Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Yakani ndi Mzimu”

“Yakani ndi Mzimu”

“Yakani ndi Mzimu”

“Musakhale aulesi pantchito yanu. Yakani ndi mzimu. Tumikirani Yehova monga akapolo.”​—AROMA 12:11.

1. N’chifukwa chiyani Aisiraeli ankapereka nsembe zanyama ndi nsembe zamtundu wina?

YEHOVA amayamikira nsembe zimene atumiki ake amamupatsa mwakufuna kwawo posonyeza kuti amamukonda ndiponso kuti amagonjera chifuniro chake. Kale, iye anali kulandira nsembe zanyama zosiyanasiyana ndi nsembe zamtundu wina. Aisiraeli anali kupereka nsembe zimenezi motsatira Chilamulo cha Mose pofuna kuti akhululukidwe machimo awo ndiponso pofuna kusonyeza kuyamikira kwawo. Mumpingo wachikhristu, Yehova satipempha kuti tizipereka nsembe zoterezi. Komabe, mu chaputala 12 cha kalata imene mtumwi Paulo analembera Akhristu a ku Roma, iye anasonyeza kuti tikufunikirabe kumapereka nsembe. Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.

Nsembe Yamoyo

2. Kodi Akhristufe tiyenera kukhala ndi moyo wotani ndipo timafunika kutani kuti tichite zimenezi?

2 Werengani Aroma 12:1, 2. Kumayambiriro kwa kalata yake, Paulo anafotokoza momveka bwino kuti Akhristu odzozedwa, kaya akhale Ayuda kapena Akunja, anali kuonedwa kuti ndi olungama pamaso pa Mulungu chifukwa cha chikhulupiriro, osati ntchito. (Aroma 1:16; 3:20-24) Mu chaputala 12, Paulo anafotokoza kuti Akhristu ayenera kusonyeza kuti akuyamikira zimenezi mwa kukhala moyo wodzimana. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kusintha maganizo athu. Tonsefe tili pansi pa “chilamulo cha uchimo ndi cha imfa” chifukwa cha kupanda ungwiro kumene tinabadwa nako. (Aroma 8:2) Motero tiyenera kusandulika, ‘kukhala atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo athu,’ mwa kusintha kwambiri mitima yathu. (Aef. 4:23) Sizingatheke kuti munthu asinthe kwambiri choncho popanda thandizo la Mulungu ndi mzimu wake. Pamafunikanso kuti ifeyo tichite khama kwambiri pogwiritsa ntchito ‘luntha lathu la kulingalira.’ Zimenezi zikutanthauza kuti tiyenera kuyesetsa kuti ‘tisamatengere nzeru za dongosolo lino la zinthu,’ limene limatsatira makhalidwe onyansa, zosangalatsa zoipa ndi maganizo opotoka.​—Aef. 2:1-3.

3. Kodi n’chifukwa chiyani timachita ntchito zachikhristu?

3 Paulo akutiuzanso kuti tizigwiritsa ntchito “luntha la kulingalira” kuti titsimikizire tokha “chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro.” Kodi n’chifukwa chiyani timawerenga Baibulo tsiku lililonse? N’chifukwa chiyani timasinkhasinkha zimene tawerenga, kupemphera, kupita kumisonkhano ya mpingo, ndiponso kulalikira nawo uthenga wabwino wa Ufumu? Kodi n’chifukwa chakuti akulu amatiuza kuti tizichita zimenezi? N’zoona kuti timayamikira ngati akulu atikumbutsa kuchita zimenezi. Koma chifukwa chachikulu chimene timachitira ntchito zachikhristu ngati zimene tatchulazi, n’chakuti mzimu wa Mulungu umatilimbikitsa kuchita zinthu zosonyeza kuti timakonda Yehova kuchokera pansi pa mtima. Komanso, ifeyo patokha ndife otsimikiza kuti tikamachita zinthu zimenezi, ndiye kuti tikuchita chifuniro cha Mulungu. (Zek. 4:6; Aef. 5:10) Timasangalala kwambiri ndiponso timakhala okhutira podziwa kuti tikamakhala moyo umene ulidi wachikhristu, timakhala ovomerezeka kwa Mulungu.

Mphatso Zosiyanasiyana

4, 5. Kodi akulu achikhristu ayenera kugwiritsa ntchito motani mphatso zawo?

4 Werengani Aroma 12:6-8, 11. Paulo anafotokoza kuti “tili ndi mphatso zosiyanasiyana mogwirizana ndi kukoma mtima kwa m’chisomo kumene tinapatsidwa.” Zina mwa mphatso zimene Paulo anatchula, monga kuchenjeza ndi kutsogolera, zikukhudza makamaka akulu achikhristu, amene akulangizidwa kuti “atsogolere mwakhama.”

5 Paulo anati khama lomwelo liyenera kuonekeranso pamene oyang’anira akutumikira monga aphunzitsi ndiponso pamene akuchita “utumiki” wawo. Tikawerenga malemba apatsogolo ndi apambuyo pa lemba limeneli, zikuoneka kuti “utumiki” umene Paulo anali kunena pano ndi umene umachitika mumpingo, ndipo mpingowo ndiwo “thupi limodzi.” (Aroma 12:4, 5) Utumiki umenewo ndi wofanana ndi umene unatchulidwa pa Machitidwe 6:4, pamene atumwi ananena kuti: “Ife tidzipereka ndithu pa kupemphera ndi pa utumiki wokhudza mawu a Mulungu.” Kodi akulu achikhristu amachita bwanji utumiki umenewu? Iwo amagwiritsa ntchito mphatso zawo polimbikitsa anthu mumpingo. Ayenera kulangiza ndi kutsogolera mpingo mwakhama pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu. Kuti achite bwino ntchito imeneyi, ayenera kuphunzira ndi kupemphera kwambiri, kuchita kafukufuku, kuphunzitsa ndi kuweta nkhosa. Akulu akamachita zonsezi, amasonyeza kuti amaikirapo mtima ‘pochitabe utumikiwo.’ Oyang’anira ayenera kugwiritsa ntchito mphatso zawo ndi mtima wonse ndiponso ayenera kusamalira nkhosa “mokondwa.”​—Aroma 12:7, 8; 1 Pet. 5:1-3.

6. Kodi tingatsatire bwanji malangizo amene ali pa Aroma 12:11, lomwe ndi lemba lotsogolera m’nkhani ino?

6 Paulo anapitiriza kuti: “Musakhale aulesi pantchito yanu. Yakani ndi mzimu. Tumikirani Yehova monga akapolo.” Ngati tikuona kuti tayamba kuchita ulesi ndi utumiki wathu, tiyenera kuonanso bwinobwino mmene tikumaphunzirira. Tingafunikenso kupemphera mwakhama kwambiri ndiponso pafupipafupi kuti Yehova atipatse mzimu wake. Mzimu umenewu ungatithandize kuti tisakhale ofunda ndiponso kuti tiyambirenso kukhala achangu. (Luka 11:9, 13; Chiv. 2:4; 3:14, 15, 19) Mzimu woyera unapatsa mphamvu Akhristu oyambirira kuti alankhule za “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Mac. 2:4, 11) Ukhozanso kutithandiza ifeyo kuti tikhale achangu mu utumiki, ndiponso kuti ‘tiyake ndi mzimu.’

Kudzichepetsa Ndiponso Kudziwa Malire Athu

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kutumikira modzichepetsa ndiponso kudziwa malire athu?

7 Werengani Aroma 12:3, 16. Mphatso zimene tili nazo, tili nazo chifukwa cha “kukoma mtima kwa m’chisomo” kwa Yehova. Paulo ananena palemba lina kuti: “Kukhala kwathu oyenerera bwino lomwe kuchokera kwa Mulungu.” (2 Akor. 3:5) Chotero sitiyenera kudzitama. Tiyenera kuzindikira modzichepetsa kuti zilizonse zimene zatiyendera bwino pa utumiki wathu, zachitika chifukwa cha madalitso a Mulungu, osati chifukwa chakuti ndife odziwa bwino zinthu. (1 Akor. 3:6, 7) Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, Paulo anati: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire koposa mmene muyenera kudziganizira.” N’zoona kuti timafunika kudziona kuti ndife ofunika ndiponso kukhala osangalala ndi okhutira pamene tikuchita ntchito ya Ufumu. Komabe, kudziwa malire athu kungatithandize kuti tisamangoumirira maganizo athu. M’malomwake, tiyenera ‘kuganiza m’njira yakuti tikhale anthu oganiza bwino.’

8. Kodi tingatani kuti tipewe ‘kudziyesa anzeru’?

8 Kungakhale kupusa kudzitama chifukwa cha zinthu zimene takwanitsa kuchita. Mulungu ndiye “amakulitsa.” (1 Akor. 3:7) Paulo anati Mulungu wagawira munthu aliyense mumpingo “chikhulupiriro.” M’malo modziona kuti ndife apamwamba, tiyenera kuonanso zinthu zimene ena akuchita mogwirizana ndi chikhulupiriro chimene ali nacho. Paulo ananenanso kuti: “Muziona ena mmene inuyo mumadzionera nokha.” M’kalata yake ina, mtumwiyu anatiuza kuti ‘tisachite kanthu kalikonse ndi mzimu wandewu kapena wodzikuza, koma modzichepetsa, tikumaona ena kukhala otiposa.’ (Afil. 2:3) Pamafunika kudzichepetsa kwenikweni ndi kuganizira nkhani imeneyi mozama kuti tiziona kuti m’bale ndi mlongo wathu aliyense ndi wotiposa mwanjira inayake. Kudzichepetsa kungatithandize kuti ‘tisadziyese anzeru.’ Ngakhale kuti zimene enafe tikuchita zimaonekera kwambiri kwa anthu chifukwa chakuti tili ndi maudindo apadera autumiki, tonse tingapeze chimwemwe pochita ntchito zotsika, kapena kuti zooneka ngati zonyozeka zimene nthawi zambiri anthu sazizindikira n’komwe.​—1 Pet. 5:5.

Kugwirizana Mumpingo

9. N’chifukwa chiyani Paulo anayerekezera Akhristu obadwa ndi mzimu, ndi ziwalo za thupi?

9 Werengani Aroma 12:4, 5, 9, 10. Paulo anayerekezera Akhristu odzozedwa ndi ziwalo za thupi zimene zikutumikira mogwirizana pansi pa Khristu, amene ali Mutu wawo. (Akol. 1:18) Iye anakumbutsa Akhristu obadwa ndi mzimu kuti thupi limakhala ndi ziwalo zambiri zimene zimagwira ntchito zosiyanasiyana ndiponso kuti iwowo, ‘ngakhale kuti ndi ambiri, ali thupi limodzi mwa Khristu.’ Pamfundo yomweyi, Paulo analimbikitsa Akhristu odzozedwa a ku Efeso kuti: “Tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzera m’chikondi, pansi pa iye amene ali mutu, Khristu. Kuchokera kwa iye, thupi lonselo limakula podzimanga lokha mwachikondi, pokhala lolumikizika bwino ndi logwirizana mwa mfundo iliyonse yogwira ntchito yake yofunikira, malinga ndi ntchito yoyenerera ya chiwalo chilichonse.”​—Aef. 4:15, 16.

10. Kodi a “nkhosa zina” ayenera kugonjera ndani?

10 Ngakhale kuti a “nkhosa zina” sali mbali ya thupi la Khristu, akhoza kuphunzira zambiri pa fanizo limeneli. (Yoh. 10:16) Paulo ananena kuti Yehova “anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi a [Khristu], namuika mutu wa zinthu zonse kaamba ka mpingo.” (Aef. 1:22) Masiku ano, a nkhosa zina ali mbali ya “zinthu zonse” zimene Yehova anaziika pansi pa Mwana wake. Alinso mbali ya “zinthu” zimene Khristu waziika m’manja mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mat. 24:45-47) Choncho anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala padziko lapansi ayenera kuona Khristu monga Mutu wawo. Ayeneranso kugonjera kapolo wokhulupirika ndi wanzeru limodzi ndi Bungwe Lolamulira, komanso amuna amene aikidwa kukhala oyang’anira mumpingo. (Aheb. 13:7, 17) Kuchita zimenezi kumabweretsa mgwirizano mumpingo.

11. Kodi mgwirizano wathu umazikidwa pa chiyani, nanga Paulo anapereka malangizo enanso otani?

11 Mgwirizano umenewo umazikidwa pa chikondi, chimene ndi “chomangira umodzi changwiro.” (Akol. 3:14) M’chaputala 12 cha Aroma, Paulo anagogomezera mfundo imeneyi ponena kuti chikondi chathu “chisakhale cha chiphamaso” ndiponso kuti ‘posonyezana chikondi chaubale tikhale ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake.’ Kuchita zimenezi kumathandiza kuti tizilemekezana. Mtumwiyu ananena kuti: “Posonyezana ulemu wina ndi mnzake, khalani patsogolo.” Komabe, tisaganize kuti chikondi chimatanthauza kumangolekerera zinthu. Tiyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti mpingo ukhalebe woyera. Popereka malangizo ake okhudza chikondi, Paulo anapitiriza kuti: “Nyansidwani ndi choipa, gwiritsitsani chabwino.”

Khalani Ochereza

12. Pa nkhani yochereza ena, kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Akhristu a ku Makedoniya anachita?

12 Werengani Aroma 12:13. Chifukwa chokonda abale athu, timafunitsitsa ‘kugawana ndi oyerawo malinga ndi zosowa zawo’ ndiponso mogwirizana ndi zimene tingakwanitse kuchita. Ngakhale titakhala osauka, tikhoza kugawanabe ndi ena zinthu zimene tili nazo. Polemba kalata kwa Akhristu a ku Makedoniya, Paulo anati: “Pamene iwo anali pakuyesedwa kwakukulu chifukwa cha mavuto, chimwemwe chawo chachikulu ndi umphawi wawo waukulu zinachititsa kuwolowa manja kwawo kochulukako kuwirikiza. Pakuti anachita malinga ndi zimene akanatha, inde, komanso ndikuwachitira umboni kuti anachita ngakhale zoposa pamenepo, napitiriza kutipempha mochokera pansi pa mtima ndi mochonderera kwambiri, kuti tiwapatse mwayi wopereka nawo mphatso za chifundo ndi kutinso achite nawo utumiki wothandiza oyerawo [ku Yudeya].” (2 Akor. 8:2-4) Ngakhale kuti Akhristu a ku Makedoniyawo anali osauka, iwo anali owolowa manja kwambiri. Anaona kuti ndi mwayi wapadera kugawana zimene anali nazo ndi abale awo a ku Yudeya amene anali osowa.

13. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘tikhale ochereza’?

13 Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “khalani ochereza,” amanenanso za kusadikira kuti wina achite kutipempha. Baibulo lina limamasulira mawu amenewa kuti, “muzifunafuna mipata yocherezera ena.” (The New Jerusalem Bible) Nthawi zina timasonyeza kuti ndife ochereza poitana munthu kuti abwere kudzadya chakudya kunyumba kwathu, ndipo ngati tikuchita zimenezi chifukwa cha chikondi, ndiye kuti tikuchita bwino kwambiri. Koma ngati titangoganiza mozamirapo pang’ono, tikhoza kupeza njira zina zambiri zocherezera anzathu. Mwachitsanzo, ngati sitingakwanitse kuitana munthu kunyumba kwathu chifukwa choti ndife odwaladwala kapena tilibe ndalama, tikhoza kumuitana kuti tidzangocheza basi mwinanso kungomuphikira chakudya chilichonse chimene tili nacho. Imeneyi ndi njira inanso yosonyezera kuti ndife ochereza alendo.

14. (a) Kodi mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “ochereza” amachokera ku mawu awiri ati? (b) Tikakhala mu utumiki, kodi tingasonyeze bwanji kuti timadera nkhawa anthu achilendo?

14 Kukhala ochereza kumadalira mmene timaonera anthu ena. Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “ochereza,” amachokera ku mawu awiri amene amatanthauza “chikondi” ndi “mlendo.” Kodi anthu achilendo kapena ochokera kumayiko ena timawaona bwanji? Akhristu amene amayesetsa kuphunzira chinenero china kuti azilalikira uthenga wabwino kwa anthu achilendo amene asamukira m’gawo la mpingo wawo, ali m’gulu la anthu ochereza. Komabe, mwina ambiri a ife sitingakwanitse kuphunzira chinenero china. Ngakhale zili choncho, tonsefe tikhoza kuthandiza anthu achilendo pogwiritsa ntchito bwino kabuku kathu kakuti Uthenga Wabwino wa Anthu a Mitundu Yonse, kamene kali ndi uthenga wa m’Baibulo m’zinenero zambiri. Kodi ndi zinthu zosangalatsa zotani zimene mwakumanapo nazo chifukwa chogwiritsa ntchito kabuku kameneka mu utumiki?

Muziganizirana

15. Kodi Yesu anasonyeza bwanji mmene tingatsatirire malangizo amene ali pa Aroma 12:15?

15 Werengani Aroma 12:15. Mfundo yaikulu ya Paulo m’vesi limeneli ndi yakuti: Muziganizirana. Tiyenera kuyesetsa kumadziwa ndiponso kukhudzidwa ndi zimene zikuchitikira anthu anzathu, kaya akusangalala kapena akumva chisoni. Ngati tikuyaka ndi mzimu, ena akamasangalala kapena akamamva chisoni, savutika kuona kuti ifenso tikumva chimodzimodzi. Pamene ophunzira 70 a Khristu anabwera kuchokera ku ntchito yapadera yolalikira, n’kufotokoza zinthu zimene zinawachitikira pamene anali kugwira ntchitoyo, Yesu “anakondwera kwambiri mwa mzimu woyera.” (Luka 10:17-21) Anasangalala nawo limodzi. Koma pamene mnzake Lazaro anamwalira, Yesu ‘analira ndi anthu amene anali kulira.’​—Yoh. 11:32-35.

16. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira ena, ndipo ndani makamaka amene ayenera kuchita zimenezi?

16 Nafenso tiyenera kutsatira chitsanzo cha Yesu choganizira ena. Mkhristu mnzathu akamasangalala, tiyenera kusangalalira naye limodzi. Komanso, tiyenera kukhudzidwa abale ndi alongo athu akamakumana ndi mavuto ndiponso akakhala ndi nkhawa. Nthawi zambiri tikhoza kutsitsimutsa kwambiri okhulupirira anzathu amene akuvutika maganizo. Tingachite zimenezi mwa kuwamvetsera modekha ndi mwachifundo pamene iwo akutiuza mavuto awo. Nthawi zina tikhoza kukhudzidwa mtima kwambiri chifukwa chowamvera chifundo moti tingafike mpaka potulutsa misozi. (1 Pet. 1:22) Makamaka akulu ayenera kutsatira malangizo amene Paulo anapereka pa nkhani yoganizira ena.

17. Kodi taphunzira chiyani m’mavesi amene takambirana a mu chaputala 12 cha Aroma, nanga mu nkhani yotsatira tidzakambirana chiyani?

17 Mavesi amene takambirana a mu chaputala 12 cha Aroma, atipatsa malangizo amene tingagwiritse ntchito pa moyo wathu monga Akhristu ndiponso mmene tingakhalire ndi abale athu. Koma kodi anthu amene sali mumpingo wachikhristu, kuphatikizapo anthu amene amatitsutsa ndi kutizunza, tiyenera kuwaona bwanji? Nanga tiyenera kuchita nawo zinthu bwanji? M’nkhani yotsatira, tidzakambirana mavesi otsala a m’chaputala chimenechi. Mavesiwa amayankha mafunso amenewa.

Tibwereze

• Kodi timasonyeza bwanji kuti ‘tikuyaka ndi mzimu’?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kutumikira Mulungu modzichepetsa ndi kudziwa malire athu?

• Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaganizira okhulupirira anzathu ndiponso kuti timawamvera chifundo?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 4]

N’chifukwa chiyani timachita ntchito zachikhristu izi?

[Chithunzi patsamba 6]

Kodi aliyense wa ife angatani kuti athandize kuphunzitsa anthu achilendo za Ufumu?