Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulambira kwa Pabanja N’kofunika Kwambiri Kuti Tidzapulumuke

Kulambira kwa Pabanja N’kofunika Kwambiri Kuti Tidzapulumuke

Kulambira kwa Pabanja N’kofunika Kwambiri Kuti Tidzapulumuke

“NKHONDO ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” idzakhala yoopsa kwambiri. (Chiv. 16:14) Pogwiritsa ntchito mawu ophiphiritsa opereka chithunzi chabwino m’maganizo, mneneri Mika analemba kuti: “Mapiri adzasungunuka . . . , ndi zigwa zidzang’ambika, ngati sera pamoto, ngati madzi otsanulidwa potsetseremba.” (Mika 1:4) Kodi anthu amene sakutumikira Yehova adzakumana ndi tsoka lotani? Mawu a Mulungu amati: “Akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera kumalekezero ena a dziko lapansi kumka kumalekezero ena a dziko lapansi.”​—Yer. 25:33.

Poganizira machenjezo ngati amenewa, mitu ya mabanja, imene ikuphatikizapo makolo ambiri amene akulera okha ana, iyenera kuganizira za ana awo amsinkhu woti ali ndi nzeru zotha kupanga okha zosankha, n’kudzifunsa kuti, ‘Kodi ana amenewa adzapulumuka nkhondo imeneyo?’ Baibulo limatitsimikizira kuti akhoza kudzapulumuka ngati adzakhale olimba mwauzimu malinga ndi msinkhu wawowo.​—Mat. 24:21.

Kufunika Kokhala ndi Nthawi ya Kulambira kwa Pabanja

Monga kholo, yesetsani kuchita zonse zimene mungathe kuti mulere ana anu “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.” (Aef. 6:4) Kuti muchite zimenezi, kuphunzira Baibulo ndi ana anu n’kofunika kwambiri. Tikufuna kuti ana athu akhale ngati Akhristu a ku Filipi, amene Paulo anawayamikira chifukwa anali kumvera Yehova mwakufuna kwawo. Iye analemba kuti: “Okondedwa anga, mmene mwakhalira omvera nthawi zonse, osati kokha ine ndikakhalapo, koma mofunitsitsa kwambiri tsopano pamene ine kulibe, pitirizani kukonza chipulumutso chanu, mwa mantha ndi kunjenjemera.”​—Afil. 2:12.

Kodi ana anu amatsatira malamulo a Yehova inuyo kulibe? Bwanji akakhala kusukulu? Kodi mungathandize bwanji ana anu kuti azindikire kuti malamulo a Yehova ndi opindulitsa n’cholinga chakuti aziwatsatira ngakhale inuyo kulibe?

Kulambira kwa pabanja kungathandize kwambiri kulimbitsa chikhulupiriro cha mwana wanu kuti azichita zimenezi. Chotero tiyeni tikambirane mfundo zitatu zofunika kwambiri kuti phunziro lanu la Baibulo la banja likhale lopindulitsa.

Kuzichitika Nthawi Zonse

M’chinenero choyambirira chimene analembera Baibulo, mawu amene anamasuliridwa kuti “panali tsiku lakuti” pa Yobu 1:6, amasonyeza kuti angelo a Mulungu ali ndi nthawi yoikika imene amakasonkhana pamaso pake. Inunso muzichita zomwezo ndi ana anu. Musankhe tsiku ndi nthawi yoti muzikhala ndi Kulambira kwa Pabanja ndipo musamaphonye mlungu uliwonse. Komanso, musankhe tsiku lina loti ngati mutalephera kukhala ndi kulambira kwa pabanja pa tsiku limene munasankhalo chifukwa cha zinthu zogwa mwadzidzidzi, mukhoza kuchita pa tsiku linalo.

Miyezi ikamadutsa, musalole kuti kulambira kwa pabanja panu kuyambe kuchitika mwa apa ndi apo. Musaiwale kuti ana anu ndiwo maphunziro anu a Baibulo ofunika kwambiri. Koma Satana angakonde kuwadya ngati mkango. (1 Pet. 5:8) Mukapanda kukhala ndi Kulambira kwa Pabanja patsiku limene munayenera kukhala nako, m’malomwake n’kuonera TV kapena kuchita zinthu zina zosafunikira kwenikweni, ndiye kuti Satana wakugonjetsani.​—Aef. 5:15, 16; 6:12; Afil. 1:10.

Kuzikhala Kopindulitsa

Kulambira kwa Pabanja sikuyenera kukhala nthawi yongophunzira zinthu kuti tingozidziwa basi. Muziyesetsa kuti zimene mukuphunzirazo zizikhala zoti ana atha kuzigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Nthawi zina muzisankha nkhani zimene mwana wanu akumane nazo m’masiku kapena milungu imene ikubwera. Mwachitsanzo, mukhoza kukhala ndi nthawi yoyeseza ulaliki. Ana amasangalala kuchita zinthu zimene amazichita bwino. Choncho muziyeseza nawo ulaliki wosiyanasiyana ndiponso mmene angayankhire anthu amene sakufuna kuwalalikira. Zimenezi zidzawathandiza kuti asamadzikayikire akamachita nawo mbali zosiyanasiyana za ntchito yathu yolalikira za Ufumu.​—2 Tim. 2:15.

Mukhozanso kukhala ndi nthawi yoyeseza kuchita zinthu zimene zingathandize ana anu kuti asamatengere zimene anzawo akuchita. Mukhoza kugwiritsa ntchito mutu 15 m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, pophunzira ndi banja lanu. Pabokosi lakuti “Mmene Mungakonzekerere,” pamasamba 132 ndi 133 m’bukuli, pali zitsanzo za zinthu zina zimene mungakambirane. Palinso mafunso amene amapereka mpata kwa mwana wanu kuti aganize ndi kuyankha m’njira yosavuta kwa iyeyo. Mawu amene ali m’munsi mwa tsamba 133 amalimbikitsa achinyamata kuti: “Yeserani ndi makolo anu kapena munthu wina wamkulu zimene mungachite.” Bwanji osamayesera zinthu ngati zimenezi nthawi ndi nthawi mukamachita Kulambira kwa Pabanja?

Kulambira kwa pabanja kumapatsa makolo mpata wothandiza ana awo kuona ubwino wokhala ndi zolinga zauzimu. Pa nkhani imeneyi, buku la Zimene Achinyamata Amafunsa, lili ndi mfundo zabwino kwambiri m’mutu 38, wakuti “Kodi Ndidzachite Zotani Pamoyo Wanga?” Pokambirana mutu umenewu, thandizani mwana wanu kuzindikira kuti ngati akufuna kudzakhala ndi moyo wabwino, kutumikira Yehova kuyenera kukhala chinthu chofunika kuposa china chilichonse pa moyo wake. Limbikitsani mwana wanu kukhala ndi mtima wofuna kudzachita upainiya, kudzatumikira ku Beteli, kudzapita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki, kapena kudzachita utumiki wina wa nthawi zonse.

Koma nali chenjezo: Makolo ena amene ali ndi zolinga zabwino amangoganizira kwambiri zimene akufuna kuti mwana wawo adzachite moti amaiwala kumuyamikira mwanayo pa zimene akuchita. Zoona, ndi bwino kulimbikitsa mwana wanu kukhala ndi zolinga zabwino monga kudzatumikira ku Beteli ndi kudzakhala mmishonale. Koma pochita zimenezo, samalani kuti musatopetse mwanayo pomangokhalira kumuuza zimene mukufuna kuti adzachite, chifukwa mukamatero angamapsinjike maganizo. (Akol. 3:21) Nthawi zonse muzikumbukira kuti mwana wanu ayenera kukonda Yehova chifukwa chakuti iyeyo akufuna, osati chifukwa chakuti n’zimene inuyo mukufuna. (Mat. 22:37) Choncho muziyamikira mwana wanu pa zimene akuchita, ndipo musamangokhalira kunena zimene sakuchita. Muthandizeni kuyamikira zinthu zonse zimene Yehova wachita. Ndiyeno mulole kuti mtima wa mwana wanuyo umulimbikitse kuchitapo kanthu poyamikira zabwino zimene Yehova amachita.

Kuzikhala Kosangalatsa

Mfundo yachitatu yothandiza kuti Kulambira kwa Pabanja kukhale kopindulitsa, ndi yoti kuzikhala kosangalatsa. Kodi mungachite bwanji zimenezi? Mwina nthawi zina mukhoza kumamvetsera masewero kapena kuonerera mavidiyo a Mboni za Yehova, kenako n’kukambirana zimene mwamvetsera kapena kuonererazo. Kapenanso mukhoza kuwerengera limodzi nkhani inayake ya m’Baibulo, mwa kugawana kuti aliyense awerengeko mawu a munthu wina wa m’Baibulomo.

M’magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! mumakhala nkhani zosiyanasiyana zimene zimathandiza kwambiri pophunzira monga banja. Mwachitsanzo, mukhoza kugwiritsa ntchito chigawo chimene chimakhala patsamba 31 mu Galamukani! iliyonse, cha mutu wakuti “Kodi Mungayankhe Bwanji?” Pa miyezi iwiri iliyonse, mu Nsanja ya Olonda yogawira mumatuluka nkhani imene mungagwiritse ntchito pophunzira ya mutu wakuti “Zoti Achinyamata Achite.” Miyezi imene kulibe nkhani zimenezi, kumakhala nkhani zina za ana za mutu wakuti “Phunzitsani Ana Anu.”

Makolo amene ali ndi ana achinyamata, angakonde kwambiri kugwiritsa ntchito nkhani zakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa” zimene zimatuluka mu Galamukani! ndiponso buku lakuti Zimene Achinyamata Amafunsa. Mukamagwiritsa ntchito buku limeneli, musaiwale kabokosi kakuti “Mukuganiza Bwanji?” kamene kali kumapeto kwa mutu uliwonse. Kabokosi kameneka sikongobwerezera zimene zili m’mutuwo ayi. Mukhoza kugwiritsa ntchito mafunso amene amakhala m’kabokosika pokambirana paphunziro lanu la banja.

Koma samalani kuti nthawi ya phunziro la banja isakhale nthawi yofunsana mafunso ambirimbiri ngati kupolisi. Mwachitsanzo, musakakamize mwana wanu kuti akuwerengereni zimene walemba pamasamba amene ali ndi kamutu kakuti “Mfundo Zanga” kapena m’mbali zina za bukuli zofuna kuti wowerenga azilemba maganizo ake. Pakamutu kakuti “Makolo Dziwani Izi” kamene kali patsamba 3, bukuli limati: “Kuti ana anu alembe zakukhosi kwawo m’bukuli, musamaone zimene alemba. Anawo akafuna angathe kukusonyezani okha zimene alembazo.”

Mukamayesetsa kuchita kulambira kwa pabanja nthawi zonse, ndiponso kukamakhala kopindulitsa ndi kosangalatsa, Yehova adzadalitsa kwambiri khama lanu. Nthawi yapadera yophunzirira pamodzi monga banja imeneyi, idzathandiza kuti anthu a m’banja mwanu amene mumawakonda akhalebe olimba mwauzimu.

[Bokosi patsamba 31]

Muzichita Zinthu Zosiyanasiyana

“Pophunzira ndi ana athu aakazi ang’onoang’ono, ine ndi mwamuna wanga tinkaphunzira nawo buku limene mwachokera nkhani yoti tikaphunzire kumpingo, kenako tinkauza ana athuwo kuti ajambule zithunzi zofotokoza mwachidule mfundo zazikulu za nkhaniyo. Nthawi zina tinkachita kasewero ka nkhani za m’Baibulo kapena tinkayeseza ulaliki wosiyanasiyana. Tinkayesetsa kuti phunzirolo lizikhala logwirizana ndi msinkhu wawo, losangalatsa, lolimbikitsa ndiponso losatopetsa.”​—J.M., United States.

“Pofuna kuthandiza mwana wa mayi amene ndinkaphunzira naye Baibulo kuti amvetsetse kuvuta kogwiritsa ntchito mpukutu mu nthawi za m’Baibulo, tinasindikiza buku la m’Baibulo la Yesaya titachotsamo manambala osonyeza machaputala ndi mavesi. Ndiyeno tinalumikiza mapepalawo kuti akhale chipepala chimodzi chachitali. Kenako tinamata timapaipi kumbali zonse ziwiri zakumapeto kwa chipepalacho. Tsopano mwanayo anayesera kuchita zimene Yesu anachita m’sunagoge ku Nazareti. Nkhani yolembedwa pa Luka 4:16-21 imati Yesu ‘anafunyulula mpukutuwo [wa Yesaya] napeza pamene panalembedwa mawu’ amene anali kufuna. (Yes. 61:1, 2) Koma mwanayo atayesera kuchita zomwezo, anavutika kuti apeze Yesaya 61 mumpukutu wautali wopanda machaputala ndi mavesiwo. Mnyamatayo anazindikira kuti Yesu anali waluso kwambiri popeza malemba mumpukutu, ndipo anati: ‘Ndamugomera kwabasi Yesu!’”​—Y.T., Japan.

[Chithunzi patsamba 30]

Kuyeserera kungathandize ana anu kuti asamatengere zochita za anzawo

[Chithunzi patsamba 31]

Yesetsani kuti Kulambira kwa Pabanja kuzikhala kosangalatsa