Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Gwiritsani Ntchito Mwaluso “Lupanga la Mzimu”

Gwiritsani Ntchito Mwaluso “Lupanga la Mzimu”

Gwiritsani Ntchito Mwaluso “Lupanga la Mzimu”

‘Landirani . . . lupanga la mzimu, lomwe ndi mawu a Mulungu.’​—AEF. 6:17.

1, 2. Popeza kuti pakufunika olengeza Ufumu ambiri, kodi tiyenera kutani?

YESU ataona mmene khamu la anthu linalili losowa mwauzimu, anauza ophunzira ake kuti: “Zokolola n’zochuluka, koma antchito ndi ochepa. Choncho, pemphani Mwini zokolola kuti atumize antchito kukakolola.” Koma Yesu sanalekere pompo. Atanena mawu amenewa, “anaitana ophunzira ake khumi ndi awiri” n’kuwatumiza kokalalikira kapena kuti kukagwira ntchito ‘yokolola.’ (Mat. 9:35-38; 10:1, 5) Panthawi inanso, Yesu “anasankha ena 70 ndi kuwatumiza awiriawiri” kuti akagwire ntchito yomweyi.​—Luka 10:1, 2.

2 Masiku anonso, pakufunika olengeza Ufumu ambiri. Padziko lonse, anthu amene anapezeka pa Chikumbutso m’chaka cha utumiki cha 2009 analipo 18,168,323. Pa anthu amenewa, oposa 10 miliyoni sanali Mboni za Yehova. Apatu zikuonekeratu kuti m’munda mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola. (Yoh. 4:34, 35) Choncho, tiyenera kupemphera kuti antchito ambiri apezeke. Koma kodi tingatani kuti tichite zinthu mogwirizana ndi pempho lathuli? Tifunika kukhala atumiki aluso tikamalalikira mwachangu Ufumu ndiponso kupanga ophunzira.​—Mat. 28:19, 20; Maliko 13:10.

3. Kodi mzimu wa Mulungu umatithandiza bwanji kukhala atumiki aluso?

3 Nkhani yoyamba ija inafotokoza mmene mzimu wa Mulungu umatithandizira “kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.” (Mac. 4:31) Mzimu umenewu ungatithandizenso kukhala atumiki aluso. Njira ina imene ingatithandize kuti tikhale aluso mu utumiki, ndiyo kugwiritsira ntchito bwino buku limene Yehova Mulungu watipatsa. Bukulo ndi Baibulo lomwe ndi Mawu ake ndipo linalembedwa mwa kugwiritsa ntchito mzimu woyera. (2 Tim. 3:16) Uthenga wake unauziridwa ndi Mulungu. Choncho, tikamagwiritsa ntchito Baibulo mwaluso pophunzitsa anthu, mzimu woyera umakhala ukutitsogolera. Tisanaone mmene tingachitire zimenezi, tiyeni tikambirane kaye za mphamvu imene Mawu a Mulungu ali nayo.

‘Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu’

4. Kodi uthenga wa Mulungu wa m’Baibulo ungam’sinthe bwanji munthu?

4 Ndithudi, mawu a Mulungu kapena kuti uthenga wake, ndi amphamvu kwambiri. (Aheb. 4:12) Mophiphiritsira, uthenga wochokera m’Baibulo ndi wakuthwa kuposa lupanga lopangidwa ndi anthu chifukwa uthengawu umapyoza mpaka kulekanitsa mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Choonadi cha m’Malemba chimalowerera m’maganizo mwa munthu mpaka kufika m’mtima mwake n’kupangitsa kuti umunthu wake wonse uonekere. Choonadi chimenechi chili ndi mphamvu ndipo chingathandize munthu kusintha. (Werengani Akolose 3:10.) Ndithudi, mawu a Mulungu angasinthe munthu.

5. Kodi Baibulo lingatitsogolere m’njira ziti, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?

5 Komanso m’Baibulo muli nzeru zimene sizingapezeke kwina kulikonse. Lili ndi malangizo othandiza anthu kuti zinthu ziziwayendera bwino m’dziko lamavutoli. Mawu a Mulungu angatiunikire njira imene tiyenera kuyenda panopo komanso m’tsogolo. (Sal. 119:105) Limathandiza kwambiri pamavuto, pa nkhani ya kusankha mabwenzi, zosangalatsa, ntchito, zovala ndiponso zinthu zina. (Sal. 37:25; Miy. 13:20; Yoh. 15:14; 1 Tim. 2:9) Kugwiritsa ntchito mfundo zopezeka m’Mawu a Mulungu kumatithandiza kukhala bwino ndi anthu ena. (Mat. 7:12; Afil. 2:3, 4) Tikamalola mawu a Mulungu kutiunikira pamoyo wathu, timadziwiratu zimene zingadzachitike chifukwa cha zimene tingasankhe. (1 Tim. 6:9) Malemba amaloseranso zimene Mulungu akufuna kudzachita m’tsogolo ndipo zimenezi zimatithandiza kuti tizikhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. (Mat. 6:33; 1 Yoh. 2:17, 18) Munthu amakhala ndi moyo wabwino kwambiri akamalola mfundo za Mulungu kum’tsogolera.

6. Pa nkhondo yathu yauzimu, kodi Baibulo ndi chida cha mphamvu motani?

6 Taganiziraninso mmene Baibulo lilili chida cha mphamvu kwambiri pa nkhondo yathu yauzimu. Paulo ananena kuti mawu a Mulungu ndi “lupanga la mzimu.” (Werengani Aefeso 6:12, 17.) Uthenga wa m’Baibulo ukafotokozedwa bwinobwino ungapulumutse anthu kwa Satana. Uthengawu ndi lupanga limene limapulumutsa anthu osati kuwapha. Motero, tifunikira kuligwiritsira ntchito bwino kwambiri.

Muziwalondoloza Bwino Mawu a Mulungu

7. N’chifukwa chiyani tifunika kuphunzira kugwiritsa ntchito mwaluso “lupanga la mzimu”?

7 Msilikali sangagwiritse ntchito mwaluso zida zake ngati sanayesererepo kapena kuphunzitsidwa bwino. N’chimodzimodzi ndi kugwiritsa ntchito “lupanga la mzimu” pa nkhondo yathu yauzimu. Paulo analemba kuti: “Chita chilichonse chotheka kuti udzisonyeze wekha wovomerezeka pamaso pa Mulungu, wantchito wopanda chochita nacho manyazi, wowalondoloza bwino mawu a choonadi.”​—2 Tim. 2:15.

8, 9. N’chiyani chingatithandize kumvetsa zimene Baibulo limanena pa nkhani inayake? Perekani chitsanzo.

8 N’chiyani chingatithandize ‘kulondoloza bwino Mawu a choonadi’ tikakhala mu utumiki? Tisanauze ena zimene Baibulo limanena pa nkhani inayake, tifunika kuimvetsa bwino kaye nkhaniyo. Kuti zimenezi zitheke, tifunika kuona mmene nkhani yonse yokhudza lembalo ilili.

9 Kuti tidziwe molondola zimene vesi linalake likutanthauza, tifunika kuona mavesi oyandikana nalo. Mawu a Paulo pa Agalatiya 5:13 akusonyeza kufunika kochita zimenezi. Iye analemba kuti: “Munaitanidwa kuti mukhale aufulu, musayese konse kugwiritsa ntchito ufulu umenewu kulimbikitsira zilakolako za thupi, koma kudzera m’chikondi tumikiranani wina ndi mnzake.” Kodi pamenepa Paulo ankanena za ufulu uti? Kodi ankanena za ufulu wa kumasuka ku uchimo ndi imfa, ku ukapolo wokhulupirira ziphunzitso zonyenga, kapena ku zinthu zina? Nkhani yonse yokhudza lembali ikusonyeza kuti Paulo ankanena za ufulu umene anthu amakhala nawo ‘akamasulidwa ku temberero la Chilamulo.’ (Agal. 3:13, 19-24; 4:1-5) Iye ankatanthauza za ufulu umene munthu amakhala nawo chifukwa chotsatira Khristu. Akhristu amene ankazindikira ubwino wa ufulu umenewu ankatumikirana chifukwa chokondana. Koma amene sankakondana, ankachita miseche ndiponso ankakangana.​—Agal. 5:15.

10. Kuti tidziwe bwino tanthauzo la Malemba, kodi tifunika kona zinthu ziti, ndipo tingazipeze bwanji zimenezi?

10 Kuti timvetse bwino tanthauzo la lemba, tiyenera kuona mfundo zina monga amene analemba buku la m’Baibulolo, nthawi imene analilemba komanso mmene zinthu zinalili panthawiyo. N’zothandizanso kuona chifukwa chake bukulo linalembedwa ndipo ngati n’kotheka kuona miyambo, chikhalidwe ndiponso chipembedzo cha anthu a panthawiyo. *

11. Tikamafotokoza malemba, kodi tiyenera kukhala osamala kuti tisachite chiyani?

11 ‘Kuwalondoloza bwino mawu a choonadi’ sikumangotanthauza kufotokoza Malemba molondola. Tifunika kusamala kuti tisamagwiritse ntchito Baibulo kuopsezera anthu. Ngakhale kuti tingagwiritse ntchito Malemba poikira kumbuyo choonadi ngati mmene Yesu anachitira atayesedwa ndi Mdyerekezi, Baibulo si chibonga choopsezera anthu kuti atsatire zofuna zathu. (Deut. 6:16; 8:3; 10:20; Mat. 4:4, 7, 10) Tifunika kutsatira malangizo a mtumwi Petulo akuti: “Pangani Khristu kukhala woyera m’mitima mwanu, monga Ambuye. Khalani okonzeka nthawi zonse kuyankha aliyense wofuna kudziwa chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho, koma ayankheni ndi mtima wofatsa ndi mwa ulemu waukulu.”​—1 Pet. 3:15.

12, 13. Kodi ndi “zinthu zozikika molimba” ziti zimene Mawu a Mulungu angagwetse? Perekani chitsanzo.

12 Tikamafotokoza bwino Mawu a Mulungu, kodi zotsatira zake zimakhala zotani? (Werengani 2 Akorinto 10:4, 5.) Malemba angathe kugwetsa “zinthu zozikika molimba” kutanthauza kuti angam’thandize munthu kuzindikira ziphunzitso zonyenga, makhalidwe oipa ndiponso mfundo zimene zimasonyeza nzeru za anthu opanda ungwiro. Tingagwiritse ntchito Baibulo kuthetsa maganizo onse ‘otsutsana ndi kudziwa kwathu Mulungu.’ Tingagwiritse ntchito zimene Baibulo limaphunzitsa kuti tithandize anthu kusintha maganizo awo n’kuyamba kuganiza mogwirizana ndi choonadi.

13 Mwachitsanzo, mayi wina wazaka 93 ku India, kuyambira ali wakhanda anaphunzitsidwa kuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake. Atayamba kuphunzira Baibulo mochita kulemberana makalata ndi mwana wake amene amakhala kudziko lina, mayiyu sizinamuvute kukhulupirira zimene anali kuphunzira zokhudza Yehova ndi malonjezo ake. Koma chiphunzitso chakuti munthu akamwalira amakabadwanso kwinakwake, chinali chozikika kwambiri m’maganizo ake moti pamene mwana wake anam’lembera nkhani yonena zimene zimachitika munthu akamwalira, anatsutsa kwambiri. Mayiyu anati: “ Malemba akowa sindikuwamvetsa n’komwe. Zipembedzo zonse zimaphunzitsa kuti anthufe tili ndi chinachake m’thupi mwathu chimene sichifa. Ineyo ndimakhulupirira kuti thupi likafa, chinthu chinachake chosaoneka chimakabadwanso m’thupi lina ndipo izi zimachitika mobwerezabwereza mpaka maulendo pafupifupi 8,400,000. Kodi zimenezi zingakhale zabodza? Moti zipembedzo zonse zimaphunzitsa zabodza?” Kodi “lupanga la mzimu” lingagwetse chikhulupiriro chozikika molimba chimenechi? Atakambirana Malemba osiyanasiyana okhudza nkhaniyi, mayiyu analemba mawu otsatirawa patapita milungu ingapo: “Tsopano ndayamba kumvetsa zimene zimachitikadi munthu akamwalira. Ndasangalala kwambiri kudziwa kuti akufa adzauka ndipo tidzatha kuonananso ndi okondedwa athu amene anamwalira. Ndikulakalaka kuti Ufumu wa Mulungu ubwere msanga.”

Muzigwiritsa Ntchito Baibulo Mokopa

14. Kodi kukopa anthu amene amatimvetsera kumatanthauza chiyani?

14 Kugwiritsa ntchito bwino Baibulo mu utumiki sikungowerenga malemba basi. Paulo ankalankhula ‘mokopa’ ndipo ifenso tizitero. (Werengani Machitidwe 19:8, 9; 28:23.) ‘Kukopa’ kumatanthauza “kukhutiritsa.” Munthu amene wakopedwayo “amaona kuti zimene wamvazo n’zoona ndipo amayamba kuzikhulupirira.” Tikamakopa munthu kuti avomereze zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhani inayake, cholinga chathu chimakhala kum’khutiritsa kuti akhulupirire zimene akuphunzirazo. Kuti zimenezi zitheke, tifunika kum’chititsa munthuyo kukhulupirira kuti zimene tikunenazo n’zoona. Zimene tingachite ndi izi:

15. Kodi mungafotokoze bwanji zimene zili m’Baibulo mwa njira yakuti anthu azililemekeza?

15 Fotokozani Mawu a Mulungu mwanjira yoti anthu aziwalemekeza. Mukamatchula lemba limene mukufuna kuwerenga ndi mwininyumba, sonyezani kuti cholinga chowerengera lembalo n’kudziwa maganizo a Mulungu pa nkhani imeneyo. Mukafunsa funso ndipo mwininyumbayo akayankha, munganene zangati izi: ‘Tiyeni tione mmene Mulungu amaonera nkhani imeneyi.’ Kapena mungafunse kuti: ‘Kodi Mulungu akuti bwanji pa nkhaniyi?’ Kuchita zimenezi tikafuna kuwerenga lemba kumathandiza anthu amene tikuwalalikira kuti aziona kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu ndiponso kuti azililemekeza. Zimenezi zimakhala zofunika kwambiri makamaka tikamalalikira munthu amene amakhulupirira Mulungu koma sadziwa kwenikweni zimene Baibulo limaphunzitsa.​—Sal. 19:7-10.

16. Kodi mungatani kuti muzifotokoza bwino malemba?

16 Musamangowerenga malemba koma muziwafotokozanso. Paulo anali ndi chizolowezi ‘chofotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa’ wa zinthu zimene ankaphunzitsa. (Mac. 17:3) Nthawi zambiri Lemba limodzi limakhala ndi mfundo zingapo, choncho mungagogomezere mfundo imene ikugwirizana ndi zimene mukukambiranazo. Mungachite zimenezi mwa kubwereza mawu amene akugwirizana ndi mfundoyo kapena kufunsa mafunso amene angathandize mwininyumba kuzindikira mfundoyo. Kenako mufotokozereni zimene mawu amenewo akutanthauza. Pomaliza, muthandizeni mwininyumbayo kuti aone mmene lembalo likumukhudzira iyeyo.

17. Kodi mungatani kuti muzikambirana ndi anthu Malemba mogwira mtima?

17 Kambiranani Malemba mogwira mtima. Paulo ‘ankakambirana ndi anthu kuchokera m’Malemba,’ mfundo zosavuta kumva. (Mac. 17:2, 4) Nanunso muziyesetsa kumufika pa mtima womvera wanu. ‘Mudzitunga’ kapena kuti kudziwa zimene zili mu mtima mwake mwa kugwiritsa ntchito mafunso abwino osonyeza kuti mumamuganizira. (Miy. 20:5) Koma pewani kulankhula mokhadzula. Fotokozani mfundo zomveka bwino ndiponso m’njira yosavuta kumva. Mfundo zanuzo zizikhala ndi umboni wokhutiritsa. Zolankhula zanu zizikhala zochokera m’Mawu a Mulungu. Ndi bwino kugwiritsa ntchito lemba limodzi pofotokoza kapena kuchitira chitsanzo mfundo inayake, kusiyana n’kuwerenga malemba awiri kapena atatu mothamanga. Kugwiritsa ntchito umboni wina kungathandizenso kuti ‘milomo yathu’ itulutse mawu okopa. (Miy. 16:23) Nthawi zina, ndi bwino kufufuza nkhaniyo kuti mupeze mfundo zina zowonjezereka. Mayi wa zaka 93 amene tamutchula uja, ankafunika kudziwa zimene zinachititsa kuti chiphunzitso chakuti munthu ali ndi mzimu wosafa, chifalikire kwambiri. Kuti akopeke n’kuvomereza zimene Baibulo limaphunzitsa pa nkhaniyi, ankafunika kumvetsa bwino kumene chiphunzitsochi chinayambira komanso mmene chinafalikira m’zipembedzo zambiri. *

Pitirizani Kugwiritsa Ntchito Baibulo Mwaluso

18, 19. N’chifukwa chiyani tifunika kupitiriza kugwiritsa ntchito mwaluso “lupanga la mzimu”?

18 Baibulo limati: “Zochitika za padzikoli zikusintha.” Anthu oipa akuipiraipirabe. (1 Akor. 7:31; 2 Tim. 3:13) Choncho, m’pofunika kwambiri kuti tipitirize kugwetsa “zinthu zozikika molimba” pogwiritsa ntchito ‘lupanga la mzimu, lomwe ndi mawu a Mulungu.’

19 Tili ndi mwayi kwambiri kukhala ndi Baibulo, lomwe ndi Mawu a Mulungu limene uthenga wake tikugwetsera ziphunzitso zonyenga ndiponso kuphunzitsira anthu oona mtima. Palibe chinthu chozikika molimba chimene sichingagwe ndi uthenga umenewu. Choncho, tiyeni tiziyesetsa kugwiritsa ntchito mwaluso “lupanga la mzimu” limeneli pa ntchito imene Mulungu watipatsa yolengeza Ufumu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Zimene zingatithandize kwambiri kupeza mfundo zina kapena zinthu zina zokhudza mabuku a m’Baibulo ndi izi: Nkhani za mu Nsanja ya Olonda zakuti, “Mawu a Yehova Ndi Amoyo,” ndiponso mabuku achingelezi akuti, “All Scripture Is Inspired of God and Beneficial,” ndi Insight on the Scriptures.

^ ndime 17 Onani kabuku ka Chingelezi kakuti What Happens to Us When We Die? masamba 5 mpaka 16.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• Kodi Mawu a Mulungu ndi amphamvu motani?

• Kodi tingatani kuti ‘tiziwalondoloza bwino mawu a choonadi’?

• Kodi n’chiyani chimene uthenga wa m’Baibulo ungachite ku “zinthu zozikika molimba”?

• Kodi mungatani kuti muzikopa kwambiri anthu mu utumiki?

[Mafunso]

[Bokosi/​Chithunzi patsamba 12]

Zimene Mungachite Kuti Muzigwiritsa Ntchito Mawu a Mulungu Mokopa

▪ Muzithandiza anthu kuti azilemekeza Baibulo

▪ Muzifotokoza tanthauzo la Malemba

▪ Muzikambirana ndi anthu mokhutiritsa kuti muwafike pa mtima

[Chithunzi patsamba 11]

Phunzirani kugwiritsa ntchito “lupanga la mzimu” mwaluso