Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima’

‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima’

‘Lankhulani Mawu a Mulungu Molimba Mtima’

“Iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera, ndipo anali kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.”​—MAC. 4:31.

1, 2. N’chifukwa chiyani tifunika kuyesetsa kulalikira mogwira mtima?

KUTATSALA masiku atatu kuti Yesu afe, iye anauza ophunzira ake kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.” Iye ataukitsidwa, koma asanabwerere kumwamba, analamula otsatira ake kuti ‘apange ophunzira mwa anthu a mitundu yonse, ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene anawalamulira.’ Iye anawalonjeza kuti adzakhala nawo pamodzi “masiku onse mpaka mapeto a dongosolo lino la zinthu.”​—Mat. 24:14; 26:1, 2; 28:19, 20.

2 Ife Mboni za Yehova timagwira ntchito imeneyi imene inayambika m’nthawi ya atumwi. Ntchito yopulumutsa moyo imeneyi, yomwe ndi yolalikira za Ufumu ndiponso kupanga ophunzira ndi yofunika kwambiri kuposa ntchito iliyonse. Choncho, m’pofunika kwambiri kuti tizilalikira mogwira mtima. M’nkhani ino tiona mmene mzimu woyera ungatithandizire kulankhula molimba mtima tikakhala mu utumiki. M’nkhani ziwiri zotsatira tiona mmene mzimu wa Yehova ungatithandizire kuphunzitsa mwaluso ndiponso kulalikira nthawi zonse.

Tifunika Kukhala Olimba Mtima

3. N’chifukwa chiyani kugwira nawo ntchito yolalikira Ufumu kumafuna kulimba mtima?

3 Ndi mwayi waukulu kuti Mulungu watipatsa ntchito yolalikira Ufumu. Komabe kugwira ntchito imeneyi kuli ndi mavuto ake. Ngakhale kuti anthu ena amamvetsera uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, ambiri amaukana ngati mmene anthu a m’nthawi ya Nowa ankachitira. Yesu anati anthu amenewa “sanazindikire kanthu mpaka chigumula chinafika ndi kuwaseseratu onsewo.” (Mat. 24:38, 39) Palinso anthu ena amene amatinyoza kapena kutitsutsa. (2 Pet. 3:3) Nthawi zina, anthu amene angatitsutse ndi akuluakulu a boma, anzathu a kusukulu kapena a ku ntchito, ngakhalenso achibale athu enieni. Kuwonjezera pamenepa, tilinso ndi mavuto athu monga manyazi ndiponso kukayikira kuti anthu sangamvetsere uthenga wathu. Pali zinthu zambiri zimene zingatilepheretse kukhala ndi “ufulu wa kulankhula” kuti tizilalikira mawu a Mulungu “molimba mtima.” (Aef. 6:19, 20) Koma kuti tipitirizebe kulankhula mawu a Mulungu, tifunika kulimba mtima. Ndiyeno n’chiyani chingatithandize kuti tikhale olimba mtima?

4. (a) Kodi kulimba mtima n’kutani? (b) Kodi n’chiyani chinathandiza mtumwi Paulo kuti athe kulalikira ku Tesalonika?

4 Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kulimba mtima” amatanthauza “kulankhula momasuka kapena mosapita m’mbali.” Mawu amenewo, amatanthauzanso “kulankhula mopanda mantha.” Komabe kulimba mtima sikutanthauza kulankhula mokhadzula kapena mwamwano. (Akol. 4:6) Inde, kulimba mtima kumafunanso kuti tizikhala pamtendere ndi anthu onse. (Aroma 12:18) Tikamalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu tifunika kulankhula molimba mtima koma tiyenera kusamala kwambiri kuti tisakhumudwitse anthu amene tikuwalalikirawo. Ndithudi kuti tizilankhula molimba mtima tifunika kuyesetsa kukhalanso ndi makhalidwe ena. Koma sitingakhale olimba mtima chonchi mwa mphamvu zathu zokha. Kodi mtumwi Paulo ndi anzake ‘atachitidwa za chipongwe ku Filipi,’ n’chiyani chinawathandiza kuti ‘alimbe mtima’ kulalikira anthu a ku Tesalonika? Paulo ananena kuti analimba mtima chifukwa chakuti Mulungu anawathandiza. (Werengani 1 Atesalonika 2:2.) Ifenso, Yehova Mulungu angatichotsere mantha amene tingakhale nawo n’kutithandiza kukhala olimba mtima.

5. Kodi Yehova anathandiza bwanji Petulo, Yohane ndiponso ophunzira ena kuti akhale olimba mtima?

5 Mtumwi Petulo ndiponso mtumwi Yohane atawopsezedwa ndi “olamulira [a anthu] ndi akulu ndiponso alembi,” anati: “Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” M’malo mopempha Mulungu kuti athetse chizunzocho, iwo ndi Akhristu anzawo anapemphera kuti: “Yehova, imvani ziopsezo zawo, ndipo lolani akapolo anu alankhulebe mawu anu molimba mtima.” (Mac. 4:5, 19, 20, 29) Kodi Yehova anayankha bwanji pemphero lawoli? (Werengani Machitidwe 4:31.) Yehova anawathandiza ndi mzimu wake kuti akhale olimba mtima. Mzimu wa Mulungu ungatithandizenso ifeyo kukhala olimba mtima. Komano kodi tingatani kuti tilandire mzimu wa Mulungu kuti uzititsogolera mu utumiki wathu?

Zimene Tingachite Kuti Tikhale Olimba Mtima

6, 7. Kuti tilandire mzimu woyera wa Mulungu m’njira yosavuta, kodi tingachite chiyani? Perekani zitsanzo.

6 Njira yosavuta imene tingalandirire mzimu woyera wa Mulungu, ndi mwa kupempha Mulungu kuti atipatse mzimuwo. Yesu anauza anthu amene ankamumvetsera kuti: “Ngati inu, ngakhale muli oipa, mumadziwa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Iye adzapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Ndithudi, nthawi zonse tifunika kupempha Mulungu kuti atipatse mzimu woyera. Ngati mbali zina za utumiki monga kulalikira mumsewu, mwamwayi, kapena m’gawo la malonda kumatichititsa mantha, tingapemphe Yehova kuti atipatse mzimu wake ndiponso kuti atithandize kukhala olimba mtima.​—1 Ates. 5:17.

7 Izi n’zimene mkazi wina wachikhristu dzina lake Rosa anachita. * Tsiku lina iye ali ku ntchito, mphunzitsi wina yemwe amagwira naye ntchito ankawerenga lipoti lochokera kusukulu ina lomwe linkanena zakuti ana ena ankazunzidwa. Mphunzitsiyo anasokonezeka maganizo ndi zimene anawerengazo, ndipo anati: “Kodi dzikoli likulowera kuti?” Rosa anaona kuti uwu unali mwayi wake woti alalikire. Kodi iye anatani kuti alimbe mtima kulalikira? Iye anati: “Ndinapemphera kwa Yehova kuti andithandize ndi mzimu wake.” Atatero, Rosa anakwanitsa kulalikira ndipo anagwirizana zoti adzakambiranenso nkhaniyi. Taganiziraninso za Milane, mtsikana wina wa zaka 5 amene amakhala ku New York City. Iye anati: “Nthawi zonse ndisanapite kusukulu, ine ndi amayi anga timapemphera kwa Yehova.” Kodi iwo amapempha chiyani? Kuti Milane akhale wolimba mtima n’cholinga choti adzitha kufotokoza zimene amakhulupirira zokhudza Mulungu. Amayi ake anati: “Zimenezi zathandiza Milane kufotokoza zimene amakhulupirira pa nkhani ya kukumbukira masiku obadwa ndiponso maholide. Zathandizanso kuti asamachite nawo zinthu zimenezi.” Zitsanzo zimenezi zikusonyezadi kuti pemphero limathandiza munthu kukhala wolimba mtima.

8. Kodi tikuphunzira chiyani kwa mneneri Yeremiya pa nkhani ya kulimba mtima?

8 Taganiziraninso zimene zinathandiza mneneri Yeremiya kuti akhale wolimba mtima. Yehova atamusankha kuti akhale mneneri wake kwa anthu amitundu, Yeremiya anati: “Sindithai kunena pakuti ndili mwana.” (Yer. 1:4-6) Koma Yeremiya anasintha maganizo akewa n’kuyamba kulalikira mwamphamvu, moti anthu ambiri anayamba kumuona ngati munthu wokonda kumangokamba za tsoka. (Yer. 38:4) Iye analengeza molimba mtima ziweruzo za Yehova kwa zaka zoposa 65. Anali wodziwika bwino m’dziko lonse la Isiraeli chifukwa cholalikira mopanda mantha ndiponso molimba mtima. Ndipo patatha zaka pafupifupi 600, kuchokera nthawi imeneyo, anthu ena ankati Yeremiya wauka ataona mmene Yesu ankalankhulira molimba mtima. (Mat. 16:13, 14) Kodi mneneri Yeremiya amene poyamba anali wamantha anatani kuti akhale wolimba mtima? Iye anati: ‘M’mtima mwanga [mawu a Mulungu] ali ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.’ (Yer. 20:9) Inde, mawu a Yehova anam’patsa mphamvu Yeremiya ndipo anamulimbitsa mtima kuti azilankhula.

9. N’chifukwa chiyani mawu a Mulungu angatipatse mphamvu ngati mmene zinalili ndi Yeremiya?

9 M’kalata imene analembera Aheberi, mtumwi Paulo anati: “Mawu a Mulungu ndi amoyo ndi amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amapyoza mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu, mfundo za mafupa ndi mafuta a m’mafupa. Amathanso kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” (Aheb. 4:12) Uthenga wa Mulungu, kapena kuti mawu ake, ungatipatse mphamvu ngati mmene zinalili ndi Yeremiya. Ngakhale kuti anthu ndi amene anagwiritsidwa ntchito kulemba Baibulo, tisaiwale kuti anthuwo sanalembe nzeru zawo koma anauziridwa ndi Mulungu. Lemba la 2 Petulo 1:21 limati: “Ulosi sunayambe wadzapo mwa kufuna kwa munthu, koma anthu analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa ndi mzimu woyera.” Tikamapeza nthawi yophunzira Baibulo patokha bwinobwino, m’maganizo mwathu mumakhala uthenga wouziridwa ndi mzimu woyera. (Werengani 1 Akorinto 2:10.) Uthenga umenewu ungakhale “ngati moto wotentha” m’maganizo mwathu, moti sitingathe kungousunga osauzako ena.

10, 11. (a) Kuti tizilankhula molimba mtima, kodi tiyenera kuphunzira bwanji Baibulo? (b) Tchulani zimene mwasankha kuchita n’cholinga chakuti mukamaphunzira Mawu a Mulungu muzipindula kwambiri.

10 Kuti kuphunzira Baibulo patokha kukhale kothandiza kwambiri, tiyenera kuliphunzira m’njira yakuti uthenga wake utifike pamtima. Mwachitsanzo, mneneri Ezekieli m’masomphenya anauzidwa kuti adye mpukutu wa buku wokhala ndi uthenga wamphamvu woti akauze anthu osamvera. Iye anafunikira kuudziwa bwino uthengawo. Kuchita zimenezi kunachititsa kuti ntchito yofotokoza uthengawo ikhale yokoma ngati uchi.​—Werengani Ezekieli 2:8–3:4, 7-9.

11 Umu ndi mmene zililinso ndi ifeyo. Masiku ano, anthu ambiri safuna n’komwe kumva zimene Baibulo limanena. Kuti tizilankhula mawu a Mulungu molimba mtima, tifunika kuphunzira Malemba m’njira yoti tizimvetsa bwino zomwe tikuphunzirazo. Tiyenera kukhala ndi chizolowezi chophunzira Mawu a Mulungu nthawi zonse, osati mwa apa ndi apo. Tiyenera kukhala ndi mtima ngati wa wamasalmo amene anaimba kuti: “Mawu a m’kamwa mwanga ndi maganizo a m’mtima wanga avomerezeke pamaso panu, Yehova, thanthwe langa, ndi Mombolo wanga.” (Sal. 19:14) M’pofunika kwambiri kuti tizisinkhasinkha zimene tawerenga n’cholinga chakuti choonadi cha m’Baibulo chikhazikike mu mtima mwathu. Ndithudi, tifunika kuyesetsa kuti tizipindula kwambiri tikamaphunzira patokha Mawu a Mulungu. *

12. N’chifukwa chiyani tinganene kuti misonkhano yampingo imatithandiza kuti mzimu woyera uzititsogolera?

12 Njira inanso imene tingalandirire mzimu woyera wa Yehova ndiyo ‘kuganizirana wina ndi mnzake, kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino ndiponso kusaleka kusonkhana kwathu pamodzi.’ (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zonse tikamayesetsa kupezeka pa misonkhano yampingo, kumvetsera mwatcheru ndiponso kugwiritsa ntchito mfundo zimene timaphunzirazo, mzimu wa Mulungu umatitsogolera. Ndipotu mzimu wa Yehova umatitsogolera kudzera mu mpingo.​—Werengani Chivumbulutso 3:6.

Ubwino wa Kulimba Mtima

13. Kodi zimene Akhristu oyambirira anakwanitsa kuchita pa ntchito yolalikira zikutiuza chiyani?

13 Mzimu woyera ndi wamphamvu kuposa china chilichonse ndipo ungapatse anthu mphamvu kuti achite zimene Yehova amafuna. Mzimu woyera ndi umene unathandiza kwambiri Akhristu oyambirira kugwira ntchito yolalikira. Iwo analalikira uthenga wabwino “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Tikaganizira kuti ambiri mwa Akhristuwo anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” n’zoonekeratu kuti mzimu woyera ndi umene unkawathandiza.​—Mac. 4:13.

14. N’chiyani chingatithandize kuti ‘tiziyaka ndi mzimu’?

14 Kukhala ndi makhalidwe amene angachititse kuti mzimu woyera uzititsogolera, kungatithandizenso kukhala olimba mtima pa ntchito yathu yolalikira. Nthawi zonse tikamapempha mzimu woyera, kuphunzira mwakhama Mawu a Mulungu patokha, kusinkhasinkha zimene tawerenga ndiponso kupezeka pamisonkhano yampingo, ‘timayaka ndi mzimu.’ (Aroma 12:11) Baibulo limati: “Myuda wina dzina lake Apolo, mbadwa ya ku Alesandiriya, wokhala ndi mphatso ya kulankhula, anafika ku Efeso. . . . Ndipo pokhala wotentha [kapena kuti woyaka] ndi mzimu, anali kulankhula ndi kuphunzitsa molondola za Yesu.” (Mac. 18:24, 25) ‘Kuyaka ndi mzimu,’ kungatithandize kuti tizilimba mtima kwambiri polalikira ku nyumba ndi nyumba kapenanso polalikira mwamwayi.​—Aroma 12:11.

15. Kodi ubwino wa kulankhula molimba mtima kwambiri ndi wotani?

15 Kukhala wolimba mtima kwambiri polalikira kuli ndi ubwino wake. Timayamba kuona kufunika ndiponso ubwino wa ntchito yathu. Komanso timayamba kukonda kwambiri utumiki chifukwa timasangalala tikamalalikira mogwira mtima. Timachita khama kwambiri chifukwa timadziwa kuti ntchito yolalikira ndi yofunika kuigwira mwamsanga.

16. Kodi tiyenera kutani ngati sitikuchitanso khama pochita utumiki wathu?

16 Bwanji ngati panopa sitikuchitanso khama pa ntchito yathu yolalikira ngati mmene tinkachitira poyamba? Ngati zili choncho, ndi bwino kuti muonenso mmene moyo wanu ulili. Paulo analemba kuti: “Pitirizani kudziyesa nokha kuti muone ngati muli m’chikhulupiriro. Pitirizani kudzidziwa nokha motsimikiza kuti ndinu otani.” (2 Akor. 13:5) Choncho dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikuyakabe ndi mzimu? Kodi ndimapemphera kwa Yehova kuti andipatse mzimu wake? Kodi mapemphero anga amasonyeza kuti ndimadalira Mulungu kuti andithandiza kuchita zimene amafuna? Ndikamapemphera, kodi ndimanena mawu osonyeza kuyamikira utumiki umene watipatsa? Kodi chizolowezi changa n’chotani pa nkhani ya kuphunzira Mawu a Mulungu? Kodi ndimatenga nthawi yochuluka bwanji ndikusinkhasinkha zimene ndawerenga kapena kumva? Kodi ndimatenga nawo mbali pamisonkhano ya mpingo?’ Kuganizira mafunso ngati amenewa kungatithandize kuzindikira mbali zimene sitikuchita bwino ndiponso zimene tingachite.

Lolani Mzimu wa Mulungu Kuti Ukuthandizeni Kukhala Olimba Mtima

17, 18. (a) Kodi ntchito yolalikira ikugwirika motani masiku ano? (b) Kodi tingakhale bwanji ndi “ufulu wonse wa kulankhula” polengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu?

17 Yesu ataukitsidwa anauza ophunzira ake kuti: “Mudzalandira mphamvu pamene mzimu woyera udzafika pa inu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Ntchito yomwe inayamba nthawi imeneyo, masiku ano ikugwiridwa kwambiri kuposa kale lonse. Mboni za Yehova pafupifupi 7 miliyoni zikulalikira uthenga wa Ufumu m’mayiko oposa 230, ndipo zikuthera maola pafupifupi 1.5 miliyoni mu utumiki chaka chilichonse. N’zosangalatsa kwambiri kugwira nawo mwa khama ntchito imeneyi imene sidzabwerezedwanso.

18 Mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, mzimu wa Mulungu ndi umene ukutsogolera ntchito yolalikira yomwe ikuchitika padziko lonse. Tikamalola mzimu kutitsogolera, tidzakhala ndi “ufulu wonse wa kulankhula” mu utumiki wathu. (Mac. 28:31) Motero, tiyeni tiziyesetsa kuti mzimu woyera uzititsogolera pamene tikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Maina tawasintha.

^ ndime 11 Kuti muzipindula kwambiri mukamawerenga Baibulo ndiponso mukamaphunzira panokha, onani mutu wakuti “Chitani Khama pa Kuwerenga” ndi wakuti “Kuphunzira Kumapindulitsa” m’buku la Pindulani ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, masamba 21 mpaka 32.

Kodi Mwaphunzira Chiyani?

• N’chifukwa chiyani tifunika kulimba mtima polankhula mawu a Mulungu?

• Kodi n’chiyani chinathandiza ophunzira oyambirira kuti azilankhula molimba mtima?

• Kodi tingatani kuti tikhale olimba mtima?

• Kodi ubwino wa kukhala wolimba mtima ndi wotani?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale olimba mtima?

[Zithunzi patsamba 8]

Pemphero lachidule lingakuthandizeni kuti mulalikire molimba mtima