Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Musalole Mabodza a Satana Kukusokonezani Maganizo

Musalole Mabodza a Satana Kukusokonezani Maganizo

Musalole Mabodza a Satana Kukusokonezani Maganizo

‘MUSANYENGEDWE. Mulungu wanu sadzakuthandizani. Ingodziperekani kukhala akapolo athu chifukwa mukapanda kutero tikuonetsani zoopsa.’ Izi n’zimene Rabusake, yemwe anali kazembe wa Mfumu Sanakeribu ya ku Asuri, anauza anthu a ku Yerusalemu. Asilikali a mfumuyi anali atalowa mu Yuda. Ananena mawuwa m’njira yakuti afooketse anthu a ku Yerusalemu kuti angogonjera chifukwa cha mantha.​—2 Maf. 18:28-35.

Asuri ankadziwika kuti anali anthu a nkhanza zoopsa. Iwo ankaopseza adani awo mwa kuwauza nkhanza zimene amachitira akapolo awo. Malinga ndi wolemba mbiri wina dzina lake Philip Taylor, Asuri ankakonda “kulankhula mawu abodza ndiponso oopseza, ochititsa kuti akapolo awo afookeretu ndiponso anthu amene akufuna kumenyana nawo asokonezeke maganizo kuti asavutevute.” Njira yoopseza anthu ndi mabodzayi ndi yoopsa kwambiri. Taylor uja anati, ‘imathadi kusokoneza maganizo a munthu.’

Akhristu enieni ‘salimbana ndi anthu a thupi la magazi ndi nyama ayi, koma ndi makamu a mizimu yoipa m’malo a kumwamba,’ kutanthauza angelo amene anapandukira Mulungu. (Aef. 6:12) Satana Mdyerekezi ndiye mdani wamkulu kwambiri. Nayenso amagwiritsa ntchito njira zowopsezera anthu kuti awasokonezeke maganizo.

Satana amati angalepheretse anthu onse kukhala ndi mtima wosagawanika. Masiku a Yobu, Satana anauza Yehova Mulungu kuti: “Munthu adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake.” Pamenepa tingati kwenikweni Satana amati munthu akangofika poti mavuto amukwana angathe kusiya kutumikira Mulungu ndi mtima wonse. (Yobu 2:4) Kodi pamenepa Satana amanena zoona? Kodi tonsefe tilidi ndi malire a zimene tingathe kupirira moti zinthu zikapitirira malire amenewo tingalolere kuphwanya mfundo zolungama kuti tipulumutse moyo wathu? Izitu n’zimene Satana amafuna kuti tizikhulupirira. Motero amagwiritsira ntchito mabodza osiyanasiyana pofuna kutisokoneza maganizo kuti akwaniritse cholinga chakechi. Tiyeni tione mabodza ena amene amagwiritsira ntchito komanso zimene tiyenera kuchita kuti Satanayu asatichenjerere.

‘Maziko Awo Ali M’fumbi’

Satana anagwiritsira ntchito Elifazi, mmodzi wa anthu atatu amene anapita kukazonda Yobu, kunena mfundo yabodza yakuti anthu sangalimbelimbe akakumana ndi ziyeso za Satana. Iye ananena kuti anthu ndi ‘okhala m’nyumba zadothi,’ ndipo anauza Yobu kuti ‘maziko awo ali m’fumbi. Angothudzulidwa ngati gulugufe. Kuyambira m’mawa kufikira madzulo athudzuka; awonongeka kosatha, osasamalirako munthu.’​—Yobu 4:19, 20.

Malemba ena amayerekezera anthu ndi “zotengera zadothi,” zomwe sizichedwa kusweka. (2 Akor. 4:7) N’zoona kuti uchimo umene tinatengera kwa makolo athu oyambirira komanso kupanda ungwiro zimachititsa kuti tikhale ofooka. (Aroma 5:12) Moti patokha sitingathe kulimbana ndi Satana. Komabe, poti ndife Akhristu, Yehova amatithandiza. Ngakhale kuti tili ndi zofooka, ndife amtengo wapatali kwambiri pamaso pa Mulungu. (Yes. 43:4) Komanso Yehova amapereka mzimu woyera kwa amene am’pempha. (Luka 11:13) Mzimu wake ungathe kutipatsa “mphamvu yoposa yachibadwa,” yomwe ingatithandize kulimbana ndi mavuto aliwonse amene Satana amatibweretsera. (2 Akor. 4:7; Afil. 4:13) Tikamayesetsa kulimbana ndi Mdyerekezi, n’kukhala “olimba m’chikhulupiriro,” Mulungu angathe kutilimbitsa n’kukhala amphamvu. (1 Pet. 5:8-10) Motero sitiyenera kumuopa Satana Mdyerekezi.

Munthu ‘Amamwa Chosalungama’

Elifazi anafunsa kuti: “Munthu n’chiyani kuti akhale woyera, wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?” Ndiyeno anayankha funso lakeli ponena kuti: “Taona, Mulungu sakhulupirira opatulika ake; ngakhale m’mwamba simuyera pamaso pake. Koposa kotani nanga munthu wonyansa ndi wodetsa, wakumwa chosalungama ngati madzi.” (Yobu 15:14-16) Pamenepatu Elifazi ankamuuza Yobu kuti palibe munthu amene Yehova amamuona kuti ndi wolungama. Mdyerekezi naye amagwiritsira ntchito maganizo ofoola oterewa. Amafuna kuti tizingokhalira kudandaula chifukwa cha zolakwa zathu zakale, n’kumaona kuti palibe chilichonse chakupsa chimene tikuchita ndiponso kuti ndife okanikiratu basi. Amafuna kutipatsa maganizo akuti Yehova amafuna kumuchitira zinthu zovuta kwambiri kuzikwanitsa. Amafunanso kuti tizichepetsa chifundo chake, kukhululuka kwake, komanso thandizo lake.

N’zoona kuti tonsefe ‘ndife ochimwa ndipo ndife operewera pa ulemerero wa Mulungu.’ Palibe munthu aliyense wopanda ungwiro amene angafikire miyezo yolungama ya Yehova. (Aroma 3:23; 7:21-23) Komabe, zimenezi sizikutanthauza kuti ndife opanda ntchito kwa iye. Yehova amadziwa kuti “njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana,” ndi amene akutengerapo mwayi pa kupanda ungwiro kwathu. (Chiv. 12:9, 10) Mulungu amatimvetsa pozindikira kuti “ndife fumbi,” motero “samatsutsana nafe nthawi zonse.”​—Sal. 103:8, 9, 14.

Tikasiya njira yoipa n’kumufikira Yehova ndi mtima wolapadi, iye ‘adzatikhululukira koposa.’ (Yes. 55:7; Sal. 51:17) Ngakhale machimo athu atafika ‘pofiira,’ Baibulo limati ‘adzayera ngati matalala.’ (Yes. 1:18) Motero, tiyeni titsimikize mtima kusafooka kuchita chifuniro cha Mulungu.

N’zosatheka kukhala olungama pamaso pa Mulungu tidakali ochimwa chonchi. Adamu ndi Hava anataya moyo wangwiro ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha ndipo zimenezi zinakhudzanso tonsefe. (Aroma 6:23) Komabe, chifukwa choti Yehova amakonda kwambiri anthu, iye anakonza zoti machimo athu akhululukidwe ngati titakhulupirira nsembe ya dipo ya Mwana wake, Yesu Khristu. (Mat. 20:28; Yoh. 3:16) Apatu Mulungu anasonyeza kukoma mtima ndiponso chisomo chachikulu. (Tito 2:11) Ndithu, anthufe siife okanikiratu ayi, tingathe kuwomboledwa. Motero tisalole Satana kutipangitsa kuganiza ngakhale pang’ono chabe kuti ndife okanika.

‘Khudzani Fupa Lake ndi Mnofu Wake’

Satana ananena kuti Yobu atati ayambe kudwala angathe kusiya kukhulupirika kwa Mulungu. Potsutsa Yehova, Mdyerekezi anati: “Tambasulani dzanja lanu, ndi kukhudza fupa lake ndi mnofu wake, ndipo adzakuchitirani mwano pamaso panu.” (Yobu 2:5) N’zoonekeratu kuti Mdani wa Mulunguyu angasangalale kwambiri ngati atatipangitsa kumva kuti ndife opanda ntchito chifukwa choti thanzi lathu silili bwino.

Komabe, Yehova satitaya chifukwa choti sitikukwanitsanso zimene tinkachita kale mu utumiki wake. Kodi ngati mnzanu atavulazidwa mungayambe kumuona kuti ndi wosafunika kwenikweni chifukwa choti panopo sangathe kukuchitirani zinthu zina? Ayi ndithu simungatero. Ndipotu mukhoza kumam’konda kwambiri makamaka ngati anavulala pofuna kukuthandizani. Izi n’zimenenso Yehova angachite. Baibulo limati: “Mulungu si wosalungama woti angaiwale ntchito yanu ndi chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake.”​—Aheb. 6:10.

Malemba amanena za “mkazi wina wamasiye wosauka” amene ayenera kuti ankapereka zinthu zochirikiza kulambira Mulungu kwa zaka zambiri. Yesu atamuona m’kachisi “akuponya timakobili tiwiri tating’ono” moponya zopereka, sanaone kuti timakobiri taketo n’topanda ntchito. M’malomwake iye anamuyamikira kwambiri chifukwa chopereka ndalama zimene akanakwanitsa pochirikiza kulambira koona.​—Luka 21:1-4.

Tikapitiriza kukhala ndi mtima wosagawanika, ubwenzi wathu ndi Yehova udzakhalabe wolimba ngakhale titamakumana ndi mavuto obwera chifukwa cha kupanda ungwiro monga ukalamba ndi matenda. Mulungu sangataye anthu okhulupirika amene akulephera kumutumikira chifukwa cha mavuto.​—Sal. 71:9, 17, 18.

“Landirani Chisoti Cholimba cha Chipulumutso”

Kodi tingadziteteze bwanji ku misampha ya Satana? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pitirizani kupeza mphamvu mwa Ambuye ndi mwa nyonga zake zazikulu. Valani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu kuti muthe kuchirimika polimbana ndi machenjera a Mdyerekezi.” Chimodzi mwa zida zimenezi ndi “chisoti cholimba cha chipulumutso.” (Aef. 6:10, 11, 17) Popeza tikudziwa njira zimene Satana amagwiritsa ntchito tiyenera kuvala chisoti cholimba cha chipulumutso. Chisoti cholimba chimateteza mutu wa msilikali. Nachonso “chiyembekezo cha chipulumutso” chomwe chimatanthauza mtima wosakayikira malonjezo a Mulungu okhudza dziko latsopano, chingatiteteze kuti tisakhulupirire mabodza a Satana. (1 Ates. 5:8) Tiyenera kulimbitsa chiyembekezo chimenechi pochita khama patokha kuphunzira Malemba.

Yobu anapirira atazunzidwa mwankhanza ndi Satana. Chikhulupiriro cha Yobu chinali champhamvu kwambiri moti ngakhale imfa sankaiopa. M’malomwake anauza Yehova kuti: “Mukadaitana, ndipo ndikadakuyankhani; mukadakhumba ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:15) Yobu ankadziwa kuti Mulungu ndi wachikondi ndipo ngati atumiki ake atamwalira ali okhulupirika, Mulunguyo adzawaitana kuti auke.

Tiyeni tonsefe tizikhulupirira kwambiri Mulungu ngati mmene Yobu anachitira. Yehova angathe kusintha zinthu zoipa zonse zimene Satana ndi gulu lake angatichitire. Tisaiwalenso kuti Paulo anatitsimikizira kuti “Mulungu ndi wokhulupirika ndipo sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapirire, koma pamene mukukumana ndi mayeserowo iye adzapereka njira yopulumukira kuti muthe kuwapirira.”​—1 Akor. 10:13.

[Chithunzi patsamba 20]

Yehova amaona kuti ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri kuti mukumutumikira mokhulupirika

[Chithunzi patsamba 21]

Landirani ndi kuvalabe chisoti cholimba cha chipulumutso