Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Muzilemekeza Mulungu Tsiku ndi Tsiku

Muzilemekeza Mulungu Tsiku ndi Tsiku

Muzilemekeza Mulungu Tsiku ndi Tsiku

WAMASALMO Davide anapemphera kwa Yehova kuti: “Mundimvetse chifundo chanu mamawa. . . . Mundidziwitse njira ndiyendemo.” (Sal. 143:8) Mukadzuka m’mawa, muyenera kuti mumathokoza Yehova chifukwa chakuti muli ndi moyo. Ndiyeno kodi mofanana ndi Davide mumamupemphanso kuti Yehova akutsogolereni posankha zinthu ndiponso kuti muchite zinthu zoyenera? N’zosakayikitsa kuti mumatero.

Popeza ndife atumiki a Yehova odzipereka, ‘kaya tikudya kapena kumwa kapena kuchita china chilichonse,’ timayesetsa ‘kuchita zonse ku ulemerero wa Mulungu.’ (1 Akor. 10:31) Timadziwa kuti zochita zathu za tsiku lililonse, zingalemekeze kapena kunyozetsa Yehova. Timakumbukiranso kuti Mawu a Mulungu amanena kuti “usana ndi usiku,” Satana amaneneza abale a Khristu ndiponso atumiki onse a Mulungu padziko lapansi. (Chiv. 12:10) Choncho timafunitsitsa kusonyeza kuti Satana ndi wabodza ndiponso kukondweretsa mtima wa Yehova yemwe ndi Atate wathu wakumwamba mwa kum’chitira utumiki wopatulika “usana ndi usiku.”​—Chiv. 7:15; Miy. 27:11.

Tiyeni tikambirane mwachidule njira ziwiri zofunika kwambiri zimene tingalemekezere Mulungu tsiku ndi tsiku. Njira yoyamba ikukhudza zinthu zofunika kuziika pamalo oyamba, ndipo yachiwiri ikukhudza kuganizira ena.

Zochita Zathu Zizisonyeza Kuti Tinadzipereka

Mwa kudzipereka kwa Yehova, tinasonyeza kuti tikufunitsitsa kumutumikira. Tinamulonjezanso Yehova kuti tidzayenda m’njira zake “tsiku ndi tsiku” mpaka muyaya. (Sal. 61:5, 8) Ndiyeno kodi tingatani kuti tikwaniritse lonjezo lathulo? Kodi tsiku lililonse, tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yehova ndi mtima wathu wonse?

Mawu a Mulungu amatiuza momveka bwino zimene Yehova amafuna kuti tizichita. (Deut. 10:12, 13) Zina mwa zinthu zimenezi zalembedwa m’kabokosi kakuti,  “Zimene Mulungu Amafuna Kuti Tizichita,” patsamba 22. Mulungu amafuna kuti tizichita zinthu zonse zimene zili m’kabokosika, choncho zonsezi ndi zofunika. Ndiyeno ngati pali zinthu ziwiri kapena zingapo zofunika kuti muzichite pa nthawi imodzi, kodi mungadziwe bwanji chofunika kuyamba kuchita?

Zinthu monga kuphunzira Baibulo, pemphero, misonkhano yachikhristu ndiponso ntchito yolalikira, ndi zimene ziyenera kukhala pa malo oyamba chifukwa zili mbali ya utumiki wathu wopatulika. (Mat. 6:33; Yoh. 4:34; 1 Pet. 2:9) Komabe, sikuti tingamangokhalira kuchita zinthu zauzimu tsiku lonse. Tiyenera kupezanso nthawi yogwira ntchito, kupita kusukulu ndiponso kugwira ntchito zina za pakhomo. Komabe timaonetsetsa kuti ntchito ndiponso zinthu zina, zisasokoneze zinthu zokhudza utumiki wathu wopatulika, monga kupezeka pamisonkhano yachikhristu. Mwachitsanzo, tikamakonzekera kupita ku tchuthi, timaonetsetsa kuti tisaphonye zinthu monga mlungu wapadera, tsiku la msonkhano wapadera, msonkhano wadera ndiponso wachigawo. Nthawi zina, tikhoza kuchita zinthu zingapo nthawi imodzi. Mwachitsanzo, ndi bwino kuti banja lonse lizikambirana tsiku loyeretsa Nyumba ya Ufumu kuti lizigwirira limodzi ntchitoyo. Tikhozanso kulalikira kwa anzathu kusukulu kapena kuntchito panthawi yopuma. Tikamasankha zochita pankhani ya ntchito, maphunziro kapena anzathu ocheza nawo, timaonetsetsa kuti zosankha zathuzo zikhale zogwirizana ndi kulambira Atate wathu wakumwamba Yehova, komwe ndi chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu.​—Mlal. 12:13.

Muziganizira Ena

Yehova amafuna kuti tiziganizira anthu ena ndiponso tiziwachitira zabwino. Koma Satana amafuna kuti tikhale anthu odzikonda. M’dziko lakeli mwadzaza anthu “odzikonda, . . . okonda zosangalatsa” ndiponso ‘ofesera thupi.’ (2 Tim. 3:1-5; Agal. 6:8) Ambiri saganizira n’komwe mmene zochita zawo zingakhudzire anthu ena. “Ntchito za thupi” zili mbwee m’dzikoli.​—Agal. 5:19-21.

Koma anthu amene amatsogoleredwa ndi mzimu wa Yehova, pochita zinthu ndi ena amasonyeza chikondi, ubwino ndiponso kukoma mtima. (Agal. 5:22) Mawu a Mulungu amatiuza kuti tiziika zofuna za ena patsogolo pa zathu. Choncho ngakhale kuti sitilowerera m’nkhani za ena, timachita zinthu moganizira ena. (1 Akor. 10:24, 33; Afil. 2:3, 4; 1 Pet. 4:15) Akhristu anzathu ndi amene timawaganizira kwambiri. Komabe, timayesetsanso kuthandiza anthu omwe si Mboni. (Agal. 6:10) Kodi inuyo mungafufuze mpata leroli kuti muchitire munthu wina zinthu zosonyeza kukoma mtima?​—Onani bokosi lakuti  “Anthu Ofunika Kuwaganizira,” patsamba 23.

Sikuti timangosonyeza kuganizira ena pa nthawi inayake kapena pa zochitika zinazake basi. (Agal. 6:2; Aef. 5:2; 1 Ates. 4:9, 10) Tsiku lililonse timayesetsa kudziwa zimene zikuchitikira anthu ena, n’kuona zimene tingachite kuti tiwathandize ngakhale ngati kuchita zimenezo kungasokoneze zimene timafuna kuchita pa tsikulo. Tisamaumire nthawi, chuma, luso komanso nzeru zathu pothandiza ena. Timakhulupirira zimene Yehova watilonjeza kuti tikakhala owolowa manja kwa ena, iyenso adzakhala wowolowa manja kwa ifeyo.​—Miy. 11:25; Luka 6:38.

Kuchita Utumiki Wopatulika “Usana ndi Usiku”

Kodi n’zothekadi kuchita utumiki wopatulika kwa Yehova “usana ndi usiku”? Inde n’zotheka ngati nthawi zonse timachita khama m’mbali zonse za kulambira kwathu. (Mac. 20:31) Tingachite utumiki wopatulika nthawi zonse mwa kuwerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu tsiku lililonse, kupemphera kosaleka, kupezeka pamisonkhano yonse ndiponso kuyesetsa kugwiritsa ntchito mpata uliwonse kuti tilalikire.​—Sal. 1:2; Luka 2:37; Mac. 4:20; 1 Ates. 3:10; 5:17.

Kodi ifeyo timachita utumiki wopatulika kwa Yehova m’njira imeneyi? Ngati ndi choncho, zochita zathu tsiku lililonse zidzasonyeza kuti timafunitsitsa kum’kondweretsa ndiponso kusonyeza kuti Satana ndi wabodza. Timayesetsa kulemekeza Yehova pa zochita zathu zonse kaya tikumane ndi zotani. Timalola kuti mfundo zake zizititsogolera pa zolankhula, zochita ndiponso zosankha zathu. Timayamikira kuti iye amatisamalira mwachikondi ndiponso kutithandiza. Timasonyeza kuyamikirako mwa kum’khulupirira ndi mtima wathu wonse komanso kum’tumikira ndi mphamvu zathu zonse. Timakhala okonzeka kulandira uphungu umene amatipatsa ngati talakwitsa zinazake chifukwa cha kupanda ungwiro kwathu.​—Sal. 32:5; 119:97; Miy. 3:25, 26; Akol. 3:17; Aheb. 6:11, 12.

Tiyeni tipitirizebe kulemekeza Mulungu tsiku lililonse. Tikatero, tidzapeza mpumulo wa miyoyo yathu ndipo Atate wathu wakumwamba adzatisamalira kwamuyaya.​—Mat. 11:29; Chiv. 7:16, 17.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 22]

 Zimene Mulungu Amafuna Kuti Tizichita

• Kupemphera pafupipafupi.​—Aroma 12:12.

• Kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo ndiponso kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo.​—Sal. 1:2; 1 Tim. 4:15.

• Kulambira Yehova limodzi ndi mpingo.​—Sal. 35:18; Aheb. 10:24, 25.

• Kusamalira banja lathu mwauzimu ndiponso mwakuthupi.​—1 Tim. 5:8.

• Kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira.​—Mat. 24:14; 28:19, 20.

• Kudzisamalira mwakuthupi ndiponso mwauzimu. Zimenezi zimaphatikizapo kupeza nthawi yochita masewera enaake olimbitsa thupi kuti tikhale ndi thanzi labwino.​—Maliko 6:31; 2 Akor. 7:1; 1 Tim. 4:8, 16.

• Kusamalira maudindo akumpingo.​—Mac. 20:28; 1 Tim. 3:1.

• Kuonetsetsa kuti nyumba yathu ndiponso Nyumba ya Ufumu ikuoneka bwino.​—1 Akor. 10:32.

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 23]

 Anthu Ofunika Kuwaganizira

• M’bale kapena mlongo wokalamba.​—Lev. 19:32.

• Munthu amene akudwala kapena amene akuvutika maganizo.​—Miy. 14:21.

• Mkhristu amene akufunika thandizo linalake limene mungathe kupereka.​—Aroma 12:13.

• M’bale wanu.​—1 Tim. 5:4, 8.

• Mkhristu amene mwamuna kapena mkazi wake wamwalira.​—1 Tim. 5:9.

• Mkulu wakhama kwambiri mumpingo wanu.​—1 Ates. 5:12, 13; 1 Tim. 5:17.