Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mapemphero Anu Amasonyeza Chiyani za Inuyo?

Kodi Mapemphero Anu Amasonyeza Chiyani za Inuyo?

Kodi Mapemphero Anu Amasonyeza Chiyani za Inuyo?

“Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.”​—SAL. 65:2.

1, 2. N’chifukwa chiyani atumiki a Yehova amapemphera kwa iye ndi chikhulupiriro chonse kuti awayankha?

NTHAWI zonse Yehova amamva mapemphero a atumiki ake okhulupirika. Tili ndi chikhulupiriro chonse kuti amamva mapemphero athu. Ngakhale Mboni za Yehova mamiliyoni ambirimbiri zitati zipemphere kwa Mulungu pa nthawi imodzi, Mulungu sangalephere kumva mapemphero awo chifukwa choti mapempherowo achuluka.

2 Wamasalmo Davide ankakhulupirira kuti Mulungu amayankha mapemphero ake. N’chifukwa chake anaimba kuti: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.” (Sal. 65:2) Mulungu ankayankha mapemphero a Davide chifukwa chakuti Davideyo ankalambira Yehova mokhulupirika. Ifeyo tingachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi mapemphero anga amasonyeza kuti ndimakhulupirira Yehova ndiponso kuti kulambira koyera ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wanga? Kodi mapemphero anga amasonyeza chiyani za ineyo?’

Muzipemphera kwa Yehova Modzichepetsa

3, 4. (a) Kodi tiyenera kupemphera kwa Mulungu motani? (b) Kodi tiyenera kutani ngati tikuvutika ndi “zolingalira” chifukwa cha tchimo lalikulu limene tachita?

3 Kuti mapemphero athu ayankhidwe, tiyenera kupemphera kwa Mulungu modzichepetsa. (Sal. 138:6) Tiyenera kupempha Yehova kuti atifufuze, ngati mmene Davide anachitira pamene ananena kuti: “Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nawo mayendedwe oipa, nimunditsogolere pa njira yosatha.” (Sal. 139:23, 24) Tisamangopemphera, koma tizilolanso kuti Mulungu atifufuze ndiponso tizilandira uphungu wa m’Mawu ake. Yehova angatitsogolere pa “njira yosatha” n’kutithandiza kukhala ndi makhalidwe omwe angatithandize kudzapeza moyo wosatha.

4 Nanga bwanji ngati tikuvutika ndi “zolingalira” chifukwa cha tchimo lalikulu limene tachita? (Werengani Salmo 32:1-5.) Kunyalanyaza chikumbumtima chimene chikutiuza kuti talakwitsa chinachake, kungatifooketse n’kukhala ngati mtengo umene ukuuma chifukwa cha kutentha kwa m’chilimwe. Chifukwa cha tchimo limene anachita, Davide sankasangalala ndiponso n’kutheka kuti anadwala. Koma atavomereza tchimo lake kwa Mulungu, anapeza mpumulo. Taganizirani mmene Davide anasangalalira atadziwa kuti Yehova ‘wamukhululukira tchimo lake.’ Munthu amapeza mpumulo akavomereza tchimo lake kwa Mulungu, ndipo thandizo la akulu achikhristu ndi lofunika kwambiri kuti munthu wolakwayo achire mwauzimu.​—Miy. 28:13; Yak. 5:13-16.

Muzipembedzera Mulungu Ndiponso Muzimuyamika

5. Kodi kupembedzera Yehova kumatanthauza chiyani?

5 Ngati tili ndi nkhawa chifukwa cha zinthu zinazake, tiyenera kutsatira uphungu wa Paulo wakuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa chilichonse, mwa pemphero ndi pembedzero, limodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.” (Afil. 4:6) “Kupembedzera” kumatanthauza “kuchonderera modzichepetsa.” Tiyenera kupembedzera Yehova kuti atithandize ndi kutitsogolera makamaka moyo wathu ukakhala pa ngozi kapena tikamazunzidwa.

6, 7. Kodi tiyenera kuyamika Mulungu m’mapemphero athu pa zifukwa ziti?

6 Komabe ngati timangopemphera pamene tikufuna zinazake basi, kodi zingasonyeze kuti tili ndi mtima wotani? Paulo anati zopempha zathu ziyenera kudziwika kwa Mulungu “limodzi ndi chiyamiko.” Kunena zoona, ife mofanana ndi Davide, tili ndi zifukwa zoyamikira Mulungu. Davide anati: “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi za padziko lapansi ndi zanu; ufumu ndi wanu, Yehova; ndipo mwakwezeka mutu wa pa zonse. . . . Mulungu wathu, tikuyamikani ndi kulemekeza dzina lanu lokoma.”​—1 Mbiri 29:11-13.

7 Yesu anayamika Mulungu chifukwa cha chakudya ndiponso mkate ndi vinyo zimene anagwiritsa ntchito pa Mgonero wa Ambuye. (Mat. 15:36; Maliko 14:22-23) Ifenso tiyenera kukhala ndi mtima woyamikira ngati umenewu. Kuwonjezera pamenepo, tiyeneranso ‘kuyamika Yehova’ chifukwa cha “zodabwiza zake za kwa ana a anthu,” ‘maweruzo ake olungama,’ ndiponso chifukwa cha mawu ake, kapena kuti uthenga umene uli m’Baibulo.​—Sal. 107:15; 119:62, 105.

Muzipempherera Anthu Ena

8, 9. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupempherera Akhristu anzathu?

8 Tikamapemphera sitilephera kutchula nkhani zokhudza ifeyo, koma tisamaiwale kupemphereranso anthu ena, ngakhalenso Akhristu amene sitikuwadziwa mayina awo. Paulo ayenera kuti sankadziwa Akhristu onse a ku Kolose, koma analemba kuti: “Timayamika Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. Timatero chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu, ndi chikondi chanu pa oyera onse.” (Akol. 1:3, 4) Paulo anapemphereranso Akhristu a ku Tesalonika. (2 Ates. 1:11, 12) Mapemphero otero amasonyeza mmene ife tilili ndiponso mmene timaonera abale ndi alongo athu.

9 Tikamapempherera Akhristu odzozedwa ndi anzawo a “nkhosa zina,” timasonyeza kuti timadera nkhawa gulu la Mulungu. (Yoh. 10:16) Paulo anapempha olambira anzake kumupempherera kuti ‘apatsidwe mphamvu ya kulankhula kuti adziwitse ena chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino.’ (Aef. 6:17-20) Kodi ife timapempherera Akhristu anzathu mwanjira imeneyi?

10. Kodi kupempherera ena kungatithandize bwanji?

10 Kupempherera ena kungatithandize kusiya kudana nawo. Tikutero chifukwa chakuti ngati sitisangalala ndi munthu wina koma timamupempherera, sizingatheke kudana nayebe. (1 Yoh. 4:20, 21) Mapemphero oterewa amalimbikitsa ndiponso amathandiza kuti tizigwirizana ndi abale athu. Komanso mapemphero oterowo amasonyeza kuti tili ndi chikondi ngati cha Khristu. (Yoh. 13:34, 35) Khalidwe limeneli ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu. Kodi ifeyo patokha timapempha Yehova kuti atipatse mzimu woyera ndiponso kuti atithandize kusonyeza zipatso za mzimuwo zomwe ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, chikhulupiriro, kufatsa ndi kudziletsa? (Luka 11:13; Agal. 5:22, 23) Ngati timatero, zolankhula ndi zochita zathu zingasonyeze kuti tikuyenda ndiponso tikukhala mwa mzimu.​—Werengani Agalatiya 5:16, 25.

11. Kodi n’chifukwa chiyani si zolakwika kupempha anthu ena kuti azitipempherera?

11 Tikadziwa kuti ana athu akukumana ndi mayesero akuti abere mayeso kusukulu, tiyenera kuwapempherera ndi kuwapatsa malangizo a m’Malemba amene angawathandize kukhala oona mtima ndiponso kupewa kuchita cholakwa chilichonse. Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti: “Tikupemphera kwa Mulungu kuti musachite cholakwa chilichonse.” (2 Akor. 13:7) Tikamapemphera modzichepetsa chonchi, Yehova amasangalala ndipo mapemphero oterowo amamusonyeza kuti tili ndi mtima wabwino. (Werengani Miyambo 15:8.) Tingapemphenso anthu ena kuti azitipempherera, ngati mmene anachitira mtumwi Paulo. Iye anati: “Pitirizani kutipempherera, pakuti tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choona, popeza timafuna kuchita zinthu zonse moona mtima.”​—Aheb. 13:18.

Zinanso Zimene Mapemphero Athu Amasonyeza

12. Kodi ndi mfundo ziti zimene ziyenera kukhala nkhani yaikulu m’mapemphero athu?

12 Kodi mapemphero athu amasonyeza kuti ndife Mboni za Yehova zachangu ndiponso zosangalala? Kodi mapembedzero athu amasonyeza kuti timakonda kwambiri kuchita chifuniro cha Mulungu ndiponso kulalikira uthenga wa Ufumu? Kodi amasonyeza kuti timaganizira kwambiri zakuti Yehova ndiye woyenera kulamulira ndiponso kuti dzina lake liyenera kuyeretsedwa? Mfundo zimenezi ziyenera kukhala nkhani yaikulu m’mapemphero athu, ngati mmene Yesu anasonyezera m’pemphero lake lachitsanzo, limene limayamba ndi mawu akuti: “Atate wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”​—Mat. 6:9, 10.

13, 14. Kodi mapemphero athu amasonyeza chiyani za ife?

13 Mapemphero athu amavumbula zimene zili mumtima mwathu, zimene timakonda ndiponso zimene timalakalaka. Ndipo Yehova amadziwa kuti ndife munthu wotani. Lemba la Miyambo 17:3 limati: “Siliva ali ndi mbiya yosungunulira, golidi ali ndi ng’anjo; koma Yehova ayesa mitima.” Inde, Mulungu amaona zimene zili mumtima mwathu. (1 Sam. 16:7) Amadziwa mmene timaonera misonkhano yathu, utumiki wathu ndiponso abale ndi alongo athu. Yehova amadziwa zimene timaganiza za “abale” a Khristu. (Mat. 25:40) Iye amadziwa ngati tikufunadi zimene tikupemphazo kapena ngati tikungobwereza mawu amene tinawazolowera. Yesu anati: “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza, muja amachitira amitundu, chifukwa iwo amaganiza [molakwa] kuti akanena mawu ambirimbiri awamvera.”​—Mat. 6:7.

14 Zimene timanena m’pemphero zimasonyezanso ngati timadalira kwambiri Mulungu. Davide anati: “[Yehova] munakhala pothawirapo panga; nsanja yolimba pothawa mdani ine. Ndidzagoneragonerabe m’chihema mwanu; ndidzathawira mobisalamo m’mapiko anu.” (Sal. 61:3, 4) Mulungu ‘akafunyulula [mophiphiritsa] hema wake pa ife,’ timakhala pa mtendere ndiponso timatetezeka. (Chiv. 7:15) N’zolimbikitsa kwambiri kuyandikira Yehova mwa kupemphera, tili ndi chikhulupiriro chakuti iye ‘ndi wathu,’ kapena kuti ali kumbali yathu, tikakumana ndi zinthu zilizonse zoyesa chikhulupiriro chathu.​—Werengani Salmo 118:5-9.

15, 16. Kodi pemphero lingatithandize kuzindikira chiyani za zolinga zathu zofuna kukhala ndi udindo mumpingo?

15 Kupemphera moona mtima kwa Yehova za zolinga zathu kungatithandize kuzindikira chifukwa chenicheni chimene tilili ndi zolingazo. Mwachitsanzo, ngati tikufuna kukhala woyang’anira m’gulu la anthu a Mulungu, kodi n’chifukwa chakuti tilidi ndi mtima wodzichepetsa wofuna kuthandiza ena ndi kuchita zonse zimene tingathe popititsa patsogolo zinthu za Ufumu? Kapena kodi chingakhale chifukwa chakuti tikufuna kukhala “woyamba” mwinanso tikufuna ‘kuchita ulamuliro’ pa ena? Mmenemu si mmene zinthu ziyenera kukhalira m’gulu la Yehova. (Werengani 3 Yohane 9, 10; Luka 22:24-27.) Ngati tili ndi zolinga zolakwika, kupemphera kwa Yehova Mulungu moona mtima kungavumbule zolingazo ndipo kungatithandize kusintha, zolinga zathuzo zisanakhazikike mumtima mwathu.

16 Akazi achikhristu angamalakalake kuti amuna awo akhale atumiki othandiza, mwinanso kukhala oyang’anira kumene, kapena kuti akulu. Alongo amenewa ayenera kuchita mogwirizana ndi zimene amanena m’mapemphero awo apaokha okhudza nkhaniyo mwa kuyesetsa kukhala chitsanzo chabwino pa khalidwe lawo. Zimenezi n’zofunika kwambiri, chifukwa chakuti mmene mpingo umaonera mwamunayo, zimadalira zolankhula ndi zochita za banja lake.

Kuimira Ena M’pemphero Pagulu

17. Kodi n’chifukwa chiyani ndi bwino kukhala patokha tikamapereka pemphero laumwini?

17 Nthawi zambiri Yesu ankachoka pagulu kupita kwayekha kuti akapemphere kwa Atate wake. (Mat. 14:13; Luka 5:16; 6:12) Ifenso tiyenera kupeza nthawi yokhala patokha. Kupemphera tili pamalo abata ndiponso mtima uli m’malo, kungatithandize kupanga zosankha zimene zingasangalatse Yehova ndiponso zimene zingatithandize kukhala olimba mwauzimu. Komabe, Yesu ankapempheranso pagulu, ndipo ndi bwino kuti tikambirane mmene ifenso tingachitire zimenezi m’njira yoyenera.

18. Kodi ndi mfundo ziti zimene abale ayenera kukumbukira akamaimira mpingo m’pemphero?

18 Pamisonkhano yathu, amuna okhulupirika amaimira mpingo wonse m’pemphero. (1 Tim. 2:8) Pamapeto pa pemphero, anthu onse osonkhana afunika kunena kuti “amen,” kutanthauza “zikhale momwemo.” Koma kuti anene zimenezi, afunika kugwirizana ndi zimene zanenedwa m’pempherolo. M’pemphero lake lachitsanzo, Yesu sananene zinthu zoimitsa mutu kapena kulankhula zinthu zosonyeza kuti sanaganize bwino. (Luka 11:2-4) Ndiponso, iye sanafotokoze zosowa kapena mavuto onse a munthu aliyense amene anali pagulupo. Mavuto amene munthu mmodzi ndi mmodzi akukumana nawo ndi ofunika kuwatchula popemphera patokha, osati pagulu. Ndipo tikamaimira gulu m’pemphero, tizipewa kutchula nkhani zachinsinsi.

19. Kodi tiyenera kupewa khalidwe lotani pemphero lapagulu likamaperekedwa?

19 Munthu wina akamatiimira m’pemphero pagulu, tiyenera kusonyeza ulemu ndiponso ‘kuopa Mulungu.’ (1 Pet. 2:17) Pali zinthu zina zoyenera kuchita pa nthawi ndi malo ena koma osati pamisonkhano yachikhristu. (Mlal. 3:1) Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti munthu wina akuuza anthu onse pagulu kuti agwirane manja popemphera. Izi zikhoza kukhumudwitsa kapena kudodometsa anthu ena, makamaka alendo amene amabwera pamisonkhano yathu omwe si Mboni. Pa pemphero lapagulu, anthu ena okwatirana angagwirane manja mosaonetsera, koma ngati atachita kukumbatirana anthu ena oona akhoza kukhumudwa. Iwo angaone kapena kuganiza kuti banjalo likungoganizira za chikondi chawo osati kupereka ulemu kwa Yehova. Choncho tiyenera kupereka ulemu waukulu kwa Mulungu mwa ‘kuchita zonse ku ulemerero’ wake, ndiponso kupewa khalidwe lililonse limene lingasokoneze, kuimitsa mutu kapena kukhumudwitsa ena.​—1 Akor. 10:31, 32; 2 Akor. 6:3.

Kodi Tiyenera Kupempha Chiyani?

20. Kodi mungalifotokoze bwanji lemba la Aroma 8:26, 27?

20 Zingachitike nthawi zina kuti sitikudziwa zoti tinene m’pemphero laumwini. Paulo ananena kuti: “Pakuti chimene tiyenera kupempherera monga mmene tiyenera kupemphera sitikuchidziwa, koma mzimu [woyera] umachonderera m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. Koma iye [Mulungu] amene amasanthula mitima amadziwa zimene mzimu ukutanthauza.” (Aroma 8:26, 27) Yehova anaonetsetsa kuti mapemphero ambiri alembedwa m’Malemba. Iye amalandira mapemphero ouziridwa amenewa ngati kuti akuchokera kwa ife, ndipo amatichitira zimene tinafuna kupemphazo. Mulungu amatidziwa bwino ndipo amadziwanso tanthauzo la zimene anauzira mzimu wake kuti ulankhule kudzera mwa anthu amene analemba Baibulo. Yehova amayankha mapembedzero athu mzimu ‘ukamachonderera’ m’malo mwathu. Koma tikayamba kuwadziwa bwino Mawu a Mulungu, mfundo zoti titchule m’pemphero zimabwera msanga m’maganizo mwathu.

21. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

21 Taphunzira kuti mapemphero athu amasonyeza zambiri za ife. Mwachitsanzo, angasonyeze ngati tili oyandikana kwambiri ndi Yehova ndiponso ngati timadziwa bwino Mawu ake. (Yak. 4:8) M’nkhani yotsatira, tidzakambirana mapemphero ndi mawu ena a m’mapemphero olembedwa m’Baibulo. Kodi mfundo za m’Malemba zimene tidzakambiranezo, zingatithandize bwanji pamene tikupemphera kwa Mulungu?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi tiyenera kupemphera kwa Yehova motani?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupempherera okhulupirira anzathu?

• Kodi mapemphero athu angasonyeze chiyani za ifeyo ndiponso zolinga zathu?

• Kodi tiyenera kupewa khalidwe lotani pemphero lapagulu likamaperekedwa?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 4]

Kodi nthawi zonse mumatamanda ndi kuyamika Yehova?

[Chithunzi patsamba 6]

Khalidwe lathu pa nthawi ya pemphero lapagulu liyenera kulemekeza Yehova