Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muziona Kuti Abale ndi Alongo Anu Osamva Ndi Ofunika Kwambiri

Muziona Kuti Abale ndi Alongo Anu Osamva Ndi Ofunika Kwambiri

Muziona Kuti Abale ndi Alongo Anu Osamva Ndi Ofunika Kwambiri

ANTHU a Mulungu masiku ano ndi banja lalikulu la abale ndi alongo auzimu limene linayamba ndi anthu akale monga Samueli, Davide, Samsoni, Rahabi, Mose, Abulahamu, Sara, Nowa ndi Abele. Pakati pa atumiki okhulupirika a Yehova, pali anthu ambiri osamva. Mwachitsanzo, anthu awiri oyambirira kukhala Mboni za Yehova ku Mongolia, anali mwamuna ndi mkazi wake ndipo onse anali osamva. Ndipo abale athu osamva a ku Russia anachititsa kuti mlandu utiyendere bwino ku European Court of Human Rights chifukwa cha mtima wawo wosagawanika.

Masiku ano, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wakonza mabuku a m’chinenero cha manja ndipo amakonzanso misonkhano yadera ndi yachigawo ya m’chinenerochi. (Mat. 24:45) Zinthu zimenezi zathandiza kwambiri anthu osamva. * Koma kodi munayamba mwaganizapo mmene zinalili kalelo? Kodi popanda zinthu zimenezi anthu osamva ankaphunzira bwanji za Mulungu woona mpaka kumapita patsogolo m’choonadi? Kodi munayamba mwaganizapo zimene mungachite kuti muthandize anthu osamva m’dera lanulo?

Mmene Zinthu Zinalili Kalelo

Kodi mutafunsa achikulire osamva kuti akuuzeni mmene anaphunzirira choonadi angakuuzeni zotani? Mwina angakuuzeni mmene anamvera atazindikira kuti Mulungu ali ndi dzina. Angakuuzeninso mmene mfundo imeneyi inasinthiratu moyo wawo wonse ndiponso mmene inawalimbikitsira kwa zaka zambirimbiri mpaka kufika nthawi imene gulu linayamba kukonza ma DVD a anthu osamva, kuti awathandize kuphunzira choonadi chozama cha m’Malemba. Angathe kukuuzani mmene zinthu zinalili pa nthawi imene misonkhano siinkachitidwa kapena kumasuliridwa m’chinenero cha manja. Pa nthawiyo munthu wina ankakhala pambali pawo n’kumalemba manotsi papepala kuti mwina wosamvayo atolepo zina ndi zina. M’bale wina wosamva anaphunzira choonadi cha m’Baibulo m’njira imeneyi kwa zaka 7 pasanapezeke munthu womasulira.

Abale ndi alongo osamva omwe ndi achikulire amakumbukira mavuto amene ankakumana nawo kale pamene ankalowa m’munda limodzi ndi abale ena mumpingo n’kumakalalikira kwa anthu akumva. M’dzanja limodzi ankanyamula khadi lomwe ankalembapo mawu okasonyeza mwininyumba ndipo dzanja linalo ankanyamula magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ankavutika kwambiri kuphunzira Baibulo ndi munthu wosamva mnzawo chifukwa choti ngakhale iwowo sankamvetsa zimene ankawerenga m’mabuku othandiza pophunzira Baibulo. N’zosakayikitsa kuti ofalitsa achikulire omwe ndi osamva amakumbukira mmene ankakhumudwira chifukwa choti munthu amene akuphunzira naye akulephera kuwamvetsa. Ndipo izi zinkachititsa kuti asakambirane mfundo za choonadi zambiri. Iwo amadziwanso bwino mmene zimakhalira munthu ukamakonda Yehova kwambiri koma n’kumalephera kusonyeza chikondi chimenechi chifukwa chodzikayikira. N’chifukwa chiyani ankadzikayikira? Chifukwa choti sankakhala otsimikiza kuti iwowo pawokha akumvetsadi mfundo ina yake.

Ngakhale kuti anali ndi mavuto onsewa, abale ndi alongo athu osamva akhalabe ndi mtima wosagawanika. (Yobu 2:3) Chifukwa cha chikondi, iwowa akhala akuyembekeza Yehova. (Sal. 37:7) Ndipo panopo iye akuwadalitsa powapatsa zinthu zambiri zomwe sankaziyembekezera n’komwe.

Taganizirani zimene ankachita m’bale wina wosamva yemwe, ndi wokwatira ndipo ali ndi ana. Mavidiyo a chinenero cha manja asanayambe kupangidwa, iye ankachititsa phunziro la banja nthawi zonse. Mwana wake wamwamuna akukumbukira kuti: “Bambo ankavutika kwambiri pochititsa phunziro la banja, chifukwa ankatiphunzitsira mabuku basi, popanda mavidiyo alionse a chinenero cha manja. Nthawi zambiri iwo sankamvetsa zimene zalembedwa m’mabukumo. Anafe tinkawonjezeranso vutolo kwambiri, chifukwa akalephera kufotokoza zinthu molondola, nthawi yomweyo tinkawauza kuti si zimene akutanthauza. Komabe mavuto onsewa ali apo, iwo nthawi zonse ankachititsa phunziro la banja. Ankaona kuti kutiphunzitsa za Yehova n’kofunika kwambiri moti sankadandaula ngakhale kuti nthawi zina ankalakwitsa chifukwa cholephera kumvetsa bwino Chingelezi.”

Chitsanzo china ndi cha Richard, m’bale wa zaka zoposa 70 amene ndi wosamva ndiponso wosaona. Iye amakhala ku Brooklyn, New York, m’dziko la United States. Aliyense amadziwa kuti Richard sajomba kumisonkhano. Amapita yekha kumisonkhano ndipo amakwera sitima. Kuti adziwe potsikira, amawerenga masiteji amene sitimayo yaima. Tsiku lina m’nyengo yachisanu, kunja kunagwa chipale chofewa chadzaoneni moti abale anaganiza zoti misonkhano isachitike. Anthu onse mumpingo anauzidwa kupatulapo Richard. Abale atazindikira zimenezi, anapita kukamufuna ndipo anam’peza ataima pa Nyumba ya Ufumu, kudikirira kuti wina adzam’tsegulire. Atamufunsa kuti n’chifukwa chiyani anayenda ulendo umenewu kunja kutaipa choncho, iye anayankha kuti, “Ndimakonda kwambiri Yehova.”

Kodi Inuyo Mungathandize Bwanji?

Kodi m’dera lanu muli anthu osamva? Kodi mungathe kuphunzira chinenero cha manja kuti muzitha kulankhula nawo? Nthawi zambiri anthu osamva amakhala oleza mtima kwambiri pophunzitsa ena chinenero chawo. Mwina mungakumane ndi munthu wosamva mwamwayi kapena mu utumiki. Kodi zikatero muyenera kutani? Yesani kulankhula naye. Gwiritsani ntchito manja, manotsi, zithunzi zojambula nokha kapena za m’buku, mwinanso mungagwiritse ntchito njira zonsezi. Ngakhale munthuyo atasonyeza kuti alibe chidwi ndi choonadi, uzani m’bale kapena mlongo wosamva kapena amene amadziwa chinenero cha manja kuti munakumana ndi munthuyo. Mwina munthu wosamvayo angachite chidwi ndi uthenga wabwino ataumva m’chinenero cha manja.

N’kutheka kuti mukuphunzira chinenero cha manja ndipo mumapita kumpingo wa chinenerochi. Kodi mungatani kuti mukulitse luso lanu ndiponso kuti muzichimvetsa chinenerochi? Ngakhale kuti mwina mumpingo mwanu muli ofalitsa akumva, ndi bwino kusalankhula mukakhala nawo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muziganiza ngati mmene munthu wosamva amaganizira. N’zoona kuti nthawi zina mungafune kuti mungolankhula. Komabe, pophunzira chinenero chilichonse pamafunika kupirira kuti mufike podziwa bwino chinenerocho.

Kuchita khama kulankhula m’chinenero cha manja kumasonyeza kuti abale athu osamva timawakonda ndipo timawalemekeza. Taganizirani mavuto amene anthu osamva amakumana nawo tsiku lililonse chifukwa chosamvana bwinobwino ndi anthu kuntchito kapena kusukulu. M’bale wina wosamva ananena kuti: “Tsiku lililonse, anthu amene ndimakumana nawo amalankhula. Nthawi zambiri ndimasungulumwa ndipo zimenezi zimandikwiyitsa kwambiri. Ndi zovuta kufotokoza mmene ndimamvera nthawi zina.” Misonkhano yathu iyenera kukhala malo osangalatsa amene abale ndi alongo athu osamva angatsitsimulidweko polandira chakudya chauzimu ndiponso posangalala ndi macheza komanso chikondi cha abale awo.​—Yoh. 13:34, 35.

Ndi bwinonso osanyalanyaza magulu ang’onoang’ono a abale osamva amene amasonkhana limodzi ndi mipingo ya anthu akumva. Pamisonkhano ya mipingoyi, nkhani amazimasulira m’chinenero cha manja. Kuti osamva a mumpingomo apindule ndi misonkhanoyo, amakhala kutsogolo m’Nyumba ya Ufumuyo. Zimenezi zimawathandiza kuti azitha kuona bwinobwino amene akumasulira komanso amene akukamba nkhanizo. Sizitenga nthawi yaitali kuti mpingo wonse uzolowere dongosolo limeneli ndipo sizisokoneza chilichonse. Dongosolo lomweli limatsatiridwanso pamisonkhano yadera ngakhalenso yachigawo imene imakhala ndi omasulira m’chinenero cha manja. Mumpingo, abale ndi alongo amene amachita khama kumasulira ndi kufotokoza mfundo momveka bwino ndiponso mwachibadwa ngati munthu wosamva, ayenera kuyamikiridwa kwambiri.

N’kutheka kuti muli mumpingo umene uli ndi kagulu ka chinenero cha manja kapena umene uli ndi anthu ochepa osamva ndipo pali ena amene amamasulira nkhani zonse pamisonkhano. Kodi mungatani kuti muzisonyeza kuti mumaganizira abale osamva amenewa? Aitaneni kunyumba kwanu. Ngati n’zotheka, phunzirani kunena zinthu zina ndi zina m’chinenero cha manja. Musachite mantha kuti simuzimvana. Simungalephere kumvana zina ndi zina, ndipo chikondi chimene mungasonyeze m’njira imeneyi sichiiwalika. (1 Yoh. 4:8) Pali zambiri zimene tingaphunzire kwa abale ndi alongo athu osamva. Iwo ndi anthu okonda kucheza, ozindikira zinthu ndiponso okonda nthabwala. M’bale wina amene makolo ake onse ndi osamva anati: “Moyo wanga wonse ndakula ndi anthu osamva, ndipo andichitira zinthu zambiri zoti sindingathe kuwabwezera. Kunena zoona, pali zinthu zambiri zimene tingaphunzire kwa abale ndi alongo athu osamva.”

Yehova amakonda atumiki ake okhulupirika, kuphatikizapo osamva onse. Chitsanzo cha kukhulupirika ndiponso kupirira kwawo ndi china mwa zinthu zimene zimachititsa kuti gulu la Yehova likhale lapadera. Motero tiyenera kuona abale ndi alongo athu osamva kuti ndi ofunika kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Onani nkhani yakuti “Yehova Wawalitsa Nkhope Yake pa Iwo,” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2009.

[Chithunzi patsamba 31]

Munthu wosamva angachite chidwi ndi uthenga wa Ufumu ataumva m’chinenero cha manja

[Zithunzi patsamba 32]

Misonkhano yathu iyenera kukhala malo osangalatsa amene abale ndi alongo athu osamva angatsitsimulidweko mwauzimu