Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinapeza Cholinga cha Moyo

Ndinapeza Cholinga cha Moyo

Ndinapeza Cholinga cha Moyo

Yosimbidwa ndi Gaspar Martínez

Nkhani yangayi ndi yosiyana ndi nkhani za anthu ena. Ndinali mnyamata wosauka, wakumudzi ndipo kenako ndinasamukira mumzinda wina, komwe zinthu zinayamba kundiyendera bwino. Komabe monga muonere, chuma chomwe ndinapeza mumzindamo, si chimene ndinkayembekezera kuti ndikapeza.

NDINABADWA cha m’ma 1930, m’dera lina lopanda chonde ku Rioja cha kumpoto kwa dziko la Spain. Ndinasiya sukulu ndili ndi zaka 10, komabe pa nthawiyi n’kuti nditadziwa kuwerenga ndi kulemba. Ineyo, achimwene anga atatu ndi achemwali anga atatu, tinkangokhalira kuweta nkhosa kapena kulima m’timinda tathu.

Chifukwa cha umphawi, tinkaganiza kuti chofunika kwambiri pa moyo ndi ndalama ndi chuma. Tinkasirira anthu amene anali ndi zinthu zambiri kuposa ifeyo. Ngakhale zinali choncho, bishopu wina ananena kuti: “Mudayosizi yonse ino, mudzi wanuwu ndi umene uli ndi anthu okonda kwambiri kupemphera.” Iye sankadziwa kuti pa nthawi ina anthu ambiri m’mudzimo adzasiya Chikatolika.

Ndinayamba Kufufuza Moyo Wabwino

Ndinakwatira mtsikana wina wa m’mudzi momwemo dzina lake Mercedes. Pasanapite nthawi yaitali, tinali ndi mwana wamwamuna. Mu 1957, tinasamukira kumzinda wapafupi wotchedwa Logroño, ndipo kenako banja lathu lonse linasamukiranso komweko. Koma pasanapite nthawi, ndinazindikira kuti ine monga munthu wosadziwa ntchito ina iliyonse, sindingathe kupeza ntchito yamalipiro abwino. Sindinkadziwa kuti ndingapeze kuti malangizo othandiza. Ndinayamba kumafufuza mulaibulale yakumeneko ngakhale kuti sindinkadziwa buku limene lingandithandize.

Kenako, ndinamva kuti pali pulogalamu ina ya pawailesi imene imathandiza anthu kuphunzira Baibulo kudzera m’makalata. Nditalembera kalata ku pulogalamuyi, apulotesitanti a Evangelical anandipeza. Ndikapita kumalo amene ankapempherera, nthawi zambiri ndinkaona kuti akuluakulu akumeneko ankalimbirana udindo. Ndinasiya kupitako poganiza kuti zipembedzo zonse ndi zotero.

Maso Anga Anatseguka

Mu 1964, mnyamata wina dzina lake Eugenio anabwera kwathu. Iye anali wa Mboni za Yehova ndipo ndinali ndisanamvepo za chipembedzo chimenechi. Koma ndinkafunitsitsa kukambirana naye za m’Baibulo. Poyamba ndinkaganiza kuti ndimawadziwa bwino Malemba. Ndinkamuyankha pogwiritsa ntchito malemba ochepa amene ndinawadziwa pa nthawi imene ndinkaphunzira Baibulo kudzera m’makalata. Ngakhale kuti ndinkayesetsa kuikira kumbuyo ziphunzitso za Chipulotesitanti, sindinkazikhulupirira kwenikweni.

Titakambirana kwa nthawi yaitali, sindinachitire mwina koma kuvomereza kuti Eugenio anali katswiri pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Zinandidabwitsa kuona mmene ankapezera malemba ndiponso mmene ankafotokozera tanthauzo lake. Iye ankachita zimenezi ngakhale kuti sukulu yake sanapite nayo patali, moti nkhasako ineyo. Eugenio anandisonyeza kuchokera m’Baibulo kuti tikukhala m’masiku otsiriza ndiponso kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu udzabweretsa paradaiso padziko lapansi. Ndinagoma kwambiri.​—Sal. 37:11, 29; Yes. 9:6, 7; Mat. 6:9, 10.

Nthawi yomweyo, ndinavomera kuphunzira Baibulo. Pafupifupi chilichonse chimene ndinkaphunzira chinali chatsopano ndipo chinkandifika pamtima. Ndinayamba kuona kuti ndili ndi tsogolo lowala ndipo ndapeza cholinga cha moyo. Ntchito yanga yofufuza ija inathera pomwepa. Tsopano ndinaona kuti panalibenso chifukwa chovutikira kuti nditukule moyo wanga, ndipo nkhondo yanga yofufuza ntchito yabwino sinalinso nkhani yaikulu. Ndinadziwanso kuti matenda ndi imfa zidzatha.​—Yes. 33:24; 35:5, 6; Chiv. 21:4.

Nthawi yomweyo ndinayamba kuuza achibale anga zimene ndinkaphunzira. Ndinkawafotokozera motsindika kuti Mulungu walonjeza zoti adzabweretsa paradaiso padziko lapansi ndipo anthu okhulupirika adzakhala mmenemo kosatha.

Achibale Anga Analandira Choonadi cha M’Baibulo

Pasanapite nthawi, tinayamba kumakumana anthu 12 Lamlungu lililonse madzulo m’nyumba ya bambo anga aang’ono, n’kumakambirana malonjezo a m’Baibulo. Tinkachita zimenezi mlungu uliwonse kwa maola awiri kapena atatu. Eugenio ataona kuti gulu la abale anga amene ankafuna kuphunzira Baibulo ndi lalikulu chonchi, anakonza zoti aziphunzira ndi banja lililonse palokha.

Ndinali ndi achibale enanso m’katawuni kena kotchedwa Durango, komwe kanali pamtunda wamakilomita 120 kuchokera komwe tinkakhala ndipo pa nthawiyi panalibe wa Mboni aliyense amene ankakhala kumeneko. Choncho patapita miyezi itatu, ndinagwiritsa ntchito masiku anga a tchuti kuti ndikawaone ndiponso kuwafotokozera za chipembedzo changa chatsopanocho. Ndili kumeneko, tinkasonkhana anthu pafupifupi 10 n’kumakambirana mpaka cha m’ma 1 kapena 2 koloko usiku. Anthu onsewa ankamvetsera mosangalala. Masiku anga ochepa okhala kumeneko atatha, ndinawasiyira Mabaibulo ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo. Ndipo nditachokako, tinkalemberanabe makalata.

Pamene Mboni zinafika ku Durango, zinapeza kuti kunali anthu 18 amene ankafunitsitsa kuphunzira Baibulo, ngakhale kuti panalibe aliyense amene anali atalalikirako. Mbonizi zinakonza zoti ziziphunzira ndi banja lililonse palokha.

Mercedes anali asanayambebe kuphunzira choonadi. Sikuti iye sankagwirizana ndi ziphunzitso za m’Baibulo ayi, koma vuto lake linali kuopa anthu. Pa nthawiyi ntchito ya Mboni za Yehova inali italetsedwa ku Spain, choncho Mercedes ankaganiza kuti akuluakulu a boma adzawachotsa sukulu ana athu awiri, ndiponso kuti anthu azitisala. Koma ataona kuti banja lathu lonse likulandira choonadi cha m’Baibulo, iyenso anayamba kuphunzira.

M’zaka ziwiri zokha, achibale anga okwana 40 anali atabatizidwa n’kukhala a Mboni posonyeza kuti adzipereka kuti atumikire Mulungu. Inde, tsopano achibale anga analinso ndi cholinga chofanana ndi changa. Ndinkaona kuti ndakwanitsa kuchita chinthu chofunika kwambiri ndipo kuti tadalitsidwa ndi chuma chauzimu chambirimbiri.

Nditayamba Kukalamba M’pamenenso Moyo Unayamba Kukhala Wosangalatsa Kwambiri

M’zaka 20 zotsatira, ndinaika maganizo anga onse pa kusamalira anyamata athu awiri ndiponso kuthandiza mpingo wakwathu. Ine ndi Mercedes titasamukira kumzinda wa Logroño, womwe unali ndi anthu 100,000, tinapeza Mboni zokwana pafupifupi 20 zokha. Pasanapite nthawi, ndinakhala ndi maudindo ambiri mumpingo.

Ndiyeno ndili ndi zaka 56, kampani yathu mosayembekezereka inatseka fakitale imene ndinkagwirako ntchito ndipo ine ndinakhala pa ulova. Kuyambira kale ndinkafunitsitsa kuchita utumiki wa nthawi zonse, choncho ndinapezerapo mwayi woyamba upainiya. Ndalama za penshoni zimene ndinalandira zinali zochepa, ndipo zinali zovuta kupeza zofunika pa moyo. Pofuna kuthandiza, Mercedes ankagwira ntchito yoyeretsa. Tinatha kusamalira bwinobwino banja lathu ndipo tinkapeza zofunika pa moyo. Ndidakali mpainiya ndipo mkazi wanga amachita upainiya wothandiza nthawi ndi nthawi. Iye amakonda kwambiri ntchito yolalikira.

Zaka zingapo zapitazo, Mercedes ankapereka magazini athu kwa mayi wachitsikana dzina lake Merche, amene anaphunzirapo Baibulo ali mwana. Merche anali ndi chidwi chowerenga mabuku athu, ndipo Mercedes anazindikira kuti Merche adakali ndi mtima wokonda choonadi cha m’Baibulo. Pamapeto pake, Merche anayamba kuphunzira Baibulo ndipo anapita patsogolo kwambiri. Koma mwamuna wake Vicente, anali chidakwa ndipo sankakhazikika pa ntchito. Chifukwa cha zimenezi, iye sankapatsa mkazi wake ndalama. Uchidakwa wakewo unatsala pang’ono kuwononga banja lawo.

Mkazi wanga anauza Merche kuti Vicente angachite bwino kulankhula nane, ndipo kenako anaterodi. Titacheza maulendo angapo, anavomera kuphunzira Baibulo. Vicente anayamba kusintha ndipo ankatha masiku angapo osamwa. Kenako, ankatha mlungu umodzi kapena kuposerapo osamwa. Pamapeto pake, anasiyiratu kumwa mowa. Khalidwe ndi maonekedwe ake zinasintha kwambiri, ndipo banja lake linayamba kugwirizana. Panopa iye, mkazi wake ndiponso mwana wawo wamkazi, onse pamodzi monga banja, amathandiza kwambiri mpingo wina waung’ono ku Canary Islands komwe akukhala.

Moyo Wosangalatsa Womwe Ndakhala Nawo

Ngakhale kuti achibale anga ena amene anaphunzira Baibulo zaka zambiri zapitazo anamwalira, banja lathu lapitiriza kukula ndipo Mulungu watidalitsa kwambiri. (Miy. 10:22) N’zosangalatsa kwambiri kuona kuti pafupifupi anthu onse amene anayamba kuphunzira Baibulo zaka 40 zapitazo, akupitiriza kutumikira Yehova mokhulupirika pamodzi ndi ana ndiponso zidzukulu zawo.

Panopa achibale anga ambirimbiri ndi Mboni ndipo ambiri mwa iwo ndi akulu, atumiki othandiza ndiponso apainiya. Mwana wanga wamkulu ndi mkazi wake akutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Madrid, ku Spain. Pa nthawi imene ndinakhala Mboni, tinalipo Mboni 3,000 zokha ku Spain. Panopa kuli Mboni zoposa 100,000. Ndimasangalala kwambiri ndi utumiki wa nthawi zonse, ndipo ndimayamikira kwambiri Mulungu chifukwa cha moyo wabwino womwe ndakhala nawo pomutumikira. Ngakhale kuti sindine wophunzira, ndimatumikira monga woyang’anira dera wogwirizira.

Zaka zingapo zapitazo, ndinapeza kuti pafupifupi anthu onse m’mudzi womwe ndinakulira uja anachoka. Chifukwa cha umphawi, anthu onse kumeneko anasiya minda ndi nyumba zawo kuti akafunefune moyo wabwino. Chosangalatsa n’chakuti anthu ambiri amene anachoka m’mudzi wakwathu, kuphatikizapo ineyo, tapeza chuma chauzimu. Tadziwa kuti moyo uli ndi cholinga ndiponso kuti kutumikira Yehova kumabweretsa chimwemwe chosaneneka.

[Chithunzi patsamba 32]

Pafupifupi anthu onse a m’banja la M’bale Martínez amene ali m’choonadi