Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yamikirani Malo Anu Mumpingo wa Mulungu

Yamikirani Malo Anu Mumpingo wa Mulungu

Yamikirani Malo Anu Mumpingo wa Mulungu

“Mulungu anaika ziwalo m’thupi, chilichonse m’malo ake, mmene iye anafunira.”​—1 AKOR. 12:18.

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chimene chikusonyeza kuti aliyense mumpingo angakhale ndi malo ofunika kuwayamikira? (b) Kodi m’nkhani ino tikambirana mafunso ati?

KUYAMBIRA nthawi ya Aisiraeli, Yehova wakhala akugwiritsa ntchito mpingo pofuna kupereka chakudya chauzimu ndi malangizo. Mwachitsanzo, Aisiraeli atagonjetsa mzinda wa Ai, Yoswa “anawerenga mawu onse a chilamulo, dalitso ndi temberero, monga mwa zonse zolembedwa m’buku la chilamulo . . . pamaso pa msonkhano [mpingo] wonse wa Israyeli.”​—Yos. 8:34, 35.

2 M’nthawi ya atumwi, mtumwi Paulo anauza Timoteyo yemwe anali mkulu wachikhristu, kuti mpingo wachikhristu ndi “nyumba ya Mulungu” ndiponso “mzati ndi mchirikizo wa choonadi.” (1 Tim. 3:15) Masiku ano, “nyumba” ya Mulungu ndi gulu lapadziko lonse la Akhristu oona. Mu chaputala 12 cha kalata youziridwa yoyamba ya Paulo yopita kwa Akorinto, iye anayerekezera mpingo ndi thupi la munthu. Iye ananena kuti ngakhale kuti chiwalo chilichonse chili ndi ntchito yosiyana ndi chinzake, zonse ndi zofunika. Paulo analemba kuti: “Mulungu anaika ziwalo m’thupi, chilichonse m’malo ake, mmene iye anafunira.” Iye ananenanso kuti “mbali za thupi zimene timaziona ngati zosalemekezeka kwambiri, n’zimene timazipatsa ulemu wochuluka.” (1 Akor. 12:18, 23) Motero malo a Mkhristu wina wokhulupirika m’nyumba ya Mulungu saposa malo a Mkhristu wina wokhulupirikanso. Malowo amangokhala osiyana basi. Ndiyeno kodi tingatani kuti tidziwe malo athu m’makonzedwe a Mulungu ndi kuwasunga bwino? Kodi ndi zinthu ziti zimene zimakhudza malo athu? Kodi tingatani kuti ‘kupita kwathu patsogolo kuonekere kwa anthu onse’?​—1 Tim. 4:15.

Kodi Tingasonyeze Bwanji Kuti Timayamikira Malo Athu Mumpingo wa Mulungu?

3. Kodi njira ina imene tingapezere malo athu mumpingo, ndiponso imene tingasonyezere kuti timawayamikira, ndi iti?

3 Njira ina imene tingapezere malo athu mumpingo ndiponso imene tingasonyezere kuti timawayamikira ndiyo kumvera ndi mtima wonse “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndi Bungwe Lolamulira limene amagwiritsa ntchito. (Werengani Mateyo 24:45-47.) Tifunika kudzifufuza n’kuona ngati ifeyo timamvera malangizo amene kapolo amatipatsa. Mwachitsanzo pa zaka zapitazi, takhala tikulandira malangizo osapita m’mbali onena za kavalidwe ndi kaonekedwe kathu, zosangalatsa ndiponso onena za njira yolakwika yogwiritsira ntchito Intaneti. Kodi timatsatira mosamalitsa uphungu wabwino umenewu n’cholinga chakuti tikhale otetezeka mwauzimu? Nanga bwanji za malangizo akuti tikhale ndi pulogalamu ya kulambira kwa pabanja? Kodi tatsatira malangizo amenewa mwa kupatula nthawi yochita kulambira kwa pabanja? Ngati sitili pa banja, kodi timakhala ndi nthawi yophunzira Malemba patokha? Ngati ife tonse payekhapayekha ndiponso mabanja titsatira malangizo a kapolo, Yehova adzatidalitsa.

4. Kodi tiyenera kuganizira chiyani tikamapanga zosankha zokhudza nkhani zaumwini?

4 Anthu ena angaganize kuti nkhani ya kavalidwe ndi kaonekedwe kathu ndiponso zosangalatsa, si nkhani yosankhirana koma munthu angasankhe yekha. Komabe, Mkhristu wodzipereka amene amayamikira malo ake mumpingo, samangoyendera zokonda zake popanga zosankha. Iye makamaka amafunika kuyendera maganizo a Yehova ofotokozedwa m’Mawu ake, Baibulo. Uthenga wa m’Baibulo uyenera kukhala ‘nyali yakumapazi athu, ndi kuunika kwa panjira pathu.’ (Sal. 119:105) Komanso ndi bwino kuganizira mmene zosankha zathu zimakhudzira utumiki wathu ndiponso anthu ena, mumpingo ndi kunja komwe.​—Werengani 2 Akorinto 6:3, 4.

5. Kodi n’chifukwa chiyani tifunika kusamala kuti tisakhale ndi mzimu wopandukira?

5 “Mzimu umene tsopano ukugwira ntchito mwa ana a kusamvera,” uli paliponse mofanana ndi mpweya umene timapuma. (Aef. 2:2) Chifukwa cha mzimu umenewu, tingayambe kuganiza kuti sitikufunikira malangizo ochokera ku gulu la Yehova. Ifetu sitikufuna kukhala ngati Diotirefe, amene ‘sankalandira chilichonse mwaulemu kuchokera kwa mtumwi Yohane.’ (3 Yoh. 9, 10) Tifunika kusamala kuti tisakhale ndi mzimu wopandukira. Tisayese ngakhale pang’ono kulankhula kapena kuchita zinthu zimene zingasonyeze kuti sitilemekeza njira imene Yehova akulankhulira nafe masiku ano. (Num. 16:1-3) Koma tiyeni tiziyamikira mwayi umene tili nawo womvera ndiponso wogwira ntchito limodzi ndi kapolo. Ndiponso tiyenera kuyesetsa kumvera komanso kugonjera amene akutitsogolera mumpingo wathu.​—Werengani Aheberi 13:7, 17.

6. Kodi n’chifukwa chiyani nthawi ndi nthawi tifunika kumaona mmene zinthu zilili pa moyo wathu?

6 Njira inanso imene timasonyezera kuti timayamikira malo athu mumpingo, ndi kuona nthawi ndi nthawi mmene zinthu zilili pa moyo wathu n’cholinga chakuti tizichita zonse zomwe tingathe kuti ‘tilemekeze utumiki wathu’ ndiponso Yehova. (Aroma 11:13) Ena amatha kuyamba upainiya wokhazikika. Padziko lonse lapansi, ena amachita mitundu ina ya utumiki wapadera monga umishonale, kukhala oyang’anira oyendayenda ndi kutumikira pa Beteli. Abale ndi alongo ambiri amathandiza pa ntchito yomanga Nyumba za Ufumu. Ndiponso pali anthu ambiri a Yehova amene akuyesetsa kusamalira mabanja awo mwauzimu ndipo amalalikira mwachangu mlungu uliwonse. (Werengani Akolose 3:23, 24.) Tili ndi chikhulupiriro chakuti ngati tidzipereka mwa kufuna kwathu pa utumiki wa Mulungu ndi kumutumikira ndi moyo wathu wonse, sitidzasowa malo m’gulu la Mulungu.

Zinthu Zimene Zimakhudza Malo Athu

7. Kodi mmene zinthu zilili pa moyo wathu, zimakhudza bwanji malo athu mumpingo?

7 Tifunika kumaona mmene zinthu zilili pa moyo wathu chifukwa chakuti, mwanjira inayake, malo athu mumpingo amadalira zimene timachita kapena zimene tingathe kuchita. Mwachitsanzo, malo amene abale ali nawo mumpingo amasiyana mwa njira zina ndi a alongo. Zimene timatha kuchita potumikira Yehova zimadaliranso zaka zathu, thanzi ndi zinthu zina. Lemba la Miyambo 20:29 limati: “Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yawo; kukongola kwa nkhalamba ndi imvi.” Achinyamata mumpingo angathe kugwira ntchito zambiri chifukwa ali ndi mphamvu, pamene achikulire amathandiza kwambiri mpingo chifukwa cha nzeru yawo ndiponso zinthu zambiri zimene aona pa moyo wawo. Tifunikanso kukumbukira kuti chilichonse chimene tingachite m’gulu la Yehova, chimatheka chifukwa cha kukoma mtima kwa m’chisomo cha Mulungu.​—Mac. 14:26; Aroma 12:6-8.

8. Kodi zimene mtima wathu umafuna, zimakhudza bwanji zochita zathu mumpingo?

8 Pali chinthu chinanso chimene chimakhudza malo athu mumpingo. Tiyerekeze kuti pali alongo awiri achitsikana apachibale. Onse awiri amaliza sukulu ndipo ali ndi moyo wofanana. Makolo awo anayesetsa kuwalimbikitsa kuti akamaliza sukulu, adzakhale apainiya. Koma atamaliza sukulu, mmodzi akuyamba upainiya, pamene winayo akuyamba ntchito. N’chifukwa chiyani asankha kuchita zosiyana? Chifukwa cha cholinga chimene aliyense anali nacho. Aliyense akuchita zimene ankafuna. Kodi izi si zimenenso zimachitika kwa ambirife? Tiyenera kuganizira bwinobwino zimene tikufuna kuchita mu utumiki wa Mulungu. Kodi tingathe kuwonjezera utumiki wathu, ngakhale ngati zimenezi zingafune kuti tisinthe zina ndi zina pa moyo wathu?​—2 Akor. 9:7.

9, 10. Kodi tingachite chiyani ngati tilibe mtima wofuna kuchita zambiri mu utumiki wa Yehova?

9 Nanga bwanji ngati tilibe mtima wofuna kuchita zambiri mu utumiki wa Yehova ndipo timangokhutira ndi zochepa zimene timachita mumpingo? M’kalata yake yopita kwa Afilipi, Paulo anati: “Mwa kufuna kwake, Mulungu ndiye amene akugwira ntchito pakati panu, kuti inu mufune ndi kuchita.” Zoonadi, Yehova angagwire ntchito mwa ife ndi kutithandiza kuti tikhale ndi mtima wofunitsitsa kuchita zambiri.​—Afil. 2:13; 4:13.

10 Ngati Yehova amachita zimenezi, kodi sitiyenera kumupempha kuti atithandize kukhala ndi mtima wofuna kuchita chifuniro chake? Zimenezi ndi zimene Mfumu Davide ya Isiraeli inachita. Iye anapemphera kuti: “Mundidziwitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse; pakuti Inu ndinu Mulungu wa chipulumutso changa; Inu ndikuyembekezerani tsiku lonseli.” (Sal. 25:4, 5) Nafenso tingachite zimenezi mwa kupempha Yehova kuti atipatse mtima wofuna kuchita zinthu zimene iye amasangalala nazo. Tikamaganizira mmene Yehova Mulungu ndi Mwana wake amaonera zimene timachita popititsa patsogolo zolinga zawo, mitima yathu imadzaza ndi chiyamiko. (Mat. 26:6-10; Luka 21:1-4) Mtima woyamikira umenewu, ungatilimbikitse kupempha Yehova kuti atipatse maganizo ofuna kupita patsogolo mwauzimu. Mneneri Yesaya anatipatsa chitsanzo cha mtima umene tiyenera kukhala nawo. Iye anamva Yehova akufunsa kuti: “Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife?” Atamva zimenezi, anayankha kuti: “Ndine pano; munditumize ine.”​—Yes. 6:8.

Kodi Tingatani Kuti Tipite Patsogolo?

11. (a) N’chifukwa chiyani abale afunika kuyesetsa kuti akhale ndi maudindo m’gulu? (b) Kodi m’bale angachite chiyani kuti ayenerere kupatsidwa udindo mumpingo?

11 M’chaka cha utumiki cha 2008, anthu 289,678 anabatizidwa padziko lonse. Chifukwa cha zimenezi, n’zoonekeratu kuti pakufunikira abale ambiri otsogolera. Kodi kudziwa zimenezi kuyenera kulimbikitsa m’bale aliyense kuchita chiyani? Kunena mosapita m’mbali, m’bale aliyense ayenera kuyesetsa kukwaniritsa ziyeneretso za atumiki othandiza ndi akulu zofotokozedwa m’Malemba. (1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9) Kodi m’bale angatani kuti akwaniritse ziyeneretso za m’Malemba zimenezi? Angachite zimenezi mwa kulalikira mwachangu, kugwira mwakhama ntchito zimene amapatsidwa mumpingo, kuyesetsa kuti azipereka ndemanga zatanthauzo pamisonkhano yachikhristu ndiponso kusonyeza chidwi kwa okhulupirira anzake. Akamachita zimenezi amasonyeza kuti amayamikira malo ake mumpingo.

12. Kodi anyamata angasonyeze bwanji kuti amakonda choonadi?

12 Kodi abale achinyamata, makamaka amene ali ndi zaka za pakati pa 13 ndi 19, angatani kuti apite patsogolo mumpingo? Ayenera kuyesetsa kuti akule mu ‘nzeru ndi kumvetsetsa zinthu zauzimu’ mwa kuphunzira Malemba. (Akol. 1:9) Kuti zimenezi zitheke, iwo ayenera kukhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu mwakhama ndiponso kukonzekera ndi kutenga nawo mbali m’misonkhano ya mpingo. Anyamata angachitenso zambiri mwa kuyesetsa kuchita zinthu zimene zingawathandize kuyenerera kulowa pa “khomo la ntchito yaikulu.” Ndipo ntchito yakeyo ndi mitundu yosiyanasiyana ya utumiki wanthawi zonse. (1 Akor. 16:9) Kugwira ntchito yotumikira Yehova ndiye chinthu chosangalatsa kwambiri pa moyo ndiponso kumabweretsa madalitso ankhaninkhani.​—Werengani Mlaliki 12:1.

13, 14. Kodi alongo angasonyeze bwanji kuti amayamikira malo awo mumpingo?

13 Alongo nawonso angasonyeze kuti amayamikira mwayi umene ali nawo wothandiza kukwaniritsa lemba la Salmo 68:11. Lembali limati: “Ambuye anapatsa mawu: Akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.” Njira yaikulu imene alongo angasonyezere kuti amayamikira malo awo mumpingo, ndiyo kugwira nawo ntchito yopanga ophunzira. (Mat. 28:19, 20) Choncho, alongo akamadzipereka kwambiri pa ntchito yolalikira, ndiponso akamadzimana mwa kufuna kwawo chifukwa cha ntchito imeneyi, amasonyeza kuti amayamikira malo awo mumpingo.

14 Polembera Tito kalata, Paulo anati: “Akazi achikulire akhale ndi khalidwe loyenera anthu opembedza, . . . [akhale] aphunzitsi a zinthu zabwino; kuti akumbutse akazi ocheperapo msinkhu kukonda amuna awo, kukonda ana awo, kukhala oganiza bwino, oyera, ogwira ntchito zapakhomo, abwino, omvera amuna awo, kuti mawu a Mulungu asanyozedwe.” (Tito 2:3-5) Zoonadi, alongo achikulire angathandize kwambiri mumpingo. Iwo akamalemekeza abale omwe amatsogolera, ndiponso akamapanga zosankha zanzeru pa nkhani monga za kavalidwe ndi kaonekedwe komanso zosangalatsa, amapereka chitsanzo chabwino kwa ena ndipo amasonyeza kuti amalemekeza kwambiri malo awo mumpingo.

15. Kodi mlongo wosakwatiwa angapirire bwanji vuto la kusungulumwa?

15 Nthawi zina mlongo wosakwatiwa angavutike kupeza malo ake mumpingo. Mlongo wina amene izi zamuchitikirapo anati: “Ukakhala wosakwatiwa, nthawi zina umasungulumwa.” Atafunsidwa zimene amachita kuti apirire vuto lakelo, iye anati: “Pemphero ndi phunziro n’zimene zimandithandiza kupezanso malo anga. Ndikamaphunzira, ndimayesetsa kuti ndidziwe mmene Yehova amandionera. Kenako ndimayesetsa kuthandiza ena mumpingo. Zimenezi zimandithandiza kuti ndisamangoganiza za ineyo basi.” Malinga ndi lemba la Salmo 32:8, Yehova anauza Davide kuti: “Ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.” Zoonadi, Yehova amachita chidwi ndi mtumiki wake aliyense, kuphatikizapo alongo osakwatiwa, ndipo amathandiza aliyense kupeza malo ake mumpingo.

Sungani Malo Anu

16, 17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani kuvomera chiitano cha Yehova chakuti tikhale m’gulu lake, ndi chosankha chabwino kwambiri? (b) Kodi tingatani kuti tisunge malo athu m’gulu la Yehova?

16 Chifukwa cha chikondi chake, Yehova wakoka mtumiki wake aliyense kuti akhale naye pa ubwenzi. Yesu anati: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” (Yoh. 6:44) Pa anthu mabiliyoni amene ali padziko lapansili, Yehova waitana ifeyo aliyense payekhapayekha kuti tikhale mumpingo wake. Povomera chiitano chimenechi, tinasankha bwino kwambiri. Chifukwa cha zimenezi, moyo wathu ndi watanthauzo kwambiri. Ndipotu timasangalala komanso tili ndi mtendere chifukwa chokhala ndi malo mumpingo.

17 Wamasalmo anati: “Yehova, ndikonda chikhalidwe cha nyumba yanu.” Iye anaimbanso kuti: “Phazi langa liponda pachidikha: M’masonkhano ndidzalemekeza Yehova.” (Sal. 26:8, 12) Mulungu woona ali ndi malo a munthu aliyense m’gulu lake. Tikamatsatira malangizo a gulu la Mulungu ndi kutanganidwa mu utumiki wake, timasunga malo athu amtengo wapatali m’kakonzedwe ka Yehova.

Kodi Mukukumbukira?

• N’chifukwa chiyani m’pomveka kunena kuti Mkhristu aliyense ali ndi malo ake mumpingo?

• Kodi timasonyeza bwanji kuti timayamikira malo athu m’gulu la Mulungu?

• Kodi ndi zinthu ziti zimene zimakhudza malo athu mumpingo?

• Kodi Akhristu achinyamata ndi achikulire omwe angasonyeze bwanji kuti amayamikira malo awo m’kakonzedwe ka Mulungu?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 16]

Kodi abale angatani kuti ayenerere maudindo mumpingo?

[Chithunzi patsamba 17]

Kodi alongo angasonyeze bwanji kuti amayamikira malo awo mumpingo?