Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kubatizidwa M’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera

Kubatizidwa M’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera

Kubatizidwa M’dzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera

“Choncho pitani mukapange ophunzira . . . , Muziwabatiza m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.”​—MAT. 28:19.

1, 2. (a) Kodi n’chiyani chinachitika ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E.? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambiri anabatizidwa?

PA Pentekosite mu 33 C.E., mzinda wa Yerusalemu unali utadzaza ndi anthu ochokera m’madera osiyanasiyana. Pa tsiku limeneli kunali mwambo wofunika kwambiri ndipo alendo ambiri anali nawo pamwambowu. Koma chinachake chapadera chinachitika, ndipo kenako mtumwi Petulo anakamba nkhani yokhudza mtima kwambiri. Anthu okwana 3,000, omwe anali Ayuda ndiponso ena otembenukira ku Chiyuda, anakhudzidwa ndi zimene anamva ndipo analapa n’kubatizidwa m’madzi. Motero chiwerengero cha anthu amene anali mumpingo wachikhristu, womwe unali utangoyamba kumene, chinawonjezeka kwambiri. (Mac. 2:41) N’kutheka kuti ku Yerusalemu kunali phokoso pa nthawi imene anthu amenewa ankabatizidwa m’maiwe kapena m’madamu.

2 N’chiyani chinachititsa kuti anthu ambiri chonchi abatizidwe? Tsiku lomweli, zimene tanenazi zisanachitike, “kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu.” M’chipinda chapamwamba cha nyumba ina munali ophunzira a Yesu okwana 120 ndipo anadzazidwa ndi mzimu woyera. Kenako, amuna ndi akazi oopa Mulungu anasonkhana ndipo anadabwa kumva ophunzirawo ‘akulankhula malilime osiyanasiyana.’ Atamva zimene Petulo ananena, kuphatikizapo mfundo zake zosapita m’mbali zokhudza imfa ya Yesu, anthu ambiri ‘analasidwa mtima.’ Kodi iwo anafunika kutani? Petulo anawauza kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Khristu. . . .  Pamenepo mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera.”​—Mac. 2:1-4, 36-38.

3. Kodi Ayuda ndiponso anthu otembenukira ku Chiyuda anafunika kuchita chiyani pa tsiku la Pentekoste?

3 Taganizirani za moyo wauzimu wa Ayuda ndiponso anthu otembenukira ku Chiyuda amene anamva mawu a Petulo. Iwo ankaona kuti Yehova ndi Mulungu wawo. Kuchokera m’Malemba a Chiheberi, iwo ankadziwanso za mzimu woyera womwe ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito yomwe anagwiritsa ntchito polenga zinthu ndiponso atalenga kale zinthu. (Gen. 1:2; Ower. 14:5, 6; 1 Sam. 10:6; Sal. 33:6) Koma pali zinthu zinanso zimene anafunika kuchita. Iwo ankafunika kudziwa kuti Yesu, yemwe ndi Mesiya, ndiye njira ya Mulungu yopulumutsira anthu. N’chifukwa chake Petulo anatsindika mfundo yakuti anafunika ‘kubatizidwa m’dzina la Yesu Khristu.’ Masiku angapo izi zisanachitike, Yesu ataukitsidwa analamula Petulo ndi anzake kuti azibatiza anthu “m’dzina la Atate, ndi la Mwana, ndi la mzimu woyera.” (Mat. 28:19, 20) Izi zinali zofunika kwambiri nthawi ya atumwi ndipo n’zofunikanso masiku ano. N’chifukwa chiyani tikutero?

M’dzina la Atate

4. Kodi panali kusintha kotani kokhudza anthu amene anali paubwenzi ndi Yehova?

4 Monga tanenera, anthu amene anamvetsera nkhani ya Petulo ankalambira Yehova ndipo anali naye kale paubwenzi. Iwo ankayesetsa kutsatira Chilamulo, n’chifukwa chake anachoka m’madera ena n’kubwera ku Yerusalemu. (Mac. 2:5-11) Koma pa nthawiyi, Mulungu anali atasintha njira yochitira zinthu ndi anthu. Iye anasiya kuona Ayuda ngati mtundu wake wapadera ndipo kutsatira Chilamulo sikukanawachititsanso kukhala ovomerezeka kwa Mulungu. (Mat. 21:43; Akol. 2:14) Ngati anthu amenewa ankafuna kuti akhalebe paubwenzi ndi Yehova anafunika kuchita zinthu zina.

5, 6. M’nthawi ya atumwi, kodi Ayuda ndiponso anthu otembenukira ku Chiyuda anafunika kuchita chiyani kuti akhale paubwenzi ndi Mulungu?

5 Iwo anafunika kuyang’ana kwa Yehova yemwe anawapatsa moyo. (Mac. 4:24) Anthu amene anali kutsatira zimene Petulo anafotokoza anayamba kuona kuti Yehova ndi Atate wokoma mtima. Iye anatumiza Mesiya kuti adzawapulumutse ndipo anali wofunitsitsa kukhululukira anthu onse, kuphatikizapo amene Petulo anawauza kuti: “Nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu, kuti Yesu ameneyu, amene inu munam’pachika, Mulungu anamuika kukhala Ambuye ndi Khristu.” Ndipotu anthu amene anatsatira mawu a Petulo anali ndi zifukwa zomveka zoyamikira Atate chifukwa cha zimene anachitira anthu amene ankafuna kukhala naye paubwenzi.​—Werengani Machitidwe 2:30-36.

6 Ndithudi, Ayuda ndiponso anthu otembenukira ku Chiyuda anayamba kuona kuti munthu angakhale paubwenzi ndi Yehova ngati atazindikira kuti Iye amapulumutsa anthu kudzera mwa Yesu. Tsopano mungamvetse chifukwa chake analapa machimo awo kuphatikizapo tchimo lawo lopha Yesu, kaya modziwa kapena mosadziwa. Mungamvetsenso chifukwa chake iwo “anapitiriza kulabadira zimene atumwiwo anali kuphunzitsa.” (Mac. 2:42) Iwo anali ndi mwayi ‘wofika ndi ufulu wa kulankhula ku mpando wachifumu wa kukoma mtima kwa m’chisomo.’​—Aheb. 4:16.

7. Kodi anthu ambiri masiku ano asintha motani maganizo awo pa nkhani ya Mulungu n’kubatizidwa m’dzina la Atate?

7 Masiku ano anthu osiyanasiyana aphunzira kuchokera m’Baibulo choonadi chonena za Yehova. (Yes. 2:2, 3) Ena sankakhulupirira kuti kuli Mulungu ndipo ena ankakhulupirira kuti Mulungu aliko, kungoti alibe chidwi ndi anthu. Koma anthu amenewa anayamba kukhulupirira kuti kuli Mlengi ndipo angathe kukhala naye paubwenzi. Ena ankalambira utatu kapena mafano osiyanasiyana. Koma anaphunzira kuti Yehova yekha ndiye Mulungu Wamphamvuyonse ndipo iwo tsopano amagwiritsa ntchito dzina lake. Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo imene Yesu anena kuti ophunzira ake ayenera kubatizidwa m’dzina la Atate.

8. Kodi anthu amene sankadziwa kuti anatengera uchimo kwa Adamu anayenera kuzindikira mfundo iti yokhudza Atate?

8 Iwo anaphunziranso kuti anatengera uchimo kwa Adamu. (Aroma 5:12) Kwa iwo mfundo imeneyi inali yatsopano ndipo anafunika kuivomereza. Anthu amenewa tingawayerekeze ndi munthu amene akudwala koma sakudziwa matenda ake. Nthawi zina iye angamamve kupweteka ndiponso angamakhale ndi zizindikiro zina. Koma ngati sanakayezetse, iye angamaganize kuti ali bwinobwino. Komatu zimenezi sizingakhale zoona. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:4.) Kodi angachite chiyani ngati atakayezetsa n’kumupeza ndi matenda? Chinthu cha nzeru chimene angachite ndi kulandira mankhwala oyenera amene angamuthandize pa matenda akewo. N’zimenenso anthu amene aphunzira choonadi chakuti anatengera uchimo achita. Iwo adzifufuza pogwiritsa ntchito Baibulo ndipo azindikira kuti Mulungu amapereka thandizo pa vuto lawolo. Ndithudi, anthu onse amene ndi otalikirana ndi Atate ayenera kupita kwa iye chifukwa ndi amene angawathandize.​—Aef. 4:17-19.

9. Kodi Yehova anachita chiyani kuti tithe kukhala naye paubwenzi?

9 Ngati munadzipereka kale kwa Yehova Mulungu ndipo ndinu Mkhristu wobatizidwa, mukudziwa kuti kukhala paubwenzi ndi iye ndi chinthu cha mtengo wapatali kwambiri. Mukudziwanso kuti Yehova ndi Atate wachikondi kwambiri. (Werengani Aroma 5:8.) Ngakhale kuti Adamu ndi Hava anachimwira Mulungu, iye anakonza zoti mbadwa zawo, kuphatikizapo ifeyo, tikhale naye paubwenzi wabwino. Kuti achite zimenezi, Mulungu anayenera kuona Mwana wake akuvutika mpaka kufa ndipo zimenezi zinamupweteka kwambiri. Kudziwa zimenezi, kumatithandiza kuzindikira ulamuliro wa Mulungu ndiponso kumvera malamulo ake chifukwa chomukonda. Ngati panopa simunadzipereke kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa, mfundo zimenezi ziyenera kukulimbikitsani kuti mutero.

M’dzina la Mwana

10, 11. (a) Kodi Yesu anakuchitirani zotani? (b) Kodi mumamva bwanji ndi mfundo yakuti Yesu anafa monga dipo?

10 Taganiziraninso zimene Petulo anauza khamu la anthu lija. Iye anatsindika kufunika kodziwa Yesu ndipo zimenezi n’zogwirizana ndi kubatizidwa “m’dzina . . . la Mwana.” Kodi n’chifukwa chiyani zimenezi zinali zofunika kalelo ndiponso masiku ano? Kudziwa Yesu ndiponso kubatizidwa m’dzina lake, kumatanthauza kuzindikira udindo wake wotithandiza kukhala paubwenzi ndi Mlengi. Yesu anayenera kupachikidwa pamtengo wozunzikirapo n’cholinga chakuti achotsere Ayuda temberero la Chilamulo. Koma imfa yake inalinso ndi phindu lina lalikulu. (Agal. 3:13) Iye anapereka nsembe ya dipo imene anthu onse ankafunikira. (Aef. 2:15, 16; Akol. 1:20; 1 Yoh. 2:1, 2) Kuti zimenezi zitheke, Yesu anachitiridwa zinthu zopanda chilungamo, kunyozedwa, kuzunzidwa ndiponso kuphedwa. Kodi mumayamikira kwambiri nsembe yakeyi? Tayerekezerani kuti ndinu mnyamata wa zaka 12 amene anakwera sitima yapamadzi ya Titanic mu 1912, yomwe inaomba madzi oundana n’kuyamba kumira. Ndiyeno, mukufuna kulumphira m’boti lopulumutsira anthu koma mukuona kuti ndi lodzaza. Kenako, munthu wina m’botilo akutsanzikana ndi mkazi wake, n’kulumphira mu sitima yomirayo kudzakunyamulani n’kukuikani m’botilo. Kodi mungamve bwanji? Munthu ameneyu mungamuyamikire kwambiri. Mungamvetse mmene mnyamata wina amene zimenezi zinamuchitikira anamvera. * Komatu Yesu anakuchitirani zambiri kuposa zimenezi. Iye anafa n’cholinga chakuti inuyo mupeze moyo osati kwa zaka zochepa chabe, koma kosatha.

11 Kodi munamva bwanji mutadziwa zimene Mwana wa Mulungu anakuchitirani? (Werengani 2 Akorinto 5:14, 15.) N’zodziwikiratu kuti munayamikira kwambiri. Zimenezi zinakulimbikitsani kuti mudzipereke kwa Mulungu ndi kuti ‘musamadzikhalire moyo wa inu eni, koma mukhalire moyo iye amene anakuferani.’ Kubatizidwa m’dzina la Mwana kumatanthauza kuzindikira zimene Yesu wakuchitirani ndiponso kuvomereza udindo wake monga “Mtumiki Wamkulu wa moyo.” (Mac. 3:15; 5:31) Poyamba simunali paubwenzi ndi Mlengi, choncho tingati munalibe chiyembekezo. Koma panopa muli paubwenzi ndi Atate chifukwa mumakhulupirira nsembe ya dipo ya Yesu Khristu ndiponso chifukwa chakuti munabatizidwa. (Aef. 2:12, 13) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Inu amene kale munali otalikirana naye ndi adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa, tsopano [Mulungu] wakuyanjaninso pogwiritsa ntchito thupi la nyama la [Yesu] kudzera mwa imfa yake. Wachita izi kuti akuperekeni pamaso pa iye mwini, muli opatulika ndi opanda chilema.”​—Akol. 1:21, 22.

12, 13. (a) Ngati munthu wina wakulakwirani, kodi muyenera kuchita chiyani pokumbukira kuti munabatizidwa m’dzina la Mwana? (b) Popeza ndinu Mkhristu wobatizidwa m’dzina la Yesu, kodi muli ndi udindo wotani?

12 Ngakhale kuti munabatizidwa m’dzina la Mwana, mukudziwa kuti mwachibadwa ndinu wochimwa. Kukumbukira zimenezi n’kothandiza tsiku lililonse. Mwachitsanzo, munthu wina akakulakwirani, kodi mumakumbukira kuti nonse awiri ndinu ochimwa? Awiri nonsenu mumafuna kuti Mulungu akukhululukireni, choncho nonse mufunikira kukhala okhululuka. (Maliko 11:25) Potsindika mfundo imeneyi, Yesu anapereka fanizo lonena za mbuye wina amene anakhululukira kapolo wake ngongole ya matalente 10,000 (kapena kuti madinari 60 miliyoni). Koma kenako, kapoloyo sanakhululukire kapolo mnzake yemwe anali naye ngongole ya madinari 100. Ndiyeno Yesu anamveketsa mfundo ya fanizoli kuti: Yehova sadzakhululukira munthu aliyense amene sakhululukira m’bale wake. (Mat. 18:23-35) Choncho, kubatizidwa m’dzina la Mwana kumatanthauza kuzindikira udindo wa Yesu. Kumatanthauzanso kuyesetsa kutsatira chitsanzo chake ndiponso zimene anaphunzitsa, kuphatikizapo kukhala wofunitsitsa kukhululukira ena.​—1 Pet. 2:21; 1 Yoh. 2:6.

13 Popeza ndife opanda ungwiro, sitingatsanzire Yesu bwinobwino. Koma chifukwa chakuti tinadzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse, timayesetsa kuti tizitsanzira Yesu mmene tingathere. Zimenezi zimafuna kuti tipitirize kuvula umunthu wakale ndi kuvala watsopano. (Werengani Aefeso 4:20-24.) Anthufe timayesetsa kutengera chitsanzo ndiponso makhalidwe a munthu amene timam’patsa ulemu. N’chimodzimodzinso ndi Khristu, timafuna kuphunzira kwa iye ndiponso kumutsanzira.

14. Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumazindikira udindo wa Yesu monga Mfumu yakumwamba?

14 Palinso njira ina imene mungasonyezere kuti mumadziwa tanthauzo la kubatizidwa m’dzina la Mwana. Mulungu ‘anaika zinthu zonse pansi pa mapazi a [Yesu], namuika mutu wa zinthu zonse kaamba ka mpingo.’ (Aef. 1:22) Choncho, muyenera kulemekeza njira imene Yesu akutsogolera anthu amene anadzipereka kwa Yehova. M’mipingo, Khristu akugwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro. Iye akugwiritsa ntchito makamaka akulu ndipo iwo anaikidwa kuti “awongolere oyerawo, . . . amange thupi la Khristu.” (Aef. 4:11, 12) Ngati munthu wopanda ungwiro walakwitsa chinachake, Yesu yemwe ndi Mfumu ya Ufumu wakumwamba angakonze zinthu pa nthawi yoyenera ndiponso m’njira yoyenera. Kodi inuyo mumakhulupirira zimenezi?

15. Kodi mudzapeza madalitso ati mukadzabatizidwa?

15 Komabe, pali anthu ena omwe mpaka pano sanadzipereke kwa Yehova n’kubatizidwa. Ngati inuyo simunabatizidwe, mutha kuona kuchokera pa zimene tafotokoza pamwambapa kuti kudziwa Mwana, ndiye chinthu chanzeru chimene mungachite posonyeza kuti ndinu woyamikira. Kubatizidwa m’dzina la Mwana kudzakuthandizani kuti mulandire madalitso ambiri.​—Werengani Yohane 10:9-11.

M’dzina la Mzimu Woyera

16, 17. Kodi kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera kumatanthauza chiyani kwa inu?

16 Kodi kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera kumatanthauza chiyani? Monga tafotokozera poyamba paja, anthu amene anamvetsera nkhani ya Petulo pa tsiku la Pentekosite, ankadziwa kale mzimu woyera. Ndipotu anaona ndi maso awo kuti Mulungu akupitirizabe kugwiritsa ntchito mzimu woyera. Petulo anali mmodzi mwa anthu amene “anadzazidwa ndi mzimu woyera [ndipo anayamba] kulankhula malilime osiyanasiyana.” (Mac. 2:4, 8) Sikuti nthawi zonse mawu akuti “m’dzina la,” amanena za munthu. Masiku ano, pali zinthu zambiri zimene zimachitidwa “m’dzina la boma” koma bomalo si munthu. Zimangotanthauza kuti zinthuzo zimachitidwa m’mphamvu ya boma. N’chimodzimodzinso ndi munthu amene wabatizidwa m’dzina la mzimu woyera. Iye amadziwa kuti mzimu woyera si munthu koma ndi mphamvu ya Mulungu yogwira ntchito. Ndipo ubatizo woterewu umatanthauza kuti munthuyo amazindikira ntchito ya mzimu woyera pokwaniritsa cholinga cha Mulungu.

17 Inu muyenera kuti mwadziwa zambiri zokhudza mzimu woyera chifukwa chophunzira Baibulo. Mwachitsanzo, mukudziwa kuti Baibulo linalembedwa mouziridwa ndi mzimu woyera. (2 Tim. 3:16) Mutayamba kupita patsogolo mwauzimu, muyenera kuti munamvetsa mfundo yakuti ‘Atate wakumwamba amapereka mowolowa manja mzimu woyera kwa amene akum’pempha,’ kuphatikizapo inuyo. (Luka 11:13) N’kuthekanso kuti pa moyo wanu mwaona mzimu woyera ukukuthandizani. Ngati panopa simunabatizidwe m’dzina la mzimu woyera, mawu a Yesu akuti Atate amapereka mzimu woyera akusonyeza kuti mukadzabatizidwa, mudzapeza madalitso ambiri chifukwa cholandira mzimuwo.

18. Kodi anthu amene anabatizidwa m’dzina la mzimu woyera amapeza madalitso otani?

18 N’zoonekeratu kuti masiku anonso Yehova akutsogolera mpingo wachikhristu kudzera mwa mzimu woyera. Mzimu umenewu umatithandizanso aliyense payekha tsiku lililonse. Popeza tinabatizidwa m’dzina la mzimu woyera, timazindikira ntchito imene mzimuwo umagwira pamoyo wathu ndiponso timakhala ndi makhalidwe amene angathandize kuti uzititsogolera. Mwina mungafunse kuti, kodi tingatani kuti tizichita zinthu zosonyeza kuti tinadzipereka kwa Yehova, ndipo kodi mzimu woyera umatithandiza bwanji pa mbali imeneyi? Tidzakambirana zimenezi m’nkhani yotsatira.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 10 Onani Galamukani! yachingelezi ya October 22, 1981, masamba 3 mpaka 8.

Kodi Mukukumbukira?

• Kodi kubatizidwa m’dzina la Atate kumatanthauza chiyani?

• Kodi kubatizidwa m’dzina la Mwana kumatanthauza chiyani?

• Kodi mungasonyeze bwanji kuti mumadziwa tanthauzo la kubatizidwa m’dzina la Atate ndi la Mwana?

• Kodi kubatizidwa m’dzina la mzimu woyera kumatanthauza chiyani?

[Mafunso]

[Zithunzi patsamba 10]

Pambuyo pa Pentekosite mu 33 C.E., kodi ophunzira atsopano anakhala paubwenzi wotani ndi Atate?

[Mawu a Chithunzi]

By permission of the Israel Museum, Jerusalem