Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Achinyamata, Khalani ndi Mtima Wokonda Kwambiri Kutumikira Yehova

Achinyamata, Khalani ndi Mtima Wokonda Kwambiri Kutumikira Yehova

Achinyamata, Khalani ndi Mtima Wokonda Kwambiri Kutumikira Yehova

“Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.”​—MLAL. 12:1.

1. Kodi ana m’nthawi ya Isiraeli anauzidwa kuchita chiyani?

PAFUPIFUPI zaka 3,500 zapitazo, Mose yemwe anali mneneri wa Yehova anauza ansembe ndi amuna akulu a Isiraeli kuti: “Sonkhanitsani anthu, amuna ndi akazi ndi ana aang’ono . . .  kuti amve, ndi kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu, ndi kusamalira kuchita mawu onse a chilamulo ichi.” (Deut. 31:12) Onani kuti amuna, akazi, ndiponso ana anauzidwa kuti azipezeka pamisonkhano yolambira Yehova. N’zochititsa chidwi kuti ngakhale ana anali pakati pa anthu amene anauzidwa kuti azimvera, kuphunzira ndiponso kutsatira malangizo a Yehova.

2. Kodi Yehova anasonyeza bwanji kuti ankaganizira achinyamata m’nthawi ya atumwi?

2 M’nthawi ya atumwi, Yehova ankasonyezanso kuti amaganizira achinyamata. Mwachitsanzo, anauzira mtumwi Paulo kulembanso malangizo okhudza achinyamata m’makalata amene anatumiza kumipingo. (Werengani Aefeso 6:1; Akolose 3:20.) Akhristu achinyamata amene anagwiritsa ntchito malangizo amenewa ankayamikira kwambiri Atate wawo wakumwamba ndipo anadalitsidwa.

3. Kodi achinyamata masiku ano amasonyeza bwanji kuti akufuna kutumikira Mulungu?

3 Kodi masiku anonso, achinyamata amauzidwa kuti azisonkhana ndi cholinga choti alambire Yehova? Inde! Anthu a Mulungu onse amasangalala kuona kuti achinyamata ambiri amene akutumikira Mulungu akutsatira malangizo a Paulo akuti: “Tiyeni tiganizirane wina ndi mnzake, kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga chilili chizolowezi kwa ena, koma tilimbikitsane wina ndi mnzake. Tiwonjezeredi kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheb. 10:24, 25) Ana ambiri amalalikiranso limodzi ndi makolo awo uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Mat. 24:14) Posonyeza kuti amakonda Yehova ndi mtima wonse, chaka chilichonse achinyamata ambiri amabatizidwa ndipo amadalitsidwa chifukwa chokhala ophunzira a Khristu.​—Mat. 16:24; Maliko 10:29, 30.

Yambani Panopo

4. Kodi ndi liti pamene achinyamata ayenera kuyamba kutumikira Mulungu?

4 Lemba la Mlaliki 12:1 limati: “Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.” Kodi achinyamatanu muyenera kukhala ndi zaka zingati kuti muyambe kulambira ndi kutumikira Yehova ngati mmene lembali likunenera? Malemba satchula zaka zimene munthu ayenera kukhala nazo. Choncho, musalephere kumvera ndi kutumikira Yehova poganiza kuti ndinu mwana. Kaya muli ndi zaka zingati, yambani panopo kuchita zimene lembali likunena.

5. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti apite patsogolo mwauzimu?

5 Ambiri a inu, makolo anu akukuthandizani kuti mupite patsogolo mwauzimu. Choncho, muli ngati Timoteyo wotchulidwa m’Baibulo. Kuyambira ali wakhanda, anaphunzitsidwa malemba opatulika ndi amayi ake a Yunike, ndiponso agogo ake a Loisi. (2 Tim. 3:14, 15) N’kutheka kuti inunso, makolo anu akukuthandizani mwa kuphunzira nanu Baibulo, kupemphera nanu, kupita nanu ku misonkhano ya mpingo ndiponso ikuluikulu. Amakuthandizaninso mwa kupita nanu mu utumiki wa kumunda. Ndithudi, Yehova wapatsa makolo anu udindo waukulu kwambiri wokuphunzitsani njira Zake. Kodi mumayamikira kuti makolo anu amakukondani ndiponso kukuganizirani?​—Miy. 23:22.

6. (a) Malinga ndi lemba la Salmo 110:3, kodi ndi kulambira kotani kumene kumasangalatsa Yehova? (b) Kodi tikambirana chiyani?

6 Koma Yehova amafuna kuti mukamakula, muzichita khama ‘kuzindikira chimene chili chifuniro cha Mulungu, chabwino ndi chovomerezeka ndi changwiro,’ ngati mmene Timoteyo anachitira. (Aroma 12:2) Mukamatero, muzichita nawo zinthu zosiyanasiyana mumpingo chifukwa chakuti muli ndi mtima wofunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu osati chifukwa chakuti n’zimene makolo anu akufuna. Yehova adzasangalala mukamamutumikira mwa kufuna kwanu. (Sal. 110:3) Ndiyeno mungachite chiyani kuti mukhale ndi mtima wokonda kwambiri kumvera Yehova ndiponso kutsatira malangizo ake? Tikambirana njira zitatu zofunika zimene zingakuthandizeni kuchita zimenezi. Njira zake ndi izi: kuphunzira Baibulo, kupemphera, ndiponso kukhala ndi makhalidwe abwino. Tiyeni tione njira iliyonse payokha.

M’dziweni Bwino Yehova

7. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chotani pa nkhani yophunzira Malemba, ndipo n’chiyani chinam’thandiza kuchita zimenezi?

7 Njira yoyamba imene mungasonyezere kuti mukufuna muzikonda kwambiri kutumikira Yehova, ndiyo kuwerenga Baibulo tsiku lililonse. Kuwerenga Mawu a Mulungu nthawi zonse kungakuthandizeni kukwaniritsa zosowa zanu zauzimu ndiponso kudziwa bwino Baibulo. (Mat. 5:3) Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi Yesu. Pa nthawi ina, ali ndi zaka 12, makolo ake anamupeza m’kachisi “atakhala pakati pa aphunzitsi. Anali kuwamvetsera ndi kuwafunsa mafunso.” (Luka 2:44-46) Kuyambira ali mwana, Yesu anali ndi mtima wofuna kumvetsa Malemba. Kodi n’chiyani chinam’thandiza kukhala ndi mtima umenewu? N’zoonekeratu kuti makolo ake, Mariya ndi Yosefe, ndi amene anam’thandiza kwambiri. Iwo anali atumiki a Mulungu ndipo anaphunzitsa Yesu malangizo a Mulungu kuyambira ali mwana.​—Mat. 1:18-20; Luka 2:41, 51.

8. (a) Kodi makolo ayenera kuyamba liti kuphunzitsa ana awo kukonda Mawu a Mulungu? (b) Fotokozani chitsanzo chosonyeza ubwino wophunzitsa mwana kuyambira ali wakhanda.

8 Masiku anonso, makolo oopa Mulungu amadziwa ubwino wothandiza ana awo kudziwa choonadi cha m’Baibulo kuyambira ali akhanda. (Deut. 6:6-9) Izi n’zimene mlongo wina dzina lake Rubi anachita mwana wake woyamba Joseph, atangobadwa. Tsiku lililonse ankamuwerengera Bukhu langa la Nkhani za Baibulo. Pamene ankakula, ankamuthandiza kuloweza malemba osiyanasiyana. Kodi Joseph anapindula ndi maphunziro amenewa? Iye atangodziwa kulankhula, ankatha kufotokoza nkhani zambiri za m’Baibulo. Ndipo ali ndi zaka 5, anakamba nkhani yake yoyamba m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu.

9. N’chifukwa chiyani kuwerenga Baibulo ndi kusinkhasinkha zimene mwawerenga kuli kofunika?

9 Achinyamatanu kuti mupite patsogolo mwauzimu, yesetsani kukhala ndi chizolowezi chowerenga Baibulo tsiku lililonse pamene muli achinyamata ndiponso mukadzakula. (Sal. 71:17) N’chifukwa chiyani kuwerenga Baibulo kungakuthandizeni kupita patsogolo mwauzimu? Onani zimene Yesu ananena popemphera kwa Atate ake. Iye anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona.” (Yoh. 17:3) Ndithudi, mukamaphunzira zambiri za Yehova, mudzamudziwa bwino ndipo mudzayamba kum’konda kwambiri. (Aheb. 11:27) Choncho, nthawi iliyonse mukamawerenga Baibulo, yesetsani kuphunzira zambiri zokhudza Yehova. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhani imeneyi ikundiphunzitsa kuti Yehova ndi Mulungu wotani? Kodi nkhani ya m’Baibulo imeneyi imasonyeza bwanji kuti Mulungu amandikonda ndiponso amandiganizira?’ Kusinkhasinkha mafunso amenewa kudzakuthandizani kudziwa mmene Yehova amaganizira, mmene amaonera zinthu ndiponso zimene amafuna kuti muzichita. (Werengani Miyambo 2:1-5.) Mofanana ndi Timoteyo yemwenso anali wachinyamata, ‘mudzakhulupirira mutakhutira’ ndi zimene mwaphunzira m’Malemba, ndipo mudzakhala ndi mtima wofunitsitsa kulambira Yehova​—2 Tim. 3:14.

Kodi Pemphero Lingakuthandizeni Bwanji Kuti Muzikonda Kwambiri Yehova?

10, 11. Kodi pemphero lingakuthandizeni bwanji kuti mukhale ndi mtima wokonda kwambiri kutumikira Mulungu?

10 Njira yachiwiri imene ingakuthandizeni kuti mukhale ndi mtima wokonda kwambiri kutumikira Yehova, ndiyo kupemphera. Lemba la Salmo 65:2, limati: “Wakumva pemphero Inu, zamoyo zonse zidzadza kwa Inu.” Ngakhale nthawi imene Mulungu anachita pangano ndi Isiraeli, alendo omwe ankabwera kukachisi wa Yehova ankapemphera kwa Iye. (1 Maf. 8:41, 42) Mulungu alibe tsankhu. Anthu amene amamvera malamulo ake, amadziwa kuti Mulungu amayankha mapemphero awo. (Miy. 15:8) Ndithudi, “zamoyo zonse” zimene zatchulidwa palembali zikuphatikizapo achinyamatanu.

11 Monga mukudziwira, ubwenzi uliwonse umalimba ngati anthuwo amalankhulana bwino. N’kutheka kuti mumakonda kuuzako mnzanu wapamtima maganizo anu, zimene zikukudetsani nkhawa ndiponso mmene mukumvera. Mofananamo, tikamapemphera mochokera pansi pamtima, timakhala tikulankhula ndi Mlengi wathu Wamkulu. (Afil. 4:6, 7) Muzilankhula ndi Yehova momasuka ngati mmene mungalankhulire ndi kholo limene limakukondani kapena mnzanu wapamtima. Ndipotu, pali kugwirizana kwambiri pakati pa zimene mumanena m’mapemphero anu, ndi mmene mumaonera Yehova. Mudzaona kuti ubwenzi wanu ndi Yehova ukakhala wolimba, mapemphero anu amakhala ochokera mumtima.

12. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mapemphero ochokera mumtima amaphatikizapo zambiri? (b) N’chiyani chingakuthandizeni kuzindikira kuti Yehova ali pafupi nanu?

12 Koma dziwani kuti pemphero lochokera mumtima limaphatikizapo zambiri osati kungogwiritsa ntchito mawu abwino. Limakhudzanso mmene mukumvera. Mukamapemphera sonyezani kuti mumakonda Yehova, mumamulemekeza ndiponso kuti mumamudalira. Mukaona kuti Yehova wayankha mapemphero anu, mumazindikira kuti “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye.” (Sal. 145:18) Yehova adzakhala bwenzi lanu lapamtima ndipo adzakuthandizani kukaniza Mdyerekezi ndiponso kusankha bwino zochita pamoyo wanu.​—Werengani Yakobe 4:7, 8.

13. (a) Kodi kukhala paubwenzi ndi Mulungu kunamuthandiza bwanji mlongo wina? (b) Kodi kukhala paubwenzi ndi Mulungu kungakuthandizeni bwanji kuti musamangotengera zofuna za anzanu?

13 Taonani mmene kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova kunalimbikitsira mtsikana wina dzina lake Cherie. Ali kusekondale, anapata mphoto chifukwa anakhoza bwino maphunziro ake ndiponso ankachita bwino masewera. Atakhoza mayeso, anapatsidwa mwayi wolipiriridwa maphunziro apamwamba. Cherie anati: “Zinali zovuta kukana, chifukwa akochi ndi ana a sukulu anzanga ankandiumiriza kuti ndivomere.” Komabe iye anadziwa kuti maphunziro apamwamba akanamuonongera nthawi yambiri, chifukwa bwenzi akungokhalira kuwerenga ndi kukonzekera masewera osapeza mpata wotumikira Yehova. Ndiye kodi iye anatani? Cherie anati: “Nditapemphera kwa Yehova, ndinakana mwayiwo ndipo ndinayamba upainiya wokhazikika.” Panopa Cherie wakhala akuchita upainiya kwa zaka 5. Iye anati: “Sindikunong’oneza bondo ngakhale pang’ono. Ndimasangalala podziwa kuti Yehova amakondwera ndi zimene ndinasankha. N’zoona kuti munthu akaika Ufumu wa Mulungu patsogolo, Yehova amamuonjezera zina zonse.”​—Mat. 6:33.

Khalidwe Lanu Labwino Limasonyeza Kuti Ndinu Woyera Mtima

14. N’chifukwa chiyani khalidwe lanu labwino ndi lofunika kwambiri pamaso pa Yehova?

14 Njira yachitatu imene mungasonyezere kuti mukutumikira Yehova mwa kufuna kwanu, ndiyo kukhala ndi makhalidwe abwino. Yehova amadalitsa achinyamata amene ali ndi khalidwe labwino. (Werengani Salmo 24:3-5.) Samueli ali wachinyamata sanatengere khalidwe lachiwerewere la ana a Mkulu wa Ansembe Eli. Yehova ndiponso anthu ena ankaona khalidwe labwino la Samueli. Baibulo limati: “Ndipo mwanayo Samueli anakulakula, ndipo Yehova ndi anthu omwe anam’komera mtima.”​—1 Sam. 2:26.

15. N’chifukwa chiyani mumayesetsa kukhalabe ndi khalidwe labwino?

15 Tikukhala m’dziko limene malinga ndi zimene Paulo analemba, anthu ndi odzikonda, odzikweza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, owopsa, otukumuka chifukwa cha kunyada ndiponso okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu. (2 Tim. 3:1-5) Popeza tikukhala m’dziko loipa limeneli, zingakhale zovuta kuti mukhale chitsanzo chabwino pa nkhani ya makhalidwe. Koma nthawi iliyonse imene mwapewa kuchita zoipa, mumasonyeza kuti pa nkhani ya ulamuliro muli kumbali ya Yehova. (Yobu 2:3, 4) Mumakhalanso osangalala chifukwa chodziwa kuti mwachita zinthu mogwirizana ndi pempho la Yehova lakuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.” (Miy. 27:11) Ndipo kudziwa kuti Yehova akusangalala ndi zimene mukuchita, kudzakuthandizani kukhalabe ndi mtima wokonda kumutumikira.

16. Kodi mlongo wina anachita zotani zimene zinasangalatsa mtima wa Yehova?

16 Mlongo wina dzina lake Carol, ankayesetsa kutsatira mfundo za m’Baibulo ali wachinyamata kusukulu, ndipo anthu ena ankaona khalidwe lake labwino. Koma kodi chinkachitika ndi chiyani? Anzake a kusukulu ankamunyoza chifukwa chikumbumtima chake chophunzitsidwa Baibulo sichinkamulola kuchita nawo maholide ndiponso miyambo yosonyeza kukonda dziko. Nthawi zina, iye ankagwiritsa ntchito mwayi umenewu kufotokozera anthu ena zimene amakhulupirira. Patapita zaka zambiri, Carol analandira khadi kuchokera kwa munthu wina yemwe anali naye kalasi limodzi. Iye analemba kuti: “Ndakhala ndikukufufuza kwa nthawi yaitali kuti ndikuyamikire. Tinkaona kuti unali Mkhristu wachinyamata wa khalidwe labwino komanso wolimba mtima pa nkhani yosachita nawo maholide. Unali wa Mboni za Yehova woyamba kukumana naye.” Khalidwe labwino la Carol linachititsa chidwi kwambiri mnzakeyu moti kenako anayamba kuphunzira Baibulo. M’khadi limene anatumizira Carol, mnzakeyu analembamo kuti wakhala Mboni yobatizidwa kwa zaka zoposa 40. Mofanana ndi Carol, achinyamatanu amene mumalimba mtima kutsatira mfundo za m’Baibulo, mungachititse kuti anthu a mitima yabwino adziwe Yehova.

Achinyamata Akutamanda Yehova

17, 18. (a) Kodi mumamva bwanji mukaona achinyamata mumpingo wanu? (b) Kodi achinyamata oopa Mulungu ali ndi tsogolo lotani?

17 Ife tonse m’gulu la Yehova padziko lonse, tikusangalala kuona achinyamata ambiri amene akuchita nawo mwachangu zinthu zokhudza kulambira koona. Zinthu monga kuwerenga Baibulo tsiku lililonse, kupemphera, ndiponso kukhala ndi khalidwe logwirizana ndi zimene Mulungu amafuna, n’zimene zathandiza achinyamata amenewa kukhalabe ndi mtima wokonda kulambira Yehova. Achinyamata achitsanzo chabwino amenewa, amasangalatsa makolo awo ndiponso anthu onse a Yehova.​—Miy. 23:24, 25.

18 M’tsogolomu, achinyamata okhulupirika adzakhala m’gulu la anthu amene adzapulumuke n’kulowa m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. (Chiv. 7:9, 14) M’dziko limenelo, adzapeza madalitso osaneneka ndipo adzapitiriza kuyamikira Yehova komanso kum’tamanda mpaka kalekale.​—Sal. 148:12, 13.

Kodi Mungafotokoze?

• Kodi achinyamata masiku ano, angachite zotani pa nkhani ya kulambira koona?

• N’chifukwa chiyani kusinkhasinkha n’kofunika kuti kuwerenga Baibulo kukhale kopindulitsa?

• Kodi kupemphera kungakuthandizeni bwanji kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova?

• Kodi chimachitika n’chiyani ngati Mkhristu ali ndi khalidwe labwino?

[Mafunso]

[Chithunzi patsamba 5]

Kodi muli ndi chizolowezi chowerenga Baibulo tsiku lililonse?