Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kukulitsa Chikondi Chanu Chaubale

Pitirizani Kukulitsa Chikondi Chanu Chaubale

Pitirizani Kukulitsa Chikondi Chanu Chaubale

“Yendanibe m’chikondi, monganso Khristu anakukondani.”​—AEF. 5:2.

1. Kodi Yesu anati otsatira ake adzadziwika kwambiri ndi chiyani?

MBONI ZA YEHOVA zimadziwika kwambiri ndi ntchito yawo yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kunyumba ndi nyumba. Komabe, Khristu Yesu anatchula chinthu china kuti ndicho chimadziwikitsa ophunzira ake kuti ndi Akhristu enieni. Iye anati: “Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana wina ndi mnzake. Mmene ine ndakukonderani, inunso muzikondana wina ndi mnzake. Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.”​—Yoh. 13:34, 35.

2, 3. Kodi chikondi chathu chaubale chimakhudza bwanji anthu amene amabwera kumisonkhano yathu?

2 Palibenso anthu amene ali ndi chikondi ngati chimene chili pakati pa abale enieni achikhristu. Monga momwe maginito amakokera chitsulo, chikondi chimakokera atumiki a Yehova pamodzi, n’kuwachititsa kukhala ogwirizana. Chikondi chimachititsanso anthu oona mtima kukopeka ndi chipembedzo choona. Mwachitsanzo, taganizirani za Marcelino, mwamuna wa ku Cameroon amene maso ake anawonongeka chifukwa cha ngozi imene inachitika kuntchito kwawo. Ngoziyo itachitika, anthu anayamba kufalitsa mabodza oti maso ake anachita khungu chifukwa chakuti ndi mfiti. M’malo momutonthoza, abusa ndi anthu ena akutchalitchi kwawo anamuchotsa mumpingo. Kenako mmodzi wa Mboni za Yehova anapempha Marcelino kuti apite naye limodzi ku misonkhano koma iye anakayika kaye pang’ono. Sanafune kuti anthu ena akamusalenso.

3 Koma Marcelino atavomera kupita, anadabwa ndi zimene zinachitika ku Nyumba ya Ufumuko. Anthu anamulandira mwansangala ndipo mfundo za m’Baibulo zimene anaphunzira zinamutonthoza. Iye anayamba kupita kumisonkhano yonse ya mpingo, anapita patsogolo ndi phunziro lake la Baibulo, ndipo anabatizidwa mu 2006. Panopa amakambirana choonadi ndi anthu a m’banja lake ndiponso anthu ena a m’dera lake, ndipo amaphunzira Baibulo ndi anthu angapo. Marcelino akufuna kuti anthu amene akuwaphunzitsa Baibulo amve kuti akukondedwa ngati mmene iyeyo anamvera atakumana ndi anthu a Mulungu.

4. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera malangizo a Paulo akuti ‘tiyendebe m’chikondi’?

4 Tonsefe timakopeka ndi chikondi chaubale chimenechi. Koma kuti chipitirire, tiyenera kuchilimbitsa. Tayerekezerani kuti anthu akuwotha moto usiku, kunja kukuzizira. Ngati atasiya kusonkhezera nkhuni pamotopo, motowo ungazime. Mofanana ndi zimenezi, chikondi cha pakati pa anthu a mumpingo chikhoza kuzilala ngati Mkhristu aliyense atapanda kuchita mbali yake. Kodi tingalimbikitse bwanji chikondi? Mtumwi Paulo anayankha kuti: “Yendanibe m’chikondi, monganso Khristu anakukondani nadzipereka yekha chifukwa cha inu. Iye anadzipereka yekha monga chopereka ndi monga nsembe ya fungo lokoma kwa Mulungu.” (Aef. 5:2) Funso limene aliyense wa ife ayenera kuliganizira n’lakuti, Kodi ndingatani kuti ndipitirizebe kuyenda m’chikondi?

“Inunso Futukulani Mtima Wanu”

5, 6. N’chifukwa chiyani Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti ‘afutukule mtima wawo’?

5 Paulo analembera Akhristu a ku Korinto kuti: “Takhala tikulankhula kwa inu mosabisa mawu Akorinto, tafutukula mtima wathu. Malo sakukucheperani mu mtima mwathu, koma m’chikondi chanu ndimo muli malo ochepa. Choncho, mutibwezere zomwezo zimene takuchitirani​—ndikulankhula nanu ngati ana anga​—inunso futukulani mtima wanu.” (2 Akor. 6:11-13) N’chifukwa chiyani Paulo analimbikitsa Akorinto kuti afutukule mtima wawo posonyeza chikondi?

6 Taganizirani mmene mpingo wa ku Korinto unayambira. Paulo anapita ku Korinto chakumapeto kwa chaka cha 50 C.E. Ngakhale kuti poyamba zinali zovuta kuti mtumwiyu alalikire kumeneko, iye anapirira. Patapita nthawi yochepa, anthu ambiri a mumzindawo anakhulupirira uthenga wabwino. Kwa “chaka ndi miyezi isanu ndi umodzi,” Paulo anadzipereka ndi mtima wake wonse pophunzitsa ndi kulimbitsa mpingo watsopanowo. N’zoonekeratu kuti Paulo anali kukonda kwambiri Akhristu a ku Korinto. (Mac. 18:5, 6, 9-11) Choncho iwo anayenera kumukondanso iyeyo ndi kumulemekeza. Koma ena mumpingowo sanafune kumukonda. Mwina ena sankasangalala ndi mmene anali kuwapatsira uphungu mosapita m’mbali. (1 Akor. 5:1-5; 6:1-10) Mwinanso ena ankamvera mabodza amene ‘atumwi opambana’ ankamuneneza. (2 Akor. 11:5, 6) Paulo anali kufuna kuti abale ndi alongo ake onse azimukonda kuchokera pansi pa mtima. Choncho anawalimbikitsa kuti ‘afutukule mtima wawo’ pomukonda iyeyo ndi Akhristu ena.

7. Kodi ‘tingafutukule bwanji mtima wathu’ posonyeza chikondi chaubale?

7 Nanga bwanji ifeyo? Kodi ‘tingafutukule bwanji mtima wathu’ posonyeza chikondi chaubale? Mwachibadwa, sizikhala zovuta kuti anthu a msinkhu umodzi kapena a fuko limodzi azikondana. Ndipo anthu amene amakonda zosangalatsa zofanana nthawi zambiri amachezera limodzi. Koma ngati zinthu zimene timachitira limodzi ndi Akhristu ena zikutilepheretsa kucheza ndi ena, tiyenera ‘kufutukula mtima wathu.’ N’chinthu chanzeru kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndi nthawi zingati pamene ndimapita mu utumiki kapena kuchita zinthu zosangalatsa ndi abale ndi alongo amene si anzanga apamtima? Ndikakhala ku Nyumba ya Ufumu, kodi ndimapewa kucheza ndi anthu atsopano chifukwa chokhulupirira kuti payenera kupita kaye nthawi asanakhale anzanga? Kodi ndimapereka moni kwa achikulire ndi ana omwe mumpingo?’

8, 9. Kodi malangizo a Paulo olembedwa pa Aroma 15:7, angatithandize bwanji kupatsana moni m’njira imene imalimbitsa chikondi chathu chaubale?

8 Pa nkhani yopatsana moni, mawu amene Paulo analembera Aroma angatithandize kuona Akhristu anzathu moyenera. (Werengani Aroma 15:7.) M’vesili, mawu achigiriki amene anawamasulira kuti “landiranani,” amatanthauza “kulandira munthu mokoma mtima kapena mochereza, kumulola kuti akhale m’gulu la anthu amene timacheza nawo ndiponso kuti akhale bwenzi lathu.” Mu nthawi za m’Baibulo, munthu wochereza akalandira alendo, ankawauza kuti wasangalala kwambiri kuwaona. Mophiphiritsira, Khristu watilandira mwanjira imeneyi ndipo ifeyo tikulimbikitsidwa kumutsanzira polandiranso Akhristu anzathu.

9 Tikamapereka moni kwa abale athu pa Nyumba ya Ufumu ndiponso malo ena, tizifunafuna makamaka anthu amene papita nthawi tisanawaone kapena kulankhula nawo. Zingakhale bwino kucheza ndi anthu amenewa kwa mphindi zingapo. Pamsonkhano wotsatira, tingacheze ndi anthu enanso. Tikamachita zimenezi, tidzaona kuti posakhalitsa tacheza ndi abale ndi alongo athu onse. Komabe sitiyenera kudandaula ngati talephera kulankhula ndi anthu onse tsiku limodzi. Palibe amene ayenera kukwiya chifukwa chakuti talephera kum’patsa moni pamsonkhano wina.

10. Kodi anthu onse mumpingo ali ndi mwayi wamtengo wapatali wotani, ndipo tingaugwiritse ntchito bwanji?

10 Kupereka moni kwa ena ndi njira yoyamba yosonyeza kuti tawalandira. Kuchita zimenezi kungatithandize kucheza bwino ndi abale athu ndiponso kupalana nawo ubwenzi wokhalitsa. Mwachitsanzo, anthu osadziwana amene ali pamsonkhano wachigawo kapena wadera, akapatsana moni, kucheza ndiponso kudziwana, amafuna kuti adzaonanenso nthawi ina. Antchito odzipereka omanga Nyumba za Ufumu komanso anthu amene amagwira ntchito zothandiza ena pakagwa zamwadzidzidzi, nthawi zambiri amapeza mabwenzi abwino pakati pa anthu amene akugwira nawo ntchito. Izi zimatero chifukwa chakuti zimene zimachitika akamagwira ntchito, zimathandiza kuti aliyense adziwe makhalidwe abwino a mnzake. M’gulu la Yehova muli mipata yambiri yopezera mabwenzi abwino. ‘Tikafutukula mtima wathu,’ tidzakhala ndi anzathu ambiri ndipo zimenezi zidzakulitsa chikondi chimene chimatigwirizanitsa pa kulambira koona.

Khalani Ochezeka

11. Monga mmene lemba la Maliko 10:13-16 likusonyezera, kodi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani?

11 Akhristu onse akhoza kuyesetsa kukhala ochezeka, ngati mmene Yesu analili. Taonani zimene Yesu anachita pamene ophunzira ake ankaletsa makolo kuti asabweretse ana kwa iye. Iye anawauza kuti: “Alekeni ana aang’onowo abwere kwa ine; musawaletse iyayi, pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa onga amenewa.” Kenako “anatenga anawo m’manja mwake ndi kuyamba kuwadalitsa, mwa kuwaika manja.” (Maliko 10:13-16) Ndithu, anawo ayenera kuti anasangalala kwambiri poona mmene Mphunzitsi Waluso anawasonyezera chikondi.

12. Kodi n’chiyani chingatilepheretse kucheza ndi anthu ena?

12 Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimapeza mpata wocheza ndi anthu, kapena nthawi zambiri ndimaoneka kuti ndilibe nthawi yocheza ndi anthu?’ Zinthu zina zomwe pazokha si zoipa, zikhoza kutilepheretsa kucheza ndi anthu. Mwachitsanzo, ngati nthawi zambiri tikakhala pa gulu timangokhalira kulankhula pafoni kapena kumvetsera mahedifoni, anthu akhoza kuona ngati sitikufuna kuti azitilankhulitsa. Ndiponso ngati nthawi zambiri anthu amationa tikugwiritsa ntchito kompyuta ya m’manja, angaone kuti sitikufuna kucheza nawo. N’zoona kuti pali “mphindi yakutonthola.” Koma tikakhala pa gulu, nthawi zambiri imeneyi imakhala “mphindi yakulankhula.” (Mlal. 3:7) Ena anganene kuti, “Sindikonda zolankhulalankhula,” kapena “Ndikangodzuka kumene sindifuna kulankhula.” Komabe, tikamayesetsa kulankhula mosangalala ndi anzathu, ngakhale pa nthawi imene sitikufuna, timasonyeza kuti tili ndi chikondi chimene “sichisamala zofuna zake zokha.”​—1 Akor. 13:5.

13. Kodi Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti aziwaona bwanji abale ndi alongo achikhristu?

13 Paulo analimbikitsa mnzake wachinyamata Timoteyo kuti azilemekeza anthu onse mumpingo. (Werengani 1 Timoteyo 5:1, 2.) Nafenso tiyenera kuona Akhristu achikulire ngati amayi ndiponso abambo athu, ndipo achinyamata tiziwaona monga achimwene ndi achemwali athu, kapena kuti ana a makolo athu enieni. Mtima umenewu, ungathandize kuti tikakhala ndi abale ndi alongo athu okondedwa, asamadzione ngati alendo.

14. Kodi ubwino wocheza ndi ena nkhani zolimbikitsa ndi wotani?

14 Tikamacheza ndi anzathu nkhani zolimbikitsa, timawathandiza kuti akhale anthu auzimu ndiponso osangalala. M’bale wina, amene akutumikira pa ofesi ina ya nthambi amakumbukira kuti atangofika kumene pa Beteli, panali abale achikulire angapo amene ankakonda kumulankhulitsa. Mawu olimbikitsa amene anali kumuuza, anamuchititsa kuti asamadzione ngati mlendo pa Beteli. Panopa, iye amatsanzira abale amenewo pocheza ndi anzake ena a pa Beteli.

Kudzichepetsa Kumatithandiza Kukhala Mwamtendere ndi Anzathu

15. Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti ngakhale pakati pa Akhristufe, pamakhala kusagwirizana nthawi zina?

15 Zikuoneka kuti Eodiya ndi Suntuke, alongo awiri achikhristu a ku Filipi, ankalephera kuthetsa vuto limene linali pakati pawo. (Afil. 4:2, 3) Mkangano woopsa wa pakati pa Paulo ndi Baranaba unadziwika kwa anthu ndipo unachititsa kuti asiye kuyendera limodzi kwakanthawi. (Mac. 15:37-39) Nkhani zimenezi zikusonyeza kuti ngakhale pakati pa olambira oona, pamakhala kusagwirizana nthawi zina. Yehova amatithandiza kuthetsa kusamvana ndi kukhazikitsanso mtendere ndi anzathu. Koma iye amafuna kuti tichite kaye kanthu kenakake.

16, 17. (a) Kodi kudzichepetsa n’kofunika motani pothetsa kusamvana? (b) Kodi nkhani ya mmene Yakobo anafikira kwa Esau, ikusonyeza bwanji kufunika kodzichepetsa?

16 Tayerekezerani kuti inuyo ndi mnzanu mukukonzekera kuyenda ulendo pagalimoto. Kuti munyamuke, muyenera kuiliza galimotoyo ndi kiyi wake. Kuthetsa kusagwirizana kumayambanso ndi kiyi yemwe ndi kudzichepetsa. (Werengani Yakobe 4:10.) Monga momwe chitsanzo cha m’Malemba chotsatirachi chikusonyezera, kiyi ameneyu amathandiza anthu amene akhumudwitsana kuti ayambe kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo.

17 Esau anakwiyira kwambiri Yakobo, m’bale wake amene anabadwa naye mapasa, chifukwa chomulanda ukulu ndipo ankafuna kumupha. Patadutsa zaka 20 chichitikireni zimenezi, mapasawa anatsala pang’ono kukumananso, “ndipo Yakobo anaopa kwambiri, navutidwa.” Iye anali kuganiza kuti mwina Esau amupha. Koma atayandikira m’bale wakeyo, Yakobo anachita chinthu chimene Esau sankayembekezera. Iye ‘anawerama pansi.’ Kodi chinachitika n’chiyani kenako? “Esau anathamangira kukomana naye nam’fungatira, nagwa pankhope pake, nam’psompsona; ndipo analira iwo.” Nkhondo imene ikanatha kuchitika pamenepa inapewedwa. Kudzichepetsa kwa Yakobo kunagonjetsa chidani chilichonse chimene mwina Esau anali nachobe.​—Gen. 27:41; 32:3-8; 33:3, 4.

18, 19. (a) Pakakhala kusagwirizana, n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamba ndife kugwiritsa ntchito malangizo a m’Malemba? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya mtima ngati pofuna kukhazikitsa mtendere, munthu winayo sakulabadira pa ulendo woyamba?

18 M’Baibulo muli malangizo abwino kwambiri a mmene tingathetsere kusagwirizana. (Mat. 5:23, 24; 18:15-17; Aef. 4:26, 27) * Koma kuti tithetsedi kusagwirizanako, tiyenera kugwiritsa ntchito malangizowo. Sitiyenera kuganiza kuti munthu winayo ndi amene ayenera kuyamba kudzichepetsa, chifukwa ifenso tili ndi kiyi wothetsera vutolo.

19 Ngati tayesetsa kukhazikitsa mtendere koma zikuoneka kuti sizikutheka, tisataye mtima. Mwina munthu winayo akufunika nthawi kuti mtima wake ukhale kaye m’malo. Abale ake a Yosefe anamuchitira zoipa kwambiri. Panapita nthawi yaitali kufikira pamene anadzamuonanso ali nduna yaikulu ya dziko la Iguputo. Koma pa nthawiyi anali atasintha maganizo ndipo anapempha Yosefe kuti awakhululukire. Yosefe anawakhululukiradi, ndipo ana a Yakobo anakhala mtundu umene unali ndi mwayi wapadera wotchedwa ndi dzina la Yehova. (Gen. 50:15-21) Tikamakhala mwamtendere ndi abale ndi alongo athu, timalimbikitsa mgwirizano ndi chimwemwe mumpingo.​—Werengani Akolose 3:12-14.

Tizikondana “mwa Zochita ndi Choonadi”

20, 21. Kodi zimene Yesu anachita posambitsa mapazi a atumwi ake, zikutiphunzitsa chiyani?

20 Yesu atatsala pang’ono kuphedwa, anauza atumwi ake kuti: “Ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.” (Yoh. 13:15) Iye anali atangomaliza kumene kusambitsa mapazi a atumwi ake 12. Yesu sanachite zimenezi pongotsatira mwambo kapena pongofuna kusonyeza kuti anali munthu wokoma mtima. Yohane asanafotokoze nkhani yonena zosambitsa mapaziyi, analemba kuti: “Popeza kuti [Yesu] anali kuwakonda akewo amene anali m’dzikoli, anawakonda mpaka mapeto.” (Yoh. 13:1) Chikondi chimene Yesu anali nacho pa ophunzira akewo, n’chimene chinamupangitsa kuwachitira zinthu zimene nthawi zambiri ankazichita ndi kapolo. Tsopano nawonso anayenera kuchitirana zinthu mwachikondi ndi modzichepetsa. Chikondi chenicheni chaubale chiyenera kutichititsa kuganizira ndi kusamalira abale ndi alongo athu onse achikhristu.

21 Mtumwi Petulo, amene anasambitsidwa mapazi ndi Mwana wa Mulungu, anamvetsetsa tanthauzo la zimene Yesu anachita. Iye analemba kuti: “Tsopano, popeza kuti mwayeretsa miyoyo yanu mwa kukhala omvera choonadi ndipo zotsatira zake n’zakuti muli ndi chikondi chaubale chopanda chinyengo, kondanani kwambiri kuchokera mu mtima.” (1 Pet. 1:22) Mtumwi Yohane, amene mapazi akenso anasambitsidwa ndi Ambuye, analemba kuti: “Ana anga apamtimanu, tisakondane ndi mawu okha kapena ndi lilime lokha, koma mwa zochita ndi choonadi.” (1 Yoh. 3:18) Tiyeni tizisonyeza chikondi kwa abale athu mwa zochita zathu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 18 Onani buku la Gulu Lochita Chifuniro cha Yehova, tsamba 144-150.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi ‘tingafutukule bwanji mtima wathu’ posonyezana chikondi?

• Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tikhale ochezeka?

• Kodi kudzichepetsa kumathandiza bwanji pokhazikitsa mtendere?

• Kodi n’chiyani chiyenera kutichititsa kusamalira Akhristu anzathu?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 21]

Muzilandira mwansangala Akhristu anzanu

[Chithunzi patsamba 23]

Musamalole kuti mpata wocheza ndi anthu ena ukudutseni