“Mwana Ali ndi Ufulu Wokula Mwauzimu”
“Mwana Ali ndi Ufulu Wokula Mwauzimu”
PA December 9, 2008, Bungwe Loona za Ufulu wa Ana ku Sweden linachititsa msonkhano wochititsa chidwi wa mutu wakuti, “Mwana Ali ndi Ufulu Wokula Mwauzimu.” Pali mfundo zambiri zimene zinatchulidwa ndi anthu oimira zipembedzo zosiyanasiyana amene analankhulapo pamsonkhanowu, monga Asilamu, a Church of Sweden ndiponso anthu okhulupirira chiphunzitso chakuti munthu ndiye wofunika kwambiri pa zonse.
Ena mwa anthu amene analankhulawo anali m’busa amene ananena kuti: “Kunena zoona, nkhani za m’Baibulo n’zofunika kwambiri kuti ana akule mwauzimu.” Kodi nkhani za m’Malemba zimathandiza bwanji ana kukula mwauzimu?
M’busayo anati: “Nkhanizi zimathandiza ana kupeza mfundo zoti angathe kumaziganizira akakhala paokha n’kumazisinkhasinkha.” Iye anatchulapo “nkhani ya Adamu ndi Hava, ya Kaini ndi Abele, ya Davide ndi Goliati, ya kubadwa kwa Yesu, ya Zakeyu wokhometsa misonkho, fanizo la mwana wolowerera ndi la Msamariya wachifundo.” Iye anatchula nkhani zimenezi monga “zitsanzo za nkhani zophunzitsa [mwana] makhalidwe abwino pa zinthu monga chinyengo, kukhululuka, kupepesa, chidani, makhalidwe oipa, kuyanjana, chikondi chaubale ndiponso chikondi chololera kuvutikira ena.” Iye anatinso: “Nkhani zimenezi zimam’patsa munthu nzeru zothandiza zimene zimayamba kuonekera m’zochita zake.”
Kunena zoona, ndi bwino kwambiri kulimbikitsa anthu kuti aziwerenga Baibulo. Komabe, kodi ana akamawerenga Malemba angakwanitsedi “kupeza mfundo zoti angathe kumaziganizira akakhala paokha n’kumazisinkhasinkha”?
Ngakhale munthu wamkulu amafunika kum’fotokozera nkhani za m’Malemba. Mwachitsanzo, Baibulo limatiuza zoti panali achikulire ena amene analephera “kupeza mfundo zoti angathe kumaziganizira akakhala paokha n’kumazisinkhasinkha.” Wachikulire ameneyu anali mdindo wa ku Aitiopiya. Iye ankawerenga ulosi wa Yesaya koma sankamvetsa tanthauzo lake. Popeza ankafuna kudziwa zimene mneneriyu ankatanthauza, iye analola kuti Filipo amufotokozere. (Mac. 8:26-40) Si mdindo yekhayu amene anafunika kuthandizidwa kumvetsa Malemba. Tonsefe timafunikira kuthandizidwa, makamaka ana.
Baibulo limachenjeza kuti: “Utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” (Miy. 22:15) Ana amafunikira malangizo ndipo makolo ali ndi udindo wowaphunzitsa kukhala anthu a makhalidwe abwino ndiponso okonda Mulungu mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena komanso zimene timaphunzira kumisonkhano yachikhristu. Ana ali ndi ufulu wophunzitsidwa zimenezi. Kuyambira adakali aang’ono, ana amafunika kuthandizidwa kuti azikonda kwambiri Baibulo n’cholinga choti azikula mwauzimu n’kudzafika pokhala ‘anthu okhwima amene pogwiritsa ntchito luntha lawo la kuzindikira, aphunzitsa lunthalo kusiyanitsa choyenera ndi cholakwika.’—Aheb. 5:14.