Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumayamikira Zimene Yehova Wachita Kuti Akupulumutseni?

Kodi Mumayamikira Zimene Yehova Wachita Kuti Akupulumutseni?

Kodi Mumayamikira Zimene Yehova Wachita Kuti Akupulumutseni?

“Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli, chifukwa wacheukira anthu ake ndi kuwapatsa chipulumutso.”​—LUKA 1:68.

1, 2. Kodi kukula kwa mavuto amene tili nawo tingakuyerekezere ndi chiyani, nanga tikambirana mafunso ati?

TAYEREKEZERANI kuti mwagonekedwa m’chipatala. Ndipo matenda amene mukudwala ndi oti aliyense m’chipindamo akudwalanso omwewo. Ndi akupha ndipo mankhwala ake sanapezeke. Kenako mwamva kuti dokotala wina akuyesetsa kuti apeze mankhwala ake ndipo izi zikukupatsani chiyembekezo. Mukufunitsitsa mutamva chilichonse chokhudza nkhaniyi. Ndiyeno tsiku lina mukumva kuti mankhwala aja apezeka. Dokotala amene watulukira mankhwalawo anadzimana kwambiri kuti zimenezi zitheke. Kodi inuyo mungamve bwanji? N’zosachita kufunsa kuti mungagome naye ndiponso kumuyamikira kwambiri munthu amene wayesetsa kuti inuyo limodzi ndi odwala enawo musafe.

2 Mwina mungaganize kuti nkhani imeneyi ndi yongoyerekezera, koma ndi mmene zinthu zilili ndi tonsefe. Munthu aliyense ali ndi vuto lalikulu kwambiri kuposa limene tafotokozali. Tikufunika kwambiri kuti wina atipulumutse. (Werengani Aroma 7:24.) Kuti atipulumutse, Yehova anadzimana kwambiri. Mwana wakenso anadzimana kwambiri. Tsopano tiyeni tikambirane mafunso anayi. N’chifukwa chiyani tikufunika kupulumutsidwa? Kodi Yesu anadzimana chiyani kuti tipulumutsidwe? Nanga kodi Yehova anadzimana chiyani? Kodi ifeyo tingasonyeze bwanji kuti timayamikira zimene Mulungu wachita kuti atipulumutse?

N’chifukwa Chiyani Tikufunika Kupulumutsidwa?

3. Kodi uchimo ukufanana bwanji ndi mliri?

3 Kafukufuku akusonyeza kuti fuluwenza ya ku Spain, yomwe inayamba mu 1918, ndi umodzi mwa miliri yoopsa kwambiri imene inachitika ndipo inapha anthu mamiliyoni ambiri. Pali matenda ena omwe tingati ndi akupha kwambiri kuposa pamenepa. Akhoza kugwira anthu ochepa, koma pa anthu ochepa amene adwalawo ambiri amafa nawo. * Ndiyeno n’chifukwa chiyani tinganene kuti uchimo ndi woopsa kwambiri kuposa mliri ngati umenewu? Kumbukirani mawu a pa Aroma 5:12 akuti: ‘Uchimo unalowa m’dziko kudzera mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo, imfayo nifalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa.’ Uchimo ndi mliri umene wagwira munthu aliyense chifukwa anthu onse opanda ungwiro amachimwa. (Werengani Aroma 3:23.) Kodi ndi anthu ochuluka bwanji amene amafa chifukwa cha uchimo? Paulo analemba kuti uchimo umapha “anthu onse.”

4. Kodi Yehova amaona bwanji nthawi imene anthufe timakhala ndi moyo, ndipo kodi zimenezi zimasiyana bwanji ndi mmene anthu ambiri masiku ano amaonera nkhaniyi?

4 Anthu ambiri masiku ano akaganizira za uchimo ndi imfa, amangoona kuti ndi mmene moyo wakhalira basi. Iwo amaopa kwambiri imfa yomwe amati ndi yamwamsanga, koma imfa imene imabwera chifukwa cha ukalamba amangoti ndi “yachilengedwe.” N’zosavuta kuti anthu aiwale kuona zinthu mmene Mlengi amaonera. Moyo wathuwu ndi waufupi kwambiri poyerekezera ndi mmene Mlengiyo anafunira. Ndipo zoona zake ndi zakuti malinga ndi mmene Yehova amaonera zinthu, tonsefe timafa tisanakwanitse ndi “tsiku limodzi” lomwe. (2 Pet. 3:8) Mawu a Mulungu amanena kuti moyo wathu ndi waufupi kwambiri ndipo uli ngati udzu kapena mpweya wotuluka tikamapuma. (Sal. 144:4; 1 Pet. 1:24) N’chifukwa chiyani tiyenera kukumbukira zimenezi? Chifukwa chakuti tikamvetsa kuopsa kwa uchimo, womwe ndi matenda amene tikudwala, m’pamene timayamikira kwambiri mankhwala ake. Ndipo mankhwala akewo ndi zimene Mulungu wachita kuti atipulumutse.

5. Kodi uchimo watiwonongera chiyani?

5 Kuti tidziwe kuopsa kwa uchimo ndi zotsatira zake, tiyenera kuyesetsa kumvetsa zimene uchimowo unatiwonongera. Koma poyamba, kuchita zimenezi kungakhale kovuta chifukwa chakuti zinthu zimene uchimo unatiwonongera, ndi zoti sitinakhalepo nazo. Pachiyambi, Adamu ndi Hava ankasangalala ndi moyo wangwiro. Popeza anali ndi maganizo ndiponso matupi angwiro, iwo akanatha kulamulira bwinobwino mtima, zoganiza ndi zochita zawo. Motero, iwo anali ndi mwayi wokhala atumiki a Yehova Mulungu abwino, ndipo palibe chimene chikanawalepheretsa kuchita zimenezi. Koma iwo anataya mphatso imeneyi. Anasankha kuchimwira Yehova, ndipo iwo limodzi ndi mbadwa zawo anataya moyo umene Yehova ankafuna kuti iwo akhale nawo. (Gen. 3:16-19) Chifukwa cha zimenezi anatipatsira matenda oopsa kwambiri amene tafotokoza aja. M’pake kuti Yehova anawaweruza kuti ayenera kufa. Komabe ifeyo watipatsa chiyembekezo cha chipulumutso.​—Sal. 103:10.

Yesu Anadzimana Kwambiri Kuti Atipulumutse

6, 7. (a) Kodi Yehova anasonyeza bwanji kalelo, kuti padzafunika kudzimana kwambiri kuti anthu apulumutsidwe? (b) Kodi nsembe zimene Abele, ndiponso makolo amene anakhalako Chilamulo chisanaperekedwe, anapereka, zimatiphunzitsa chiyani?

6 Yehova ankadziwa kuti panafunika kudzimana kwambiri kuti apulumutse mbadwa za Adamu ndi Hava. Ulosi wa pa Genesis 3:15, umasonyeza zimene zinafunika kuti tipulumutsidwe. Unati Yehova adzapereka “mbewu,” yomwe ndi mpulumutsi amene adzawononge kotheratu Satana. Komabe, mpulumutsi ameneyu anali woti adzavutika ndipo mophiphiritsa adzalaliridwa chitende. Zimenezi zikumveka zopweteka ndiponso zosautsa kwambiri. Ngakhale zili choncho, kodi zikutanthauza chiyani? Kodi Wosankhidwa wa Yehova anafunika kupirira zinthu ziti?

7 Kuti apulumutse anthu ku uchimo, mpulumutsiyu anayenera kutsegula njira yotetezera anthu n’kuwayanjanitsa ndi Mulungu mwa kuchotsa zotsatira za uchimo. Kodi zimenezi zinaphatikizapo chiyani? Kuyambira kale, panali zizindikiro zosonyeza kuti padzafunika nsembe. Yehova anasangalala pamene Abele, yemwe anali munthu woyamba wokhulupirika, anapereka nsembe ya nyama. Kenako makolo oopa Mulungu monga Nowa, Abulahamu, Yakobo ndi Yobu anaperekanso nsembe za nyama zimene zinasangalatsa Mulungu. (Gen. 4:4; 8:20, 21; 22:13; 31:54; Yobu 1:5) Zaka zambiri pambuyo pake, Chilamulo cha Mose chinathandiza anthu kumvetsa nkhani ya nsembe.

8. Kodi mkulu wa ansembe ankachita chiyani chaka ndi chaka pa Tsiku la Chitetezo?

8 Zina mwa nsembe zofunika kwambiri m’Chilamulo, zinkaperekedwa pa Tsiku la Chitetezo. Pa tsiku limeneli, mkulu wa ansembe ankachita zinthu zingapo zophiphiritsa. Choyamba, ankapereka kwa Yehova nsembe zotetezera machimo a fuko la ansembe, ndipo kenako ankaperekanso nsembe zotetezera machimo a mafuko ena. Mkulu wa ansembe ankalowa Malo Opatulikitsa a chihema chokumanako kapena kachisi. Iye yekha ndi amene anali woyenera kulowa mmenemo ndipo ankalowamo kamodzi pachaka, pa tsiku lokhali. Ali mmenemo, ankawaza magazi a nsembe patsogolo pa likasa la chipangano. Pamwamba pa likasalo nthawi zina pankaoneka mtambo wowala, ndipo unkaimira kukhalapo kwa Yehova Mulungu.​—Eks. 25:22; Lev. 16:1-30.

9. (a) Pa Tsiku la Chitetezo, kodi mkulu wa ansembe ankaimira ndani, ndipo kodi nsembe zimene ankapereka zinkaimira chiyani? (b) Pamene mkulu wa ansembe analowa Malo Opatulikitsa, zinaimira chiyani?

9 Mtumwi Paulo anauziridwa kufotokoza tanthauzo la zinthu zophiphiritsa zimenezi. Iye anasonyeza kuti mkulu wa ansembe anaimira Mesiya, Yesu Khristu, pamene nsembe zinaimira imfa ya nsembe ya Khristu. (Aheb. 9:11-14) Nsembe yangwiro imeneyo, imatetezadi machimo a anthu a magulu awiri. Gulu loyamba ndi la ansembe, amene ndi abale a Khristu odzozedwa ndi mzimu okwanira 144,000, ndipo lina ndi la “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Pamene mkulu wa ansembe analowa Malo Opatulikitsa, zinaimira zimene Yesu anachita pamene analowa kumwamba kwenikweniko kukapereka kwa Yehova Mulungu mtengo wa nsembe ya dipo.​—Aheb. 9:24, 25.

10. Kodi ulosi wa m’Baibulo unasonyeza kuti Mesiya adzakumana ndi zotani?

10 Apa n’zoonekeratu kuti ntchito yopulumutsa mbadwa za Adamu ndi Hava inafunika kudzimana kwambiri. Mesiya anafunika kupereka moyo wake nsembe. Aneneri amene analemba Malemba Achiheberi anafotokoza mfundoyi mwatsatanetsatane. Mwachitsanzo, mneneri Danieli ananena kuti “wodzozedwayo, ndiye kalonga,” kapena kuti Mesiya Mtsogoleri, “adzalikhidwa” kuti ‘ateteze mphulupulu.’ (Dan. 9:24-26) Yesaya analosera kuti Mesiya adzakanidwa, kuzunzidwa ndi kuphedwa, kapena kuti kulasidwa, n’cholinga chakuti asenze machimo a anthu opanda ungwiro.​—Yes. 53:4, 5, 7.

11. Kodi Mwana wa Yehova anasonyeza bwanji kuti anali wokonzeka kudzipereka nsembe kuti atipulumutse?

11 Asanabwere padziko lapansi, Mwana wobadwa yekha wa Mulungu ankadziwa kuti adzafunika kudzimana kwambiri kuti atipulumutse. Iye anali woti adzavutika kwambiri ndipo kenako kuphedwa. Kodi Atate wake atamuphunzitsa mfundo zimenezi, iye anabwerera m’mbuyo kapena kupanduka? Ayi. Iye anagonjera Atate wake ndi mtima wonse ndipo anamvera zonse zimene anaphunzitsidwa. (Yes. 50:4-6) Atabwera padziko lapansi, Yesu anamveranso ndi kuchita chifuniro cha Atate wake. Chifukwa chiyani anatero? Mwini wakeyu anapereka yankho ili: “Ndimakonda Atate.” Ndipo anatinso: “Palibe amene ali ndi chikondi choposa ichi, chakuti wina n’kupereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.” (Yoh. 14:31; 15:13) Choncho, chipulumutso chathu chikutheka makamaka chifukwa cha chikondi cha Mwana wa Yehova. Ngakhale kuti anafunika kutaya moyo wake wangwiro, Yesu analolera kuchita zimenezo kuti ife tipulumuke.

Yehova Anadzimana Kwambiri Kuti Atipulumutse

12. Kodi dipo ndi chifuniro cha ndani, ndipo n’chifukwa chiyani analikonza?

12 Yesu sindiye anakonza nsembe ya dipo. Njira yopulumutsira anthu imeneyi, inali mbali yaikulu ya chifuniro cha Yehova. Mtumwi Paulo anasonyeza kuti guwa la nsembe limene linali kukachisi, linkaimira chifuniro cha Yehova. (Aheb. 10:10) Choncho chipulumutso chimene timalandira kudzera mu nsembe ya Khristu, kwenikweni chimachokera kwa Yehova. (Luka 1:68) Ndi njira imene iye amasonyezera chifuniro chake changwiro ndiponso chikondi chake chachikulu kwa anthu.​—Werengani Yohane 3:16.

13, 14. Kodi chitsanzo cha Abulahamu chingatithandize bwanji kumvetsa ndiponso kuyamikira zimene Yehova watichitira?

13 Kodi Yehova anafunika kudzimana chiyani kuti atisonyeze chikondi m’njira imeneyi? N’zovuta kumvetsa. Komabe m’Baibulo muli nkhani imene ingatithandize kumvetsako bwino zimenezi. Yehova anauza munthu wokhulupirika Abulahamu kuti achite chinthu chovuta kwambiri. Anamuuza kuti apereke nsembe mwana wake Isake. Abulahamu anali bambo wachikondi kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti pomuuza Abulahamu za Isake, Yehova anati “mwana wako, wamwamuna wayekhayo . . . amene ukondana naye.” (Gen. 22:2) Ngakhale zinali choncho, Abulahamu anaona kuti kuchita chifuniro cha Yehova kunali kofunika kwambiri kuposa chikondi chake kwa Isake. Abulahamu anamvera ndipo anali wokonzeka kuchita zimene anauzidwazo. Komabe, Yehova sanalole kuti Abulahamu achite zimene Iye anali kudzachita m’tsogolo. Abulahamu atangotsala pang’ono kupereka nsembe mwana wake, Mulungu anatumiza mngelo kuti akamuletse. Abulahamu anali atatsimikiza kumvera Mulungu wake pa mayeso amenewa moti anakhulupiriradi kuti mwana wakeyo angadzamuonenso ngati Mulungu atamuukitsa. Koma anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Mulungu adzamuukitsadi. Pa nkhaniyi, Paulo ananena kuti Abulahamu analandira Isake kuchokera kwa akufa ‘m’njira ya fanizo.’​—Aheb. 11:19.

14 N’zovuta kumvetsa ululu umene Abulahamu ankamva mumtima mwake pamene ankakonzekera kupereka nsembe mwana wake. Tingati zimene Abulahamu anachita zimatithandiza kudziwa mmene Yehova anamvera popereka amene anamutcha kuti “Mwana wanga wokondedwa.” (Mat. 3:17) Koma dziwani kuti Yehova ayenera kuti anamva ululu woposa pamenepa. Iye ndi Mwana wake anakhala limodzi kwa zaka mamiliyoni kapenanso mabiliyoni osawerengeka. Mwana ameneyu ankagwira ntchito mosangalala limodzi ndi Atate wake monga “mmisiri” wokondedwa ndiponso monga “Mawu” kapena kuti Wom’lankhulira. (Miy. 8:22, 30, 31; Yoh. 1:1) Sitingamvetse ululu wonse umene Yehova anamva pamene Mwana wake ankazunzidwa, kunyozedwa ndipo kenako kuphedwa ngati chigawenga. Yehova anadzimanatu kwambiri kuti atipulumutse. Ndiyeno kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira chipulumutso chathu?

Sonyezani Kuti Mumayamikira Chipulumutso Chanu

15. Kodi Yesu anatsiriza bwanji ntchito yoteteza anthu, ndipo kodi zimenezi zinabweretsa madalitso otani?

15 Yesu anatsiriza ntchito yoteteza anthu pamene anaukitsidwa n’kupita kumwamba. Atafika kwa Atate wake wokondedwa, iye anapereka kwa Atate wakewo mtengo wa nsembe yake. Zimenezi zinabweretsa madalitso aakulu. Tsopano zinali zotheka kukhululukira machimo a abale odzozedwa a Khristu komanso a “dziko lonse.” Chifukwa cha nsembe imeneyi, anthu onse amene amalapadi machimo awo n’kukhala otsatira enieni a Khristu, amakhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova Mulungu. (1 Yoh. 2:2) Kodi zimenezi zikukukhudzani bwanji?

16. Perekani chitsanzo chosonyeza chifukwa chake tiyenera kuyamikira zimene Yehova wachita kuti atipulumutse.

16 Tiyeni tionenso chitsanzo chimene takambirana poyamba chija. Tiyerekeze kuti dokotala amene watulukira mankhwala uja wabwera m’chipinda chomwe inu muli ndipo akunena kuti, wodwala aliyense amene angalandire mankhwalawo ndi kutsatira malangizo onse achira. Mungamve bwanji ngati odwala ambiri akukana kutsatira zimene dokotalayo akunena, n’kumanena kuti kumwa mankhwalawo ndi chintchito ndipo ndi zovuta kutsatira malangizo amene waperekawo? Kodi mungagwirizane nawo ngati inuyo mukuona kuti mankhwalawo n’ngothandizadi? Ayi simungatero. Mosakayikira mungayamikire dokotalayo chifukwa cha mankhwalawo, mungatsatire bwinobwino malangizo akewo, ndipo mwina mungauze ena zimene mwasankhazo. Mofanana ndi zimenezi, aliyense wa ife ayenera kukhala wofunitsitsa kumusonyeza Yehova kuti amayamikira kwambiri chipulumutso chimene Yehovayo wapereka kudzera mu nsembe ya dipo ya Mwana wake.​—Werengani Aroma 6:17, 18.

17. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumayamikira zimene Yehova wachita kuti akupulumutseni?

17 Ngati timayamikira zimene Yehova ndi Mwana wake achita kuti atipulumutse, zochita zathu zidzasonyeza zimenezi. (1 Yoh. 5:3) Tidzamenya nkhondo yolimbana ndi chibadwa chathu chofuna kuchimwa. Sitidzalola kukhala ndi chizolowezi chochimwira dala n’kumakhala ndi moyo wachiphamaso. Kuchita zimenezi kungasonyeze kuti sitiyamikira m’pang’ono pomwe dipo. M’malomwake tiyenera kusonyeza kuyamikira mwa kuyesetsa kukhala anthu oyera pamaso pa Mulungu. (2 Pet. 3:14) Tidzachita zimenezi mwa kuuza ena chiyembekezo chathu cha chipulumutso n’cholinga choti nawonso akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova n’kukhalanso ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. (1 Tim. 4:16) Zoonadi, m’pake kuti tiyenera kugwiritsa ntchito nthawi ndi mphamvu zathu zonse potamanda Yehova ndi Mwana wake. (Maliko 12:28-30) Tangoganizani, tikuyembekezera nthawi imene tidzachiriratu ku uchimo. Tikhoza kukhala ndi moyo wangwiro kosatha ngati mmene Mulungu anafunira. Ndipo zonsezi zidzatheka chifukwa cha zimene Yehova wachita kuti atipulumutse.​—Aroma 8:21.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Akuti fuluwenza ya ku Spain inagwira pafupifupi theka la anthu onse amene anali padzikoli pa nthawiyo. Matendawa ayenera kuti anapha pafupifupi 10 peresenti ya anthu amene anadwala. Mosiyana ndi fuluwenzayi, mliri wa Ebola sugwaigwa, koma pamene unagwa unapha pafupifupi 90 peresenti ya anthu amene anadwala.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani mufunika kupulumutsidwa mwamsanga?

• Kodi mukumva bwanji ndi kudzimana kumene Yesu anachita?

• Kodi mumamva bwanji ndi mphatso ya dipo imene Yehova anapereka?

• Kodi ndinu wokonzeka kuchita chiyani chifukwa cha zimene Yehova wachita kuti akupulumutseni?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 27]

Pa Tsiku la Chitetezo, mkulu wa ansembe ku Isiraeli ankaimira Mesiya

[Chithunzi patsamba 28]

Abulahamu anali wokonzeka kupereka mwana wake nsembe ndipo izi zimatiphunzitsa kuti Yehova anadzimana kwambiri