Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi Mukukumbukira?

Kodi mwapindula powerenga magazini aposachedwapa a Nsanja ya Olonda? Tayesani kuyankha mafunso otsatirawa:

• Kodi Mulungu angakuchititseni kukhala wolemera m’njira yotani?

Kale Yehova anadalitsa anthu ena monga Abulahamu ndi Solomo powapatsa chuma chakuthupi. Koma chuma chimene Akhristu amafunikira kwambiri ndiponso chimene Mulungu angathandize munthu kuchipeza chimaphatikizapo chikhulupiriro, mtendere, kukhutira ndi zomwe uli nazo komanso chimwemwe.​—9/1, masamba 3-7.

• Kodi tikuphunzirapo chiyani pa zimene Yesu anachita populumutsa Petulo pamene anali kumira panyanja? (Mat. 14:28-31)

Tikazindikira kuti chikhulupiriro cha m’bale wathu chikufooka, tingam’gwire dzanja mophiphiritsira ndi kum’thandiza kuti chikhulupiriro chake chilimbe.​—9/15, tsamba 8.

• Kodi Yehova anadzimana chiyani kuti atipulumutse?

Yehova anapirira pamene anali kuona Mwana wake akuzunzidwa ndi kunyozedwa. Monga mmene Abulahamu anasonyezera mwaulosi pamene anali kufunitsitsa kupereka Mwana wake, Yehova anapirira poona Mwana wake akuphedwa ngati chigawenga.​—9/15, masamba 28-29.

• N’chifukwa chiyani tinganene kuti Baibulo la Vatican Codex ndi chuma?

Baibulo limeneli linalembedwa m’Chigiriki patapita zaka zosakwana 300 kuchokera pamene mabuku onse a m’Baibulo analembedwa. Ilo lili ndi pafupifupi Malemba onse achiheberi ndi achigiriki. Baibulo limeneli ndi limodzi mwa zolembedwa zimene akatswiri amagwiritsa ntchito pofuna kudziwa zimene zinali m’Malemba oyambirira a m’Baibulo.​—10/1, masamba 18-20.

• Kodi lemba la Miyambo 24:27 limatiphunzitsa chiyani pa nkhani ya ‘kumanga nyumba’?

Mwamuna amene akufuna kukwatira ayenera kukonzekera udindo wake. Izi zikuphatikizapo kukonzekera kupezera banja lake zinthu zakuthupi ndiponso kutsogolera banja lake pa zinthu zauzimu.​—10/15, tsamba 12.

• N’chifukwa chiyani n’kulakwa kunena kuti Mboni za Yehova ndi chipembedzo chachipolotesitanti?

Chipolotesitanti chinayambika m’zaka za m’ma 1500 ku Ulaya ndi anthu omwe ankafuna kukonza zina ndi zina m’tchalitchi cha Roma Katolika. Mawu akuti “Apolotesitanti” amanena za anthu amene amatsatira zolinga za anthu ofuna kukonza zinthu m’tchalitchi cha Katolika. Mboni za Yehova sizivomereza zoti papa ali ndi ulamuliro padziko lonse ndipo zimakhulupirira kuti Baibulo ndi buku lofunika koposa. Koma sizivomerezanso ziphunzitso ndi miyambo yambiri imene imapezeka m’zipembedzo zachipolotesitanti.​—11/1, tsamba 19.

• Kodi munthu amafunikira kuphunzira Chiheberi ndi Chigiriki kuti amvetse Baibulo?

Ayi. Kungodziwa zinenero zimenezi sikutanthauza kuti munthu angalimvetse mosavuta Baibulo. Munthu wodziwa zinenero zimenezi amadalirabe mabuku otanthauzira mawu ndiponso mabuku a malamulo a chilankhulo. Mulungu anasunga mawu a Mtumiki wake wamkulu koposa, m’zolemba zomasuliridwa m’chinenero china. Izi zimasonyeza kuti munthu angathe kugwiritsa ntchito Mabaibulo omasuliridwa m’zinenero za masiku ano n’kuphunzira choonadi.​—11/1, masamba 20-23.

• Kodi Yehova ndi Yesu anatipatsa chitsanzo chotani pa nkhani ya ulemu?

Ngakhale kuti Yehova ndi wokwezeka kwambiri, iye amasonyeza anthu kukoma mtima ndiponso ulemu. Polankhulana ndi Abulahamu komanso Mose, iye anagwiritsa ntchito mawu achiheberi amene amasonyeza kuti munthu akupempha mwaulemu osati kulamula. (Gen. 13:14; Eks. 4:6) Mulungu amamvetseranso anthu akamamulankhula. (Gen. 18:23-32) Yesu nayenso anali kumvetsera anthu akamamulankhula ndipo anali kukhala wokonzeka ndi wofunitsitsa nthawi zonse kuthandiza anthu amene anali naye pafupi ndipo nthawi zambiri polankhula nawo anali kuwatchula mayina.​—11/15, tsamba 25.

• N’chifukwa chiyani Akhristu oona sachita nawo chikondwerero cha Chaka Chatsopano?

Chikondwerero cha Chaka Chatsopano ndi chofunika kwambiri ku Asia. Pachikondwererochi anthu amachita zinthu zina kuti akhale ndi mwayi ndiponso amalemekeza mizimu. Akhristu amalemekeza makolo awo koma iwo sachita nawo mapwando olemekeza makolo akufa n’cholinga choti awateteze kapenanso kupempha kuti milungu imene mabanja ena amaipembedza iwathandize.​—12/1, masamba 20-23.