Buku Lothandiza Achinyamata Kukumbukira Mlengi Wawo
Buku Lothandiza Achinyamata Kukumbukira Mlengi Wawo
ZAKA 3,000 zapitazo Mfumu yanzeru Solomo inalemba kuti: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” (Mlal. 12:1) Masiku ano, achinyamata ali ndi buku limene lingawathandize kuchita zimenezi. Buku lake ndi lakuti, Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri. Bukuli linatuluka pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wakuti, “Mzimu wa Mulungu Umatitsogolera” umene unachitika padziko lonse kuyambira mu May 2008 mpaka mu January 2009.
Mkati mwa chikuto choyambirira muli kalata imene Bungwe Lolamulira linalembera achinyamata. M’kalatayi muli mawu akuti: “Tikupempherera kuti mfundo zimene zili m’buku lino zikuthandizeni polimbana ndi mayesero amene achinyamata ambiri amakumana nawo ndiponso kuti muzichita zinthu zogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna.”
Makolo amafuna kulera ana awo “m’malango a Yehova ndi kuwaphunzitsa kalingaliridwe kake.” (Aef. 6:4) Anawo akamakula amayamba kudzikayikira ndipo amafuna kupatsidwa malangizo. Ngati muli ndi ana omwe ndi achinyamata, kodi mungawathandize bwanji kuti apindule kwambiri ndi bukuli? Mfundo zotsatirazi zingakuthandizeni.
▪ Pezani buku lanu ndipo lidziweni bwino. Mukamawerenga bukuli yesetsani kumvetsa mzimu wa nkhani zake. Bukuli silimangowauza achinyamata kuti zabwino ndi izi zoipa ndi izi, koma limaphunzitsanso “luntha lawo la kuzindikira.” (Aheb. 5:14) Limawapatsanso malangizo owathandiza kuti asasiye kuchita zabwino. Mwachitsanzo, Mutu 15 wakuti, (“Kodi Ndingapewe Bwanji Kutengera Zochita za Anzanga?”), sumangowauza kuti azikana zakutizakuti. Umawauza mfundo za m’Baibulo zowathandiza kuthana ndi mavuto komanso kupeza njira zabwino ‘zoyankhira wina aliyense.’—Akol. 4:6.
▪ Gwiritsani ntchito bwino mbali zofuna kukambirana m’bukuli. Ngakhale kuti bukuli ndi la achinyamata, inunso makolo muyenera kukhala ndi lanu ndipo muzilembamo mfundo * Mwachitsanzo, mukafika patsamba 16 pamene pali mafunso okhudza chibwenzi muzikumbukira zimene munkaganiza pa nthawi imene munali wachinyamata ngati mwana wanuyo. Mwina mukhoza kulembapo mayankho amene mukuona kuti mukanapereka pa nthawi imene munali msinkhu wa mwana wanuyo. Ndiyeno mungadzifunse kuti: ‘Kodi maganizo anga pa nkhani imeneyi akhala akusintha bwanji kudzafika panopa? Kodi ndi zinthu zotani zimene ndaphunzira kuchokera pa nthawi imeneyo kufika pano ndipo ndingamuphunzitse bwanji mwana wanga zimenezi?
zanu.▪ Musamaone zinthu zachinsinsi za mwana wanu. Cholinga cha mbali zokambirana ndi mwana wanu ndi kumuthandiza kuti azifotokoza zakukhosi kwake mwa kulemba m’bukulo kapena kungoziganizira. Cholinga chanu chizikhala kuona zimene zili mumtima mwake osati m’buku lake. Patsamba 3, pansi pa chigawo chakuti, “Makolo Dziwani Izi,” bukuli limati: “Kuti ana anu alembe zakukhosi kwawo m’bukuli, musamaone zimene alemba. Anawo akafuna angathe kukusonyezani okha zimene alembazo.”
Ndi Lothandiza Pophunzira Baibulo ndi Banja
Buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, ndi lothandiza kwambiri pa Kulambira kwa Pabanja. Popeza bukuli lilibe mafunso a ndime iliyonse, kodi mungaligwiritse ntchito bwanji? Chofunika ndi kungokonza nokha njira yophunzirira bukuli imene mukuona kuti ingakhale yabwino pa banja lanu.
Mwachitsanzo, mabanja ena amafuna kuyeserera akafika pa kamutu kakuti, “Mmene Mungakonzekerere,” patsamba 132 ndi 133. Funso loyamba pa kamutuka lingathandize kuti mwana wanu atchule nkhani imene akuona kuti ndi yovuta kwambiri. Funso lachiwiri ndi lothandiza kudziwa malo amene zimenezi zingachitikire. Pambuyo poganizira mavuto amene angakhalepo iye akalolera kapena kukana zimene anzakewo akumukakamiza kuchita, mwana wanuyo ayenera kukonzekera zimene angachite kuti ayankhe m’njira yowavomereza, kukana kapena kuwapanikiza. Thandizani mwana wanu kupeza njira zoyankhira zimene akuona kuti ndi zosavuta ndiponso zoti angathe kuzigwiritsa ntchito momasuka komanso molimba mtima.—Sal. 119:46.
Ndi Lothandiza Kuti Muzilankhulana Momasuka
Bukuli, ndi lothandiza kwambiri kuti achinyamata azilankhulana momasuka ndi makolo awo. Mwachitsanzo, bokosi lakuti, “Kodi Ndingafunse Bwanji Bambo Kapena Mayi Anga Nkhani Zokhudza Kugonana?” (patsamba 63 ndi 64), ndiponso lakuti, “Kambiranani ndi Makolo Anu” (patsamba 189) lili ndi mfundo zothandiza kuti muyambe kukambirana nkhani zimene ambiri amachita nazo manyazi kuzilankhula. Mtsikana wina wa zaka 13 analemba kuti: “Buku limeneli linandithandiza kuti ndilimbe mtima n’kukambirana ndi makolo anga zinthu zimene ndinkaganiza ngakhalenso zimene ndinazichitapo.”
Pali njira zinanso zimene Bukuli limathandiza pa nkhani ya kukambirana momasuka. Kumapeto kwa mutu uliwonse kuli kabokosi kakuti, “Mukuganiza Bwanji?” Cholinga cha kabokosika si kungobwereza zimene mwaphunzira koma kali ngati autilaini yokuthandizani pokambirana ndi banja lanu. Chapafupi ndi kumapeto kwa mutu uliwonse kulinso kabokosi kakuti, “Zoti Ndichite.” Kabokosi kameneka kamathandiza achinyamata kuti alembe mmene angagwiritsire ntchito mfundo zimene aphunzira m’mutuwo. Chigawo chomaliza cha kabokosi kameneka chili ndi chiganizo chakuti, “Zimene ndikufuna kufunsa makolo anga pankhaniyi ndi izi: . . . ” Chiganizo chimenechi chingathandize achinyamata kuti azidalira kwambiri makolo awo kuti awapatse malangizo.
Afikeni Pamtima
Cholinga chanu chizikhala kum’fika pamtima mwana wanu. Bukuli lingakuthandizeni kuchita zimenezi. Taonani mmene bukuli linathandizira bambo wina kukambirana zakukhosi ndi mwana wake wamkazi.
Iye anati: “Ine ndi Rebekah tili ndi malo osiyanasiyana amene timakonda kupitako kukayenda. Ndipo nthawi zina timapita wapansi, panjinga kapena pagalimoto. Ndimaona kuti kuchita zimenezi kumatipatsa mpata woti iye azilankhula zakukhosi kwake.
“Mbali imene tinayamba kukambirana m’bukuli ndi kalata yochokera ku Bungwe Lolamulira ndiponso mbali yakuti, ‘Makolo Dziwani Izi.’ Ndinkafuna kuti mwana wanga adziwe kuti ayenera kukhala womasuka kulemba m’buku lakelo ngati mmene afotokozera patsamba 3. Sindinkaona zimene iye walemba.
“Ndinamuuza Rebekah kuti asankhe mitu imene akufuna kuti tidzakambirane komanso imene akufuna kuti idzakhale yoyambirira kukambirana. Mutu wina umene anasankha kuti tikambirane moyambirira ndi wakuti, ‘Kodi Ndiyenera Kuchita Masewera a Pakompyuta?’ Sindinkaganiza n’komwe kuti iye angasankhe mutu umenewu. Komabe anasankha mutuwu pa zifukwa zomveka. Anzake ambiri ankachita masewera oipa kwambiri. Sindinkadziwa zinthu zachiwawa komanso mawu oipa amene anali m’masewerawa. Koma ndinadziwa zonsezi pamene tinkakambirana mbali yakuti, “Zoti ndichite,” patsamba 251. Bokosi limeneli linathandiza Rebekah kudziwa zimene angayankhe ngati anzakewo atamukakamiza kuchita masewerawo.
“Panopa, Rebekah sachita manyazi kundiuza zimene walemba m’buku lake. Phunziro lathu likakhala lokambirana. Timasinthanasinthana powerenga ndipo iye amafuna kufotokoza zonse zimene tawerenga ndiponso zithunzi ndi mabokosi. Izi zimandipatsa mpata wokambirana naye mmene ndinkamvera ndili msinkhu wake ndipo iye amandiuza mmene zinthu zilili masiku ano. Iye sandibisira chilichonse.”
Ngati ndinu kholo, n’kutheka kuti munasangalala kwambiri pamene bukuli linatulutsidwa. Tsopano ino ndi nthawi yoti muligwiritse ntchito bwino. Bungwe Lolamulira likukhulupirira kuti buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku lachiwiri, likuthandizani kwambiri m’banja lanu. Tikukhulupirira kuti bukuli likuthandizani nonsenu, makamaka achinyamatanu kuti ‘mupitirize kuyenda mwa mzimu woyera.’—Agal. 5:16.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Mbali zina zofunika kukambirana m’bukuli, zili ndi mfundo zimene zingathandize anthu a misinkhu yonse. Mwachitsanzo, bokosi lakuti, “Yesetsani Kuti Musapse Mtima Kwambiri,” patsamba 221 lingathandize inuyo limodzi ndi ana anu. N’chimodzimodzinso ndi timabokosi takuti, “Mmene Mungakonzekerere,” (patsamba 132 ndi 133) “Bajeti ya Mwezi Uliwonse,” (patsamba 163) ndiponso kakuti, “Zolinga Zanga” (patsamba 314).
[Chithunzi patsamba 30]
Zimene Achinyamata Ena Akunena
“Bukuli ndi lofunika kuliwerenga n’kumasinkhasinkha cholembera chili m’manja. Alikonza m’njira yothandiza kuti tizilembamo mfundo zathu zachinsinsi n’cholinga choti tisinthe moyo wathu n’kukhala anthu abwino kwambiri.”—Nicola.
“Anthu ambiri amandikakamiza kuti ndikhale ndi chibwenzi. Ena amene amachita zimenezi amakhala ndi zolinga zabwino ndithu. Chigawo choyamba cha bukuli chandithandiza kuona kuti kaya anthu anena zotani, ine ndikuona kuti sindine wokonzeka kukhala ndi chibwenzi.”—Katrina.
“Bokosi lakuti, ‘Kodi Mukufuna Kubatizidwa?’ landithandiza kuona kuti ubatizo wanga ndi nkhani yaikulu kwambiri. Landilimbikitsa kuonanso zimene ndimachita pa nkhani ya kuphunzira Baibulo pandekha ndiponso pemphero.”—Ashley.
“Ngakhale kuti makolo anga ankandiphunzitsa kuyambira ndili mwana, bukuli landithandiza kudziwa pandekha zoyenera kuchita pamoyo wanga. Landithandizanso kulankhula momasuka ndi makolo anga.”—Zamira.
[Chithunzi patsamba 31]
Makolo muyenera kulidziwa bwino bukuli
[Chithunzi patsamba 32]
Cholinga chanu chizikhala kuwafika pamtima ana anu