Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Maphunziro Ochokera kwa Mulungu Ndi Opambanadi

Maphunziro Ochokera kwa Mulungu Ndi Opambanadi

Maphunziro Ochokera kwa Mulungu Ndi Opambanadi

“Ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa cha kudziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, kumene ndi kwa mtengo wopambanadi.”​—AFIL. 3:8.

1, 2. Kodi Akhristu ena asankha kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani asankha zimenezo?

KUYAMBIRA ali mwana, Robert ankakhoza bwino kusukulu. Ali ndi zaka 8, mphunzitsi wake anapita kunyumba kwawo ndipo anamuuza kuti akhoza kukwanitsa kuchita chilichonse pa moyo wake. Anamuuzanso kuti akukhulupirira kuti adzakhala dokotala. Robert anakhoza bwino mayeso akusekondale ndipo akanatha kupita kuyunivesite yapamwamba iliyonse m’dzikolo. Koma iye anasankha kusiya zimene ambiri ankaona ngati mwayi wosafunika kuuphonya, n’cholinga choti azichita upainiya wokhazikika.

2 Mofanana ndi Robert, Akhristu ambiri, aakulu ndi achinyamata omwe, ali ndi mwayi woti akhoza kuchita zambiri m’dongosolo lino. Koma ena amasankha kuti asagwiritse ntchito mokwanira mwayi umenewo n’cholinga choti akwaniritse zolinga zauzimu. (1 Akor. 7:29-31) Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu ngati Robert amaika maganizo awo onse pa ntchito yolalikira? Chifukwa chachikulu n’chakuti iwo amakonda Yehova. Chinanso n’chakuti iwo amazindikira kuti maphunziro ochokera kwa Mulungu ndi opambanadi. Kodi posachedwapa mwaganizirapo mmene moyo wanu ukanakhalira mukanakhala kuti simunaphunzire choonadi? Kuganizira madalitso amene tapeza chifukwa chophunzitsidwa ndi Yehova, kungatithandize kuti tizionabe kufunika kwa uthenga wabwino ndiponso kuti tiziuza ena uthengawo mwachangu.

Ndi Mwayi Waukulu Kuphunzitsidwa ndi Mulungu

3. N’chifukwa chiyani tikutsimikiza kuti Yehova amalakalaka kuphunzitsa anthu opanda ungwiro?

3 Chifukwa chakuti Yehova ndi wabwino, amalakalaka kuphunzitsa anthu opanda ungwiro. Polosera za Akhristu odzozedwa, lemba la Yesaya 54:13 limati: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa “nkhosa zina” za Khristu. (Yoh. 10:16) Zimenezi zikuoneka bwino mu ulosi umene ukukwaniritsidwa masiku ano. Yesaya anaona m’masomphenya anthu a mitundu yonse akukhamukira ku kulambira koona. Iye anafotokoza kuti anthuwo akuuzana kuti: “Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.” (Yes. 2:1-3) Ndi mwayi waukuludi kuphunzitsidwa ndi Mulungu.

4. Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene amawaphunzitsa akhale otani?

4 Kodi chofunika ndi chiyani kuti tipindule ndi maphunziro ochokera kwa Mulungu? Chofunika kwambiri ndi kukhala munthu wofatsa ndi wophunzitsika. Wamasalmo Davide analemba kuti: “Yehova ndiye wabwino ndi wolunjika mtima. . . . Adzaphunzitsa ofatsa njira yake.” (Sal. 25:8, 9) Ndipo Yesu ananena kuti: “Atate ndikutamandani pamaso pa onse, inu Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa zinthu izi mwazibisa kwa anzeru ndi ozama m’maphunziro, koma mwaziulula kwa tiana.” (Luka 10:21) Kodi zimenezi sizikukuchititsani kukonda kwambiri Mulungu amene ‘amasonyeza kukoma mtima kwa m’chisomo chake kwa odzichepetsa’?​—1 Pet. 5:5.

5. Kodi zatheka bwanji kuti tidziwe Mulungu?

5 Monga atumiki a Yehova, kodi tinganene kuti tadziwa choonadi chifukwa cha nzeru kapena luso lathu? Ayi. Zoona zake n’zakuti, patokha sitikanatha kudziwa Mulungu. Yesu anati: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” (Yoh. 6:44) Kudzera mwa ntchito yolalikira ndiponso mzimu woyera, Yehova akukoka anthu onga nkhosa, ndipo anthu amenewa ndi “zofunika za amitundu onse.” (Hag. 2:7) Kodi inuyo simukuyamikira kukhala m’gulu la anthu amene Yehova wawakokera kwa Mwana wake?​—Werengani Yeremiya 9:23, 24.

Maphunzirowa Ali ndi Mphamvu Yosintha Munthu

6. Kodi chinthu chodabwitsa chimene chimachitika munthu ‘akadziwa Yehova’ ndi chiyani?

6 Yesaya anagwiritsa ntchito mawu okuluwika polosera mmene anthu akusinthira masiku ano. Anthu amene anali achiwawa, tsopano ndi okonda mtendere. (Werengani Yesaya 11:6-9.) Anthu amene poyamba ankadana chifukwa chosiyana khungu, mayiko, mitundu kapena chikhalidwe aphunzira kukhala limodzi mogwirizana. Mophiphiritsa tingati iwo ‘asula malupanga awo kukhala zolimira.’ (Yes. 2:4) Kodi zikutheka bwanji anthu kusintha m’njira yodabwitsa chonchi? Anthu ‘adziwa Yehova’ ndipo akugwiritsa ntchito zimene aphunzirazo pa moyo wawo. Ngakhale kuti atumiki a Mulungu ndi opanda ungwiro, iwo apanga gulu la abale enieni padziko lonse. Mphamvu imene uthenga wabwino umakhala nayo pa anthu, ndiponso zotsatira zake zabwino, ndi umboni wakuti maphunziro ochokera kwa Mulungu ndi opambanadi.​—Mat. 11:19.

7, 8. (a) Kodi maphunziro ochokera kwa Mulungu athandiza anthu kusiya “zinthu zozikika molimba” monga ziti? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti maphunziro ochokera kwa Mulungu amachititsa anthu kutamanda Yehova?

7 Mtumwi Paulo anayerekezera ntchito yolalikira imene atumiki a Mulungu amagwira ndi nkhondo yauzimu. Iye analemba kuti: “Zida za nkhondo yathu si zili za kuthupi, koma zili zamphamvu mwa Mulungu zogwetsa nazo zinthu zozikika molimba. Pakuti tikugubuduza malingaliro komanso chokwezeka chilichonse chotsutsana ndi kudziwa kwathu Mulungu.” (2 Akor. 10:4, 5) Kodi maphunziro ochokera kwa Mulungu amamasula anthu ku “zinthu zozikika molimba” ziti? Zina mwa zinthu zimenezi ndi ukapolo wa ziphunzitso zonyenga, kukhulupirira mizimu ndiponso nzeru za anthu. (Akol. 2:8) Maphunziro ochokera kwa Mulungu amathandiza anthu kusiya zizolowezi zoipa ndi kukhala ndi makhalidwe abwino. (1 Akor. 6:9-11) Amathandizanso kuti mabanja akhale abwino. Ndiponso amathandiza anthu amene analibe chiyembekezo, kukhala ndi cholinga pa moyo wawo. Amenewatu ndiye maphunziro amene anthu akufunikira masiku ano.

8 Khalidwe lina limene Yehova amathandiza anthu kukhala nalo, ndi kuona mtima ndipo chitsanzo chotsatirachi chikusonyeza bwino zimenezi. (Aheb. 13:18) Mayi wina wa ku India anayamba kuphunzira Baibulo ndipo kenako anakhala wofalitsa wosabatizidwa. Tsiku lina mayiyu akuchokera kukagwira ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu, anatola tcheni cha golide chovala, pafupi ndi depoti ya basi ndipo mtengo wake unali madola 800 a ku United States. Ngakhale kuti mayiyu ndi wosauka, iye anapita ndi tchenichi kupolisi, kuti apolisiwo akapeze mwini wake. Wapolisi amene anamupeza sanamvetse zimenezi. Kenako wapolisi wina anamufunsa mayiyo kuti: “N’chifukwa chiyani mwabweretsa tchenichi?” Mayiyu anayankha kuti: “Zimene ndaphunzira m’Baibulo zandisintha ndipo panopa ndimachita zinthu moona mtima.” Podabwa ndi zimenezi, wapolisiyo anauza mkulu wachikhristu amene anatsagana ndi mayiyu kuti: “M’boma lino muli anthu aposa 38 miliyoni. Ngati mutathandiza anthu ngakhale 10 okha kukhala ngati mayiyu, mungagwire ntchito yotamandika kwabasi.” Ndiye tikaganizira za anthu mamiliyoni ambiri amene asintha moyo wawo chifukwa cha maphunziro ochokera kwa Mulungu, kodi sitili ndi zifukwa zomveka zotamandira Yehova?

9. Kodi n’chiyani chimathandiza anthu kusintha kwambiri moyo wawo?

9 Mphamvu yosintha anthu imene Mawu a Mulungu ali nayo, ndiponso thandizo limene Yehova amapereka kudzera mwa mzimu woyera, zimathandiza anthu kusintha kwambiri miyoyo yawo. (Aroma 12:2; Agal. 5:22, 23) Lemba la Akolose 3:10 limati: “Muvale umunthu watsopano, umene kudzera mwa kudziwa zinthu molondola ukukhalitsidwa watsopano, kukhala wogwirizana ndi chifaniziro cha Iye amene anaulenga.” Uthenga wa m’Mawu a Mulungu, Baibulo, uli ndi mphamvu yosonyeza zimene zili mumtima mwathu ndipo ungatithandize kusintha maganizo athu komanso mmene timaonera zinthu. (Werengani Aheberi 4:12.) Munthu akadziwa Malemba molondola, n’kusintha moyo wake kuti ugwirizane ndi mfundo zolungama za Yehova, amakhala bwenzi la Mulungu ndipo amakhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha.

Kukonza Tsogolo

10. (a) N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndi amene angatithandize kukonza tsogolo lathu? (b) Kodi posachedwapa zinthu zidzasintha bwanji padziko lonse?

10 Yehova yekha ndi amene angatithandize kukonza tsogolo lathu chifukwa amadziwa zimene zichitike m’tsogolomu. Iye amadziwa tsogolo la anthu. (Yes. 46:9, 10) Ulosi wa m’Baibulo umasonyeza kuti “tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.” (Zef. 1:14) Pa tsiku limeneli, mawu a pa Miyambo 11:4, adzakwaniritsidwa. Lembali limati: “Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa ku imfa.” Nthawi yakuti Yehova aweruze dziko la Satanali ikadzafika, chimene chidzakhale chofunika kwambiri ndi kuyanjidwa ndi Mulungu. Ndalama zidzakhala zopanda ntchito. Pajatu lemba la Ezekieli 7:19 limati: “Adzataya siliva wawo kumakwalala, nadzayesa golide wawo chinthu chodetsedwa.” Kudziwiratu zimenezi, kungatithandize kuchita zinthu mwanzeru panopa.

11. Kodi njira ina imene maphunziro ochokera kwa Mulungu amatithandizira kukonza tsogolo ndi iti?

11 Njira yapadera imene maphunziro ochokera kwa Mulungu amatikonzekeretsera tsiku la Yehova, ndi mwa kutithandiza kuika zinthu zofunika patsogolo m’moyo wathu. Mtumwi Paulo analembera Timoteyo kuti: “Lamula achuma m’dongosolo ili la zinthu kuti asakhale odzikweza, ndi kuti asadalire chuma chosadalirika, koma adalire Mulungu.” Ngakhale ngati tilibe ndalama zambiri, malangizo ouziridwa ndi Mulungu amenewa angatithandize. Kodi zimenezi zimafuna kuti tichite chiyani? M’malo mokundika chuma chakuthupi, tiyenera kuyesetsa ‘kuchita zabwino’ ndiponso ‘kukhala olemera pa ntchito zabwino.’ Tikamaika zinthu zauzimu patsogolo m’moyo wathu, ‘timadzisungira tokha maziko abwino a tsogolo lathu.’ (1 Tim. 6:17-19) Kudzimana kotereku, kumasonyeza kuti timachita zinthu mwanzeru chifukwa malinga ndi zimene Yesu ananena, “munthu angapindulenji ngati apata dziko lonse ndi kutaya moyo wake?” (Mat. 16:26, 27) Podziwa kuti tsiku la Yehova layandikira, aliyense angachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndikukundika kuti chuma? Kodi ndine kapolo wa Mulungu kapena wa Chuma?’​—Mat. 6:19, 20, 24.

12. N’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka anthu ena akamanyoza utumiki wathu?

12 Pa “ntchito zabwino” zimene Akhristu amagwira zotchulidwa m’Mawu a Mulungu, ntchito yofunika kwambiri ndi yolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira yomwe ndi yopulumutsa moyo. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, anthu ena anganyoze utumiki wathu. (Werengani 1 Akorinto 1:18-21.) Koma zimenezi sizisintha kufunika kwa uthenga wathu. Sizisinthanso kufunika kopatsa anthu onse mwayi woti akhulupirire uthengawo nthawi isanathe. (Aroma 10:13, 14) Tikamathandiza anthu ena kuti apindule ndi maphunziro ochokera kwa Mulungu, timadalitsidwa kwambiri.

Anthu Odzimana Amadalitsidwa

13. Kodi mtumwi Paulo anasiya zinthu ziti chifukwa cha uthenga wabwino?

13 Asanakhale Mkhristu, mtumwi Paulo anaphunzira n’cholinga choti akhale munthu wochita bwino m’dongosolo la Ayuda. Zikuoneka kuti asanakwanitse zaka 13, anachoka mumzinda wa kwawo wa Tariso n’kupita ku Yerusalemu kukaphunzitsidwa pamapazi a katswiri wodziwa Chilamulo, dzina lake Gamaliyeli. (Mac. 22:3) Patapita nthawi, Paulo anayamba kupita patsogolo kwambiri m’Chiyuda kuposa anzake onse ndipo akanapitiriza, akanakhala munthu wolemekezeka kwambiri. (Agal. 1:13, 14) Koma atalandira uthenga wabwino, n’kuyamba ntchito yolalikira, anasiya zonsezi. Kodi Paulo anaganizapo kuti sanasankhe bwino? Ayi ndithu. Moti analemba kuti: “Zoonadi, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, chifukwa cha kudziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, kumene ndi kwa mtengo wopambanadi. Chifukwa cha iye, ndimaona zinthu zonse kukhala zosapindulitsa, ndipo ndimaziyesa mulu wa zinyalala.”​—Afil. 3:8.

14, 15. Popeza ndife “antchito anzake a Mulungu,” timapeza madalitso otani?

14 Mofanana ndi Paulo, Akhristu masiku ano amadzimana zinthu zina pofuna kuti azilalikira uthenga wabwino. (Maliko 10:29, 30) Kodi timasowa kanthu chifukwa cha zimenezi? Robert yemwe tinamutchula poyamba uja ananena maganizo amene iye komanso anthu ambiri ali nawo kuti: “Sindidandaula ngakhale pang’ono. Utumiki wa nthawi zonse wandithandiza kukhala wachimwemwe ndi wokhutira ndiponso wandipatsa mpata ‘wolawa, n’kuona kuti Yehova ndi wabwino.’ Nthawi zonse ndikadzimana zinthu zina zakuthupi n’cholinga choti ndikwaniritse zolinga zauzimu, Yehova ankandidalitsa ndi zinthu zambiri kuposa zomwe ndadzimanazo. Zinkakhala ngati sindinadzimane chilichonse. Ndimaona kuti ndapeza madalitso okhaokha.”​—Sal. 34:8; Miy. 10:22.

15 Ngati mwagwira nawo ntchito yolalikira kwa nthawi yaitali, muyenera kuti nanunso mwakhala ndi mpata wolawa n’kuona kuti Yehova ndi wabwino. Kodi pali nthawi yomwe munaonapo kuti mzimu woyera wakuthandizani polalikira uthenga wabwino? Kodi mwaona anthu ena akusangalala chifukwa chakuti Yehova watsegula mitima yawo kuti amvetsere uthenga? (Mac. 16:14) Kodi Yehova wakuthandizani kuthana ndi mavuto, mwinanso kukutsegulirani njira yoti muonjezere utumiki wanu? Kodi iye anakuthandizani pa nthawi ya mavuto, zimene zinakuchititsani kupitirizabe kumutumikira pa nthawi imene munkaona kuti mphamvu zanu zachepa? (Afil. 4:13) Tikamaona kuti Yehova akutithandiza mu utumiki wathu, timamudziwa bwino kuposa kale ndipo timamukonda kwambiri. (Yes. 41:10) Ndi madalitso aakuludi kukhala m’gulu la “antchito anzake a Mulungu” pa ntchito yofunika kwambiri yothandiza anthu kupeza maphunziro ochokera kwa Mulungu.​—1 Akor. 3:9.

16. Kodi mumamva bwanji mukaganizira khama ndiponso kudzimana kumene mumachita chifukwa cha maphunziro ochokera kwa Mulungu?

16 Anthu ambiri amafuna kuchita zinthu zazikulu pa moyo wawo, zoti zisadzaiwalike. Koma timaona kuti zinthu zazikulu zimene anthu ambiri amachita m’dzikoli kawirikawiri sizichedwa kuiwalika. Mosiyana ndi zimenezi, zinthu zimene Yehova akuchita masiku ano pofuna kuyeretsa dzina lake, mosakayikira zidzasungidwabe kosatha ngati mbiri ya anthu a Mulungu. Sizidzaiwalika mpaka kalekale. (Miy. 10:7; Aheb. 6:10) Tiyeni tiziyamikira mwayi wathu wamtengo wapatali wogwira nawo ntchito, yomwe sidzaiwalika, yothandiza anthu kupeza maphunziro ochokera kwa Mulungu.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yehova amafuna kuti anthu amene amawaphunzitsa akhale otani?

• Kodi maphunziro ochokera kwa Mulungu amathandiza bwanji anthu kusintha moyo wawo?

• Kodi tadalitsidwa motani chifukwa chothandiza anthu kupindula ndi maphunziro ochokera kwa Mulungu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 23]

Anthu amene amaphunzitsidwa ndi Yehova apanga gulu la abale enieni padziko lonse

[Chithunzi patsamba 24]

Ndi madalitso aakuludi kukhala m’gulu la “antchito anzake a Mulungu”