Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi mlongo akamamasulira nkhani za Baibulo m’chinenero cha manja pamsonkhano wa mpingo, wadera kapena wachigawo, ayenera kuvala chophimba kumutu?

Monga tonse tikudziwira, mkazi wachikhristu ayenera kuvala chophimba kumutu akamachita zinthu zimene ndi udindo wa mwamuna wake kapena wa m’bale mumpingo. Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo imene mtumwi Paulo ananena yakuti “mkazi aliyense amene akupemphera kapena kunenera wosavala kanthu kumutu akuchititsa manyazi mutu wake,” chifukwa chakuti “mutu wa mkazi ndi mwamuna.” (1 Akor. 11:3-10) Mlongo akavala chophimba kumutu choyenerera pa zochitika ngati zimenezi, amasonyeza kuti amagonjera dongosolo la Mulungu limene mpingo wachikhristu umayendera.​—1 Tim. 2:11, 12. *

Koma nanga bwanji ngati mlongo akumasulira m’chinenero cha manja nkhani imene m’bale akukamba? N’zoona kuti mlongoyo akungomasulira nkhaniyo. Amene akuphunzitsa ndi m’baleyo. Komabe, kumasulira nkhani m’chinenero cha manja n’kosiyana kwambiri ndi kumasulira nkhani m’zinenero zina. M’zinenero zinazi, omvera amatha kuyang’ana wokamba nkhani kwinaku akumvetsera womasulirayo. Ndiponso, alongo akamamasulira nkhani m’zinenero zinazi, nthawi zambiri sakhala pamalo oonekera kwambiri. Nthawi zina, amasankha kukhala pansi pamene akumasulira nkhaniyo kapena ngati aimirira, amasankha kuyang’ana wokamba nkhaniyo osati omvera. Choncho, m’posafunika kuti mlongo amene akumasulira m’zinenero zinazi azivala chophimba kumutu.

Komanso, chifukwa cha zipangizo zamakono zimene amagwiritsa ntchito pomasulira nkhani m’chinenero cha manja, udindo wa womasulira umaonekera kwambiri. Chithunzi cha womasulirayo chimasonyezedwa pasikirini yaikulu, ndipo mwina omverawo sayang’ana n’komwe wokamba nkhaniyo. Poganizira mfundo zimenezi, zingakhale bwino kuti mlongo amene akumasulira m’chinenero cha manja, azisonyeza kuti akuzindikira kuti iye si wokamba nkhani mwa kuvala chophimba kumutu.

Kodi malangizo atsopanowa akukhudza bwanji kumasulira m’chinenero cha manja nkhani za m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, zitsanzo, ndiponso ndemanga pa Phunziro la Baibulo la Mpingo, pa Msonkhano wa Utumiki ndi pa Phunziro la Nsanja ya Olonda? Kodi mlongo amene akumasulira m’chinenero cha manja pa zochitika zimenezi ayeneranso kuvala chophimba kumutu? Zikuoneka kuti pa zochitika zina mlongo amene akumasulira, sangafunikire kuvala chophimba kumutu, chifukwa chakuti omvera onse angadziwe kuti iye si amene akuchititsa msonkhanowo. Mwachitsanzo, iye sangavale chophimba kumutu pomasulira ndemanga za omvera, nkhani za alongo kapena zitsanzo. Komabe, akamamasulira nkhani za abale pamisonkhano imeneyi, akamamasulira zimene wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda kapena Phunziro la Baibulo la Mpingo akunena, kapenanso akamatsogolera nyimbo m’chinenero cha manja, ayenera kuvala chophimba kumutu. Popeza kuti pamsonkhano, mlongo angafunikire kumasulira zimene abale, alongo, ana ndiponso akulu mumpingo akunena, zingakhale bwino kuvala chophimba kumutu pamsonkhano wonsewo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Kuti mudziwe zochitika zosiyanasiyana pamene akazi achikhristu afunika kuvala chophimba kumutu, onani buku lakuti “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu,” masamba 209 mpaka 212.