Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Khalani Ndi Chikondi Chimene Sichitha Konse

Khalani Ndi Chikondi Chimene Sichitha Konse

Khalani Ndi Chikondi Chimene Sichitha Konse

‘Chikondi chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha konse.’​—1 AKOR. 13:7, 8.

1. (a) Kodi anthu achita zotani pa nkhani ya chikondi? (b) Kodi kwenikweni anthu amakonda chiyani?

PALI zinthu zambiri zimene zafalitsidwa zokhudza chikondi. M’nyimbo zambiri, anthu amatamanda ndi kukokomeza chikondi. Ndipotu chikondi ndi chofunika kwambiri kwa munthu aliyense. Mabuku ndiponso mafilimu ambiri, amakhala ndi nkhani zachikondi zongopeka ndipo amapezeka ambirimbiri pamsika. Komabe n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri sakonda Mulungu komanso anthu anzawo. Zimene tikuona, n’zimene Baibulo linalosera kuti zidzachitika m’masiku otsiriza ano. Anthu ndi “odzikonda, okonda ndalama, . . . okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”​—2 Tim. 3:1-5.

2. Kodi Baibulo limapereka chenjezo lotani pa nkhani yokonda zinthu zolakwika?

2 Anthu analengedwa moti angathe kusonyeza chikondi, komabe Mawu a Mulungu amatichenjeza kuti tipewe kukonda zinthu zolakwika. Ndipo Baibulo limafotokoza zimene zimachitika munthu akamakonda zinthu zolakwika mumtima mwake. (1 Tim. 6:9, 10) Kodi mukukumbukira zimene mtumwi Paulo analemba zokhudza Dema? Ngakhale kuti poyamba ankagwirizana ndi Paulo, iye anasintha n’kuyamba kukonda zinthu za m’dziko. (2 Tim. 4:10) Nayenso mtumwi Yohane anachenjeza Akhristu za vuto limeneli. (Werengani 1 Yohane 2:15, 16.) N’zosatheka kukonda dziko ndiponso zinthu zosakhalitsa za m’dzikoli, kwinaku n’kumakondanso Mulungu ndi zinthu zimene amaphunzitsa.

3. Kodi tikukumana ndi vuto lotani, nanga tingadzifunse mafunso otani?

3 Ngakhale kuti tikukhalabe m’dzikoli, sitili mbali yake. Motero, n’zovuta kuti tipewe kukonda zinthu zolakwika monga mmene anthu ambiri m’dzikoli akuchitira. M’pofunika kusamala kwambiri kuti tisakodwe mumsampha wokonda zinthu zolakwika. Ndiyeno kodi tiyenera kusonyeza chikondi kwa ndani? Kodi pali zinthu ziti zimene zingatithandize kukhala ndi chikondi chimene chimapirira zinthu zonse ndiponso chimene sichitha konse? Kodi chikondi chimenechi chingatithandize bwanji masiku ano ndipo chimakhudza bwanji tsogolo lathu? Kuti tidziwe zolondola, tifunika kupeza mayankho ochokera kwa Mulungu.

Kulitsani Chikondi Chanu pa Yehova

4. Kodi tingakulitse bwanji chikondi chathu pa Mulungu?

4 Taganizirani za mlimi amene wagwira ntchito mwakhama kukonza munda wake n’kubzala mbewu. Iye amayembekezera kuti mbewuzo zikula. (Aheb. 6:7) Mofanana ndi zimenezi, chikondi chathu pa Mulungu chiyenera kukula. Kodi chofunika n’chiyani kuti chikondicho chikule? Tiyenera kukonza bwino mtima wathu. Mtima wathuwo ndiwo nthaka imene munabzalidwa mbewu za choonadi cha Ufumu. Tingachite zimenezi mwa kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu kuti timudziwe bwino. (Akol. 1:10) Kupezeka pamisonkhano nthawi zonse ndiponso kutenga nawo mbali, kungatithandizenso kudziwa zambiri. Kodi ifeyo patokha timayesetsa kuti tidziwe zinthu zozama?​—Miy. 2:1-7.

5. (a) Kodi n’chiyani chingatithandize kuphunzira makhalidwe akuluakulu a Yehova? (b) Kodi mungafotokoze chiyani pa chilungamo, nzeru ndiponso mphamvu za Mulungu?

5 Yehova amafotokoza umunthu wake kudzera m’Mawu ake. Tikamaphunzira Malemba ndiponso kupitirizabe kudziwa za Yehova, timamvetsa makhalidwe ake akuluakulu monga chilungamo, mphamvu, nzeru ndi chikondi chake chosayerekezeka. Chilungamo cha Yehova chimaonekera m’njira zake zonse ndiponso m’malamulo ake omwe ndi angwiro. (Deut. 32:4; Sal. 19:7) Tikaganizira chinthu chilichonse chimene Yehova analenga, timamulemekeza chifukwa chakuti timaona kuti ali ndi nzeru zapamwamba. (Sal. 104:24) Chilengedwe chimasonyezanso kuti Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire.​—Yes. 40:26.

6. Kodi Mulungu wasonyeza bwanji chikondi chake kwa ife ndipo kodi zimene anachita zimatikhudza motani?

6 Kodi tinganene chiyani pa chikondi cha Mulungu, chimene ndi khalidwe lake lalikulu koposa? Khalidweli limakhudza munthu aliyense ndipo Yehova analisonyeza mwa kupereka dipo kuti atipulumutse. (Werengani Aroma 5:8.) Dipo limeneli linaperekedwa chifukwa cha munthu aliyense padziko lapansi, koma amene amapindula nalo ndi amene amayamikira chikondi cha Mulungu ndiponso kukhulupirira Mwana wake. (Yoh. 3:16, 36) Popeza Mulungu anapereka Yesu monga nsembe ya chiyanjanitso chifukwa cha machimo athu, tiyenera kum’konda posonyeza kuyamikira.

7, 8. (a) Kodi chofunika n’chiyani kuti tisonyeze kuti timakonda Mulungu? (b) Kodi atumiki a Mulungu amamvera malamulo ake ngakhale kuti akukumana ndi mavuto otani?

7 Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu chifukwa choyamikira zonse zimene watichitira? Yankho lofunika kwambiri la funso limeneli limapezeka m’Baibulo ndipo ndi lakuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake; ndipo malamulo akewo si olemetsa.” (1 Yoh. 5:3) Inde, kukonda Yehova Mulungu n’kumene kumatichititsa kumvera malamulo ake. Ichi n’chifukwa chimodzi chimene chimatilimbikitsa kuchitira umboni za dzina lake ndiponso Ufumu wake, ndipo tikamachita zimenezi timathandiza kwambiri anthu. Tikamachita zimenezi chifukwa chomuyamikira kuchokera pansi pa mtima, timasonyeza kuti tili ndi zolinga zoyenera pomvera malamulo a Mulungu.​—Mat. 12:34.

8 Padziko lonse, abale athu akupitirizabe kumvera Mulungu polalikira ngakhale kuti amakumana ndi anthu opanda chidwi ndiponso otsutsa kwambiri uthenga wa Ufumu. Iwo amachita khama kuti akwaniritse utumiki wawo bwino lomwe. (2 Tim. 4:5) Ifenso timayesetsa mmene tingathere kuti tidziwitse ena za Mulungu ndipo timayesetsanso kusunga malamulo ake onse.

Chifukwa Chake Timamvera Ambuye Wathu Yesu Khristu

9. Kodi Khristu anapirira zinthu ziti, ndipo kodi n’chiyani chinamuthandiza?

9 Kuwonjezera pa kukonda Mulungu, palinso zifukwa zambiri zokulitsira chikondi chathu pa Mwana wake. Ngakhale kuti Yesu sitinamuonepo, chikondi chathu pa iye chimakula tikamaphunzira zambiri za iye. (1 Pet. 1:8) Kodi zina mwa zinthu zimene Yesu anapirira ndi ziti? Pamene ankachita chifuno cha Atate wake, iye anadedwa popanda chifukwa, anazunzidwa, ananamiziridwa, anachitidwa chipongwe ndiponso ananyozedwa m’njira zina zosiyanasiyana. (Werengani Yohane 15:25.) Chifukwa chakuti Yesu ankakonda Atate wake wakumwamba, anapirira mayesero onsewo. Ndipo chifukwa cha chikondi, iye analolera kufa imfa ya nsembe kuti apereke dipo la anthu ambiri.​—Mat. 20:28.

10, 11. Tikaganizira zimene Khristu anatichitira, kodi tikufunitsitsa kuchita chiyani?

10 Zimene Yesu anachita, zimatilimbikitsa kum’konda. Tikamaganizira zimene Khristu anatichitira, chikondi chathu pa iye chimakula. Popeza ndife otsatira ake, tiyenera kukhala ndi chikondi ngati cha Khristu kuti tipitirizebe kumvera lamulo lake lolalikira Ufumu ndi kupanga ophunzira.​—Mat. 28:19, 20.

11 Kuyamikira chikondi chimene Khristu anasonyeza kwa anthu, kumatichititsa kuti tiyesetse kumaliza ntchito yathu mapeto asanafike. (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Chikondi chimene Yesu anasonyeza n’chofunika kwambiri pokwaniritsa cholinga cha Mulungu kwa anthu. Ndipo chitsanzo chimene Khristu anatisiyira kuti titsatire, chimathandiza kuti aliyense achite mbali yake pokwaniritsa cholinga cha Mulungu. Kuti zimenezi zitheke, tiyenera kukulitsa kwambiri chikondi chathu pa Mulungu mmene tingathere. (Mat. 22:37) Tikamamvera zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso tikamamvera malamulo ake, timasonyeza kuti timamukonda. Timasonyezanso kuti timafunitsitsa kukweza ulamuliro wa Mulungu zivute zitani, ngati mmene Yesu anachitira.​—Yoh. 14:23, 24; 15:10.

Tsatirani Njira Yopambana ya Chikondi

12. Kodi Paulo anali kutanthauza chiyani pamene ananena za “njira yopambana”?

12 Mtumwi Paulo ankatsatira mapazi a Khristu mosamala, ndipo chifukwa cha zimenezi iye anali ndi ufulu wouza abale ake kuti azimutsanzira iyeyo. (1 Akor. 11:1) Ngakhale kuti Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Korinto kuti ayesetse kukhala ndi mphatso zina za mzimu, zimene Akhristu ankakhala nazo m’nthawi ya atumwi monga kuchiritsa ndi kulankhula malilime, iye anawasonyeza kuti pali chinthu chinanso chofunika kwambiri kuchitsatira. Pa 1 Akorinto 12:31, iye ananena kuti: “Komabe, ine ndikuonetsani njira yopambana.” Mavesi otsatira, amasonyeza kuti iye ankanena za njira yopambana ya chikondi. Kodi chikondi n’chopambana m’njira yotani? Paulo anapereka fanizo losonyeza zimene anali kutanthauza. (Werengani 1 Akorinto 13:1-3.) Ngati iye akanakhala ndi luso lapadera ndiponso n’kumatha kuchita zinthu zikuluzikulu koma n’kukhala wopanda chikondi, ndiye kuti zinthuzo zikanakhala zopanda phindu. Motsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu, iye anafotokoza mfundo yochititsa chidwi imeneyi. Pamenepatu anatiuza mfundo yokhudza mtima kwambiri.

13. (a) Tchulani lemba la chaka cha 2010. (b) Kodi chikondi sichitha m’njira yotani?

13 Kenako Paulo anafotokoza zimene chikondi chimachita ndi zimene sichichita. (Werengani 1 Akorinto 13:4-8.) Ndiyeno ganizirani ngati mumakwaniritsa zimene chikondi chimafuna. Kwenikweni muganizire mbali yomaliza ya vesi 7, ndi chiganizo choyamba cha vesi 8. Pamenepa pali mawu akuti: ‘Chikondi chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha konse.’ Mawu amenewa ndi amene adzakhale lemba la chaka cha 2010. Onani kuti mu vesi 8, Paulo ananena kuti mphatso za mzimu, monga kunenera ndiponso kulankhula malilime, zimene Akhristu ankakhala nazo mpingo utangoyamba kumene, zidzatha. Sizidzakhalaponso. Koma chikondi sichidzatha. Yehova ndiye chimake cha chikondi, ndipo adzakhalako kosatha. Choncho, chikondi sichidzatha konse. Chidzakhalako kwamuyaya chifukwa ndi khalidwe la Mulungu wathu yemwenso adzakhalapo kwamuyaya.​—1 Yoh. 4:8.

Chikondi Chimapirira Zinthu Zonse

14, 15. (a) Kodi chikondi chimatithandiza bwanji kupirira mayesero? (b) N’chifukwa chiyani m’bale wina wachinyamata anakana kugonja?

14 Kodi n’chiyani chimathandiza Akhristu kupirira mayesero ndiponso mavuto osiyanasiyana amene amakumana nawo? Iwo ali ndi chikondi chimene munthu amakhala nacho chifukwa cha chikumbumtima chophunzitsidwa Baibulo. Chikondi choterechi chimafuna zambiri osati kungololera kutaya ndiponso kudzimana zinthu zakuthupi. Munthu wotere amakhala wofunitsitsa kukhalabe ndi mtima wosagawanika ndipo amalolera ngakhale kufa kumene chifukwa chokonda Khristu. (Luka 9:24, 25) Taganizirani za Mboni zokhulupirika zimene zinatsekeredwa komanso kuzunzidwa m’ndende zosiyanasiyana pa nthawi ya nkhondo yachiwiri ya padziko lonse, ndiponso nkhondoyi itatha.

15 M’bale wina wachinyamata wa ku Germany, dzina lake Wilhelm, anapereka chitsanzo chabwino pa nkhani imeneyi. Pamene asilikali a Nazi ankafuna kumuwombera, iye anakhalabe wokhulupirika ndipo sanagonje. M’kalata yotsanzika imene analembera anthu a m’banja lake iye anati: “Mogwirizana ndi zimene Mtsogoleri wathu Yesu Khristu ananena, tiyenera kukonda kwambiri Mulungu kuposa aliyense. Tikakhala kumbali yake, iye adzatipatsa mphoto.” Patapita nthawi, m’bale wake wina ananena mawu otsatirawa mu nkhani ina ya mu Nsanja ya Olonda: “Pa nthawi zonse zovuta, banja lathu lonse limaonetsetsa kuti kukonda Mulungu kukhale pamalo oyamba.” Awa ndi maganizo amenenso abale ambiri omwe atsekeredwa m’ndende ku Armenia, Eritrea, South Korea ndiponso m’mayiko ena, ali nawo. Abale amenewa salola kuti chikondi chawo pa Yehova chigwedezeke.

16. Kodi abale athu ku Malawi anakumana ndi zotani?

16 M’mayiko ambiri, chikhulupiriro cha abale athu chimayesedwa m’njira zosiyanasiyana ndipo amafunika kupirira. Mwachitsanzo kwa zaka 26, Mboni za Yehova ku Malawi zinapirira pamene boma linawaletsa kulambira, pamene ankatsutsidwa ndiponso kuchitiridwa nkhanza zosaneneka. Komabe iwo adalitsidwa chifukwa cha kupirira kwawo. Pamene mavutowa ankayamba, m’dzikoli munali Mboni pafupifupi 18,000 zokha. Koma patatha zaka 30, chiwerengerochi chinawonjezeka kwambiri kufika pa 38,393. Izi n’zimene zachitikanso m’mayiko ena.

17. Kodi anthu amene ali m’banja loti ena si Mboni, amakumana ndi mavuto otani, ndipo n’chiyani chimawathandiza kupirira?

17 N’zoona kuti atumiki a Mulungu onse amavutika akamazunzidwa ndi anthu otsutsa. Koma zimakhala zopweteka kwambiri ngati Mkhristu akuzunzidwa ndi achibale ake. Nthawi zina munthu amasowa mtendere chifukwa chotsutsidwa ndi anthu a m’banja lake kapena achibale ena. Izi ndi zimene Yesu ananena kuti zidzachitika ndipo zachitikiradi anthu ambiri. (Mat. 10:35, 36) Achinyamata ena amatsutsidwa ndi makolo awo osakhulupirira. Ndipo ena athamangitsidwa panyumba pawo n’kumakasungidwa ndi Mboni zina. Ena amakanidwa ndi makolo kapena achibale awo. Kodi n’chiyani chimathandiza anthu oterewa kupirira? Chifukwa chakuti kuwonjezera pa kukonda abale awo achikhristu, iwo amakonda kwambiri Yehova ndiponso Mwana wake.​—1 Pet. 1:22; 1 Yoh. 4:21.

18. Kodi chikondi chimene chimapirira zinthu zonse chimathandiza bwanji Akhristu okwatirana?

18 Pali zinthu zambiri m’moyo zimene zimafuna kuti tikhale ndi chikondi chimene chimapirira zinthu zonse. Chikondi chimathandiza anthu okwatirana kumvera mawu a Yesu akuti: “Chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mat. 19:6) Akhristu okwatirana akamakumana ndi “nsautso m’thupi mwawo,” ayenera kukumbukira kuti Yehova ndi woyenera kukhala pamalo oyamba mu ukwati wawo. (1 Akor. 7:28) Mawu ake amanena kuti ‘chikondi chimapirira zinthu zonse.’ Mwamuna ndi mkazi akakhala ndi chikondi choterechi, amakhala okonzeka kulimbitsa ukwati wawo ndiponso kukhala limodzi zivute zitani.​—Akol. 3:14.

19. Kodi anthu a Mulungu amatani pakachitika masoka achilengedwe?

19 Chikondi chimatithandiza kupirira zinthu zonse pakagwa masoka achilengedwe. Izi n’zimene zinachitika kum’mwera kwa dziko la Peru kutachitika chivomerezi, ndiponso mphepo yamkuntho itasakaza kum’mwera chakummawa kwa dziko la United States. Zimenezi zitachitika, nyumba ndiponso katundu wa abale athu ambiri zinawonongeka. Chifukwa cha chikondi, abale a m’mayiko osiyanasiyana anapereka zinthu zoti zithandize. Abale enanso anadzipereka kukamanga nyumba ndiponso kukonza Nyumba za Ufumu zimene zinawonongeka. Zimene anachitazi, zinasonyeza kuti abale amakondana ndiponso amasamalirana nthawi zonse.​—Yoh. 13:34, 35; 1 Pet. 2:17.

Chikondi Sichitha Konse

20, 21. (a) Kodi chikondi n’chopambana kwambiri chifukwa chiyani? (b) N’chifukwa chiyani inuyo mukufunitsitsa kutsatira njira yopambana ya chikondi?

20 Zimene zakhala zikuchitika pakati pa anthu a Yehova masiku ano, zikusonyezeratu kuti ndi nzeru ndithu kutsatira njira yopambana ya chikondi. Chikondi chimathandiza pa chilichonse. Taonani mmene Paulo anatsindikira mfundo ya choonadi imeneyi. Choyamba, iye ananena kuti mphatso za mzimu zidzatha mpingo wachikhristu ukadzakula. Ndipo anamaliza ndi mawu akuti: “Tsopano patsala zitatu izi: Chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi. Koma chachikulu pa zonsezi ndi chikondi.”​—1 Akor. 13:13

21 Zinthu zimene timakhulupirira zikadzakwaniritsidwa, chikhulupiriro chathu pa zinthuzo chidzakhala chosafunika. Chiyembekezo chimene tili nacho pa malonjezo amene timalakalaka kuwaona atakwaniritsidwa, chidzatha zinthu zonse zikadzakhala zatsopano. Nanga kodi chikondi chidzathanso? Ayi sichidzatha, chidzakhalapo mpaka kalekale. Popeza tidzakhala ndi moyo wosatha, tidzaona ndiponso kumvetsa bwino mbali zosiyanasiyana zokhudza chikondi cha Mulungu. Choncho, mwa kuchita chifuniro cha Mulungu, chomwe ndi kutsatira njira yopambana ya chikondi chimene sichitha konse, mudzakhala ndi moyo kosatha.​—1 Yoh. 2:17.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa kukonda zinthu zolakwika?

• Kodi chikondi chingatithandize kupirira chiyani?

• Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti chikondi sichitha konse?

[Mafunso]

[Mawu Otsindika patsamba 27]

Lemba la chaka cha 2010 ndi lakuti: ‘Chikondi chimapirira zinthu zonse. Chikondi sichitha konse.’​—1 Akor. 13:7, 8.

[Chithunzi patsamba 25]

Kukonda Mulungu kumatilimbikitsa kuchitira umboni

[Chithunzi patsamba 26]

Chikondi chomwe sichitha, n’chimene chinathandiza abale ndi alongo ku Malawi kupirira mayesero