Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Chipembedzochi Ndi Changa Kapena cha Makolo Anga?

Kodi Chipembedzochi Ndi Changa Kapena cha Makolo Anga?

Kodi Chipembedzochi Ndi Changa Kapena cha Makolo Anga?

KU Poland, anthu ambiri amauza Mboni za Yehova kuti: “Ndinabadwira mu chipembedzo chimenechi, ndipo ndidzafera momwemu.” Kwa iwo, chipembedzo ndi chinthu chimene makolo amasiyira ana awo. Kodi umu ndi mmenenso zilili ndi anthu a m’dera lanu? Kodi zotsatira za maganizo amenewa zimakhala zotani? Zotsatira zake zimakhala zakuti munthu amangopembedza mwamwambo ndiponso chifukwa chakuti ndi zimene akhala akuchita pabanja pawo kwa zaka zambiri. Kodi zimenezi zingachitikenso pakati pa ana a Mboni za Yehova amene anaphunzitsidwa choonadi chamtengo wapatali ndi makolo kapena agogo awo?

Izi si zimene zinachitikira Timoteyo, amene amayi ndiponso agogo ake okonda Mulungu, anamuthandiza kukhulupirira ndi kukonda Mulungu woona. Timoteyo anadziwa malemba opatulika ‘kuyambira pamene anali wakhanda.’ M’kupita kwa nthawi, Timoteyo, pamodzi ndi amayi ndiponso agogo ake, anakhutira kuti Chikhristu ndi choona. Iye ‘anakhulupirira atakhutira’ ndi zinthu zimene anamva kuchokera m’Malemba zokhudza Yesu Khristu. (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) Choncho, ngakhale kuti makolo achikhristu masiku ano amayesetsa kuthandiza ana awo kukhala atumiki a Yehova, anawo paokha ayenera kukhala ndi mtima wofuna kutumikira Yehova.​—Maliko 8:34.

Motero, kuti munthu atumikire Yehova chifukwa chomukonda ndiponso kuti asunge umphumphu zivute zitani, afunika kukhutira ndi zimene amakhulupirira. Koma kuti akhutire, ayenera kupatsidwa zifukwa zomveka. Zikatere, chikhulupiriro chake chimakhala cholimba ndiponso chozika mizu.​—Aef. 3:17; Akol. 2:6, 7.

Udindo wa Ana

Albert, * yemwe anakulira m’banja la Mboni, anati: “Ndakhala ndikukhulupirira kuti chipembedzo cha Mboni za Yehova ndi choona. Koma zinkandivuta kuvomereza zimene chipembedzochi chinkanena kuti ndiyenera kuchita.” Ngati ndinu wachinyamata, mwina inunso mumaganiza choncho. Ndiye bwanji osachita khama kuti mudziwe ubwino wa zimene Mulungu amafuna kuti tizichita pa moyo wathu? Kuchita zimenezi kudzakuthandizani kuti muzisangalala pochita chifuniro chake. (Sal. 40:8) Albert anati: “Ndinayamba kumapemphera ngakhale kuti poyamba zinali zovuta moti ndinkangodzikakamiza. Koma pasanapite nthawi, ndinayamba kuona kuti ndikhoza kukhala munthu wofunika kwambiri kwa Mulungu ngati nditamayesetsa kuchita zabwino. Zimenezi zinandipatsa mphamvu kuti ndisinthe moyo wanga.” Ngati inunso mutayesetsa kukhala pa ubwenzi ndi Yehova, mungakhale ndi mtima wofuna kuchita zimene iye amafuna.​—Sal. 25:14; Yak. 4:8.

Kodi pali masewera amene mumawakonda kwambiri? Mwina mumakonda bawo kapena masewera ena. Mukanakhala kuti simudziwa malamulo ake kapena simutha kusewera bwino, si bwenzi mukuwakonda. Koma chifukwa chodziwa malamulo ake ndiponso chifukwa chakuti mumasewera bwino, mumachita kulakalaka kuti mupeze mpata woti musewere. Ndi mmenenso zimakhalira ndi zinthu zauzimu. Choncho, muziyesetsa kukonzekera misonkhano yachikhristu ndipo muzitenga nawo mbali. Mukamatero, muzilimbikitsa ena ndi chitsanzo chanu ngakhale kuti ndinu mwana.​—Aheb. 10:24, 25.

N’chimodzimodzinso ndi kuuza ena zimene mumakhulupirira. Muyenera kuchita zimenezi chifukwa cha chikondi, osati chifukwa chokakamizidwa. Dzifunseni kuti: ‘Kodi n’chifukwa chiyani ndiyenera kuuza ena za Yehova? Kodi ndimamukonda Yehova chifukwa chiyani?’ Mufunika kumudziwa Yehova monga Atate wachikondi. Kudzera mwa Yeremiya, iye anati: “Mudzandifuna Ine, ndi kundipeza, pamene mundifuna ndi mtima wanu wonse.” (Yer. 29:13, 14) Kodi zimenezi zingafune kuti mutani? Jakub anati: “Ndinafunika kusintha kaganizidwe kanga. Kuyambira ndili mwana, ndinkapita kumisonkhano ndiponso ndinkalalikira, koma kenako ndiyamba kungochita zimenezi mwamwambo. Koma nditamudziwa bwino Yehova ndi kuyamba kukhala naye pa ubwenzi wolimba, m’pamene ndinayamba kuchikonda kwambiri choonadi.”

Kukhala ndi mabwenzi abwino ndiponso olimbikitsa, kungakuthandizeninso kuti muzisangalala ndi utumiki. Mwambi wa m’Baibulo umati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru.” (Miy. 13:20) Choncho, mukamasankha mabwenzi, muziyang’ana anthu amene ali ndi zolinga zauzimu ndiponso amene kutumikira Yehova kumawasangalatsa. Jola anati: “Kucheza ndi achinyamata ambiri okonda zinthu zauzimu kunandilimbikitsa, moti ndinayamba kusangalala kulowa nawo mu utumiki nthawi zonse.”

Udindo wa Makolo

Jola anati: “Ndikuthokoza kwambiri makolo anga chifukwa chondiphunzitsa za Yehova.” Makolo amathandizadi kwambiri kuti ana awo asankhe zinthu mwanzeru. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Inunso atate, . . . muwalere [ana anu] m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.” (Aef. 6:4) Malangizo ouziridwa amenewa akusonyeza kuti makolo ali ndi udindo wophunzitsa ana awo njira za Yehova, osati zawo ayi. M’malo moika m’maganizo mwa ana anu zimene inuyo mukufuna, mungachite bwino kwambiri kuwathandiza kuti zolinga zawo zikhale zogwirizana ndi zolinga za Yehova.

Mungathe kuphunzitsa ana anu mwachangu mawu a Yehova “pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” (Deut. 6:6, 7) Ewa ndi Ryszard ali ndi ana aamuna atatu. Iwo anati: “Tinkakambirana kwambiri za mitundu yosiyanasiyana ya utumiki wa nthawi zonse.” Kodi zotsatira zake zinali zotani? “Anyamatawa anaganiza zolembetsa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu adakali aang’ono, anakhala ofalitsa ndipo kenako anasankha okha kubatizidwa. Pambuyo pake, onse anayamba utumiki wa nthawi zonse.”

Makolo afunikanso kupereka chitsanzo chabwino. Ryszard anati: “Tinkapeweratu moyo wachiphamaso, wochita zina kumpingo koma n’kusintha tikakhala kunyumba.” Ndiye inu makolo dzifunseni kuti: ‘Kodi ana anga amaona zotani pa moyo wanga? Kodi amaona kuti ndimakondadi Yehova? Kodi mapemphero anga ndi pulogalamu yanga ya phunziro laumwini, zimawasonyeza anawo kuti ndimakonda Yehova? Kodi maganizo anga pa nkhani ya utumiki wakumunda, zosangalatsa ndiponso zinthu zakuthupi, amawasonyeza kuti ndimakondadi Yehova? Nanga bwanji zimene ndimalankhula zokhudza abale mumpingo?’ (Luka 6:40) Ana amaona zimene mumachita pa moyo wanu ndipo amazindikira ngati zochita zanu zimasemphana ndi zimene mumalankhula.

Kuti ana akule bwino, amafunikanso kuwalangiza. Mawu a Mulungu amatiuza kuti ‘phunzitsa mwana poyamba njira yake.’ (Miy. 22:6) Ewa ndi Ryszard anati: “Tinkaphunzira Baibulo ndi mwana aliyense payekha.” Izi n’zimene banjali linasankha, koma zili kwa makolo kuona ngati m’pofunika kuti aziphunzira ndi mwana aliyense payekha. Koma chachikulu n’chakuti mwana aliyense amafunika kumuona kuti ndi wosiyana ndi anzake, choncho amafunika kumuthandiza m’njira yomuyenera. Izi zimafuna kuti makolo akhale ndi mtima wololera kusintha mmene amachitira zinthu. Mwachitsanzo, m’malo mongowauza ana anu kuti nyimbo zakutizakuti si zabwino, muyenera kuwathandiza kusankha bwino ndiponso kuona mfundo za m’Baibulo zokhudza nyimbozo.

Ana anu angadziwe zimene inu mukufuna ndipo akhoza kungochita zimenezo n’cholinga choti zigwirizane ndi zofuna zanuzo. Koma inu muyenera kuwafika pamtima. Musaiwale kuti, “uphungu wa m’mtima mwa munthu ndiwo madzi akuya; koma munthu wozindikira adzatungapo.” (Miy. 20:5) Choncho, muyenera kukhala ozindikira kuti muone ngati ana anu ali ndi maganizo olakwika mumtima mwawo, n’kuwathandiza mwamsanga. Popanda kuwaimba mlandu, asonyezeni kuti mukufuna kuwathandiza ndipo afunseni mafunso oyenerera. Komabe onetsetsani kuti simukuwapanikiza ndi mafunso ambirimbiri. Mukamasonyeza kuti mumadera nkhawa ana anu, mudzatha kuwafika pamtima ndiponso kuwathandiza.

Udindo wa Mpingo

Monga mtumiki wa Mulungu, kodi mungathandize achinyamata mumpingo kuti aziyamikira choonadi chimene aphunzitsidwa ndi makolo awo? Ngakhale kuti makolo ndi amene ali ndi udindo wophunzitsa ana awo, anthu ena mumpingo, makamaka akulu, angathandize makolo pa nkhaniyi. Izi n’zofunika kwambiri makamaka kwa ana amene kholo lawo lina si Mboni.

Kodi akulu angatani kuti athandize ana kukonda Yehova, kuona kuti amawerengeredwa ndiponso kuti ndi ofunika mumpingo? Mariusz ndi mkulu mumpingo wa ku Poland. Iye anati: “Akulu ayenera kulankhulana, kukambirana ndiponso kucheza ndi ana. Zimenezi siziyenera kuchitika kokha pakakhala vuto linalake, koma zizichitikanso pa nthawi zina monga mu utumiki, misonkhano ikatha kapena pocheza nawo.” Mwina mungafunse anawo kuti anene zimene zimawasangalatsa mumpingo. Kukambirana momasuka nkhani zoterezi ndi ana kungawathandize kukonda kwambiri mpingo ndiponso kuona kuti iwo ndi ofunika kwambiri mumpingomo.

Ngati ndinu mkulu, kodi mukuyesetsa kuwadziwa bwino achinyamata a mumpingo wanu? Ngakhale kuti panopa ndi mkulu, Albert, amene tinamutchula poyamba uja, anakumana ndi mayesero ambiri pa unyamata wake. Iye anati: “Ndili wachinyamata, ndinkafunikira ulendo wa ubusa.” Komanso akulu angasonyeze kuti ali ndi chidwi ndi achinyamata mwa kuwapempherera kuti akhale olimba mwauzimu.​—2 Tim. 1:3.

Ndi bwino kuti achinyamata azichita nawo zinthu mumpingo. Chifukwa kupanda kutero, angayambe kumaika maganizo awo onse pa zolinga zakudziko. Kodi mungamapite nawo mu utumiki ndiponso kuyesetsa kukhala mabwenzi awo. Mukamacheza ndi achinyamata, iwo adzayamba kukukhulupirirani komanso adzakhala mabwenzi anu. Jola anati: “Mlongo wina, yemwe ndi mpainiya, ankandisonyeza chidwi. Ndipo ulendo woyamba umene ndinapita mu utumiki mochita kufuna ndekha, ndinapita ndi iyeyo.”

Sankhani Nokha

Inu achinyamata, dzifunseni kuti: ‘Kodi zolinga zanga ndi zotani? Ngati sindinabatizidwe, kodi ndili ndi cholinga chodzabatizidwa?’ Mukasankha kubatizidwa, chikhale chifukwa chakuti mumakonda Yehova ndi mtima wonse, osati chifukwa chofuna kutsatira mwambo wa banja lanu.

Inde, Yehova akhale Bwenzi lanu lapamtima, ndipo muzikonda kwambiri choonadi. Kudzera mwa mneneri Yesaya, Yehova anati: “Usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako.” Yehova sadzakusiyani malinga ngati muli bwenzi lake. Inde, iye adzakulimbitsani ndipo ‘adzakuchirikizani ndi dzanja lake lamanja la chilungamo.’​—Yes. 41:10.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 6 Tasintha mayina ena.

[Chithunzi patsamba 4]

Muziyesetsa kuona zimene zili mumtima wa mwana wanu

[Chithunzi patsamba 6]

Munthu amasankha kubatizidwa chifukwa chakuti amakonda Yehova ndi mtima wonse