Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi munthu angasankhe kubatizidwanso pa zifukwa zotani?

Nthawi zina, munthu wobatizidwa angamakayikire ngati ubatizo wake unali woyenerera kapena ayi, ndipo angafune kubatizidwanso. Mwachitsanzo, panthawi imene ankabatizidwa angakhale kuti mwamseri ankachita zinazake zoipa moti akanakhala kuti ndi wobatizidwa kale, akanayenera kuchotsedwa. Kodi munthu wotereyu anachita bwino kudzipereka kwa Mulungu akuchita zimenezi? Kuti kudzipereka kwake kwa Yehova kukhale koyenerera, iye anafunika kusiya kaye khalidwe lake losemphana ndi Malembalo. Motero, munthu amene anabatizidwa ali mu mkhalidwe wotere angaganizire ngati akufunika kuti abatizidwenso.

Nanga bwanji munthu amene sanali kuchita tchimo pamene ankabatizidwa, koma atangobatizidwa anachita tchimo linalake lofunika komiti yachiweruzo? Tiyerekeze kuti iye akunena kuti panthawiyo sankamvetsa bwino tanthauzo la ubatizo wake ndipo akuona kuti ubatizo wakewo unali wosayenera. Akulu akakumana ndi munthu wotereyu, sayenera kumufunsa mafunso okhudza ubatizo wake kapena kumufunsa ngati akuona kuti kudzipereka kwake kwa Mulungu ndiponso ubatizo wake zinali zoyenera. Ndipotu, iye anamvetsera nkhani ya m’Malemba yonena za kufunika kwa ubatizo ndipo anayankha motsimikiza mafunso okhudza kudzipereka ndiponso ubatizo. Kenako, anasintha zovala zake ndipo anabatizidwa mwa kumizidwa m’madzi. Choncho, m’pomveka kunena kuti ankadziwa bwinobwino zimene ankachita. Motero, akulu ayenera kumuona kuti ndi munthu wobatizidwa.

Ngati munthuyo akunena kuti ubatizo wake unali wosayenerera, akulu angam’sonyeze mfundo za mu Nsanja ya Olonda ya March 1, 1960, masamba 159 ndi 160, komanso ya February 15, 1964, masamba 123 mpaka 126. Nkhani yokhudza kubatizidwanso inafotokozedwa mwatsatanetsatane mu magazini amenewa. Ngati munthu angafune kubatizidwanso pa zifukwa zina (monga kusamvetsa bwino mfundo zina za m’Baibulo pa nthawi imene ankabatizidwa), ndi chosankha chake.

Kodi Akhristu ayenera kuganizira mfundo ziti pa nkhani ya kukhala m’nyumba imodzi ndi anthu ena?

Munthu aliyense amafunika malo okhala. Koma masiku ano, anthu ambiri alibe nyumba. Zinthu monga mavuto a zachuma, matenda, kapena zinthu zina zingachititse kuti anthu ambiri a pachibale azikhala m’nyumba imodzi. M’mayiko ena, zimatheka anthu angapo apachibale kumakhala m’chipinda chimodzi.

Gulu la Yehova lilibe udindo wopereka mndandanda wa malamulo okhudza mmene Akhristu onse padziko lapansi ayenera kukhalira m’nyumba zawo. Koma Akhristu akulimbikitsidwa kuganizira mfundo za m’Malemba kuti aone ngati akukhala mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Kodi zina mwa mfundo zimenezi ndi ziti?

Pa nkhani yokhala ndi anthu ena, chinthu chofunika kwambiri kuchiganizira, ndi kuona mmene zimenezi zingakhudzire moyo wathu wauzimu komanso mbali zina za moyo wathu. Kodi anthu amene tikukhala nawowo ndi otani? Kodi amalambira Yehova? Kodi amatsatira mfundo za m’Baibulo? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Musasocheretsedwe. Mayanjano oipa amawononga makhalidwe abwino.”​—1 Akor. 15:33.

Malemba amanena kuti Yehova amadana ndi chiwerewere ndiponso chigololo. (Aheb. 13:4) Zilizonse zimene mungakonze zokhudza malo ogona, zimene zingachititse kuti anthu osakwatirana azikhala pamodzi ngati kuti ndi okwatirana, n’zosagwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. Palibe Mkhristu amene angafune kukhala pamalo amene khalidwe lachiwerewere limavomerezedwa.

Ndiponso, Baibulo limalangiza anthu onse amene amafuna kuti Mulungu aziwayanja kuti: “Thawani dama.” (1 Akor. 6:18) Choncho, ndi bwino kuti Akhristu azipewa kuchita zinthu zimene zingapangitse kuti achite chiwerewere. Mwachitsanzo, taganizirani ngati Akhristu angapo amagona m’nyumba imodzi. Kodi zimenezi sizingachititse kuti Akhristuwa panthawi ina adzakhale pachiyeso? Kodi zingakhale bwanji ngati pa zifukwa zina Akhristu awiri osakwatirana apezeka ali awiriawiri, mwina chifukwa chakuti anthu amene amakhala nawo achokapo kaye? Zingakhalenso zoopsa ngati anthu awiri osakwatirana amene amafunana akukhala m’nyumba imodzi. Choncho, ndi nzeru kupewa zimenezi.

Sizingakhalenso zoyenera kuti anthu amene analekana ukwati azikhala m’nyumba imodzi. Popeza ndi anthu amene ankakhalira limodzi, n’kosavuta kuti iwo achite chiwerewere.​—Miy. 22:3.

Chinthu chinanso chofunika kuchiganizira kwambiri, ndi mmene anthu akuderalo angaonere zochita zathuzo. Ngakhale titaona kuti mmene tikukhalira si vuto, koma ngati anthu akuderalo amaona kuti sizoyenera, tiyenera kusintha. Sitikufuna kuti khalidwe lathu linyozetse dzina la Yehova. Pa nkhani imeneyi, Paulo anati: “Pewani kukhala okhumudwitsa kwa Ayuda, ngakhalenso kwa Agiriki, ndi mpingo wa Mulungu, monga mmene ineyo ndikukondweretsera anthu onse m’zinthu zonse. Sindingofuna zopindulitsa ine ndekha ayi, koma zopindulitsa anthu ambiri, kuti apulumutsidwe.”​—1 Akor. 10:32, 33.

Zingakhale zovuta kwambiri kwa Akhristu amene akufuna kutsatira mfundo zolungama za Yehova kupeza malo okhala oyenera. Komabe Akhristu ayenera ‘kutsimikiza kuti cholandirika kwa Ambuye n’chiti.’ Ayenera kuonetsetsa kuti palibe chosayenera chilichonse chimene chikuchitika pa nyumba pawo. (Aef. 5:5, 10) Kuti achite zimenezi, Akhristu ayenera kupempha Mulungu kuti awatsogolere, ndiponso kuchita zonse zimene angathe kuti asungirane ulemu komanso kuti asanyozetse dzina la Yehova