Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kupita Kwanu Patsogolo Kuzionekera

Kupita Kwanu Patsogolo Kuzionekera

Kupita Kwanu Patsogolo Kuzionekera

“Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.”​—1 TIM. 4:15.

1, 2. Kodi timadziwa chiyani za moyo wa Timoteyo ali mnyamata ndiponso mmene zinthu zinasinthira pamoyo wake ali ndi zaka pafupifupi 20?

TIMOTEYO ali mnyamata ankakhala kudera lina la Roma lotchedwa Galatiya, lomwe masiku ano lili m’dziko la Turkey. Patapita zaka zambiri Yesu atamwalira, mipingo yachikhristu yambiri inakhazikitsidwa m’dera limeneli. Panthawi ina, Timoteyo, amayi ake ndi agogo ake aakazi anakhala Akhristu ndipo ankatumikira mumpingo wina kumeneko. (2 Tim. 1:5; 3:14, 15) N’zosakayikitsa kuti Timoteyo ankasangalala monga Mkhristu wachinyamata m’dera la kwawolo. Koma mwadzidzidzi, zinthu zinayamba kusintha.

2 Kusinthaku kunayamba pamene mtumwi Paulo anafika kuderali paulendo wachiwiri. Pa nthawi imeneyi n’kutheka kuti Timoteyo anali ndi zaka pafupifupi 20 kapena kuposa pang’ono. Paulo atafika m’deralo, mwina ali ku Lusitara, anaona kuti abale a m’mipingo ya kumeneko “anam’chitira umboni wabwino” Timoteyo. (Mac. 16:2) Ali mnyamata, Timoteyo ankachita zinthu mwauchikulire. Ndipo motsogozedwa ndi mzimu woyera, Paulo ndi bungwe la akulu la kumeneko anaika manja pa Timoteyo n’kumusankha kuti agwire ntchito yapadera mumpingo.​—1 Tim. 4:14; 2 Tim. 1:6.

3. Kodi Timoteyo anapatsidwa utumiki wapadera wotani?

3 Timoteyo anapatsidwa mwayi wapadera woyenda limodzi ndi mtumwi Paulo. (Mac. 16:3) Timoteyo ayenera kuti anadabwa ndipo anasangalala kwambiri. Kwa zaka zambiri, Timoteyo ankayenda ndi Paulo ndipo nthawi zina ankayenda ndi abale ena. Iye ankagwira ntchito zosiyanasiyana zimene atumwi ndi akulu ankam’patsa. Paulo ndi Timoteyo anagwira ntchito yoyendayenda imene inathandiza kwambiri kuti abale alimbikitsidwe mwauzimu. (Werengani Machitidwe 16:4, 5.) Choncho, Akhristu ambiri ankam’dziwa bwino Timoteyo chifukwa cha kupita kwake patsogolo mwauzimu. Mtumwi Paulo atagwira ntchito ndi Timoteyo kwa zaka pafupifupi 10, analembera Afilipi kuti: “Ndilibe wina wa mtima ngati [Timoteyo] amene angasamaledi za inu moona mtima.  . . . Inu mukudziwa kudalirika kumene iye mwini anaonetsa, kuti monga mwana ndi bambo wake, watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.”​—Afil. 2:20-22.

4. (a) Kodi Timoteyo anapatsidwa udindo waukulu wotani? (b) Kodi ndi funso lotani limene tingafunse pa mawu a Paulo opezeka pa 1 Timoteyo 4:15?

4 Pa nthawi imene Paulo analembera Afilipi mawu amenewa, anapatsa Timoteyo udindo waukulu woika akulu ndi atumiki othandiza. (1 Tim. 3:1; 5:22) N’zoonekeratu kuti Timoteyo anakhala woyang’anira wokhulupirika ndiponso wodalirika. Ngakhale zili choncho, m’kalata imeneyi, Paulo analangiza Timoteyo kuti ‘kupita kwake patsogolo kuonekere kwa anthu onse.’ (1 Tim. 4:15) Komatu, Timoteyo anali ataonetsa kale kuti akupita patsogolo kwambiri. Ndiye kodi Paulo anatanthauza chiyani popereka malangizo amenewa ndipo tingapindule nawo bwanji?

Zimene Tingachite Kuti Kupita Kwathu Patsogolo Kuzionekera

5, 6. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikanadetsa mpingo wa ku Efeso, ndipo kodi Timoteyo akanateteza bwanji mpingowo?

5 Tiyeni tsopano tione mavesi a pambuyo ndi patsogolo pa 1 Timoteyo 4:15. (Werengani 1 Timoteyo 4:11-16.) Asanalembe mawu amenewa, Paulo anapita ku Makedoniya koma anauza Timoteyo kuti akhalebe ku Efeso. N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti anthu ena mumzindawo anayambitsa magawano mumpingo mwa kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga. Timoteyo anafunika kuteteza mpingowo kuti ukhalebe woyera mwauzimu. Kodi akanachita bwanji zimenezi? Njira imodzi inali kusonyeza chitsanzo chabwino kwa ena.

6 Paulo analembera Timoteyo kuti: “Ukhale chitsanzo kwa okhulupirika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’chikondi, m’chikhulupiriro, ndi m’chiyero.” Iye anatinso: “Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama. Kangalika nazo, kuti kupita kwako patsogolo kuonekere kwa anthu onse.” (1 Tim. 4:12, 15) Timoteyo akanaonetsa kupita patsogolo kumeneku mwa kukhala ndi makhalidwe abwino auzimu, osati ndi udindo winawake. Uku ndiko kupita patsogolo kumene Mkhristu aliyense afunika kuonetsa.

7. Kodi Akhristu onse mumpingo afunika kuchita chiyani?

7 Mofanana ndi nthawi ya Timoteyo, masiku anonso mumpingo muli maudindo osiyanasiyana. Ena ndi akulu ndipo ena ndi atumiki othandiza. Ena amachita upainiya pomwe ena ndi oyang’anira oyendayenda, atumiki a pa Beteli kapenanso amishonale. Akulu amachita mbali zophunzitsa zosiyanasiyana monga kukamba nkhani pamisonkhano ikuluikulu. Komabe, Akhristu onse, amuna, akazi ndi ana, angathe kuonetsa kupita kwawo patsogolo. (Mat. 5:16) Ndipotu, mofanana ndi Timoteyo, ngakhale Akhristu amene ali ndi maudindo apadera afunika kuonetsa makhalidwe abwino auzimu kwa onse.

Khalani Chitsanzo M’kalankhulidwe

8. Kodi zolankhula zathu zimakhudza bwanji kulambira kwathu?

8 Njira imodzi imene Timoteyo anafunikira kusonyeza chitsanzo chabwino ndi mwa zolankhula zake. Kodi tingaonetse bwanji kupita kwathu patsogolo m’njira imeneyi? Zolankhula zathu zimasonyeza kuti ndife munthu wotani. N’chifukwa chake Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukira mu mtima.” (Mat. 12:34) Yakobe, m’bale wa Yesu, nayenso anazindikira mmene zolankhula zathu zingakhudzire kulambira kwathu. Iye analemba kuti: “Ngati munthu akudziyesa wopembedza, koma salamulira lilime lake, ndipo akupitiriza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.”​—Yak. 1:26.

9. Kodi tingakhale bwanji chitsanzo mwa zolankhula zathu?

9 Zolankhula zathu zingasonyeze ena mumpingo mmene tapitira patsogolo mwauzimu. N’chifukwa chake, Akhristu achikulire mwauzimu amayesetsa kulimbikitsa ndi kutonthoza ena m’malo molankhula zinthu zopanda ulemu, zonyoza, zotsutsa kapena zokwiyitsa ena. (Miy. 12:18; Aef. 4:29; 1 Tim. 6:3-5, 20) Ngati ndife okonzeka kuuza ena mfundo za makhalidwe abwino zimene timayendera ndiponso kulankhula zinthu zosonyeza kuti malamulo apamwamba a Mulungu ndi othandiza, timaonetsa kuti ndife odzipereka kwa Mulungu. (Aroma 1:15, 16) Anthu a maganizo abwino amaona mmene timagwiritsira ntchito mphatso ya kulankhula ndipo angayambe kutitsanzira.​—Afil. 4:8, 9.

Tikhale Chitsanzo M’makhalidwe ndi M’chiyero

10. N’chifukwa chiyani timafunikira chikhulupiriro chopanda chinyengo kuti tipite patsogolo mwauzimu?

10 Kuwonjezera pa kulankhula zolimbikitsa pali zinthu zinanso zimene Mkhristu ayenera kuchita kuti akhale chitsanzo chabwino. Ngati zolankhula zake ndi zabwino koma zochita zake ndi zoipa, ndiye kuti ndi wachinyengo. Paulo ankadziwa bwino chinyengo cha Afarisi ndiponso mmene khalidwe lawo linkasokonezera anthu ena. Kangapo konse, iye anachenjeza Timoteyo kuti akhale woona mtima ndi wopanda chinyengo. (1 Tim. 1:5; 4:1, 2) Komabe sikuti Timoteyo anali munthu wachinyengo chifukwa m’kalata yachiwiri imene Paulo anamulembera anati: “Ndikukumbukira chikhulupiriro chopanda chinyengo chimene chili mwa iwe.” (2 Tim. 1:5) Komabe Timoteyo ankafunika kusonyeza ena kuti analidi Mkhristu wopanda chinyengo. Iye anayenera kukhala chitsanzo m’makhalidwe.

11. Kodi Paulo anamulangiza chiyani Timoteyo pa nkhani ya chuma?

11 M’makalata awiri amene Paulo analembera Timoteyo, iye anapereka malangizo pa mbali zingapo zokhudza khalidwe. Mwachitsanzo, Timoteyo anafunikira kupewa mtima wokonda chuma. Paulo analemba kuti: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa chikondi chimenechi, ena asocheretsedwa kuchoka pa chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pa thupi pawo.” (1 Tim. 6:10) Ngati munthu amakonda kwambiri chuma, n’chizindikiro chakuti sakonda zinthu zauzimu. Koma Akhristu amene amasangalala ndi moyo wosalira zambiri ‘pokhala ndi chakudya ndiponso zovala,’ amasonyeza kuti akupita patsogolo mwauzimu.​—1 Tim. 6:6-8; Afil. 4:11-13.

12. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikupita patsogolo pa moyo wathu?

12 Paulo anauza Timoteyo kuti akazi achikhristu anafunika ‘kudzikongoletsa mwa kuvala moyenera, mwaulemu ndi mwanzeru.’ (1 Tim. 2:9) Akazi amene amavala, kudzikongoletsa ndiponso kuchita zinthu zina zonse moyenera ndi mwaulemu, amasonyeza chitsanzo chabwino kwambiri. (1 Tim. 3:11) Mfundo imeneyi imagwiranso ntchito kwa amuna achikhristu. Paulo analangiza oyang’anira kuti akhale ‘odziletsa m’zizolowezi zawo, oganiza bwino, adongosolo.’ (1 Tim. 3:2) Tikamasonyeza makhalidwe amenewa pa moyo wathu wa tsiku ndi tsiku, kupita kwathu patsogolo kumaonekera kwa onse.

13. Mofanana ndi Timoteyo, kodi tingatani kuti tikhale chitsanzo chabwino pa nkhani ya chiyero?

13 Timoteyo anafunikanso kukhala chitsanzo chabwino pankhani ya chiyero. Pogwiritsa ntchito mawu amenewa, Paulo kwenikweni ankatanthauza kukhala woyera pa nkhani zokhudza kugonana. Timoteyo ankafunika kusonyeza khalidwe labwino makamaka pochita zinthu ndi akazi. Iye ankafunika kuona ‘akazi achikulire monga amayi ake, akazi achitsikana monga alongo ake, ndi chiyero chonse.’ (1 Tim. 4:12; 5:2) Makhalidwe oipa okhudza nkhani za kugonana amene angaoneke ngati obisika, Mulungu amawadziwa, ndipo m’kupita kwanthawi amadzadziwika ndithu kwa anthu ena. Komanso anthu amaona ntchito zabwino zimene Mkhristu amachita. (1 Tim. 5:24, 25) Anthu onse mumpingo ali ndi mwayi woonetsa kupita kwawo patsogolo m’makhalidwe ndi m’chiyero.

Chikondi ndi Chikhulupiriro N’zofunika Kwambiri

14. Kodi Malemba amatsindika motani kufunika kosonyezana chikondi?

14 Chikondi n’chofunika kwambiri kwa Akhristu oona. Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Mwa ichi onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga, ngati mukondana wina ndi mnzake.” (Yoh. 13:35) Kodi timasonyeza bwanji chikondi chimenechi? Mawu a Mulungu amatilangiza kulolerana “wina ndi mnzake m’chikondi,” kukhala “okomerana mtima wina ndi mnzake, a chifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse.” Ndipo amatilangizanso kukhala ochereza. (Aef. 4:2, 32; Aheb. 13:1, 2) Mtumwi Paulo analembanso kuti: “Posonyezana chikondi chaubale khalani ndi chikondi chenicheni kwa wina ndi mnzake.”​—Aroma 12:10.

15. N’chifukwa chiyani Akhristu onse, makamaka oyang’anira, afunika kusonyeza chikondi?

15 Timoteyo akanakhala waukali ndiponso wosakoma mtima pochita zinthu ndi Akhristu anzake, zabwino zimene ankachita monga mphunzitsi komanso woyang’anira zikanakhala zopanda phindu. (Werengani 1 Akorinto 13:1-3.) Komabe, Timoteyo ankakonda kwambiri abale ake, ankawachereza ndiponso ankawachitira zinthu zabwino. Zimenezi zinasonyeza kupita kwake patsogolo mwauzimu. Motero, mpake kuti mtumwi Paulo m’kalata yake yopita kwa Timoteyo, anatchula chikondi monga limodzi mwa makhalidwe amene Timoteyo anafunika kukhala nalo kuti akhale chitsanzo chabwino.

16. N’chifukwa chiyani Timoteyo anafunika kusonyeza chikhulupiriro cholimba?

16 Pamene Timoteyo anali ku Efeso, chikhulupiriro chake chinayesedwa. Anthu ena ankalimbikitsa ziphunzitso zina zimene sizinali zogwirizana ndi choonadi chachikhristu. Ena ankafalitsa “nkhani zonama” komanso kufufuza mfundo zimene sizikanathandiza mpingo mwauzimu. (Werengani 1 Timoteyo 1:3, 4.) Paulo ananena kuti anthu amenewa anali ‘otukumuka chifukwa cha kunyada, osamvetsa kanthu, koma odwala m’mutu pokondetsa mafunso ndi kutsutsana pa mawu.’ (1 Tim. 6:3, 4) Kodi zikanakhala zoyenera kuti Timoteyo azichita chidwi ndi ziphunzitso zonyenga zimene ena anayambitsa mumpingowo? Ayi, popeza Paulo anam’limbikitsa ‘kumenya nkhondo yabwino yosunga chikhulupiriro’ ndiponso kupewa “nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zoyera.” Anamulimbikitsanso kupewa “mitsutso pa zimene ena monama amati ndiko ‘kudziwa zinthu.’” (1 Tim. 6:12, 20, 21) N’zosakayikitsa kuti Timoteyo anatsatira malangizo abwino amenewa a Paulo.​—1 Akor. 10:12.

17. Kodi chikhulupiriro chathu chingayesedwe bwanji masiku ano?

17 N’zochititsa chidwi kuti Timoteyo anauzidwanso kuti “m’nthawi zam’tsogolo, ena adzagwa pa chikhulupiriro, posamalira mawu ouziridwa osocheretsa, ndi ziphunzitso za ziwanda.” (1 Tim. 4:1) Mofanana ndi Timoteyo, anthu onse mumpingo, kuphatikizapo amene ali ndi udindo, ayenera kusonyeza chikhulupiriro cholimba. Mwa kukana ndi kupeweratu mpatuko, timaonetsa kupita kwathu patsogolo ndipo timakhala chitsanzo chabwino pa nkhani yachikhulupiriro.

Yesetsani Kuti Kupita Kwanu Patsogolo Kuzionekera

18, 19. (a) Kodi mungatani kuti kupita kwanu patsogolo kuonekere kwa onse? (b) Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

18 Maonekedwe, luso lachibadwa, kapena kutchuka si umboni woti Mkhristu woona akupita patsogolo mwauzimu. Ndipo kupita patsogolo mwauzimu sikumangodalira zaka zimene munthu watumikira mumpingo. Koma munthu amasonyeza kupita patsogolo mwauzimu mwa kumvera Yehova pa zoganiza zake, zolankhula zake ndiponso khalidwe lake. (Aroma 16:19) Tifunikira kutsatira lamulo lakuti tizikondana ndiponso tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. Ndithudi, tiziganizira mawu amene Paulo anauza Timoteyo ndiponso kuwatsatira kwambiri kuti kupita kwathu patsogolo kuzionekera kwa onse.

19 Khalidwe lina limene limaonekera tikamapita patsogolo mwauzimu ndi chimwemwe, chomwe ndi chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. (Agal. 5:22, 23) Nkhani yotsatira ikufotokoza mmene tingakhalirebe ndi chimwemwe tikamakumana ndi mavuto.

Kodi Mungayankhe Bwanji?

• Kodi zolankhula zathu zimasonyeza chiyani kwa ena?

• Kodi kupita kwathu patsogolo kumaonekera bwanji pa nkhani ya makhalidwe ndi chiyero?

• N’chifukwa chiyani Akhristu ayenera kukhala chitsanzo chabwino pa nkhani yosonyeza chikondi ndi chikhulupiriro?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 11]

Ali mnyamata, Timoteyo ankachita zinthu mwauchikulire

[Zithunzi patsamba 13]

Kodi kupita kwanu patsogolo kumaonekera kwa onse?