Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Ndinu Mabwenzi Anga’

‘Ndinu Mabwenzi Anga’

‘Ndinu Mabwenzi Anga’

“Mukhalabe mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.”​—YOH. 15:14.

1, 2. (a) Kodi mabwenzi a Yesu kale anali ndi moyo wosiyanasiyana wotani? (b) N’chifukwa chiyani kukhala mabwenzi a Yesu kuli kofunika kwambiri?

YESU anali m’chipinda chapamwamba ku Yerusalemu limodzi ndi amuna angapo. Amunawa kale anali ndi moyo wosiyanasiyana. Petulo ndi m’bale wake Andireya, anali asodzi. Mateyo anali wokhometsa msonkho, ndipo Ayuda anali kuipidwa kwambiri ndi anthu ogwira ntchito imeneyi. Ena mwa iwo, monga Yakobe ndi Yohane, mosakayikira anadziwana ndi Yesu kuyambira ali ana. Koma ena, monga Natanayeli, mwina anangomudziwa kwa zaka zochepa. (Yoh. 1:43-50) Komabe, onse amene analipo usiku wapadera wa Pasika umenewo ku Yerusalemu, sanali kukayika ngakhale pang’ono kuti Yesu ndiye Mesiya wolonjezedwa, Mwana wa Mulungu wamoyo. (Yoh. 6:68, 69) Chotero ayenera kuti anakhudzidwa mtima kwambiri kumva Yesu akuwauza kuti: “Ndakutchani mabwenzi, chifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani.”​—Yoh. 15:15.

2 Mawu amene Yesu anauza atumwi ake okhulupirika amenewo amagwiranso ntchito makamaka kwa Akhristu onse odzozedwa masiku ano, ndipo kuwonjezera pa iwowo, tingati amagwiranso ntchito kwa anzawo a “nkhosa zina.” (Yoh. 10:16) Kaya tinali ndi moyo wotani kale, tikhoza kukhala mabwenzi a Yesu. Kukhala mabwenzi a Yesu n’kofunika kwambiri chifukwa tikakhala mabwenzi ake, timakhalanso mabwenzi a Yehova. Ndipotu sitingathe kuyandikira kwa Yehova popanda kuyandikira kaye kwa Khristu. (Werengani Yohane 14:6, 21.) Choncho, kodi tiyenera kuchita chiyani kuti tikhale mabwenzi a Yesu, ndiponso kuti ubwenziwo upitirire? Tisanakambirane nkhani yofunika imeneyi, tiyeni tione kaye mmene Yesu analili bwenzi labwino ndiponso zimene tingaphunzire ku chitsanzo chake. Tionanso zimene tingaphunzire pa zimene ophunzira ake anachita atadziwa kuti Yesu anali bwenzi lawo.

Chitsanzo cha Yesu cha Mmene Tingakhalire Mabwenzi Abwino

3. Kodi Yesu anali kudziwika monga munthu wotani?

3 Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Akukonda wolemera achuluka.” (Miy. 14:20) Mawu amenewa akufotokoza bwino zimene anthu opanda ungwiro amakonda kuchita. Amakonda kupalana ubwenzi ndi munthu chifukwa cha zimene angapezepo osati chifukwa cha zimene angamupatse munthuyo. Yesu analibe khalidwe loipa lotereli. Sanali kukopeka ndi ndalama kapena kutchuka kwa munthu. N’zoona kuti Yesu anakonda wolamulira wachinyamata wolemera ndipo anamupempha kuti akhale wotsatira wake. Koma Yesu anauza mnyamatayo kuti akagulitse zimene anali nazo ndipo azipereke kwa osauka. (Maliko 10:17-22; Luka 18:18, 23) Yesu anali kudziwika monga munthu amene anali bwenzi la anthu osauka ndi onyozeka, osati munthu wokonda kugwirizana ndi anthu olemera ndi otchuka.​—Mat. 11:19.

4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mabwenzi a Yesu anali kulakwitsa zinthu nthawi zina?

4 N’zoona kuti mabwenzi a Yesu anali kulakwitsa zinthu nthawi zina. Pa nthawi ina Petulo analephera kuona zinthu mwauzimu. (Mat. 16:21-23) Yakobe ndi Yohane anasonyeza mtima wofuna kukhala patsogolo pa anzawo pamene anapempha Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wake. Zimene anachitazi zinakwiyitsa atumwi enawo, ndipo nkhani yoti wamkulu ndani inali kuyambitsa mikangano nthawi zambiri. Koma Yesu anayesetsa kukonza maganizo a mabwenzi akewo moleza mtima ndipo sanawapsere mtima kapena kutopa nawo.​—Mat. 20:20-28.

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anakhalabe bwenzi la atumwi ake ambiri? (b) N’chifukwa chiyani Yesu anathetsa ubwenzi wake ndi Yudasi?

5 Yesu anakhalabe bwenzi la amuna opanda ungwiro amenewa. Sikuti iye anachita zimenezi chifukwa chakuti anali wolekerera zinthu kwambiri kapena sanali kuona zolakwa zawo. M’malomwake, iye anaika maganizo ake makamaka pa zolinga zawo zabwino ndiponso makhalidwe awo abwino. Mwachitsanzo, Petulo, Yakobe ndi Yohane anagona tulo m’malo mothandiza Yesu pa nthawi yake yovuta kwambiri. M’pomveka kuti Yesu anakhumudwa ndi zimene anachitazo. Ngakhale zinali choncho, iye anadziwa kuti iwo analibe zolinga zoipa, ndipo anati: “Inde, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”​—Mat. 26:41.

6 Koma Yesu anathetsa ubwenzi wake ndi Yudasi Isikarioti. Yudasi anali kunamizira kuti anali bwenzi la Yesu. Komabe, Yesu anadziwa kuti Yudasiyo, amene kale anali bwenzi lake lapamtima, analola kuti mtima wake uipitsidwe. Popeza Yudasi anakhala bwenzi la dziko, anadzisandutsa mdani wa Mulungu. (Yak. 4:4) Choncho Yesu anali atamuthamangitsa kale Yudasi pa nthawi imene anauza atumwi 11 okhulupirika otsalawo kuti anali bwenzi lawo.​—Yoh. 13:21-35.

7, 8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti anali kukonda mabwenzi ake?

7 Yesu sanali kuganiza kwambiri za zolakwa za mabwenzi ake okhulupirika koma ankawafunira zabwino. Mwachitsanzo, anapemphera kwa Atate ake kuti awateteze m’mayesero awo. (Werengani Yohane 17:11.) Yesu anasonyeza kuti anali kumvetsa kuti ophunzira ake ankatopa. (Maliko 6:30-32) Ndiponso iye sanafune kumangowauza maganizo ake nthawi zonse. Koma anafunanso kumva maganizo awo.​Mat. 16:13-16; 17:24-26.

8 Yesu anagwiritsa ntchito moyo wake kuthandiza mabwenzi ake, mpaka kufika powafera. N’zoona kuti iye anadziwa kuti ayenera kupereka moyo wake kuti akwaniritse lamulo lokhudza chilungamo cha Atate ake. (Mat. 26:27, 28; Aheb. 9:22, 28) Koma ngakhale ndi choncho, Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha chikondi. Iye anati: “Palibe amene ali ndi chikondi choposa ichi, chakuti wina n’kupereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake.”​—Yoh. 15:13.

Kodi Ophunzira Anachita Chiyani Atadziwa Kuti Yesu Anali Bwenzi Lawo?

9, 10. Kodi anthu anachita chiyani chifukwa cha kuwolowa manja kwa Yesu?

9 Yesu anasonyeza chikondi ndipo anapereka mowolowa manja nthawi yake ndi zinthu zimene anali nazo. Chifukwa cha zimenezi, anthu anali kumukonda ndipo nawonso anamupatsa zinthu zosiyanasiyana mosangalala. (Luka 8:1-3) Kuchokera pa zimene zinamuchitikira iyeyo, Yesu anatha kunena kuti: “Khalani opatsa, inunso anthu adzakupatsani. Adzakhuthulira m’matumba anu muyeso wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mukupimira ena, iwonso adzakupimirani womwewo.”​—Luka 6:38.

10 Inde, panali anthu ena amene anakhala mabwenzi a Yesu pongofuna kupezako kenakake. Mabwenzi abodzawa anamuthawa Yesu pamene sanamvetse mfundo inayake imene iye ananena. M’malo momukhulupirira Yesu, iwo anafulumira kuganiza molakwika ndipo anamusiya. Mosiyana ndi anthu amenewa, atumwi anali okhulupirika. Nthawi zambiri iwo ndi Khristu anakumana ndi mavuto pa ubwenzi wawo, koma iwo anayesetsa kumuthandiza pa nthawi zabwino ndi zovuta zomwe. (Werengani Yohane 6:26, 56, 60, 66-68.) Usiku wake womaliza padziko lapansi ali munthu, Yesu anayamikira kwambiri mabwenzi akewo chifukwa cha zimene anamuchitira. Anati: “Inu ndinu amene mwakhalabe ndi ine m’mayesero anga.”​—Luka 22:28.

11, 12. Kodi Yesu anawalimbikitsa motani ophunzira ake, ndipo iwo anachita chiyani atalimbikitsidwa?

11 Yesu atawayamikira ophunzira ake chifukwa cha kukhulupirika kwawo, sipanatenge nthawi kuti ophunzirawo amuthawire. Kwakanthawi, kuopa anthu kunakula mwa iwo kuposa chikondi chawo pa Khristu. Apanso, Yesu anawakhululukira. Yesuyo atafa ndi kuukitsidwa, anaonekera kwa iwo ndipo anawatsimikizira kuti anali bwenzi lawobe. Komanso, anawapatsa ntchito yopatulika, yoti apange ophunzira “mwa anthu a mitundu yonse” ndiponso akhale mboni zake “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mat. 28:19; Mac. 1:8) Kodi ophunzirawo anachita chiyani atamva zimenezi?

12 Ophunzirawo anagwira ntchito yofalitsa uthenga wa Ufumu ndi mtima wawo wonse. Mothandizidwa ndi mzimu woyera wa Yehova, iwo sanachedwe kudzadza Yerusalemu ndi chiphunzitso chawo. (Mac. 5:27-29) Iwo anapitirizabe kumvera lamulo la Yesu lakuti apange ophunzira ngakhale pamene anaopsezedwa kuti aphedwa. Patangopita zaka makumi ochepa kuchokera pamene ophunzirawo analandira lamulo la Yesu limeneli, mtumwi Paulo analemba kuti uthenga wabwino unali utalalikidwa “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Ndithu, ophunzirawa anasonyeza kuti ubwenzi wawo ndi Yesu unali wofunika kwambiri.

13. Kodi zimene Yesu anaphunzitsa zinakhudza ophunzira ake m’njira zotani?

13 Anthu amene anakhala ophunzira a Yesu anatsatira zimene Yesu anawaphunzitsa ndi kusintha moyo wawo. Kuti achite zimenezi, ambiri mwa iwo anafunika kusintha kwambiri khalidwe lawo ndi umunthu wawo. Anthu ena amene tsopano anali ophunzira, kale anali amuna ogonana ndi amuna anzawo, achigololo, zidakwa ndiponso akuba. (1 Akor. 6:9-11) Ena anafunika kusintha mmene anali kuonera anthu a fuko lina. (Mac. 10:25-28) Koma iwo anamverabe Yesu. Anavula umunthu wawo wakale n’kuvala watsopano. (Aef. 4:20-24) Iwo anafika podziwa bwino “maganizo a Khristu.” Anamvetsa bwino kaganizidwe kake ndi kachitidwe kake ka zinthu, ndipo anatsanzira zimenezi.​—1 Akor. 2:16.

Kukhala Mabwenzi a Khristu Masiku Ano

14. Kodi Yesu analonjeza kuti adzachita chiyani m’nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu”?

14 Ambiri mwa Akhristu oyambirirawo anakhalapo limodzi ndi Yesu kapena anamuona ataukitsidwa. Ifeyo tilibe mwayi umenewo. Choncho, kodi tingakhale bwanji mabwenzi a Khristu? Njira imodzi ndiyo kumvera malangizo amene timapatsidwa ndi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, yemwe ndi abale ake a Yesu odzozedwa amene akadali ndi moyo padziko lapansi pano. Yesu analonjeza kuti m’nthawi ya “mapeto a dongosolo lino la zinthu,” adzaika kapoloyu kuti aziyang’anira “zinthu zake zonse.” (Mat. 24:3, 45-47) Masiku ano, anthu ambiri amene akufuna kukhala mabwenzi a Khristu sali m’gulu la kapoloyu. Kodi zimene amachita akalandira malangizo ochokera kwa gulu la kapolo wokhulupirika, zimakhudza bwanji ubwenzi wawo ndi Khristu?

15. Kodi n’chiyani chidzachititse kuti munthu aikidwe m’gulu la nkhosa kapena la mbuzi?

15 Werengani Mateyo 25:31-40. Yesu anati anthu amene amapanga gulu la kapolo wokhulupirika, ndi abale ake. Mu fanizo lonena za kulekanitsa nkhosa ndi mbuzi, Yesu anasonyeza momveka bwino kuti zimene timachitira abale ake, amaziona ngati kuti tikuchitira iyeyo. Ndipo anati chinthu chimene chidzasiyanitse nkhosa ndi mbuzi, ndi zimene munthu anachitira ‘aang’ono mwa abale ake.’ Chotero, njira yaikulu imene anthu omwe ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi amasonyezera kuti akufuna kukhala mabwenzi a Khristu, ndiyo kuthandiza gulu la kapolo wokhulupirika.

16, 17. Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife mabwenzi a abale a Khristu?

16 Ngati muli ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu, kodi mungasonyeze bwanji kuti ndinu mabwenzi a abale ake a Khristu? Tiyeni tione njira zitatu zokha. Njira yoyamba ndi kugwira ntchito yolalikira ndi mtima wonse. Khristu analamula abale ake kuti alalikire uthenga wabwino padziko lonse lapansi. (Mat. 24:14) Koma abale a Khristu amene atsala padziko lapansi masiku ano angavutike kukwanitsa udindo umenewo atapanda kuthandizidwa ndi anzawo a nkhosa zina. Choncho tingati nthawi iliyonse imene anthu a nkhosa zina akugwira ntchito yolalikira, ndiye kuti akuthandiza abale a Khristu kukwanitsa ntchito yawo yopatulika imeneyo. Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, limodzi ndi Khristu, amayamikira kwambiri akamaona a nkhosa zina akuchita zimenezi posonyeza kuti ndi mabwenzi awo.

17 Njira yachiwiri imene a nkhosa zina amathandizira abale a Khristu, ndiyo kupereka ndalama zawo kuti zithandize pa ntchito yolalikira. Yesu analimbikitsa otsatira ake kuti adzipezere mabwenzi pogwiritsa ntchito “chuma chosalungama.” (Luka 16:9) Sikuti tingagule ubwenzi ndi Yesu kapena Yehova. Koma tikamagwiritsa ntchito katundu wathu popititsa patsogolo zinthu za Ufumu, timasonyeza kuti ndife mabwenzi ndiponso timasonyeza chikondi chathu, osati ndi mawu okha, koma “mwa zochita ndi choonadi.” (1 Yoh. 3:16-18) Timapereka thandizo la ndalama loterolo tikamagwiritsa ntchito ndalama zathu popita kukagwira ntchito yolalikira, tikamapereka ndalama zathu kuti zithandize pa ntchito yomanga ndi kukonzanso malo athu ochitira misonkhano, ndiponso tikamapereka ndalama kuti zipite ku thumba la ntchito yolalikira ya padziko lonse. Kaya ndalama zimene taperekazo n’zochepa kapena zambiri, Yehova ndi Yesu amayamikira tikamapereka mokondwa.​—2 Akor. 9:7.

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malangizo ochokera m’Baibulo amene akulu amapereka?

18 Njira yachitatu imene tonsefe timasonyezera kuti ndife mabwenzi a Khristu, ndiyo kutsatira malangizo amene timapatsidwa ndi akulu mumpingo. Amuna amenewa amaikidwa ndi mzimu woyera motsogozedwa ndi Khristu. (Aef. 5:23) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Muzimvera amene akutsogolera pakati panu ndipo muziwagonjera.” (Aheb. 13:17) Nthawi zina, zimativuta kuti timvere malangizo ochokera m’Baibulo amene akulu mumpingo mwathu amatipatsa. N’zachidziwikire kuti timadziwa zofooka zawo, ndipo zimenezi zingachititse kuti tiziona molakwika uphungu wawo. Komabe Khristu, yemwe ndi Mutu wa mpingo, amasangalala kugwiritsa ntchito amuna opanda ungwiro amenewa. Choncho mmene timaonera udindo wawo zimakhudzanso ubwenzi wathu ndi Khristu. Tikamanyalanyaza zofooka za akulu n’kumatsatira mokondwa malangizo awo, timasonyeza kuti timakonda Khristu.

Kumene Tingapeze Mabwenzi Abwino

19, 20. Kodi mumpingo tingapezemo chiyani, ndipo tidzakambirana chiyani munkhani yotsatira?

19 Yesu akupitirizabe kutisamalira. Amachita zimenezi kudzera mwa akulu achikondi amene amatiyang’anira, komanso potipatsa amayi, abale, ndi alongo auzimu mumpingo. (Werengani Maliko 10:29, 30.) Pamene munayamba kusonkhana ndi gulu la Yehova, kodi achibale anu anatani? Zingakhale zosangalatsa ngati anakulimbikitsani pamene munali kuyesetsa kuyandikira kwa Mulungu ndi Khristu. Koma Yesu anachenjeza kuti zingachitike kuti ‘adani a munthu angakhale am’banja lake lenilenilo.’ (Mat. 10:36) N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti mumpingo tingapezemo anthu amene angamamatire kwambiri kwa ife kuposa m’bale wathu weniweni.​—Miy. 18:24.

20 Moni amene Paulo anapereka pamapeto pa kalata yake yopita kumpingo wa ku Roma, akusonyeza kuti iye anali ndi mabwenzi ambiri apamtima. (Aroma 16:8-16) Mtumwi Yohane anamaliza kalata yake yachitatu ndi mawu akuti: “Undiperekere moni kwa mabwenzi mmodzi ndi mmodzi.” (3 Yoh. 14) Zikuoneka kuti nayenso anali ndi mabwenzi ambiri okhalitsa. Kodi tingatani kuti tiyambitse ndi kulimbitsa ubwenzi wabwino ndi abale ndi alongo athu auzimu, potsanzira chitsanzo cha Yesu ndi cha ophunzira oyambirira? M’nkhani yotsatira tidzakambirana funso limeneli.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yokhala bwenzi labwino?

• Kodi ophunzira anachita chiyani atadziwa kuti Yesu anali bwenzi lawo?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife mabwenzi a Khristu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 14]

Yesu ankafuna kudziwa maganizo a mabwenzi ake

[Zithunzi patsamba 16]

Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikufuna kukhala mabwenzi a Khristu?