Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuphunzira Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo

Kuphunzira Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo

Kuphunzira Baibulo Kungathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo

“Yehova, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu.”​—NEH. 1:11.

1, 2. N’chifukwa chiyani kukambirana mapemphero ena olembedwa m’Baibulo kungatithandize?

PEMPHERO ndiponso kuphunzira Baibulo ndi zinthu zofunika kwambiri pa kulambira koona. (1 Ates. 5:17; 2 Tim. 3:16, 17) N’zoona kuti Baibulo si buku la mapemphero. Koma lili ndi mapemphero ambirimbiri, kuphatikizapo amene amapezeka m’buku la Masalmo.

2 Mukamawerenga ndiponso kuphunzira Baibulo, mungapeze mapemphero ogwirizana ndi zimene zikukuchitikirani pa moyo wanu. Ndipotu mukamapemphera, kutchula mawu a m’mapemphero olembedwa m’Malemba kumathandiza kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo. Kodi mungaphunzire chiyani kwa anthu amene anapempha thandizo kwa Mulungu n’kuyankhidwa? Nanga mungaphunzire chiyani pa zimene ananena m’mapemphero awowo?

Fufuzani Malangizo a Mulungu ndi Kuwatsatira

3, 4. Kodi mtumiki wa Abulahamu anapatsidwa ntchito yotani, ndipo tingaphunzire chiyani pa zimene Yehova anamuchitira?

3 Mukamaphunzira Baibulo, mumaona kuti nthawi zonse muyenera kupempha Mulungu kuti akutsogolereni. Taganizirani zimene zinachitika pamene Abulahamu anatuma mtumiki wake wamkulu yemwe mwina anali Eliezere, ku Mesopotamiya kuti akapezere mwana wake Isake mkazi woopa Mulungu. Atapeza akazi akutunga madzi pachitsime china, mtumikiyu anapemphera kuti: “Yehova, . . . pakhale kuti namwali amene ndidzati kwa iye, tulatu mtsuko wako, ndimwe; ndipo iye adzati, imwa, ndipo ndidzamwetsanso ngamila zako; yemweyo akhale mkazi wosankhira mnyamata wanu Isake; ndipo chotero ndidzadziwa kuti mwam’chitira mbuyanga ufulu.”​—Gen. 24:12-14.

4 Pemphero la mtumiki wa Abulahamu linayankhidwa pamene Rebeka anamwetsa ngamila zake. Kenako anatsagana naye kupita ku Kanani ndipo anakakhala mkazi wokondedwa wa Isake. N’zoona kuti simungayembekezere Mulungu kuti akupatseni chizindikiro chinachake chakuti wayankha pemphero lanu. Komabe, iye angakutsogolereni pa moyo wanu ngati mupemphera kwa iye ndi kulola kuti mzimu wake uzikutsogolerani.​—Agal. 5:18.

Pemphero Limathandiza Kuchepetsa Nkhawa

5, 6. Kodi n’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi pemphero limene Yakobo anapereka atatsala pang’ono kukumana ndi Esau?

5 Pemphero lingathandize kuchepetsa nkhawa. Poopa kuti m’bale wake Esau amupha, Yakobo anapemphera kuti: “Yehova, . . . sindiyenera zazing’ono za zifundo zonse, ndi zoona zonse, zimene mwam’chitira kapolo wanu . . . Mundipulumutsetu ine m’dzanja la mkulu wanga, m’dzanja la Esau; chifukwa ine ndimuopa iye, kapena adzadza kudzandikantha ine, ndi amayi pamodzi ndi ana. Ndipo Inu munati, ndidzakuchitira iwe bwino ndithu, ndidzakuyesa mbewu yako monga mchenga wapanyanja yaikulu, umene sungathe kuwerengeka chifukwa cha unyinji wake.”​—Gen. 32:9-12.

6 Ngakhale kuti Yakobo chifukwa cha nkhawa anachita zonse zimene akanatha kuti m’bale wake asawaukire, pemphero lake linayankhidwa pamene iye ndi Esau anagwirizana. (Gen. 33:1-4) Werengani pemphero limeneli bwinobwino ndipo muona kuti Yakobo sanangopempha thandizo. Iye anasonyeza kuti ankakhulupirira za Mbewu yolonjezedwa ndipo ankayamikira kukoma mtima kwa Mulungu. Kodi pali zinthu zina zimene zikukuchititsani “mantha”? (2 Akor. 7:5) Ngati ndi choncho pemphero la Yakobo lingakuthandizeni kukumbukira kuti pemphero lingathandize kuchepetsa nkhawa. Komabe mapemphero sayenera kukhala ongopempha, ayeneranso kukhala ndi mawu osonyeza kuti tili ndi chikhulupiriro.

Muzipempha Nzeru

7. N’chifukwa chiyani Mose anapemphera kuti adziwe njira za Yehova?

7 Mtima wofuna kusangalatsa Yehova ungatichititse kum’pempha kuti atipatse nzeru. Mose anapemphera kuti adziwe njira za Mulungu. Iye anati: “Taonani, Inu [Yehova] munena ndi ine, kwera nawo anthu awa [kuchoka ku Iguputo] . . . Ndipo tsopano, ngati ndapeza ufulu pamaso panu, mundidziwitsetu njira zanu, . . . ndi kuti ndipeze ufulu pamaso panu.” (Eks. 33:12, 13) Poyankha pempheroli, Mulungu anathandiza Mose kudziwa bwino njira Zake, ndipo zimenezi zinali zofunika kwambiri kuti Mose athe kutsogolera anthu a Yehova.

8. Kodi kusinkhasinkha lemba la 1 Mafumu 3:7-14 kungakuthandizeni bwanji?

8 Nayenso Davide anapemphera kuti: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu.” (Sal. 25:4) Mwana wa Davide, Solomo, anapemphanso Mulungu kuti amupatse nzeru kuti athe kulamulira bwino monga mfumu ya Isiraeli. Pemphero la Solomo linasangalatsa Yehova ndipo anamupatsa zimene anapemphazo ndiponso chuma ndi ulemerero. (Werengani 1 Mafumu 3:7-14.) Ngati mwapatsidwa utumiki winawake mumpingo ndipo mukuona kuti simungaukwanitse, muyenera kupemphera kwa Mulungu kuti akupatseni nzeru ndi mtima wodzichepetsa. Mukatero, Mulungu adzakuthandizani kudziwa zinthu ndipo adzakupatsani nzeru yofunika kuti muchite utumiki wanuwo moyenera ndiponso mwachikondi.

Muzipemphera Kuchokera Mumtima

9, 10. Popeza Solomo anatchula mtima mobwerezabwereza m’pemphero lake potsegulira kachisi, kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani?

9 Kuti Mulungu ayankhe pemphero lathu, liyenera kuchokera mumtima. Anthu asanasonkhane ku Yerusalemu pa mwambo wotsegulira kachisi wa Yehova mu 1026 B.C.E., Solomo anapemphera kuchokera mumtima ndipo pemphero limeneli linalembedwa pa 1 Mafumu chaputala 8. Solomo anatamanda Mulungu likasa la chipangano litaikidwa m’Malo Opatulikitsa ndiponso mtambo wa Yehova utadzaza m’kachisi.

10 Werengani bwinobwino pemphero la Solomo ndipo onani mmene akutchulira mobwerezabwereza mawu akuti mtima. Solomo ananena kuti Yehova yekha ndi amene amadziwa mtima wa munthu. (1 Maf. 8:38, 39) Pempheroli limasonyezanso kuti pali chiyembekezo chakuti wochimwa amene ‘wabwerera kwa Mulungu ndi mtima wake wonse,’ angakhululukidwe. Ngati anthu a Mulungu atagwidwa kukhala akapolo, mapemphero awo akanamvedwa ngati mtima wawo unali wangwiro ndi Yehova. (1 Maf. 8:48, 58, 61) Motero mapemphero anu ayenera kuchokera mumtima.

Masalmo Angathandize Kuti Mapemphero Anu Azikhala Atanthauzo

11, 12. Kodi mwaphunzira chiyani pa mawu amene Mlevi wina ananena m’pemphero lake pa nthawi imene sakanatha kupita kukachisi wa Mulungu?

11 Kuwerenga bwinobwino Masalmo kungathandize kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo. Kungakuthandizeninso kuti muziyembekezera kuti Mulungu ayankhe mapemphero anuwo. Taganizirani kuleza mtima kumene Mlevi wina amene anali ku ukapolo anasonyeza. Ngakhale kuti kwa kanthawi ndithu iye sakanatha kupita kukachisi wa Yehova, anaimba kuti: “Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa mkati mwanga? Yembekeza Mulungu: Pakuti ndidzam’lemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.”​—Sal. 42:5, 11; 43:5.

12 Kodi mukuphunzira chiyani pa zimene Mleviyu anachita? Ngati muli kundende chifukwa cha chilungamo ndipo mukulephera kusonkhana ndi okhulupirira anzanu, muyenera kuyembekeza Mulungu moleza mtima kuti akuthandizeni. (Sal. 37:5) Sinkhasinkhani zinthu zimene munkasangalala nazo potumikira Mulungu ndipo pempherani kuti mupirire pamene ‘mukuyembekeza Mulungu’ kuti akuthandizeni kutuluka ndi kuyambiranso kuchita zinthu ndi anthu ake.

Pempherani mwa Chikhulupiriro

13. Mogwirizana ndi lemba la Yakobe 1:5-8, n’chifukwa chiyani muyenera kupemphera mwa chikhulupiriro?

13 Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wanu, nthawi zonse muzipemphera mwa chikhulupiriro. Ngati mukukumana ndi mayesero amene angachititse kuti musiye kukhala ndi mtima wosagawanika, tsatirani malangizo a wophunzira Yakobe. Pempherani kwa Yehova ndipo musakayikire kuti angakupatseni nzeru zimene zingakuthandizeni kupirira. (Werengani Yakobe 1:5-8.) Mulungu amadziwa nkhawa zilizonse zimene mungakhale nazo ndipo angakutsogolereni ndi kukutonthozani ndi mzimu wake. Muuzeni zakukhosi kwanu ndi chikhulupiriro chonse, “osakayika m’pang’ono pomwe,” ndipo lolani kutsogoleredwa ndi mzimu ndiponso Mawu ake.

14, 15. N’chifukwa chiyani tikunena kuti Hana anapemphera ndipo anachita zinthu mwa chikhulupiriro?

14 Hana anali mmodzi mwa akazi awiri a Mlevi wina dzina lake Elikana. Hana anapemphera ndi kuchita zinthu mwa chikhulupiriro. Iye analibe mwana ndipo mkazi mnzake Penina, yemwe anali ndi ana angapo, ankamunyoza. Ali kuchihema, Hana anawinda kuti akakhala ndi mwana wamwamuna, adzamupereka kwa Yehova. Popeza kuti milomo yake inkagwedera pamene ankapemphera, Mkulu wa Ansembe Eli anaganiza kuti waledzera. Koma Eli atadziwa kuti mayiyu sanaledzere, anati: “Mulungu wa Israyeli akupatse chopempha chako.” Ngakhale kuti Hana sanadziwe kuti zitha bwanji, iye anali ndi chikhulupiriro kuti pemphero lake lidzayankhidwa. Choncho, “nkhope yake siinakhalanso yachisoni.” Nkhawa yake yonse inatha.​—1 Sam. 1:9-18.

15 Samueli atabadwa ndipo atasiya kuyamwa, Hana anakamupereka kwa Yehova kuti azikagwira ntchito yopatulika pachihema. (1 Sam. 1:19-28) Kusinkhasinkha pemphero la Hana, kungathandize kwambiri kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo. Kungakuthandizeninso kuona kuti ngati mupemphera kwa Yehova ndi chikhulupiriro chakuti akuyankhani, mungagonjetse nkhawa zimene muli nazo pa vuto linalake.​—1 Sam. 2:1-10.

16, 17. Kodi chinachitika n’chiyani Nehemiya atapemphera ndi kuchita zinthu mwa chikhulupiriro?

16 Nayenso munthu wolungama Nehemiya, wa m’zaka za m’ma 400 B.C.E., anapemphera ndi kuchita zinthu mwa chikhulupiriro. Iye anachonderera kuti: “Yehova, mutcherere khutu pemphero la kapolo wanu, ndi pemphero la akapolo anu okondwera nako kuopa dzina lanu; ndipo mulemereze kapolo wanu lerolino, ndi kumuonetsera chifundo pamaso pa munthu uyu.” Kodi “munthu” amene ankamunenayo anali ndani? Anali Mfumu Aritasasta ya Perisiya, amene Nehemiya anali woperekera chikho wake.​—Neh. 1:11.

17 Nehemiya atamva kuti Ayuda amene anamasulidwa ku ukapolo wa ku Babulo ‘akulukutika kwakukulu, anyozedwa; ndipo linga la Yerusalemu lapasuka,’ anapemphera mwa chikhulupiriro masiku ambiri. (Neh. 1:3, 4) Mapemphero a Nehemiya anayankhidwa m’njira yodabwitsa moti iye sanakhulupirire pamene Mfumu Aritasasta inamulola kuti apite ku Yerusalemu kukamanga linga. (Neh. 2:1-8) Pasanapite nthawi, linga lonse lopasuka lija linamangidwa. Mapemphero a Nehemiya anayankhidwa chifukwa chakuti anali okhudza kulambira koona ndipo anaperekedwa mwa chikhulupiriro. Kodi mapemphero anu amakhala otero?

Musaiwale Kutamanda Mulungu ndi Kumuyamika

18, 19. Kodi mtumiki wa Yehova ayenera kumutamanda ndi kumuyamika pa zifukwa ziti?

18 Mukamapemphera, musamaiwale kutamanda ndi kuyamika Yehova. Pali zifukwa zambiri zochitira zimenezo. Mwachitsanzo, Davide anatamanda ufumu wa Yehova ndi mtima wonse. (Werengani Salmo 145:10-13.) Kodi mapemphero anu amasonyeza kuti mumayamikira mwayi wolengeza Ufumu wa Yehova? Zimene anthu olemba masalmo ananena, zingakuthandizeninso kupereka kwa Mulungu mapemphero ochokera pansi pa mtima oyamikira misonkhano ya mpingo, yadera ndi yachigawo.​—Sal. 27:4; 122:1.

19 Kuyamikira ubwenzi wanu wamtengo wapatali ndi Mulungu, kungakulimbikitseni kupemphera kuchokera pansi pa mtima ndi mawu monga akuti: “Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye: Ndidzakuimbirani mwa mitundu. Pakuti chifundo chanu n’chachikulu kufikira m’mwamba, ndi choonadi chanu kufikira mitambo. Kwezekani m’mwambamwamba, Mulungu; ulemerero wanu ukhale pamwamba m’dziko lonse lapansi.” (Sal. 57:9-11) Mawu amenewa ndi okhudza mtima kwambiri. Kodi simukuvomereza kuti mawu okhudza mtima ngati amenewa, ochokera m’Masalmo angathandize kwambiri kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo?

Muzichonderera Mulungu Mwaulemu

20. Kodi Mariya ananena chiyani posonyeza ulemu wake kwa Mulungu?

20 Mapemphero anu ayenera kusonyeza kuti mumalemekeza Mulungu. Mawu olemekeza Mulungu amene Mariya analankhula atangomva kuti adzabereka Mesiya, anali ofanana ndi amene Hana ananena pamene ankapereka mwana wake Samueli kuti azikatumikira kuchihema. Ulemu umene Mariya anali nawo kwa Mulungu umaonekera m’mawu ake akuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova. Ndipo mzimu wanga sungaleke kusefukira ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga.” (Luka 1:46, 47) Kodi mungayesetse kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo mwa kulankhula mawu ngati amenewa? M’pake kuti Mariya, mkazi woopa Mulungu ameneyu, anasankhidwa kukhala mayi wa Yesu yemwe ndi Mesiya.

21. Kodi mapemphero a Yesu amasonyeza bwanji kuti iye anali ndi ulemu ndi chikhulupiriro?

21 Yesu anapemphera mwaulemu ndiponso ndi chikhulupiriro chonse. Mwachitsanzo asanaukitse Lazaro, “Yesu anakweza maso ake kumwamba ndi kunena kuti: ‘Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse.’” (Yoh. 11:41, 42) Kodi mapemphero anu amasonyeza ulemu ndi chikhulupiriro chotero? Mukawerenga bwinobwino pemphero la Yesu lachitsanzo, mudzaona kuti mbali zazikulu zimene anatchula ndi kuyeretsedwa kwa dzina la Yehova, kubwera kwa Ufumu wake ndi kuchitika kwa chifuniro chake. (Mat. 6:9, 10) Ndiyeno ganizirani za mapemphero anu. Kodi amasonyeza kuti inuyo mumafunadi Ufumu wa Yehova, kuchita chifuniro chake ndiponso mumafuna kuona dzina lake loyera litayeretsedwa? Mapemphero anu ayenera kusonyeza zimenezi.

22. N’chifukwa chiyani mukutsimikiza kuti Yehova adzakuthandizani kulengeza uthenga wabwino molimba mtima?

22 Popeza kuti timakumana ndi chizunzo ndiponso mayesero ena, nthawi zambiri mapemphero athu amaphatikizapo kuchonderera Yehova kuti atithandize kumutumikira molimba mtima. Pamene Bungwe Lalikulu la Ayuda linalamula Petulo ndi Yohane kuti asiye “kuphunzitsa m’dzina la Yesu,” atumwiwo molimba mtima anakana. (Mac. 4:18-20) Atamasulidwa, anauza okhulupirira anzawo zomwe zinachitikazo. Kenako anthu onse amene analipo, anapempha Mulungu kuti awathandize kulankhula mawu ake molimba mtima. Iwo anasangalala kwambiri pemphero lawo litayankhidwa pamene “anadzazidwa ndi mzimu woyera, ndipo anali kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.” (Werengani Machitidwe 4:24-31.) Chifukwa cha zimenezi, anthu ambiri anayamba kulambira Yehova. Inunso pemphero lingakuthandizeni kulengeza uthenga wabwino molimba mtima.

Yesetsani Kuti Mapemphero Anu Azikhalabe Atanthauzo

23, 24. (a) Tchulani zitsanzo zina zosonyeza kuti kuphunzira Baibulo kungathandize kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo. (b) Kodi mungatani kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo?

23 Pali zitsanzo zambiri za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo, kungathandize kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo. Mwachitsanzo mofanana ndi Yona, popemphera mungasonyeze kuti mumakhulupirira kuti “chipulumutso n’cha Yehova.” (Yona 2:1-10) Ngati mukuvutika maganizo chifukwa cha tchimo lalikulu ndipo mwapempha thandizo kwa akulu, mawu a m’pemphero la Davide angakuthandizeni kufotokoza za kulapa kwanu m’mapemphero. (Sal. 51:1-12) M’mapemphero ena mungatamande Yehova ngati mmene Yeremiya anachitira. (Yer. 32:16-19) Ngati mukufuna munthu wokwatirana naye, kuwerenga bwinobwino pemphero lopezeka pa Ezara chaputala 9, komanso kupempherera nkhaniyi, kungakuthandizeni kusasiya kumvera Mulungu mwa ‘kukwatira kokha mwa Ambuye.’​—1 Akor. 7:39; Ezara 9:6, 10-15.

24 Pitirizani kuwerenga, kuphunzira ndi kufufuza m’Baibulo. Pezani mfundo zimene mungaziphatikize m’mapemphero anu. Ndipo mungathe kugwiritsa ntchito mfundo za m’Malemba zimenezo m’mapembedzero ndi m’mapemphero anu oyamika ndi kutamanda Mulungu. Mukamayesetsa kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo mwa kuphunzira Baibulo, mudzayandikira kwambiri kwa Yehova Mulungu.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kufunafuna malangizo a Mulungu ndi kuwatsatira?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupempha nzeru?

• Kodi buku la Masalmo lingathandize bwanji kuti mapemphero athu azikhala atanthauzo?

• Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kupemphera mwa chikhulupiriro ndiponso mwaulemu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 8]

Mtumiki wa Abulahamu anapempha kuti Mulungu amutsogolere. Kodi inunso mumatero?

[Chithunzi patsamba 10]

Kulambira kwa Pabanja kungathandize kuti mapemphero anu azikhala atanthauzo