Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mungathe Kukhalabe ndi Mabwenzi M’dziko Lopanda Chikondi Lino

Mungathe Kukhalabe ndi Mabwenzi M’dziko Lopanda Chikondi Lino

Mungathe Kukhalabe ndi Mabwenzi M’dziko Lopanda Chikondi Lino

“Ndikukulamulani zinthu izi, kuti muzikondana wina ndi mnzake.”​—YOH. 15:17.

1. N’chifukwa chiyani Akhristu oyambirira anafunika kukhala mabwenzi apamtima?

USIKU womaliza umene Yesu anali padziko lapansi pano, analimbikitsa ophunzira ake okhulupirika kuti alimbitse ubwenzi pakati pawo. Madzulo a tsiku lomwelo, iye anali atawauza kuti chikondi n’chimene chidzawadziwikitsa kuti ndi otsatira ake. (Yoh. 13:35) Atumwiwo anafunika kukhala mabwenzi apamtima kuti athe kupirira mayesero amene anali kudzakumana nawo m’tsogolo ndiponso kuti adzakwanitse ntchito imene Yesu anadzawapatsa. Ndipo iwo anaterodi. Akhristu oyambirira anadziwika monga anthu amene anali odzipereka kwambiri kwa Mulungu ndiponso okondana kwambiri.

2. (a) Kodi tonsefe tikufunitsitsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tikufuna kutero? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

2 Masiku ano, zimasangalatsa kwambiri kukhala m’gulu lapadziko lonse limene anthu ake amatsanzira Akhristu oyambirira. Tonsefe tikufunitsitsa kumvera lamulo la Yesu lakuti tizikondana kuchokera pansi pa mtima. Komabe m’masiku otsiriza ano, anthu ambiri ndi osakhulupirika ndipo alibe chikondi chachibadwa. (2 Tim. 3:1-3) Nthawi zambiri amakhala pa ubwenzi ndi munthu chifukwa chongofuna kupeza kenakake ndipo ubwenzi wake sukhala wolimba. Kuti tizidziwikabe monga Akhristu oona, sitiyenera kuchita zimenezo. Choncho, tiyeni tikambirane mafunso awa: Kodi maziko a ubwenzi wabwino n’chiyani? Kodi tingapeze bwanji mabwenzi abwino? Kodi ndi nthawi iti pamene tingafunike kuthetsa ubwenzi wathu? Ndipo kodi tingatani kuti tikhalebe ndi mabwenzi abwino?

Kodi Maziko a Ubwenzi Wabwino N’chiyani?

3, 4. Kodi maziko a ubwenzi wolimba kwambiri n’chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani zili choncho?

3 Ubwenzi wolimba kwambiri umazikidwa pa kukonda Yehova. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Wina akam’laka mmodziyo, awiri adzachirimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.” (Mlal. 4:12) Yehova akakhala chingwe chachitatu pa ubwenzi wanu, ubwenziwo sutha.

4 N’zoona kuti anthu amene sakonda Yehova, akhozanso kukhala ndi mabwenzi abwino. Koma ngati anthu akukondana chifukwa chakuti onsewo amakonda Mulungu, ubwenzi wawo umakhala wolimba. Pakakhala kusamvana, mabwenzi enieni amachitirana zinthu m’njira imene imasangalatsa Yehova. Adani a Mulungu akafuna kusokoneza mgwirizano wathu, amaona kuti ubwenzi wa pakati pa Akhristu oonafe ndi wolimba. Kuyambira kale, atumiki a Yehova akhala okonzeka kufa kusiyana ndi kupereka Akhristu anzawo.​—Werengani 1 Yohane 3:16.

5. N’chifukwa chiyani ubwenzi wa Rute ndi Naomi unali wokhalitsa?

5 Mosakayikira, mabwenzi abwino kwambiri amene tingakhale nawo, ndi anthu amene amakonda Yehova. Taganizirani chitsanzo cha Rute ndi Naomi. Akazi amenewa anali ndi ubwenzi umene ndi umodzi wa maubwenzi osiririka kwambiri olembedwa m’Baibulo. Kodi n’chifukwa chiyani ubwenzi wawo unali wolimba ndiponso wokhalitsa? Rute anaulula chinsinsi chake pamene anauza Naomi kuti: “Mulungu wanu ndiye Mulungu wanga; . . . andilange Yehova nawonjezeko, chilichonse chikasiyanitsa inu ndi ine, koma imfa ndiyo.” (Rute 1:16, 17) Zikuonekeratu kuti Rute ndi Naomi anali kukonda kwambiri Mulungu, ndipo pochitirana zinthu anali kutsogozedwa ndi chikondi chimenechi. Chifukwa cha zimenezi, akazi awiri onsewa anadalitsidwa ndi Yehova.

Mmene Tingapezere Mabwenzi Abwino

6-8. (a) Kodi pamafunika chiyani kuti ubwenzi ukhale wolimba ndiponso wokhalitsa? (b) Kodi mungachite chiyani kuti muyambe ndinu kupeza mabwenzi?

6 Chitsanzo cha Rute ndi Naomi chikusonyeza kuti ubwenzi wabwino sumangoyambika mwangozi. Maziko ake ndi oti anthu awiri onsewo azikonda Yehova. Koma kuti ubwenzi ukhale wolimba ndiponso wokhalitsa, mumafunika kuchita khama ndiponso kudzimana. Ngakhale ana a mimba imodzi omwe amalambira Yehova, ayenera kuchita khama kuti akhale mabwenzi apamtima. Choncho, kodi mungapeze bwanji mabwenzi abwino?

7 Yambani ndinu. Mtumwi Paulo analimbikitsa mabwenzi ake mumpingo wa ku Roma kuti ‘akhale ochereza.’ (Aroma 12:13) Kuti munthu afike pokhala wochereza alendo, amafunika kuchita zinthu zing’onozing’ono zochereza ena nthawi ndi nthawi. Kuchita zimenezi kuli ngati kuyenda ulendo, kumene kumafuna kuti munthu aziponya mwendo wake patsogolo pang’ono ndi pang’ono mpaka kutha mtunda. Choncho kuchereza alendo si chinthu choti wina angakuchitireni. (Werengani Miyambo 3:27.) Njira imodzi imene mungacherezere ena ndiyo kuitana anthu osiyanasiyana a mumpingo mwanu kuti adzadye nanu chakudya chosalira zambiri. Kodi mungathe kumaitana anthu a mumpingo mwanu n’kuwachereza kunyumba kwanu nthawi ndi nthawi?

8 Njira ina imene mungatsatire kuti muyambe ndinu kupeza mabwenzi, ndiyo kupempha anthu osiyanasiyana kuti mukalalikire limodzi. Mukaima pakhomo pa munthu wosamudziwa n’kumamva mnzanuyo akulankhula kuchokera pansi pa mtima za chikondi chake pa Yehova, simungalephere kumukonda.

9, 10. Kodi Paulo anatipatsa chitsanzo chotani, ndipo tingamutsanzire bwanji?

9 Futukulani chikondi chanu. (Werengani 2 Akorinto 6:12, 13.) Kodi mumaganiza kuti palibe aliyense mumpingo mwanu amene angakhale bwenzi lanu? Ngati ndi choncho, kodi mwina chingakhale chifukwa chakuti muli ndi mfundo zanu za amene mumafuna kuti akhale bwenzi lanu? Mtumwi Paulo anatipatsa chitsanzo chabwino chofutukulira chikondi. Pa nthawi inayake, iye sakanaganiza n’komwe zokhala ndi mabwenzi amene sanali Ayuda. Koma kenako anadzakhala “mtumwi . . . wotumidwa kwa mitundu ina.”​—Aroma 11:13.

10 Komanso, Paulo sanasankhe anthu a msinkhu wake okha kukhala mabwenzi ake. Mwachitsanzo, iye ndi Timoteyo anakhala mabwenzi apamtima ngakhale kuti anali osiyana kwambiri zaka ndiponso mmene anakulira. Masiku ano, achinyamata ambiri amanyadira kwambiri ubwenzi umene apanga ndi anthu achikulire mumpingo. Vanessa, amene ali ndi zaka za m’ma 20, anati: “Mlongo winawake amene ali ndi zaka za m’ma 50 ndi bwenzi langa lapamtima. Ndimamuuza chilichonse chimene ndingauze anthu a msinkhu wanga. Ndipo iye amandikonda kwambiri.” Kodi ubwenzi woterowo umapangika bwanji? Vanessa anati: “Ndinachita kuyambitsa ubwenzi umenewu. Sindinangokhala n’kumadikira kuti zinthu zichitika zokha.” Kodi ndinu okonzeka kuyambitsa ubwenzi ndi anthu amene si a msinkhu wanu? Yehova adzadalitsa kwambiri khama lanu mukatero.

11. Kodi tingaphunzire chiyani pa chitsanzo cha Davide ndi Jonatani?

11 Khalani okhulupirika. Solomo analemba kuti: “Bwenzi limakonda nthawi zonse; ndipo m’bale anabadwira kuti akuthandize pooneka tsoka.” (Miy. 17:17) Polemba mawu amenewo, mwina Solomo anali kuganiza za ubwenzi wa bambo ake Davide ndi Jonatani. (1 Sam. 18:1) Mfumu Sauli anali kufuna kuti mwana wake Jonatani adzakhale mfumu ya Isiraeli iye akadzamwalira. Koma Jonatani anazindikira kuti Yehova anasankha Davide kuti ndiye adzakhale ndi udindo umenewo. Mosiyana ndi Sauli, Jonatani sanachitire nsanje Davide. Iye sanaipidwe poona kuti anthu akutamanda Davide, ndiponso sanakhulupirire mabodza amene Sauli anali kufalitsa onena za Davide. (1 Sam. 20:24-34) Kodi ifeyo tili ngati Jonatani? Mabwenzi athu akapatsidwa maudindo, kodi timasangalala? Akakumana ndi mavuto, kodi timawatonthoza ndi kuwathandiza? Tikauzidwa miseche yonena za bwenzi lathu, kodi timafulumira kuikhulupirira? Kapena, mofanana ndi Jonatani, kodi timasonyeza kuti ndife okhulupirika kwa bwenzi lathulo poliikira kumbuyo?

Nthawi Yofunika Kuthetsa Ubwenzi Wathu

12-14. Kodi ophunzira Baibulo ena amakumana ndi mavuto otani, ndipo tingawathandize bwanji?

12 Wophunzira Baibulo akayamba kusintha moyo wake, akhoza kukumana ndi mavuto pa nkhani ya mabwenzi. N’kutheka kuti iye ali ndi mabwenzi amene amakonda kucheza nawo koma amene satsatira mfundo za m’Baibulo pa moyo wawo. Mwina kale anali kucheza nawo nthawi zambiri. Koma tsopano akuona kuti zinthu zimene iwo amachita zikhoza kumusokoneza, ndipo akuona kuti ayenera kuchepetsa nthawi yocheza ndi mabwenzi akewo. (1 Akor. 15:33) Komabe, akhoza kuganiza kuti ngati sazicheza nawonso, mabwenzi akewo amuona ngati ndi munthu wosakhulupirika.

13 Ngati ndinu wophunzira Baibulo ndipo mukukumana ndi vuto limeneli, kumbukirani kuti bwenzi lenileni lingasangalale kukuonani mukuyesetsa kusintha moyo wanu kuti ukhale wabwino. Mwina nalonso lingafune kuyamba kuphunzira za Yehova ngati inuyo. Koma mabwenzi abodza “amakunyozani” chifukwa simukuthamanga nawo limodzi “m’chithaphwi cha makhalidwe oipa.” (1 Pet. 4:3, 4) Zoona zake n’zakuti mabwenzi amenewa ndi amene ali osakhulupirika kwa inu, osati inuyo kwa iwowo.

14 Mabwenzi amene sakonda Mulungu akasiya kucheza ndi ophunzira Baibulo, anthu a mumpingo akhoza kukhala mabwenzi atsopano a ophunzira Baibulowa. (Agal. 6:10) Kodi mukudziwa anthu amene amabwera kumisonkhano amene akuphunzira Baibulo? Kodi nthawi zina mumacheza nawo kuti muwalimbikitse?

15, 16. (a) Kodi tiyenera kutani bwenzi lathu likasiya kutumikira Yehova? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu?

15 Nanga bwanji ngati mnzathu wa mumpingo wasankha zosiya Yehova, mwina mpaka kuchotsedwa mumpingo? Zimenezi zikhoza kukhala zopweteka kwambiri. Mlongo wina anafotokoza mmene anamvera mnzake wapamtima atasiya kutumikira Yehova. Anati: “Ndinamva ngati munthu wina amene ndimamukonda kwambiri wamwalira. Poyamba, ndinali kuganiza kuti mnzangayo anali wolimba m’choonadi, koma tsopano ndinazindikira kuti sanali wolimba. Ndinayamba kuganiza kuti mwina anali kutumikira Yehova pongofuna kusangalatsa achibale ake. Choncho ndinayamba kudzifunsa ndekha za chifukwa chimene ndinali kutumikira Yehova. Kodi ndinali kutumikira Yehova pa zifukwa zoyenera?” Kodi mlongoyu anathana nalo bwanji vuto limeneli? Iye anati: “Ndinatulira Yehova nkhawa yangayo. Panopa, ndikufuna kumusonyeza Yehova kuti ndimamukonda kuchokeradi pansi pa mtima, osati chifukwa chongoti amandipatsa mabwenzi m’gulu lake.”

16 Sitingakhalebe mabwenzi a Mulungu ngati timagwirizana ndi anthu amene asankha kukhala mabwenzi a dziko. Wophunzira Yakobe analemba kuti: “Kodi simudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko ndiko udani ndi Mulungu? Choncho, aliyense amene akufuna kukhala bwenzi la dziko akudzipanga yekha mdani wa Mulungu.” (Yak. 4:4) Timasonyeza kuti timakonda Mulungu pokhulupirira kuti ngati tikhalabe okhulupirika kwa iye, atithandiza kupirira pamene tataya bwenzi lathu. (Werengani Aheberi 13:5b.) Mlongo amene tinamugwira mawu uja anamaliza ndi mawu akuti: “Ndinaphunzira kuti sitingachititse munthu wina kukonda Yehova kapena kutikonda ifeyo. Aliyense ayenera kufuna yekha kuchita zimenezi.” Koma kodi tingatani kuti tikhalebe ndi ubwenzi wabwino ndi anthu amene atsala mumpingo?

Mmene Mungakhalirebe ndi Mabwenzi Abwino

17. Kodi mabwenzi abwino amalankhulana bwanji?

17 Kulankhulana bwino kumalimbitsa ubwenzi. Mukamawerenga nkhani za m’Baibulo zokhudza Rute ndi Naomi, Davide ndi Jonatani, ndiponso Paulo ndi Timoteyo, muona kuti mabwenzi abwino amalankhulana momasuka komanso mwaulemu. Pofotokoza mmene tiyenera kulankhulirana, Paulo analemba kuti: “Nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoleretsa ndi mchere.” Apa Paulo anali kunena za mmene tiyenera kulankhulira kwa anthu “akunja,” kutanthauza anthu amene si abale athu achikhristu. (Akol. 4:5, 6) Ndiye ngati tiyenera kulankhula mwaulemu kwa anthu osakhulupirira, kuli bwanji mabwenzi akumpingo?

18, 19. Kodi uphungu uliwonse umene tingapatsidwe ndi bwenzi lathu lachikhristu tiziuona bwanji, ndipo akulu a ku Efeso anatipatsa chitsanzo chotani?

18 Bwenzi labwino limalemekeza maganizo a mnzake. Choncho mabwenzi ayenera kulankhulana mosabisa mawu koma mwaulemu. Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Mafuta ndi zonunkhira zikondweretsa mtima, ndi ubwino wa bwenzi uteronso pakupangira uphungu.” (Miy. 27:9) Kodi uphungu uliwonse umene mumapatsidwa ndi bwenzi lanu mumaona motero? (Werengani Salmo 141:5.) Bwenzi lanu likakuuzani kuti likuda nkhawa ndi zinthu zinazake zimene mwayamba kuchita, kodi mumatani? Kodi mumaona kuti zimene akunenazo zikusonyeza kuti bwenzi lanulo limakukondani ndiponso n’lokhulupirika kwa inu, kapena mumakwiya?

19 Mtumwi Paulo anali bwenzi lapamtima la akulu akumpingo wa ku Efeso. Mosakayikira iye anadziwana ndi ena mwa amuna amenewo pa nthawi imene iwowo anakhala okhulupirira. Koma pa nthawi imene anakumana nawo komaliza, anawapatsa uphungu wosapita m’mbali. Kodi iwo anamva bwanji? Mabwenzi a Paulowo sanakhumudwe. M’malomwake, anayamikira poona kuti Paulo anali kuwafunira zabwino, ndipo analira atazindikira kuti sadzamuonanso.​—Mac. 20:17, 29, 30, 36-38.

20. Kodi bwenzi lachikondi limachita chiyani?

20 Bwenzi labwino silimangolandira uphungu, limaperekanso uphungu kwa mnzake. Komabe, tiyenera kudziwa nthawi yoti ‘tisamale zathuzathu,’ kapena kuti, tisalowerere nkhani za ena. (1 Ates. 4:11) Tiyeneranso kukumbukira kuti aliyense wa ife “adzadziyankhira yekha kwa Mulungu.” (Aroma 14:12) Koma ngati pali pofunika kutero, bwenzi labwino liyenera kukumbutsa mnzakeyo mfundo za Yehova. (1 Akor. 7:39) Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati mutaona kuti mnzanu amene sali pabanja wayamba chibwenzi ndi munthu wosakhulupirira? Kodi mungangokhala chete osamudzudzula poopa kuti ubwenzi wanu utha? Nanga ngati mnzanuyo atanyalanyaza uphungu wanu, kodi mungatani? Bwenzi labwino lingapite kwa abusa achikondi kuti athandize mnzake amene wapatuka panjira mosazindikira. Pamafunika kulimba mtima kuti munthu achite zimenezo. N’zoona kuti ubwenzi ungasokonezeke ndi zimenezi. Koma ubwenzi wozikidwa pa kukonda Yehova sungasokonezeke kwa nthawi yaitali.

21. Kodi tonsefe tingachite chiyani nthawi zina, koma n’chifukwa chiyani tiyenera kukhala ndi mabwenzi apamtima mumpingo?

21 Werengani Akolose 3:13, 14. Nthawi zina, tingachite zinthu zimene zingapangitse mabwenzi athu kukhala ndi ‘chifukwa choti adandaule’ za ife, ndipo nawonso nthawi zina angachite kapena kunena zinthu zimene sizingatisangalatse. Yakobe analemba kuti: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yak. 3:2) Koma chimene chimachititsa kuti tikhalebe pa ubwenzi ndi munthu, ndi kukhululukirana ndi mtima wonse mosaganizira za kuchuluka kwa nthawi zimene talakwirana. Kuti ubwenzi ukhale wolimba, m’pofunika kwambiri kuti tizilankhulana momasuka ndi kukhululukirana ndi mtima wonse. Tikamasonyeza chikondi choterocho, chidzakhaladi “chomangira umodzi changwiro.”

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tipeze mabwenzi abwino?

• Kodi ndi nthawi iti pamene mungafunike kuthetsa ubwenzi?

• Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhalebe ndi mabwenzi apamtima?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 18]

Kodi maziko a ubwenzi wokhalitsa wa Rute ndi Naomi anali chiyani?

[Chithunzi patsamba 19]

Kodi mumachereza ena nthawi ndi nthawi?