Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupereka Mokondwera Kuchokera Pansi pa Mtima

Kupereka Mokondwera Kuchokera Pansi pa Mtima

Kupereka Mokondwera Kuchokera Pansi pa Mtima

PA NKHANI ya zopereka, mtumwi Paulo analemba kuti: “Aliyense achite mwa kutsimikiza kwa mtima wake, osati monyinyirika kapena mokakamizika ayi, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera.” (2 Akor. 9:7) Yehova sakakamiza aliyense kupereka thandizo lochirikiza kulambira koona. M’malomwake amalola atumiki ake kusonyeza chikondi chawo kwa iye popereka zinthu mwakufuna kwawo ndiponso mokondwera. Kuyambira kale, anthu ake akhala akupereka mowolowa manja. Taganizirani zitsanzo zitatu izi.

Yehova atatulutsa Aisiraeli ku Iguputo, anawauza kuti amange chihema. Kuti zimenezi zitheke panafunika zipangizo, motero Aisiraeli anapemphedwa kuti apereke zimenezi. Atamva pempholi, “aliyense wa mtima wom’funitsa mwini” anabweretsa golidi, siliva, zinthu monga ndolo, mphete, zibangili ndiponso zipangizo zina. Anthuwo anapereka mowolowa manja kwambiri moti anachita kuuzidwa kuti asiye kupereka.​—Eks. 35:5, 21; 36:6, 7.

Patatha zaka zambiri, anthu a Mulungu anakhalanso ndi mwayi wina wochirikiza kulambira koona pa nthawi yomanga kachisi. Mfumu Davide anapereka mphatso yaikulu kwambiri yothandiza pa ntchito imeneyi ndipo anapempha ena kuti nawonso athandizepo. Iwo anathandizapodi ndi mtima wonse, moti golide ndi siliva amene anaperekedwa anali wokwana madola 100 biliyoni a ku United States tikatengera mmene ndalama ilili masiku ano. Anthuwo anasangalala kuti anapereka mphatso zawo kwa Yehova mwa kufuna kwawo.​—1 Mbiri 29:3-9; 2 Mbiri 5:1.

Otsatira oyambirira a Yesu Khristu ku Yerusalemu anasonyezanso mzimu wopereka mokondwera. Pa tsiku la Pentekoste mu 33 C.E., anthu pafupifupi 3,000 anabatizidwa, ndipo ambiri anangofika ku Yerusalemuko monga alendo. Akhristuwo anasonkherana ndalama kuti athandize alendo amene anali osowa kuti akhale mumzindawo kwakanthawi, n’cholinga choti apitirize kuphunzira zinthu zina zokhudza chipembedzo chawo chatsopanocho. Abalewo anagulitsa zinthu zawo n’kupereka ndalamazo kwa atumwi kuti athandizire osowawo. Yehova ayenera kuti anasangalala kwambiri kuona chikhulupiriro ndiponso chikondi chimene Akhristu anasonyeza pamenepa.​—Mac. 2:41-47.

Masiku ano Akhristu akuchirikizabe kulambira koona popereka nthawi, mphamvu ndiponso ndalama zawo mowolowa manja komanso mwakufuna kwawo. Bokosi lili m’munsili lili ndi njira zina zosonyeza mmene mungachitire zimenezi.

[Bokosi pamasamba 18, 19]

NJIRA ZIMENE ENA AMAPEREKERA

ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE

Ambiri amachita bajeti, kapena kuti amaika padera ndalama zoti aziponya m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Ntchito ya Padziko Lonse.”

Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalama zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova imene imayang’anira ntchito ya m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza nokha ndalama zimene mukufuna ku Accounting Office, Watch Tower Society, P. O. Box 30749, Lilongwe 3, Malawi, kapena ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu. Mukamatumiza macheke ku adiresi yomwe ili pamwambayi, musonyeze kuti ndalamazo zipite ku “Watch Tower.” Mungathenso kupereka zinthu ngati ndolo, mphete, zibangili, kapena zinthu zina zamtengo wapatali. Potumiza zinthu zimenezi, mulembe kalata yachidule yofotokoza kuti zimene mukutumizazo ndi mphatso basi.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezera pa kupereka mphatso za ndalama, pali njira zinanso zoperekera zinthu popititsa patsogolo ntchito ya Ufumu padziko lonse. Zina mwa njirazi ndi izi:

Inshuwalansi: Mungalembetse kuti Watch Tower Society ndiyo idzapatsidwe phindu la inshuwalansi kapena ndalama za penshoni.

Maakaunti Akubanki: Mukhoza kuikiza m’manja mwa Watch Tower Society maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsira ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwiritse ntchito mukadzapuma pa ntchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalira, a Watch Tower Society adzatenge zinthu zimenezi. Pochita zimenezi, mutsatire malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendera.

Masheya: Mungapereke masheya amene muli nawo m’kampani ku Watch Tower Society monga mphatso basi.

Malo ndi Nyumba: Mungapereke mphatso monga malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe, kapena ngati ili nyumba yoti mukukhalamo, mukhoza kuipereka komabe n’kupitiriza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo. Musanakonze zopereka malo kapena nyumba iliyonse, lankhulani kaye ndi ofesi ya nthambi ya m’dziko lanu.

Chuma Chamasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomerezeka ndi boma kuti Watch Tower Society idzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, ngati inuyo mutamwalira.

Ngati mukufuna kudziwa zambiri za mmene mungaperekere mphatso zimenezi, lankhulani ndi a ku Accounting Office pa telefoni kapena alembereni kalata pa adiresi imene ili pansipa kapenanso mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

Accounting Office

Watch Tower Society

P. O. Box 30749

Lilongwe 3

Malawi

Telefoni: 01 762 111