Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Maliko ‘Anali Wofunika Potumikira’

Maliko ‘Anali Wofunika Potumikira’

Maliko ‘Anali Wofunika Potumikira’

MPINGO wa ku Antiokeya unakumana ndi mavuto ambiri koma mkangano wa pakati pa mtumwi Paulo ndi mtumwi Baranaba, inali nkhani ina. Atumwiwa ankakonzekera ulendo wawo waumishonale, koma posankha amene adzapite naye paulendowu “panabuka mkangano woopsa.” (Mac. 15:39) Zitatere, anasiyana ndipo aliyense analowera kwayekha. Iwo anakangana pa nkhani yokhudza Maliko yemwenso anali m’mishonale.

Kodi Maliko anali ndani? Kodi n’chiyani chinachititsa kuti atumwi awiriwa akangane pa nkhani yokhudza iyeyo? N’chifukwa chiyani aliyense sanalolere maganizo a mnzake? Kodi iwo anasintha maganizo awowa? Kodi mukuphunzira chiyani pa nkhani ya Maliko?

Ali Kwawo ku Yerusalemu

Maliko yemwe akuoneka kuti ankachokera kubanja lochita bwino la Chiyuda, ayenera kuti anakulira ku Yerusalemu. Nthawi yoyamba pamene timamva za iye akutchulidwa mwachindunji m’Baibulo, ndi m’mbiri ya mpingo wachikhristu woyambirira. Cha m’ma 44 C.E., mngelo wa Yehova atamasula Petulo mozizwitsa mu ndende ya Herode Agripa I, Petuloyo anapita “ku nyumba ya Mariya, mayi wake wa Yohane wotchedwanso Maliko. Kumeneko anthu ambiri anali atasonkhana pamodzi ndipo anali kupemphera.”​—Mac. 12:1-12. *

Choncho, zikuoneka kuti mpingo wa ku Yerusalemu unkasonkhana m’nyumba ya amayi ake a Maliko. Popeza “anthu ambiri” ankasonkhana m’nyumba imeneyi, ndiye kuti nyumbayi inali yaikulu. Mariya anali ndi mtsikana wa ntchito dzina lake Roda, amene anayankha Petulo atagogoda “chitseko cha pa chipata.” Mfundo zimenezi, zikusonyeza kuti Mariya sanali wosauka. Ndipo Baibulo limati inali nyumba yake osati ya mwamuna wake choncho n’kutheka kuti anali mayi wamasiye ndipo panthawiyi n’kuti Maliko ali wamng’ono.​—Mac. 12:13.

Maliko ayenera kuti anali m’gulu la anthu amene anasonkhana kuti apemphere. Ayeneranso kuti ankadziwana bwino ndi ophunzira a Yesu ndiponso anthu ena amene anaona zinthu zokhudza utumiki wa Yesu. Ndipotu mnyamata amene anafunda nsalu pafupi ndi atumwi, yemwe anathawa Yesu atamangidwa, ayenera kuti anali Maliko.​—Maliko 14:51, 52.

Udindo Wake Mumpingo

Maliko ankacheza ndi Akhristu okhwima mwauzimu, ndipo mosakayikira zimenezi zinamuthandiza kwambiri. Iye anakula mwauzimu ndipo akulu ankachita naye chidwi. Cha m’ma 46 C.E., Paulo ndi Baranaba ankachita “utumiki wopereka thandizo.” Iwo anachokera ku Antiokeya kupita ku Yerusalemu kuti akathandize abale amene anakhudzidwa ndi chilala, ndipo paulendowu anachita chidwi ndi Maliko. Pamene Paulo ndi Baranaba ankabwerera ku Antiokeya, anam’tenga Maliko.​—Mac. 11:27-30; 12:25.

Kwa munthu wongowerenga, angaganize kuti panalibe mgwirizano uliwonse pakati pa anthuwa, kusiyapo kuti onse anali Akhristu. Choncho, angaone kuti Paulo ndi Baranaba anatenga Maliko chifukwa cha luso lake basi. Koma kalata ina ya Paulo imasonyeza kuti Maliko anali msuwani wa Baranaba. (Akol. 4:10) Zimenezi zingatithandize kumvetsa zinthu zina zokhudza Maliko.

Patapita mwina chaka chimodzi, mzimu woyera unatsogolera Paulo ndi Baranaba kupita paulendo waumishonale. Iwo ananyamukira ku Antiokeya kupita ku Kupuro, ndipo Yohane Maliko anapita nawo “monga wowatumikira.” (Mac. 13:2-5) N’kutheka kuti Maliko ankagwira ntchito zina ndi zina n’cholinga chakuti atumwiwo aziika maganizo awo onse pa zinthu zauzimu.

Paulo, Baranaba ndi Maliko anayendayenda ku Kupuro akulalikira uthenga wabwino ndipo kenako anapita ku Asia Minor. Ali kumeneko Yohane Maliko anachita zinthu zimene zinakhumudwitsa Paulo. Nkhaniyi imati atatuwa atafika ku Pega, “Yohane anawasiya nabwerera ku Yerusalemu.” (Mac. 13:13) Baibulo silinena chifukwa chake iye anachita zimenezi.

Patapita zaka zingapo Paulo, Baranaba ndi Maliko anakumananso ku Antiokeya. Atumwi awiriwa ankakambirana za ulendo wachiwiri wa umishonale kuti akalimbikitse anthu amene anawapeza paulendo woyamba uja. Baranaba anafuna kuti atenge msuwani wake Maliko, koma Paulo sanagwirizane nazo chifukwa chakuti Maliko anawasiya paulendo woyamba. Izi n’zimene zinayambitsa mkangano umene tautchula poyamba paja. Baranaba anatenga Maliko ndipo anapita kukalalikira kwawo ku Kupuro pamene Paulo anapita ku Suriya. (Mac. 15:36-41) Apatu zikuonekeratu kuti Paulo ndi Baranaba anaona mosiyana zimene Maliko anachita.

Anayanjananso

N’zosakayikitsa kuti Maliko anamva chisoni kwambiri ndi zimene zinachitikazi. Koma iye anapitirizabe kutumikira mokhulupirika. Patapita zaka 11 kapena 12 kuchokera pamene anasiyana ndi Paulo, Maliko anatchulidwanso m’mbiri ya mpingo woyambirira wachikhristu. Kodi mukudziwa amene anali naye pa nthawiyi? Iye anali ndi Paulo yemwe uja.

Pa nthawi imene Paulo anali m’ndende ku Roma mu 60 mpaka 61 C.E., anatumiza makalata angapo amene panopa ndi mbali ya Malemba Oyera. M’kalata yake yopita kwa Akolose iye analemba kuti: ‘Arisitako mkaidi mnzanga akuti moni nonse. Komanso Maliko msuwani wa Baranaba, (amene ndinakulangizani kuti mum’landire nthawi iliyonse akadzafika kwa inu,) akuti moni. Okhawa ndiwo antchito anzanga pa za ufumu wa Mulungu, ndipo amenewa akhala ondithandiza ndi ondilimbikitsa.’​—Akol. 4:10, 11.

Apatu zinthu zinali zitasintha kwambiri. Poyamba Paulo sankamuona bwino Maliko, koma pa nthawiyi ankamuona kuti ndi wantchito mnzake wodalirika. Zikuoneka kuti Paulo anauza Akolose kuti Maliko akhoza kuwayendera. Ngati izi zinachitikadi, ndiye kuti Maliko anagwira ntchito ngati womuimira Paulo.

Kodi poyamba Paulo ankadana ndi Maliko? Kodi Maliko anasintha chifukwa cha chilango chimene anapatsidwa? Kapena kodi zonsezi zinachitika? Mulimonsemo, koma mfundo yoti Paulo ndi Maliko anayanjananso ikusonyeza kuti anthuwa anali okhwima mwauzimu. Iwo anaiwalako zakale ndipo anayambiranso kugwira ntchito limodzi. Ichitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa Akhristu amene anasemphana maganizo.

Maliko Anayenda M’madera Ambiri

Mukamawerenga za maulendo osiyanasiyana amene Maliko anayenda, mudzaona kuti iye anayenda m’madera ambiri. Kwawo kunali ku Yerusalemu, koma anapita ku Antiokeya ndipo atachoka kumeneku anayenda ulendo wapanyanja kupita ku Kupuro ndi ku Pega. Kenako anapita ku Roma. Ndipo ali kumeneko, Paulo anafuna kumutumiza ku Kolose. Komatu sizokhazi.

Mtumwi Petulo analemba kalata yake yoyamba cha m’ma 62 mpaka 64 C.E. M’kalatayo iye anati: “Iye amene ali ku Babulo, . . . komanso mwana wanga Maliko, akupereka moni.” (1 Pet. 5:13) Motero Maliko anapita ku Babulo kukatumikira limodzi ndi mtumwi amene zaka zambiri m’mbuyomo ankachita nawo misonkhano yachikhristu m’nyumba ya amayi ake.

Paulendo wachiwiri umene Paulo anali kundende ku Roma cha m’ma 65 C.E., analembera Timoteyo kalata yomuitana ndipo panthawiyi n’kuti Timoteyoyo ali ku Efeso. M’kalatayi Paulo ananenanso kuti: “Pobwera utengenso Maliko.” (2 Tim. 4:11) Choncho, panthawiyi n’kuti Maliko ali ku Efeso. Ndipo n’zosakayikitsa kuti potsatira pempho la Paulo, Maliko anapitadi ku Roma limodzi ndi Timoteyo. Ngakhale kuti mayendedwe anali ovuta nthawi imeneyo, Maliko anadzipereka kuyenda maulendo onsewa.

Anapatsidwa Udindo Wina Wapadera

Udindo wina wapadera umene Maliko anali nawo unali wolemba Uthenga Wabwino mouziridwa ndi Yehova. Ngakhale kuti dzina la munthu amene analemba buku lachiwiri la Uthenga Wabwino silitchulidwa, zolemba zakale zimasonyeza kuti Maliko ndi amene analemba bukuli ndipo anamva zambiri kwa Petulo. Ndipotu Petulo anaona zochitika zonse zimene Maliko analemba.

Anthu amene anafufuza bwino Uthenga Wabwino wa Maliko, amakhulupirira kuti Maliko analembera anthu akunja, ndipo powathandiza kumvetsa ankafotokoza miyambo yachiyuda. (Maliko 7:3; 14:12; 15:42) Maliko anamasulira mawu a Chialamu, omwe akapanda kuwamasulira anthu amene sanali Ayuda sakanawamva. (Maliko 3:17; 5:41; 7:11, 34; 15:22, 34) Anagwiritsa ntchito mawu ambiri a Chilatini ndiponso anafotokoza mawu ena a Chigiriki pogwiritsa ntchito mawu a Chilatini. Zonsezi zikugwirizana ndi zolemba zakale zimene zimasonyeza kuti Maliko analemba Uthenga wake ali ku Roma.

“Wofunika Ponditumikira”

Pamene anali ku Roma, Maliko anachitanso zinthu zina kuwonjezera pa kulemba Uthenga Wabwino. Musaiwale kuti Paulo anauza Timoteyo kuti: “Pobwera utengenso Maliko.” Pofotokoza chifukwa chake, iye anati: “Pakuti iye ndi wofunika ponditumikira.”​—2 Tim. 4:11.

Pa Malemba amene amatchula Maliko mogwirizana ndi nthawi imene zinthu zinachitika, lemba limeneli ndi lomaliza ndipo limatiuza zambiri zokhudza Maliko. Pa ntchito zonse zimene anagwira, palibe paliponse m’Baibulo pamene pamasonyeza kuti anali mtumwi, mtsogoleri kapena mneneri. Koma iye anali mtumiki kutanthauza kuti ankatumikira ena. Panthawiyi n’kuti Paulo atatsala pang’ono kumwalira ndipo thandizo la Maliko linali la panthawi yake.

Tikaganizira nkhani zonse zokhudza Maliko, timaona kuti iye anali munthu wachangu popititsa patsogolo ntchito yolalikira uthenga wabwino kumadera osiyanasiyana. Ndipo iye ankasangalala kutumikira ena. Apatu titha kuona kuti Maliko anapatsidwa udindo wosiyanasiyana chifukwa chakuti sanafooke.

Mofanana ndi Maliko, atumiki a Mulungufe tiyenera kukhala ndi mtima wofunitsitsa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. Enafe tingathe kupita kumadera kapena mayiko ena n’cholinga chopititsa patsogolo uthenga wabwino ngati mmene anachitira Maliko. Ngakhale kuti ambirife sitingathe kusamuka, tonsefe tikhoza kutsanzira Maliko m’njira ina yofunika. Iye anayesetsa kutumikira abale ake achikhristu ndipo ifenso tiyenera kuyesetsa kuthandiza Akhristu anzathu kuti apitirize kutumikira Mulungu. Tikamatero Yehova adzapitirizabe kutidalitsa.​—Miy. 3:27; 10:22; Agal. 6:2.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 5 M’nthawi ya Maliko, anthu ankakonda kukhala ndi dzina lachiwiri la Chiheberi kapena lochokera ku chilankhulo china. Dzina la Maliko la Chiheberi linali Yohanan kapena kuti Yohane m’Chichewa. Ndipo dzina la bambo ake la Chilatini linali Marcus kapena kuti Maliko.​—Mac. 12:25.

[Mapu/​Chithunzi patsamba 8, 9]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mizinda Ina Kumene Maliko Anapita

Roma

Efeso

Kolose

Antiokeya (wa ku Suriya)

Pega

Kupuro

NYANJA YA MEDITERRANEAN

Yerusalemu

Babulo