundo ndi kukhulupirika. . . . Mumayeretsa kunja kwa chikho ndi mbale, koma mkati mwake mwadzala zolanda ndi kusadziletsa.” (Mat. 23:13, 23, 25) Ophunzira a Yesu ankafunika kukhalanso olimba mtima chonchi, chifukwa ankayembekezera kuzunzidwa mwinanso kuphedwa kumene ndi atsogoleri onyenga achipembedzo.​—Mat. 23:34; 24:9.

14 Yesu analinso wolimba mtima ngakhale polimbana ndi ziwanda. Tsiku lina, anakumana ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wonyansa ndipo anali wamphamvu kwambiri moti anthu ankalephera kumumanga ngakhale ndi unyolo. Mopanda mantha, Yesu anatulutsa ziwanda zambiri zimene zinagwira munthuyu. (Maliko 5:1-13) Masiku ano, Mulungu sanapatse Akhristu mphamvu yochitira zozizwitsa ngati zimenezi. Ngakhale zili choncho, pogwira ntchito yathu yolalikira ndi kuphunzitsa, ifenso tiyenera kumenya nkhondo yauzimu yolimbana ndi Satana amene “wachititsa khungu maganizo a anthu osakhulupirira.” (2 Akor. 4:4) Mofanana ndi Yesu, zida zathu “si zili za kuthupi, koma zili zamphamvu mwa Mulungu zogwetsa nazo zinthu zozikika molimba.” Zinthu zimenezi ndi ziphunzitso zolakwika za chipembedzo zomwe zazika mizu m’mitima ya anthu. (2 Akor. 10:4) Tikamagwiritsa ntchito zida zauzimu zimenezi, timaona mmene Yesu ankazigwiritsira ntchito ndipo timatengera chitsanzo chake.

15. Kodi n’chiyani chinachititsa Yesu kukhala wolimba mtima?

15 Yesu anali wolimba mtima chifukwa cha chikhulupiriro, osati chifukwa cha mtima wofuna kudzionetsera. Ifenso tiyenera kukhala olimba mtima chifukwa cha chikhulupiriro. (Maliko 4:40) Kodi tingatani kuti tikhale ndi chikhulupiriro chenicheni? Chitsanzo cha Yesu chingatithandizenso pa nkhani imeneyi. Iye anasonyeza kuti ankadziwa bwino Malemba ndipo ankawadalira kwambiri. Chida chimene Yesu anagwiritsa ntchito si lupanga lenileni koma lupanga la mzimu, lomwe ndi Mawu a Mulungu. Nthawi zambiri, ankapereka umboni wa m’Malemba wotsimikizira kuti zimene ankaphunzitsa ndi zoona. Iye kawirikawiri ankayamba ndi mawu monga akuti: “Malemba amati.” Ponena zimenezi, iye ankatanthauza Mawu a Mulungu. *

16. Kodi tingatani kuti chikhulupiriro chathu chizilimba?

16 Kuti tikhale ndi chikhulupiriro chimene chingathe kupirira mayesero amene amatipeza chifukwa chokhala ophunzira a Yesu, nafenso tiyenera kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo tsiku ndi tsiku ndiponso kupezeka pamisonkhano. Tikamachita zimenezi, timakhala tikulowetsa m’maganizo mwathu mfundo za choonadi zomwe ndi maziko a chikhulupiriro. (Aroma 10:17) Tiyeneranso kusinkhasinkha, kapena kuti kuganizira mozama, zimene timaphunzira kuti zikhazikike mumtima mwathu. Chikhulupiriro chamoyo n’chimene chingatithandize kukhala olimba mtima. (Yak. 2:17) Ndiponso tiyenera kupempha mzimu woyera chifukwa chakuti chikhulupiriro ndi chipatso cha mzimuwo.​—Agal. 5:22.

17, 18. Kodi mtsikana wina anasonyeza bwanji kulimba mtima kusukulu?

17 Mtsikana wina dzina lake Kitty, anaona mmene chikhulupiriro chenicheni chimathandizira munthu kukhala wolimba mtima. Kuyambira ali mwana, ankadziwa kuti akakhala kusukulu sayenera ‘kuchita nawo manyazi uthenga wabwino.’ Motero iye ankafunitsitsa kulalikira anzake akusukulu. (Aroma 1:16) Chaka chilichonse, ankayesetsa ndithu kuti auze anzake uthenga wabwino, koma ankalephera chifukwa cha mantha. Patadutsa zaka zingapo, anasintha sukulu. Atatero iye anati: “Ulendo uno ndichita zimene ndakhala ndikulephera kuchita nthawi yonseyi.” Kitty anapemphera kuti akhale wolimba mtima ngati Khristu, ndiponso kuti apeze nzeru ndi mpata wabwino woti alalikire.

18 Tsiku loyamba kupita kusukulu, aphunzitsi anauza ana a sukulu kuti aliyense anene dzina ndi mbiri yake. Ambiri anatchula chipembedzo chawo koma ananena kuti sachitsatira kwambiri. Kitty anaona kuti mpata anapempherera uja ndi umenewu. Itafika nthawi yoti alankhule, iye molimba mtima anati: “Ine ndine wa Mboni za Yehova, ndipo Baibulo ndi limene limanditsogolera pa nkhani zauzimu ndi zokhudza khalidwe limene ndiyenera kukhala nalo.” Akulankhula, anzake ena anamuyang’ana monyodola atapinda milomo. Koma ena anamvetsera ndipo pambuyo pake anamufunsa mafunso. Aphunzitsi ake ananena kuti Kitty ndi chitsanzo chabwino cha munthu wokonzeka kuikira kumbuyo zimene amakhulupirira. Kitty akusangalala kwambiri kuti anatengera chitsanzo cha Yesu cha kulimba mtima.

Khalani ndi Chikhulupiriro Ndiponso Olimba Mtima Ngati Khristu

19. (a) Kodi kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni kumatanthauza chiyani? (b) Kodi tingatani kuti tizisangalatsa Yehova?

19 Nawonso atumwi ankadziwa kuti anafunika chikhulupiriro kuti akhale olimba mtima. Iwo anapempha Yesu kuti: “Tiwonjezereni chikhulupiriro.” (Werengani Luka 17:5, 6.) Kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni sikumangotanthauza kukhulupirira kuti Mulungu alipo. Koma kumatanthauzanso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, wofanana ndi umene mwana wamng’ono amakhala nawo ndi bambo ake okoma mtima amene amamukonda. Solomo anauziridwa kulemba kuti: “Mwananga, mtima wako ukakhala wanzeru, mtima wanga wa inedi udzakondwa; impso zanga zidzasangalala, polankhula milomo yako zoongoka.” (Miy. 23:15, 16) Nafenso tikamasonyeza kuti timatsatira mfundo zolungama molimba mtima, Yehova amasangalala ndipo kudziwa zimenezi kumatithandiza kukhala olimba mtima kwambiri. Choncho, tiyeni nthawi zonse tizitsanzira Yesu ndipo tizikhala olimba mtima potsatira chilungamo.

[Mawu a M’munsi]

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe omvera ngakhale kuti ndife opanda ungwiro?

• Kodi chikhulupiriro chenicheni maziko ake n’chiyani, ndipo kodi zimenezi zingatithandize bwanji kukhala olimba mtima?

• Tikakhala omvera n’kumasonyeza kulimba mtima ngati Khristu, kodi zotsatira zake zimakhala zotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 13]

Kodi ‘mukukonza mtima wanu’ kuti muthe kulimbana ndi mayesero?

[Chithunzi patsamba 15]

Mofanana ndi Yesu, tingasonyeze kulimba mtima chifukwa cha chikhulupiriro